Mphatso yachikoka—Kodi Munthu Atamandidwe Kapena Mulungu Alemekezedwe?
“WOLAMULIRA ayenera kupambana anthu ake osati kokha mwakukhala wabwino kusiyana ndi iwowo, komanso kuti ayenera kuwakopa,” analemba motero Xenophon, kazembe wotchuka wachigiriki. Lerolino, anthu ambiri akanatcha “kuwakopa” kumeneko chikoka.
Zoonadi, si anthu onse olamulira amene ali ndi chikoka. Koma amene ali nacho amagwiritsira ntchito luso lawo kuti achititse anthu kukhala odzipereka ndi kuwalima pamsana kuti akwaniritse zolinga za iwo eni. Mwinamwake Adolf Hitler angakhale chitsanzo chotchuka kwambiri cha posachedwapa. “[Mu 1933] kwa Ajeremani ambiri Hitler anali—kapena mosakhalitsa akanakhala—mtsogoleri wachikoka,” analemba tero William L. Shirer m’buku lake lakuti The Rise and Fall of the Third Reich. “Anthu mwakhungu anali kudzamtsatira, ngati kuti anali ndi malingaliro aumulungu, kwa zaka zotsatira khumi ndi ziŵiri zamavuto.”
Mbiri ya chipembedzo ilinso ndi atsogoleri achikoka ambiri amene anasonkhezera anthu kuti akhale odzipereka kwa iwo koma anawabweretsera tsoka owatsatirawo. “Yang’anirani, asasokeretse inu munthu,” anachenjeza motero Yesu, “pakuti ambiri adzafika m’dzina langa, nadzanena, Ine ndine Kristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.” (Mateyu 24:4, 5) A Kristu onyenga achikoka sanangokhalako m’zaka za zana loyamba zokha. Mu ma 1970, Jim Jones anati iye anali “mesiya wa chipembedzo cha People’s Temple.” Anafotokozedwa kukhala “munthu wa tchalitchi wachikoka” wokhala ndi “mphamvu yachilendo pa anthu,” ndipo mu 1978 anachititsa anthu ochuluka kwambiri m’mbiri ya anthu kudzipha.a
Mwachionekere, chikoka chingakhale mphatso yoopsa. Komabe, Baibulo limanena za mphatso ina, kapena mphatso zina, yochokera kwa Mulungu imene aliyense ali nayo kaamba ka ubwino wa anthu onse. Liwu lachigiriki la mphatso imeneyi ndi khaʹri·sma, ndipo limapezeka nthaŵi 17 m’Baibulo. Wophunzira wina wachigiriki anatanthauzira liwuli kukhala ‘mphatso yaulere ndi yosamuyenera munthu, chinthu chimene munthu anapatsidwa wosachigwirira ntchito ndi wosachiyenerera, chobwera mwa chisomo cha Mulungu ndipo choti sichikanapezeka mwa zoyesayesa za munthu mwini.’
Motero kunena mwa Malemba, khaʹri·sma ndi mphatso yolandiridwa, ndi thandizo la chisomo cha Mulungu. Kodi zina za mphatsozi zimene mokoma mtima Mulungu watipatsa ndi ziti? Nanga tingazigwiritsire ntchito motani kuti timtamande nazo? Tiyeni tipende zitatu za mphatso za chisomozi.
Moyo Wosatha
Mosakayika, mphatso yaikulu kwambiri pa zonse ndi mphatso ya moyo wosatha. Paulo analembera ku mpingo wa ku Roma kuti: “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso [khaʹri·sma] yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Kuli koyenera kudziŵa kuti “mphotho” (imfa) ndi chimene tinagwirirapo ntchito, ngakhale kuti simofuna, mwa kubadwa kwathu ochimwa. Mosiyana, moyo wosatha umene Mulungu amapereka ndi chinthu chosatiyenerera kotheratu chimene sitikanatha kupeza mwa kuyenera kwa ife eni.
Mphatso ya moyo wosatha iyenera kukondedwa ndi kugaŵiridwa kwa ena. Tingathandize anthu kudziŵa Yehova, kumtumikira ndipo motero kuyanjidwa ndi mphatso ya moyo wosatha. Lemba la Chivumbulutso 22:17 limati: “Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.”
Kodi ena tingawatsogolere bwanji kumadzi opatsa moyo amenewa? Kwenikweni ndi mwa kugwiritsira ntchito bwino Baibulo mu utumiki wathu. M’malo ena anthu sakondadi kuŵerenga kapena kuganiza za zinthu zauzimu; komabe, nthaŵi zonse pali mipata ‘yogalamutsira khutu’ la munthu wina. (Yesaya 50:4) Pambaliyi, tingakhale ndi chidaliro m’mphamvu yosonkhezera ya Baibulo, “pakuti mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita,” (Ahebri 4:12) Kaya ikhale nzeru ya Baibulo yogwira ntchito, chitonthozo ndi chiyembekezo chimene limapereka, kaya kulongosola kwake chifuno cha moyo, Mawu a Mulungu angakhudze mtima ndi kupangitsa anthu kuyamba kuyenda panjira ya kumoyo.—2 Timoteo 3:16, 17.
Mabuku ozikidwa pa Baibulo angatithandizenso kunena kuti “Idzani!” Mneneri Yesaya ananeneratu kuti m’nthaŵi ino ya mdima wauzimu, ‘Yehova adzawala’ pa anthu ake. (Yesaya 60:2, NW) Mabuku ofalitsidwa ndi Watch Tower Society amasonyeza dalitso la Yehova limeneli, ndipo chaka chilichonse amatsogolera zikwi za anthu kwa Yehova, Magwero a kuunikiridwa kwauzimu. M’masamba awo onse palibe anthu amene amakwezedwa. Monga mmene mawu oyamba a Nsanja ya Olonda amalongosolera, “chifuno cha Nsanja ya Olonda ndicho kulemekeza Yehova Mulungu monga Mfumu Ambuye wa chilengedwe chonse. . . . Imalimbikitsa chikhulupiriro mwa Mfumu ya Mulungu yolamulira tsopano, Yesu Kristu, amene mwazi wake wokhetsedwa ukutsegula njira yakuti anthu apeze moyo wamuyaya.”
Mtumiki wina wa nthaŵi zonse wachikristu, amene kwa zaka zambiri wakhala ndi chipambano mu utumiki wake, ananenapo za phindu la Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pa kuthandiza anthu kuyandikira kwa Mulungu kuti: “Pamene ophunzira anga a Baibulo ayamba kuŵerenga ndi kusangalala ndi Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, amapita patsogolo mofulumira. Ndimaona kuti magaziniwa ndi ofunika kwambiri pa kuthandiza anthu kudziŵa Yehova.”
Maudindo a Utumiki
Timoteo anali wophunzira wachikristu amene anapatsidwa mphatso ina imene inali yofunikira chisamaliro chapadera. Mtumwi Paulo anamuuza kuti: “Usanyalapse mphatsoyo [khaʹri·sma] ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.” (1 Timoteo 4:14) Kodi mphatsoyi inali chiyani? Inali kuikidwa kwa Timoteo kukhala woyang’anira woyendayenda, udindo wa utumiki umene anafunikira kuusamalira. Pandime yomweyo, Paulo anachenjeza Timoteo kuti: “Usamalire kuŵerenga, kuchenjeza, kulangiza. Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.”—1 Timoteo 4:13, 16.
Akulu lerolino ayeneranso kusamalira maudindo awo autumiki. Monga momwe Paulo anasonyezera, njira imodzi imene angachitire zimenezi ndi mwa ‘kudzipenyerera ndi chiphunzitso chawo.’ M’malo motsatira atsogoleri achikoka adzikoli, iwo amachititsa anthu kuyang’ana kwa Mulungu, osati kwa iwo eni. Yesu, Chitsanzo chawo, anali mphunzitsi wotchuka amene mosakayikira anali ndi umunthu wachikoka, koma modzichepetsa anapereka ulemu kwa Atate ake. “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine,” iye anatero.—Yohane 5:41; 7:16.
Yesu analemekeza Atate ake a kumwamba mwa kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu ngati maziko a chiphunzitso chake. (Mateyu 19:4-6; 22:31, 32, 37-40) Mofananamo Paulo anagogomezera kufunika kwakuti oyang’anira ‘agwire mawu okhulupirika monga mwa chiphunzitso.’ (Tito 1:9) Mwa kuzika nkhani zawo zolimba pa Malemba, akulu adzakhaladi akunena mofanana ndi Yesu kuti: “Mawu amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha.”—Yohane 14:10.
Kodi akulu ‘angagwire mawu okhulupirika’ bwanji? Mwa kuzika nkhani ndi mbali zawo za pamisonkhano pa Mawu a Mulungu, akumalongosola ndi kugogomezera malemba amene akugwiritsira ntchito. Mafanizo oseketsa kapena njerengo, makamaka pamene zichitidwa mopambanitsa, zingapangitse omvetsera kusangalatsidwa ndi luso la mkambiyo m’malo moika maganizo awo pa Mawu a Mulungu. Mosiyana, mavesi a Baibulo ndi amene adzafika pamtima ndi kusonkhezera omvera. (Salmo 19:7-9; 119:40; yerekezerani ndi Luka 24:32.) Nkhani zoterozo zimapangitsa anthu kusaganizira kwenikweni za mkambiyo ndipo zimapereka ulemu waukulu kwa Mulungu.
Akulu angakhalenso aphunzitsi ogwira mtima kwambiri mwa kuphunzira kwa ena. Monga mmene Paulo anathandizira Timoteo, chomwechonso mkulu angathandize mkulu mnzake. “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” (Miyambo 27:17; Afilipi 2:3) Akulu amapindula pakugaŵana maganizo ndi malingaliro. Mkulu wina amene anali atangoikidwa kumene anafotokoza kuti: “Mkulu wozoloŵera ntchitoyi anayesetsa kundisonyeza mmene amakonzekerera nkhani yapoyera. M’kukonzekera kwake, anali kukonza mafunso osonkhezera kuganiza, mafanizo, zitsanzo, kapena zokumana nazo zifupizifupi, ndiponso Malemba amene anali atafufuza mosamalitsa. Ndaphunzira kwa iye kukhala wosintha m’kakambidwe kanga ka nkhani m’malo mogwiritsa ntchito njira imodzimodzi yomwe singamasangalatse.”
Tonse amene tikusangalala ndi maudindo a utumiki, kaya ndife akulu, atumiki otumikira, kapena apainiya, tiyenera kusamalira mphatso yathu. Atatsala pang’ono kufa, Paulo anakumbutsa Timoteo kuti ‘akoleze mphatso [khaʹri·sma] ya Mulungu, inali mwa iye,’ imene kwa Timoteo inaphatikizapo mphatso yapadera ya mzimu. (2 Timoteo 1:6) M’nyumba za Aisrayeli, kaŵirikaŵiri moto unali chabe wa makala. Kunali kotheka ‘kuukoleza’ kuti uyake ndi kukhala wotentha kwambiri. Motero tikulimbikitsidwa kuika mtima ndi nyonga zathu pa maudindo athu, kukoleza ngati moto mphatso yauzimu iliyonse imene taikiziridwa.
Mphatso Zauzimu Zofunika Kugaŵana
Chikondi cha Paulo pa abale ake a ku Roma chinamkakamiza kulemba kuti: “Ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagaŵire kwa inu mtulo [“mphatso”, NW] [khaʹri·sma] wina wauzimu, kuti inu mukhazikike; ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse aŵiri, chanu ndi changa.” (Aroma 1:11, 12) Paulo anaona luso lathu la kulimbikitsa chikhulupiriro cha ena mwa kukamba nawo ngati mphatso yauzimu. Kusinthana kwa mphatso zauzimu zoterozo kungachirikize chikhulupiriro ndi kulimbikitsana.
Zimenezi ndi zofunikadi. M’dongosolo loipali limene tikukhalamo, tonsefe timalefulidwa mwa njira zosiyanasiyana. Komabe, kulimbikitsana kwa nthaŵi zonse kungatithandize kupirira. Nkhani ya kusinthana—ponse paŵiri kupatsa ndi kulandira—njofunika kuti tikhalebe olimba mwauzimu. Zoonadi, tonsefe timafuna chilimbikitso nthaŵi ndi nthaŵi, komatu tingathenso kumangirirana.
Ngati tikhala tcheru pa kuona okhulupirira anzathu amene apsinjika mtima, ‘tingathe ife kutonthoza iwo okhala m’nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.’ (2 Akorinto 1:3-5) Liwu lachigiriki la chitonthozo (pa·raʹkle·sis) limatanthauza kuti “kukokera munthu wina pambali pako.” Ngati tikhala pafupi ndi mbale kapena mlongo wathu kuti timthandize pamene kuli kofunika, mosakayikira ifenso tidzachirikizidwa mwachikondinso pamene tavutika.—Mlaliki 4:9, 10; yerekezerani ndi Machitidwe 9:36-41.
Maulendo aubusa achikondi a akulu ndi opindulitsanso kwambiri. Ngakhale kuti maulendo ena amakhala okapereka uphungu wa m’Malemba pa nkhani yofunikira chisamaliro, maulendo aubusa ochuluka amakhala opereka chilimbikitso, ‘kutonthoza mitima.’ (Akolose 2:2) Pamene oyang’anira apanga maulendo olimbikitsa chikhulupiriro oterowo, iwo amakhaladi akugaŵira mphatso yauzimu. Monga Paulo, iwo adzaona kuti kupatsa kwa mtundu wapadera kumeneku ndi kofupa, ndipo adzakulitsa ‘kulakalaka’ abale awo.—Aroma 1:11.
Zinali choncho ndi mkulu wina ku Spain, amene anasimba zotsatirazi: “Ricardo, mnyamata wazaka 11, sanali kusangalatsidwa kwenikweni ndi misonkhano ngakhalenso zochitika zonse za mpingo. Choncho ndinapempha chilolezo kwa makolo ake kuti ndikacheze naye, anandilola mofunitsitsa. Anali kukhala kumapiri pamtunda woyenda ola limodzi pa galimoto kuchokera kunyumba kwanga. Ricardo mwachionekere anasangalala ndi chidwi chimene ndinamsonyeza, kotero kuti anachitapo kanthu nthaŵi yomweyo. Mosakhalitsa anakhala wofalitsa wosabatizidwa ndipo anali wachangu mumpingo. Manyazi ake anatha ndipo tsopano anali waubwenzi kwambiri. Anthu ambiri mumpingowo anali kufunsa kuti: ‘Kodi chinamchitikira Ricardo nchiyani?’ Anali kuoneka ngati kuti akumuona kwa nthaŵi yoyamba. Ndikaganiza za ulendo waubusa wofunika umenewo, ndimamva kuti ndapindula kupambana Ricardo. Akamaloŵa m’Nyunba ya Ufumu, amakhala wosangalala, ndipo amathamanga kudzandipatsa moni. Zakhaladi zosangalatsa kumuona akupita patsogolo mwauzimu.”
Mosakayikira, maulendo aubusa, onga ngati uwu, amadalitsidwa kwambiri. Maulendo oterowo ndi ogwirizana ndi kudandaulira kwa Yesu kuti: “Ŵeta nkhosa zanga.” (Yohane 21:16) Indedi, akulu si ndiwo okha amene angagaŵire mphatso zauzimu zoterozo. Aliyense mumpingo angafulumize ena ku chikondano ndi ntchito zabwino. (Ahebri 10:23, 24) Monga mmene anthu omwe amakwera mapiri amamangiriridwa pamodzi kuchingwe chokwerera, ifenso ndife olunzanitsidwa ndi zomangira zauzimu. Mosapeweka, zimene timachita ndi kunena zimakhudzanso anthu ena. Mawu odula kapena kusuliza kungaweyese zomangira zimene zimatigwirizanitsa. (Aefeso 4:29; Yakobo 3:8) Kumbali ina, mawu abwino olimbikitsa ndi chithandizo cha chikondi zingathandize abale athu kuthetsa mavuto awo. M’njira imeneyi tidzagaŵana mphatso zauzimu zokhala ndi phindu lokhalitsa.—Miyambo 12:25.
Kusonyeza Mokulirapo Ulemu wa Mulungu
Nzachionekere kuti Mkristu aliyense ali ndi mphatso yachikoka. Tapatsidwa chiyembekezo chamtengo wapatali cha moyo wosatha. Tilinso ndi mphatso zauzimu zimene tingagaŵane ndi ena. Ndipo tingayese kusonkhezera ena kuti akhale ndi zolinga zoyenera. Ena ali ndi mphatso zowonjezereka za maudindo autumiki. Mphatso zonsezi ndi umboni wa chisomo cha Mulungu. Ndipo popeza kuti mphatso iliyonse imene tingakhale nayo tailandira kuchokera kwa Mulungu, palibiretu chifukwa choti ife tizidzikuzira.—1 Akorinto 4:7.
Monga Akristu, ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzagwiritsira ntchito mphatso yachikoka imene ndingakhale nayo kuti ipereke ulemu kwa Yehova, Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro”? (Yakobo 1:17) Kodi ndidzatsanzira Yesu ndi kutumikira ena mogwirizana ndi maluso anga ndi mikhalidwe yanga?’
Mtumwi Petro analongosola za udindo wathu pankhaniyi motere: “Monga yense walandira mphatso [khaʹri·sma], mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu; akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m’zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Kristu.”—1 Petro 4:10, 11.
[Mawu a M’munsi]
a Anthu 913 anafa, kuphatikizapo Jim Jones iyemwini.
[Mawu a Chithunzi patsamba 23]
Corbis-Bettmann
UPI/Corbis-Bettmann