Ana ‘Pa Ngongole’—Kodi Kachitidweko Kali Kanzeru Motani?
“MONGA mmene udziŵira, Daniel, ndiri ndi ana ambiri,” anatero msuwani wa Daniel. “Chotero ndalingalira za kuwagawira ena a iwo pakati pa achibale.” Akumaloza kwa mtsikana wachichepere yemwe anabwera naye, msuwaniyo ananena kuti: “Uyu ndi wako.”
“Zikomo,” anatero Daniel. Komabe, chamkatikati, iye anabuula. Iye anali ndi ana okwanira a iyemwini ndipo sanafune kapena kukhumba owonjezereka. Koma mogwirizana ndi mwambo wa kumaloko, kukana choperekacho kukanalingaliridwa kukhala chimo lalikulu kwambiri—losalingalirika! Daniel tsopano anali ndi mwana wina wamkazi wowonjezereka woti asamalire.
M’maiko ambiri otukuka kumene, makamaka mu Africa, sichiri chachilendo kwa makolo kubwereketsa ana awo kwa achibale kapena mabwenzi kwa miyezi, zaka—ndipo ntahŵi zina kosatha. Mwambowo ungamvekere kukhala wachilendo ku makutu a Kumadzulo, koma mwa lamulo kuli kofanana ndi kachitidwe kotumiza ana ku sukulu zogonera komweko kapena ku misasa ya nyengo ya chirimwe yaitali. Nchiyani, ngakhale ndi tero, chimene chiri kumbuyo kwa mwambo wa kubwereketsa ana? Kodi iwo uli kachitidwe kanzeru?
Chifukwa Chimene Amabwereketsera Ana Awo
Ngakhale kuti mapindu a mwambo akusintha, kwa munthu wa ku Africa, ana sali chuma chotheratu cha makolo. M’malomwake, iwo ali a banja lofutukulidwa. Azakhali, amalume, agogo, ndi ena amalingaliridwa kukhala ndi kuyenera ndi ulamuliro pa achichepere. Monga mmene mwambi umodzi wa Kumadzulo kwa Africa umanenera: “Munthu mmodzi amabala, koma ambiri amasamalira mwanayo.”
Monga chotulukapo chake, pamene mikhalidwe ya ngozi ibuka, monga ngati imfa ya makolo a mwanayo, achibale amakhala okonzekera ndi ofunitsitsa kutenga wachichepere wamasiyeyo. Chifukwa choyambirira chobwereketsera ana kwa achibale, ngakhale kuli tero, chiri kaŵirikaŵiri cha zachuma, Pamene banja liri losauka ndipo ana ali ambiri, makolo angadzimve kuti mmodzi kapena ochulukirapo a achicheperewo angapindule mwa kukhala ndi achibale omwe ali olemerako. Iwo amalingalira kuti wachibale akachipeza icho kukhala chopepuka kukwaniritsa ndalama zolipirira sukulu, zovala, mankhawala, ndi chakudya. Chotero sikuli kusoweka kwa chikondi chaukholo koma, m’malomwake, chikhumbo cha kupereka zabwino koposa kaamba ka ana chimene chimasonkhezera makolo ena kuwasungitsa iwo kwa ena.
Chifukwa china chiri chikhumbo kaamba ka anawo kupeza maphunziro abwino. Mwinamwake sukulu yapafupi kwambiri iri kutali kwambiri ndi nyumba ya banjalo. Popeza chingakhale chovuta kapena chosatheka kwa banja lonselo kusamuka, makolowo angalingalire kuti chingakhale chabwino kwambiri kutumiza mwana wawo kwa achibale omwe amakhala pafupi ndi sukuluyo.
Achibale kaŵirikaŵiri amakhala achimwemwe kulandira ana amenewa. Pakati pa zinthu zina, kamwa ina yowonjezereka yofunikira kuidyetsa imatanthauzanso manja ena aŵiri wonjezereka ogwira ntichto ya panyumba. Ndipo makolo nathaŵi zina amathandiza ndi zowonongedwazo mwa kutumiza ndalama kapena chukudya.
Nsonga Zoyenera Kuzilingalira
Pamene ku kwakuti chiri chowona kuti pangakhale mwaŵi wina wa maphunziro ndi zakuthupi m’kubwereketsa mwana kwa ena, pali nsonga zina zimene ziyenera kulingaliridwa mosamalitsa. Kaamba ka chinthu chimodzi, ndimotani mmene mwanyo akasinthira ku omuchinjiriza ake atsopano, ndipo ndimotani mmene iwo akasinthira kwa mwanayo? Ntahŵi zina makonzedwe oterowo amagwira bwino ntchito, ndipo makolo atsopanowo amayambitsa unansi wamphamvu, wachikondi ndi mwana wawo wolera. Mwachitsanzo, mkulu mmodzi Wachikristu mu Sierra Leone anatega mwana wamwamuna wamasiye wa mbale wake. Pamene anafunsidwa zaka zingapo pambuyo pake ponena za mwana wake wolera, iye anayankha kuti: “Sindimalingalira Desmond kukhala mwana wolera—iye ali mwana wanga. Iye ali thupi langa ndi mwazi wanga.”
Si onse, ngakhale kuli tero, amene amawona ana awo olera m’njira imeneyi. Kuti tichitire chitsanzo, mu mzinda umodzi wa Kumadzulo kwa Africa panali kuwukira. Zipolopolo zinali kuuluka. “Fulumira!” anafuula tero mkazi wa m’nyumba mmodzi kwa achichepere ake aŵiri: “Arthur, bisala kunsi kwa kama! Iwe, Sorie, yang’ana pazenera ndi kutiwuza zimene zikuchitika!” Arthur anali mwana wake wobala, koma Sorie, mwana wolera, kapena wosungidwa.
Chiri chofala kaamba ka kuchita kokondera kuperekedwa kwa mwana wanu wobala m’banja. Monga chotulukapo chake, mapindu a kuthupi okhumbiridwawo kaŵirikaŵiri amalephera. Kaŵirikaŵiri ana osungidwa amagwiritsidwa ntchito mopambanitsa, kumanidwa maphunziro, ndipo amakhala omalizira pa mzera kulandira zovala limodzinso ndi chisamaliro cha mankhwala ndi mano. M’mishonale mmodzi yemwe wagwira ntchito mu Africa kwa zake zoposa 23 ananena kuti: “Ana osungidwa ali chifupifupi nthaŵi zonse ana a gulu lachiŵiri.”
Nsonga ina yoyenera kulingalira: Pamene mwana achoka panyumba, nthaŵi zonse pamakhala kuvutika kwa malingaliro. Malingaliro ndi mitima ya ana iri yozindikira ndi yosindikiza. Kuchokera ku ubwana iwo amakhumba chitonthozo ndi chisungiko cha unansi wathithithi ndi makolo awo. Kwa ana kuchotsedwa m’nyumba zawo ndi kupita kukakhala ndi alendo kotheratu kungakhale kovuta mokulira.
Mu Sierra Leone mkazi wotchedwa Comfort anatumizidwa kukakhala ndi azakhali ake pa msinkhu wa zaka zisanu ndi zinayi. Iye akukumbukira kuti: “Zaka zimene ndinatha ndiri kutali ndi nyumba zinali zovuta kwambiri. Ndinalisowa banja langa mokulira—makamaka abale ndi alongo anga. Chinali ngati kuti anadidula ine kuchokera kumene ndinayenera kukhala ndi kundiika ine kumene sindinayenera kukhala. Ngakhale kuti azakhali anga anachita nane bwino koposa, sindinathe kulankhula ndi iwo momasuka monga mmene ndikanachitira kwa amayi anga enieni . . . Mosasamala kanthu ndi mmene mkhalidwe wathu ungakhalire wovuta, sindidzatumiza ana naga kukakhala ndi wina wake.”
Francis, munthu wa Kumadzulo kwa Africa yemwenso anakula m’chisamaliro choleredwa, ali ndi ichi chonena: “Ndiri wachisoni kuti sindinali wokhoza kukulitsa unansi wathithithi ndi amayi anga enieni. Mwa njira inayake, ndimadzimva kuti tonse aŵirife tinaphonya chinachake cha mtengo wapatali.”
Zosowa Zauzimu Zimenezo Zofunika Koposa
Nsonga yofunika koposa ya zonse, ngakhale kuli tero, iri ubwino wauzimu wa mwanayo. Ndipo Mulungu mu nzeru yake amatsogoza kuti makolo iwo eni asamalire kaamba ka zosowa zauzimu za ana awo. Akumalankhula kwa makolo Achiisrayeli, uphungu wa Mulungu unali wakuti: “Ndipo mawu awa ndikuuzani lero azikhala pa mtima panu; ndipo mudziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu ndi poyenda inu pa njira ndi pogona inu pansi ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6,7) Mtumwi Paulo mofananamo analangiza atate Achikristu: “Musakwiyitse ana anu, komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].”—Aefeso 6:4.
Koma kodi ndimotani mmene mwana angaleredwere “m’maleredwe ndi m’chilangizo cha Yehova” ngati iye watumizidwa kukakhala ndi achibale osakhulupirira? Chotero, chiri kukhala ndi kawonedwe kapafupi chotani nanga, kupereka zikondwerero zauzimu za mwana kaamba ka mapindu a zakuthupi kapena maphunziro!
Bwanji ponena za kutumiza mwana kukakhala ndi okhulupirira anzathu? Pamene kuli kwakuti chiri chabwinoko kuposa kuwabwereketsa iwo kwa osakhulupirira, m’njira zambiri ichi nachonso chiri chosakhumbirika. Mwanayo angafunikirebe kuchita ndi ziwongolero zokulira za mayanjano, malingaliro, ndi maganizo. Ana ena akhala ochita tondovi kapena agwera mu msampha wa kupulupudza ndi mayanjano oipa. Ena ataya chiyamikiro chonse kaamba ka zinthu zauzimu.
Monga mmene makolo amadziŵira bwino, chimafunikira luso, kuleza mtima, ndi nthaŵi yochuluka kulowetsa mwa mwana chikondi kaamba ka Yehova. Ngati ntchito yoteroyo iri yovuta kwa makolo achibadwa a mwanayo, omwe amamudziŵa iye wamwamuna kapena wamkazi mwathithithi kuyambira pa kubadwa, ndi chovuta chotani nanga mmene chingakhalire kwa okwatirana omwe akalera mwana yemwe sali wawo weniweni! Popeza moyo wosatha wa mwanayo ungakhale pa ngozi, makolo ayenera kulingalirapo mosamalitsa ndipo mwa pemphera kuti kaya kubwereketsa mwana kuli koyenerera ngozizo.
Mosasamala kanthu za chimenecho, makolo Achikristu ayenera kugamulapo kwa iwo eni mmene akachitira ndi uphungu wa 1 Timoteo 5:8: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye ndipo aipa koposa wakhulupirira.” Ngati iwo mwaumwini sali okhoza kupereka kaamba ka zinthu zakuthupi za mwanayo, ayenera kuwona ku icho kuti zosowa zauzimu za mwanayo zikukwaniritsidwa m’njira yabwino koposa yothekera pansi pa mikhalidweyo.
Wamasalmo analemba kuti: “Ana ali mphatso yochokera kwa Mulungu; iwo ali mphoto yake.” (Salmo 127:3, The Living Bible) Chotero nyadirani achichepere anu, ndipo asungeni iwo pafupi ndi inu. Akondeni iwo, ndipo aloleni iwo kukukondani. Athandizeni iwo kukhala amuna ndi akazi auzimu, popeza kuchita tero kukatulukamo m’dalitso lawo losatha. Mwinamwake mungakhale okhoza kunena, monga mmene ananenera Yohane ponena za ana ake auzimu: “Ndiribe chimwemwe choposa ichi chakuti ndimva za ana anga kuti alinkuyenda m’chowonadi.”—3 Yohane 4.