‘Khalani Amphamvu Ndipo Limbikani Mtima’
“Limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.”—YOHANE 16:33.
1. Poganizira adani amphamvu amene Aisrayeli anali kudzakumana nawo ku Kanani, kodi anawalimbikitsa chiyani?
AISRAYELI atatsala pang’ono kuwoloka mtsinje wa Yordano kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawauza kuti: “Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuwopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu.” Ndiyeno Mose anaitana Yoswa, amene anadzatsogolera Aisrayeli kuloŵa mu Kanani, ndipo anamuuzanso payekha langizo loti alimbike mtima. (Deuteronomo 31:6, 7) Patapita nthaŵi, Yehova mwini analimbikitsa Yoswa kuti: “Khala wamphamvu, nulimbike mtima . . . Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri.” (Yoswa 1:6, 7, 9) Mawu amenewo anali a panthaŵi yake. Aisrayeli anafunika kulimba mtima kuti alimbane ndi adani amphamvu amene anali kudzakumana nawo tsidya lina la Yordano.
2. Kodi zinthu zili bwanji kwa ife masiku ano, ndipo tikufunika chiyani?
2 Masiku ano, Akristu oona atsala pang’ono kuwoloka kuloŵa m’dziko latsopano lolonjezedwa ndipo, mofanana ndi Yoswa, afunika kulimba mtima. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 7:14) Komabe, mmene zinthu zilili kwa ife, n’zosiyana ndi mmene zinalili kwa Yoswa. Yoswa anamenya nkhondo ndi malupanga ndi mikondo. Ife tikumenya nkhondo yauzimu ndipo sitigwiritsa ntchito zida zenizeni za nkhondo. (Yesaya 2:2-4; Aefeso 6:11-17) Ndiponso, Yoswa anafunika kumenya nkhondo zoopsa kwambiri ngakhale ataloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Koma ife tikumenya nkhondo zathu zoopsa kwambiri pakalipano, tisanaloŵe m’dziko latsopano. Tiyeni tione zochitika zina zimene zingafune kuti tilimbike mtima.
N’chifukwa Chiyani Tifunika Kulimba?
3. Kodi Baibulo limavumbula chiyani za mdani wathu wamkulu?
3 Mtumwi Yohane analemba kuti: “Tidziŵa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mawu ameneŵa akusonyeza chifukwa chachikulu chimene Akristu afunikira kulimba kuti akhalebe ndi chikhulupiriro. Mkristu akapitiriza kukhulupirika, pa mlingo winawake amakhala akugonjetsa Satana Mdyerekezi. Motero, Satana amakhala ngati “mkango wobuma,” kuyesetsa kuopseza ndi kulikwira Akristu okhulupirika. (1 Petro 5:8) Inde, iye amamenya nkhondo ndi Akristu odzozedwa ndi anzawo. (Chivumbulutso 12:17) Pankhondo imeneyi, iye amagwiritsa ntchito anthu amene modziŵa kapena mosadziŵa amakwaniritsa zolinga zake. Pamafunika kulimba mtima kuti tichirimike polimbana ndi Satana ndi atumiki ake onse.
4. Kodi Yesu anachenjeza kuti chiyani, koma kodi Akristu oona asonyeza khalidwe lotani?
4 Popeza Yesu anadziŵa kuti Satana ndi atumiki ake adzatsutsa mwamphamvu uthenga wabwino, Iye anachenjeza otsatira ake kuti: “[Anthu] adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:9) Mawu amenewo anakwaniritsidwadi m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, ndipo akukwaniritsidwanso masiku ano. Ndipotu, chizunzo chimene Mboni za Yehova zina za masiku ano zakumana nacho chakhala chankhanza monga mmene zinalili zizunzo zakale. Komabe, Akristu oona amalimba mtima pokumana ndi mayesero oterowo. Iwo amadziŵa kuti “kuopa anthu kutchera msampha,” ndipo iwo safuna kukodwa mu msampha.—Miyambo 29:25.
5, 6. (a) Kodi ndi zochitika ziti zimene zimafuna kuti tilimbe mtima? (b) Kodi Akristu okhulupirika amachita bwanji kulimba mtima kwawo kukayesedwa?
5 Palinso zovuta zina kuwonjezera pa chizunzo zimene zimafuna kuti tilimbe mtima. Kwa ena, kulankhula kwa anthu achilendo za uthenga wabwino n’kovuta. Kulimba mtima kwa ana a kusukulu kumayesedwa akauzidwa kunena pamtima mawu osonyeza kukhulupirika ku dziko kapena olemekeza mbendera. Popeza mawu amenewo kwenikweni ndi mawu achipembedzo, ana achikristu molimba mtima asankha kuchita zomwe zingasangalatse Mulungu, ndipo zochita zawo zabwino zimenezi zimasangalatsa kwambiri.
6 Timafunikanso kulimba mtima adani athu akamagwiritsa ntchito mawailesi, ma TV ndi manyuzipepala kufalitsa nkhani zoipa zokhudza atumiki a Mulungu kapena akamayesa kupondereza kulambira koona mwa kukonza ‘chovuta kukhala lamulo.’ (Salmo 94:20) Mwachitsanzo, kodi tiyenera kukhudzidwa bwanji manyuzipepala, mawailesi, ndi ma TV akamapotoza nkhani zokhudza Mboni za Yehova kapena kunena bodza lenileni? Kodi tiyenera kudabwa nazo? Ayi. Timayembekezera zinthu ngati zimenezo. (Salmo 109:2) Ndipo sitidabwa ngati ena akhulupirira nkhani zabodza kapena zopotoza zimene zafalitsidwazo, popeza “wachibwana akhulupirira mawu onse.” (Miyambo 14:15) Koma Akristu okhulupirika sakhulupirira nkhani iliyonse imene yanenedwa yokhudza abale awo, ndipo salola kuti nkhani zoipa zimene zafalitsidwa ziwachititse kusapita kumisonkhano yachikristu, kubwerera m’mbuyo mu utumiki wakumunda, kapena kufooketsa chikhulupiriro chawo. M’malo mwake, iwo ‘amadzitsimikizira okha monga atumiki a Mulungu . . . mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; monga [malinga ndi otsutsa] osocheretsa, angakhale [zoona zake n’zakuti] ali oona.’—2 Akorinto 6:4, 8.
7. Kodi ndi mafunso odzipenda ati amene tingadzifunse?
7 Paulo polembera Timoteo anati: “Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu . . . Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu.” (2 Timoteo 1:7, 8; Marko 8:38) Pamene taŵerenga mawu ameneŵa, tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimachita manyazi ndi chikhulupiriro changa, kapena ndine wolimba mtima? Kodi kumene ndimagwira ntchito (kapena kusukulu), kodi ndimauza anthu kumeneko kuti ndine Mboni ya Yehova, kapena kodi ndimabisa? Kodi ndimachita manyazi kukhala wosiyana ndi anthu ena, kapena ndimanyadira kuoneka wosiyana ndi anthuwo chifukwa cha ubale wanga ndi Yehova?’ Ngati munthu akuchita mantha kulalikira uthenga wabwino kapena kuchita mantha kukhala ndi chikhulupiriro chimene ena akuona ngati n’chotsalira, ayenera kukumbukira langizo la Yehova kwa Yoswa lakuti: “Khala wamphamvu, nulimbike mtima.” Osaiwala kuti chofunika kwambiri si mmene anthu amene timagwira nawo ntchito kapena anzathu a kusukulu akuganizira koma mmene Yehova ndi Yesu Kristu amaonera zinthu.—Agalatiya 1:10.
Mmene Tingakhalire Olimba Mtima
8, 9. (a) Kodi nthaŵi ina kulimba mtima kwa Akristu oyambirira kunayesedwa bwanji? (b) Kodi Petro ndi Yohane anachita bwanji ataopsezedwa, ndipo kodi n’chiyani chinawachitikira iwo ndi abale awo?
8 Kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima kuti tikhulupirikebe m’nthaŵi zovuta zino? Chabwino, kodi Akristu oyambirira anatani kuti akhale olimba mtima? Taganizirani zimene zinachitika pamene akulu a nsembe ndi akuluakulu a ku Yerusalemu anauza Petro ndi Yohane kuti asiye kulalikira m’dzina la Yesu. Ophunzirawo anakana ndipo anaopsezedwa kenako n’kuwamasula. Zitatero, iwo anadza kwa abale awo, ndipo onse anapemphera kuti: “Ambuye, penyani mawu awo akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse.” (Machitidwe 4:13-29) Poyankha, Yehova anawalimbikitsa ndi mzimu woyera ndipo, monga mmene patapita nthaŵi atsogoleri achiyuda anachitira umboni, iwo ‘anadzadza Yerusalemu’ ndi chiphunzitso chawo.—Machitidwe 5:28.
9 Tiyeni tione zimene zinachitika panthaŵi imeneyo. Ophunzirawo ataopsezedwa ndi atsogoleri achiyuda, iwo sanaganize zosiya ntchito yawoyo chifukwa cha zimenezi. M’malo mwake, ophunzirawo anapempherera kulimba mtima kuti apitirizebe kulalikira. Ndiyeno anayesetsa kuchita zimene anapemphererazo, ndipo Yehova anawalimbikitsa ndi mzimu wake. Zimene zinawachitikirazi zikusonyeza kuti zimene Paulo analemba patapita zaka zingapo m’nkhani yosiyana ndi imeneyi zimagwira ntchito kwa Akristu akamazunzidwa. Iye anati: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”—Afilipi 4:13.
10. Kodi zimene zinachitikira Yeremiya zingathandize bwanji anthu omwe ndi amanyazi mwachibadwa?
10 Tsono tiyerekezere kuti munthuyo ndi wamanyazi mwachibadwa. Kodi iye angatumikirebe Yehova molimba mtima pamene ena akumutsutsa? Kwabasi! Kumbukirani zimene Yeremiya anachita pamene Yehova anamusankha kukhala mneneri. Iye, popeza anali wachinyamata, anati: “Ndili mwana.” Mwachionekere, iye anadziona kuti sangakwanitse. Komabe, Yehova anamulimbikitsa ndi mawu akuti: “Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza. Usaope nkhope zawo; chifukwa ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe.” (Yeremiya 1:6-10) Yeremiya anadalira Yehova, ndipo zotsatira zake zinali zakuti mwa mphamvu za Yehova, iye anagonjetsa kukayikakayika kwake ndipo anakhala mboni yolimba mtima yodziŵika kwambiri mu Israyeli.
11. N’chiyani chimathandiza Akristu masiku ano kukhala ngati Yeremiya?
11 Akristu odzozedwa masiku ano ali ndi ntchito yofanana ndi ya Yeremiya, ndipo mothandizidwa ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” iwo akupitiriza kulengeza zolinga za Yehova, ngakhale kuti akukumana ndi anthu osalabadira, akunyozedwa ndiponso akuzunzidwa. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Iwo amalimbikitsidwa ndi zimene Yehova anauza Yeremiya kuti: “Usaope.” Iwo saiwala kuti alamulidwa ndi Mulungu ndipo akulalikira uthenga wake.—2 Akorinto 2:17.
Zitsanzo za Kulimba Mtima Zofunika Kuzitsanzira
12. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chabwino chotani cha kulimba mtima, ndipo analimbikitsa bwanji otsatira ake?
12 Tingapeze thandizo pa kuyesetsa kwathu kukhala olimba mtima ngati tisinkhasinkha zitsanzo za anthu ena amene, mofanana ndi Yeremiya, analimba mtima. (Salmo 77:12) Mwachitsanzo, tikamapenda utumiki wa Yesu, timachita chidwi ndi kulimba mtima kwake pamene anayesedwa ndi Satana ndiponso pamene anatsutsidwa mwamphamvu ndi atsogoleri achiyuda. (Luka 4:1-13; 20:19-47) Mwa mphamvu za Yehova, Yesu sanagwedere, ndipo atatsala pang’ono kumwalira, anauza ophunzira ake kuti: “M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.” (Yohane 16:33; 17:16) Ngati ophunzira a Yesu akanatsatira chitsanzo chake, iwonso akanalilaka dziko. (1 Yohane 2:6; Chivumbulutso 2:7, 11, 17, 26) Koma anafunika ‘kulimbika mtima.’
13. Kodi Paulo anawalimbikitsa chiyani Afilipi?
13 Patapita zaka Yesu atamwalira, Paulo ndi Sila anaikidwa m’ndende ku Filipi. Kenako, Paulo analimbikitsa mpingo wa ku Filipi kuti upitirize “[ku]chirimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino; osaopa adani m’kanthu konse.” Powalimbikitsa pa nkhani imeneyi, Paulo anati: “Chimene [kuzunzidwa kwa Akristu] chili kwa iwowa [ozunzawa] chisonyezo cha chiwonongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu; kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu chifukwa cha Kristu, si kukhulupirira kwa Iye kokha, komatunso kumva zowawa chifukwa cha Iye.”—Afilipi 1:27-29.
14. Kodi n’chiyani chinachitika ku Roma chifukwa cha kulimba mtima kwa Paulo?
14 Nthaŵi imene Paulo analembera kalata mpingo wa ku Filipi, iye analinso m’ndende kena, ndipo panthaŵiyi anali ndende ya ku Roma. Komabe, iye anapitiriza kulalikira molimba mtima kwa anthu ena. Kodi n’chiyani chinachitika chifukwa cha zimenezi? Iye analemba kuti: “Zomangira zanga zinaonekera mwa Kristu m’bwalo lonse la alonda, ndi kwa onse ena; ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m’zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mawu a Mulungu opanda mantha.”—Afilipi 1:13, 14.
15. Kodi tingapeze kuti zitsanzo zabwino za chikhulupiriro zimene zingalimbikitse kufunitsitsa kwathu kukhala olimba mtima?
15 Chitsanzo cha Paulo chimatilimbikitsa. N’chimodzimodzinso ndi zitsanzo za Akristu a m’nthaŵi yathu ino amene apirira chizunzo m’mayiko a ulamuliro wopondereza kapena mmene olamulira ake ndi atsogoleri achipembedzo. Nkhani za ambiri mwa anthu ameneŵa zalembedwa m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndiponso m’mabuku a Yearbook of Jehovah’s Witnesses. Mukamaŵerenga nkhani zimenezo, kumbukirani kuti eni ake nkhani zimene zasimbidwazo anali anthu wamba ngatinso ife; koma pamene anali m’mavuto aakulu, Yehova anawapatsa mphamvu zoposa zachibadwa ndipo anapirira. Tingatsimikize kuti iye adzatichitiranso chimodzimodzi ngati zochitika zidzafuna kuti atero.
Kulimba Mtima Kwathu Kumasangalatsa ndi Kulemekeza Yehova
16, 17. Kodi ife masiku ano tingatani kuti tikhale olimba mtima?
16 Ngati munthu achirimika poimira choonadi ndi chilungamo ndiye kuti ndi wolimba mtima. Ngati munthu achita zimenezi ngakhale ali ndi mantha mumtima, kumeneko ndi kulimbanso mtima kwakukulu. Inde, Mkristu aliyense angakhale wolimba mtima ngati akufunadi kuchita chifuniro cha Yehova, ngati akufunitsitsa kukhalabe wokhulupirika, ngati amadalira Mulungu nthaŵi zonse, ndiponso ngati amakumbukira nthaŵi zonse kuti m’mbuyomu Yehova walimbitsa anthu osaŵerengeka onga iye. Ndiponso, tikamadziŵa kuti kulimba mtima kwathu kumasangalatsa ndiponso kulemekeza Yehova, timatsimikiza mtima kwambiri kuti tisafooke. Timakhala okonzeka kupirira kunyozedwa kapenanso zinthu zina zoipa kuposa pamenepo chifukwa timamukonda kwambiri.—1 Yohane 2:5; 4:18.
17 Tisaiwale kuti tikamavutika chifukwa cha chikhulupiriro chathu, sizitanthauza kuti tachita chinachake choipa. (1 Petro 3:17) Tikuvutika chifukwa chokhalira kumbuyo Ufumu wa Yehova, kuchita zabwino, ndiponso chifukwa chosakhala mbali ya dziko. Pankhani imeneyi, mtumwi Petro anati: “Ngati pochita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapirira, kumeneko ndiko chisomo pa Mulungu.” Petro anatinso: “Iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wawo ndi kuchita zokoma m’manja a Wolenga wokhulupirika.” (1 Petro 2:20; 4:19) Inde, chikhulupiriro chathu chimasangalatsa Mulungu wathu wachikondi, Yehova, ndipo chimamulemekezetsa. Ndi chifukwa chachikulutu chimenechi chokhalira wolimba mtima!
Kulankhula ndi Olamulira
18, 19. Ngati tilimba mtima pamaso pa woweruza, kodi kwenikweni timakhala tikupereka uthenga wotani?
18 Yesu atauza otsatira ake kuti adzazunzidwa, iye anatinso: “[Anthu] adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, nadzakukwapulani inu m’masunagoge mwawo; ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.” (Mateyu 10:17, 18) Kuonekera pamaso pa woweruza kapena wolamulira chifukwa chonamiziridwa kumafuna kulimba mtima. Komabe, tikagwiritsa ntchito molimba mtima mipata imeneyo kuchitira umboni kwa anthu otero, timatengerapo mwayi pa vutolo kukwaniritsa chinthu chofunika kwambiri. Kwenikweni, timauza anthu amene amatiweruzawo mawu a Yehova amene ali mu Salmo lachiŵiri, akuti: “Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru: langikani, oweruza inu a dziko lapansi. Tumikirani Yehova ndi mantha.” (Salmo 2:10, 11) Nthaŵi zambiri, pamene Mboni za Yehova zaimbidwa mlandu wabodza m’khoti, oweruza alimbikitsa ufulu wolambira, ndipo tikuyamikira zimenezo. Komabe, oweruza ena alolera kutsatira maganizo a adani. Kwa oweruza oterowo, Lembalo limati: “Langikani.”
19 Oweruza ayenera kudziŵa kuti lamulo lapamwamba kwambiri ndi la Yehova Mulungu. Ayenera kukumbukira kuti anthu onse, ndi oweruza omwe, adzadziŵerengera mlandu kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. (Aroma 14:10) Koma ife, kaya anthu oweruza aweruze motikomera kapena ayi, tili ndi zifukwa zonse zokhalira olimba mtima chifukwa Yehova amatithandiza. Baibulo limati: “Odala onse akum’khulupirira Iye.”—Salmo 2:12.
20. N’chifukwa chiyani tingasangalale ngati tikupirira chizunzo ndiponso mabodza?
20 Mu Ulaliki wa pa Phiri, Yesu anati: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu m’Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.” (Mateyu 5:11, 12) N’zoona kuti chizunzo pachokha n’chosasangalatsa, koma kuchirimika kwathu ngakhale tikuzunzidwa, kuphatikizapo nkhani zabodza za m’manyuzipepala, mawailesi ndi ma TV, kungatichititse kusangalala. Zimatanthauza kuti tikusangalatsa Yehova ndipo tidzalandira mphoto. Kulimba mtima kwathu kumasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro chenicheni ndiponso kumatitsimikizira kuti Mulungu akutiyanja. Inde, kumasonyeza kuti timakhulupirira Yehova ndi mtima wonse. Kukhulupirira kumeneko n’kofunika kwambiri kwa Mkristu monga momwe nkhani yotsatirayi isonyezere.
Kodi Mwaphunzira Chiyani?
• Kodi ndi zochitika ziti masiku ano zimene zimafuna kulimba mtima?
• Kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima?
• Kodi ndi anthu ena ati amene ali zitsanzo zabwino za kulimba mtima?
• N’chifukwa chiyani tikufunitsitsa kuchita zinthu molimba mtima?
[Zithunzi patsamba 9]
Simone Arnold (panopa ndi Simone Liebester) ku Germany, Widdas Madona ku Malaŵi, ndiponso Lydia ndi Oleksii Kurdas ku Ukraine analimba mtima ndipo anakaniza woipayo
[Zithunzi patsamba 10]
Sitichita manyazi ndi uthenga wabwino
[Chithunzi patsamba 11]
Kulimba mtima kwa Paulo ali m’ndende kunathandiza kupititsa patsogolo uthenga wabwino
[Chithunzi patsamba 12]
Ngati tifotokoza molimba mtima chikhulupiriro chathu cha m’Malemba kwa woweruza, timapereka uthenga wofunika kwambiri