Miyambo
2 Munthu amene amachita zabwino amaopa Yehova,
Koma amene amachita zinthu mwachinyengo* amanyoza Mulungu.
3 Mawu odzikuza a munthu wopusa ali ngati chikwapu cholangira munthu,
Koma milomo ya anthu anzeru idzawateteza.
4 Ngati palibe ngʼombe, chodyeramo chimakhala choyera.
Koma zokolola zimachuluka ngati pali ngʼombe yamphongo yamphamvu.
6 Munthu wonyoza amafunafuna nzeru koma sazipeza,
Koma munthu womvetsa zinthu amaphunzira zinthu mosavuta.+
8 Nzeru zimathandiza munthu wochenjera kuzindikira njira imene akuyenda,
9 Anthu opusa akapalamula mlandu amangoseka,*+
Koma anthu owongoka mtima amakhala ofunitsitsa kugwirizananso.
10 Ngati munthu mtima ukumupweteka amadziwa yekha,
Ndipo munthu wina sangamvetse mmene mnzake akusangalalira mumtima mwake.
13 Ngakhale pamene munthu akuseka, mtima wake ukhoza kumamupweteka.
Ndipo kusangalala kungathere mʼchisoni.
14 Munthu wa mtima wosakhulupirika adzakumana ndi zotsatira za zochita zake,+
Koma munthu wabwino amapeza mphoto chifukwa cha zochita zake.+
15 Munthu amene sadziwa zambiri amakhulupirira mawu alionse,
Koma wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.+
16 Munthu wanzeru amachita zinthu mosamala ndipo amapewa zoipa,
Koma wopusa amachita zinthu mosasamala* ndipo amakhala wodzidalira.
18 Anthu osadziwa zambiri adzakhala opusa,
Koma kwa ochenjera, kudziwa zinthu kudzakhala ngati chisoti chachifumu.+
19 Anthu oipa adzagwadira anthu abwino,
Ndipo oipa adzagwada pamageti a anthu olungama.
21 Munthu amene amanyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,
Koma wosangalala ndi munthu amene amakomera mtima anthu onyozeka.+
22 Anthu okonza chiwembu amasochera,
Koma amene ali ndi mtima wofunitsitsa kuchita zabwino amawachitira zinthu mokhulupirika komanso kuwasonyeza chikondi chokhulupirika.+
24 Chisoti chaulemu cha anthu anzeru ndi chuma chawo.
Koma kupusa kumapangitsa kuti anthu opusa apitirizebe kukhala opusa.+
25 Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo ya anthu,
Koma mboni yabodza imalankhula zabodza zokhazokha.
26 Munthu woopa Yehova amamukhulupirira pa chilichonse,+
Ndipo ana a munthu ameneyu adzapeza malo othawirako.+
27 Kuopa Yehova kuli ngati kasupe wa moyo,
Chifukwa kumateteza moyo kumisampha ya imfa.
28 Kuchuluka kwa anthu kumabweretsa ulemerero kwa mfumu,+
Koma wolamulira amene alibe anthu oti aziwalamulira ulamuliro wake umatha.
29 Munthu amene sakwiya msanga ndi wozindikira zinthu kwambiri,+
Koma wosaugwira mtima amasonyeza uchitsiru wake.+
31 Amene amabera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga,+
Koma amene amakomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.+
32 Woipa adzagwetsedwa ndi kuipa kwakeko,
Koma kukhulupirika kwa munthu wolungama kudzakhala malo ake othawirako.+