Onesiforo—Wotonthoza Wolimba Mtima
“KUMBUKIRANI am’nsinga, monga am’nsinga anzawo; ochitidwa zoipa.” (Ahebri 13:3) Pamene mtumwi Paulo analemba mawu amenewo cha mu 61 C.E., iye mwiniyo anali ataikidwa m’ndende kangapo ndipo anali kudzaikidwanso m’ndende asanafe monga wofera chikhulupiriro. (Machitidwe 16:23, 24; 22:24; 23:35; 24:27; 2 Akorinto 6:5; 2 Timoteo 2:9; Filemoni 1) Panthaŵiyo kunali kofunika monga momwe kulili lerolino kuti mipingo ithandize mofulumira okhulupirira anzawo amene akuyang’anizana ndi ziyeso zokhudzana ndi chikhulupiriro chawo.
Wophunzira wina wa m’zaka za zana loyamba amene analabadira kwambiri zimenezi anali Onesiforo. Iye anachezera Paulo pamene anaikidwa m’ndende kachiŵiri ku Roma. Ponena za iye, mtumwiyo analemba kuti: “Ambuye achitire banja la Onesiforo chifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kaŵirikaŵiri, ndipo sanachita manyazi ndi unyolo wanga; komatu pokhala m’Roma iye anandifunafuna ine ndi khama, nandipeza.” (2 Timoteo 1:16, 17) Kodi munalingalirapo za zimene mawu ochepa amenewo amatanthauza kwenikweni? Kuchita zimenezo kungawonjezeredi kuzindikira kwanu Onesiforo. Mudzapeza kuti iye anali wotonthoza wolimba mtima.
Paulo Aikidwa m’Ndende Kachiŵiri
Atamasulidwa kundende ulendo woyamba, Paulo anaikidwanso m’ndende yachiroma koma kunali zochitika zosiyana. Poyamba, mabwenzi ake anali kumchezera mosavuta kunyumba yake yalendi, ndipo zikuonetsa kuti iye anali ndi chidaliro chakuti adzamasulidwa posachedwa. Panthaŵiyi pamene ambiri sanamchezere, iye anaona kuti anali pafupi kufa monga wofera chikhulupiriro.—Machitidwe 28:30; 2 Timoteo 4:6-8, 16; Filemoni 22.
Paulo anali m’ndende panthaŵiyi cha mu 65 C.E. Pafupifupi chaka chimodzi zimenezi zisanachitike—m’July 64 C.E.—moto unatentha Roma, ndipo unawononga kwambiri zigawo 10 mwa zigawo 14 za mzindawo. Malinga nkunena kwa wolemba mbiri wachiroma Tacitus, Mfumu Nero analephera “kuthetsa mphekesera zimene zinamveka zakuti iyeyo ndiye anachita kulamula kuti motowo uyatsidwe. Kenaka, pofuna kuti athetse mphekeserazo, Nero anaimba mlandu ndi kuzunza mochititsa mantha anthu amene anadedwa chifukwa cha makhalidwe awo owanyansa, anthu odziŵika ndi dzina lakuti Akristu. . . . Iwo anaphedwa mwachipongwe. Atawaveka zikopa zanyama, iwo analumidwa ndi agalu naphedwa, mwinanso anakhomedwa pamtanda ndi misomali, kapena anatenthedwa ndi moto, kuti akhale ngati zounikira usiku, pamene kunagwa mdima.”
Panali pazochitika zonga zimenezi ndiponso ndi ziyembekezo zofananazo pamene Paulo anaikidwanso m’ndende. Nzosakayikitsa konse kuti iye anali woyamikira kwambiri chifukwa cha kuchezeredwa ndi bwenzi lake Onesiforo! Koma tiyeni tione zochitika zofananazo mogwirizana ndi Onesiforo.
Kuchezera Paulo Wandende
Mwachionekere, banja la Onesiforo linali kukhala ku Efeso. (2 Timoteo 1:18; 4:19) Kaya Onesiforo anapita kulikulu la ufumuwo pazifukwa za iye mwini kapena anapita kumeneko ncholinga chochezera Paulo zimenezo sizinafotokozedwe. Mulimonse mmene zinalili, mtumwiyo anati: ‘Pokhala m’Roma Onesiforo anatsitsimutsa ine kaŵirikaŵiri.’ (2 Timoteo 1:16, 17) Kodi kunali kutsitsimutsa kwa mtundu wanji? Ngakhale kuti chithandizo cha Onesiforo chingaphatikizepo zinthu zakuthupi, kuchezera kwake kunakhalanso monga chosonkhezera Paulo kuti akhale ndi nyonga ndiponso kuti akhale wolimba mtima. Ndithudi, m’ma Baibulo ena timaŵerenga kuti: “Wasangalatsa mzimu wanga kaŵirikaŵiri,” kapena “wanditonthoza kaŵirikaŵiri.”
Kupeza mwaŵi wokachezera m’Kristu wandende ku Roma panthaŵiyo kunali kovuta kwambiri. Mosiyana ndi nthaŵi imene Paulo anaikidwa m’ndende kwa nthaŵi yoyamba, mwachionekere nthaŵi imeneyi Akristu a ku Roma analibe mwaŵi wakuti angamchezere. Mumzinda waukulu monga Roma, kunali kovuta kupeza wandende wobisika m’gulu lalikulu la andende amene ayenera kuti anali ataikidwa m’ndendemo pamilandu yosiyanasiyana. Choncho, kufunafuna mwakhama kunali kofunika. Katswiri wamaphunziro Giovanni Rostagno anati: “Mavutowo mwinamwake anali osiyanasiyana. Makamaka, anafunikira kufufuza mochenjera. Kufunafuna chidziŵitso m’madera osiyanasiyana ndiponso kuoneka kukhala wofunitsitsa kupeza ndende imene muli wandende wotengeka maganizo ndi wokalamba amene anapezeka ndi milandu yambirimbiri kukanapangitsa kuti akukayikire.”
Wolemba P. N. Harrison anafotokoza zimene zinachitika mwa fanizo lomveka bwino la mkhalidwewo mwa kunena kuti: “Timaona ngati kuti tikuona munthu wina amene ali ndi cholinga china pakati pa gulu la anthu oyenda mumsewu. Tikumuona mlendo ameneyu mwachidwi wochokera kugombe lakutali la Aegean. Akuyenda mokhwetakhweta m’misewu imene ili yachilendo kwa iye ndipo akugogoda pazitseko zambiri, ndikutsatira malangizo alionse amene wapatsidwa. Akuchenjezedwa kuti zimenezi zingampezetse mavuto koma iye akulimbikirabe kufunafuna; mpaka pamene akumva malonje a munthu wina wodziŵika kwa iye m’ndende ina yobisika, ndipo iye akupeza kuti akumlonjerayo ndi Paulo atamangiriridwa ndi unyolo kwa msilikali wachiroma.” Ngati malo amenewo anali ofanana ndi ndende zina zachiroma, ndiye kuti mwinamwake inali yozizira, yamdima, ndiponso yauve, kumene kunali unyolo wosiyanasiyana ndi kuzunza kwadzaoneni.
Kudziŵika kuti ndiwe bwenzi la wandende monga Paulo kunali koopsa. Ndipo kunalinso koopsa kwambiri kumchezera kaŵirikaŵiri. Kudzizindikiritsa kuti ndiwe Mkristu kunali kudziika pangozi ya kugwidwa kapena kuphedwa mozunzika. Koma Onesiforo sanakhutiritsidwe kumchezera mwa apo ndi apo. Iye sanachite manyazi kapena kuchita mantha kumchezera “kaŵirikaŵiri.” Onesiforo anatsatiradi tanthauzo la dzina lake, lakuti “Wopindulitsa,” akumapereka chithandizo molimba mtima ndiponso mwachikondi mosasamala kanthu za ngozi zimene zinalipo.
Kodi nchifukwa ninji Onesiforo anachita zonsezi? Brian Rapske anati: “Ndende siinali malo ozunzikirako mwakuthupi chabe ayi, koma inalinso malo a kuvutika maganizo kwakukulu chifukwa cha zipsinjo zimene inachititsa kwa wandende. Panthaŵi ngati imeneyi, kumchezera, ndi mawu olimbikitsa a othandiza zinali zinthu zimene zikanathandiza kwambiri wandendeyo kuti asapsinjike maganizo.” Mwachionekere Onesiforo anazindikira zimenezi ndipo anathandiza bwenzi lakelo molimba mtima. Paulo ayenera kuti anayamikira kwambiri chotani nanga chithandizo chimenecho!
Kodi Chinachitika Nchiyani kwa Onesiforo?
M’kalata yake yachiŵiri yolembera Timoteo, Paulo anapereka malonje kwa banja la Onesiforo ndipo anati ponena za iye: “Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo.” (2 Timoteo 1:18; 4:19) Ambiri amaganiza kuti mawu akuti “tsiku lijalo” amanena za tsiku la Mulungu la chiweruzo ndipo amati panthaŵiyi Onesiforo anali atafa. Ngati zinali choncho, ndiye kuti mwina “Onesiforo anagwidwa paulendo wake wina, ndipo analipira . . . mlanduwo mwakuphedwa,” anatero P. N. Harrison. Inde, mwina Onesiforo anali atangochoka panyumba, kapena mwinamwake Paulo anangomuphatikiza m’malonje amene anapereka kwa banja lake lonse.
Ena amakhulupirira kuti pali mfundo ina yofunika kwambiri m’mawu akuti: “Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo.” Iwo amaganiza kuti mawu ameneŵa ali m’gulu la mapemphero opempherera mizimu ya anthu akufa imene ikukhala ndiponso mwina imene ikuvutika m’dziko lina la mizimu. Komabe, lingaliro limenelo likuombana ndi chiphunzitso cha Malemba chakuti akufa sadziŵa chilichonse. (Mlaliki 9:5, 10) Ngakhale kuti mwina Onesiforo anali atafa, Paulo anali kungofotokoza chikhumbo chake chakuti Mulungu achitire chifundo bwenzi lakelo. “Timafunikira kukhala ndi chikhumbo chofananacho kwa anthu onse,” anatero R. F. Horton. “Koma kupempherera akufa, ndiponso kuwachitira Misa, nzosemphana ndi zimene [mtumwiyo] anali kulingalira.”
Tiyeni Tikhale Otonthoza Okhulupirika
Kaya Onesiforo anatayadi kapena sanataye moyo wake pamene anali kuthandiza Paulo, iye anauikadi pangozi kuti apeze mtumwiyo ndi kumchezera m’ndende. Ndipo nzosakayikitsa kuti Paulo anayamikira chithandizo ndi chilimbikitso chofunika kwambiri chimene anachilandira kwa Onesiforo.
Pamene Akristu anzathu ayang’anizana ndi chiyeso, chizunzo, kapena kuikidwa m’ndende, tiyeni tiwatonthoze ndi kuwalimbikitsa monga momwe tingathere. Choncho tiyeni tiziwapempherera ndi kuwathandiza mwachikondi mulimonse mmene tingathere. (Yohane 13:35; 1 Atesalonika 5:25) Monga Onesiforo, tiyenitu tikhale otonthoza olimba mtima.
[Chithunzi patsamba 31]
Onesiforo anatonthoza molimba mtima mtumwi Paulo wandende