Sungirirani Chikhulupiriro Chanu ndi Umoyo Wauzimu
“Gwira chitsanzo cha mawu a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chiri mwa Kristu Yesu.”—2 TIMOTEO 1:13.
1. Kodi nchifukwa ninji umoyo wabwino wakuthupi uli chuma cha mtengo kwenikweni chomwe chifunikira kusungiriridwa?
UMOYO wabwino wakuthupi uli chuma cha mtengo wake. Pamene tiri aumoyo, tingachite zinthu zambiri ndi kusangalala ndi moyo moposerapo. Koma pamene tiri odwalirira kapena okalamba, moyo umakhala wovutikira kwenikweni. Ndithudi, umoyo wabwino uyenera kusungiriridwa. Ambiri amanyalanyaza umoyo wawo kapena kuchita zinthu zomwe zimadzetsa matenda. Komabe, anthu omwe amadzisamalira iwo eni, kaŵirikaŵiri amakhala ndi mlingo wa umoyo wabwino ndi thanzi m’nthaŵi yochuluka ya moyo wawo.
2. (a) Kodi nchifukwa ninji umoyo wauzimu uli wa mtengo kwenikweni kuposa umoyo wakuthupi? (b) Kodi nchiyani chimene chimafunikira kuti tikhale aumoyo m’chikhulupiriro?
2 Umoyo wauzimu ndi wofunika kwenikweni kuposa umoyo wakuthupi. Umoyo wakuthupi wabwino koposa sungabweretse mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha. Umoyo wabwino wauzimu umachokera m’kulambira koyera ndi chikhulupiriro chozikidwa pa chidziŵitso cholongosoka. (Yohane 17:3; Ahebri 11:6; Yakobo 1:27) Mtumwi Paulo ananena kuti: “Okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, [aumoyo, NW] m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiriro.” (Tito 2:2) Aliyense wolakalaka kukhala waumoyo m’chikhulupiriro ayenera kuika kuyesayesa kwakhama ndi kusungirira kugalamuka kokhazikika. Ziwopsyezo ku umoyo wabwino wauzimu zingachokere mkati mwa ife eni kapena kuchokera kunja. Tiyenera kukhala ogalamuka za ziwopsyezo zimenezi ngati titi tisungirire chikhulupiriro ndi umoyo wauzimu m’dziko lodwalali.
Kodi Dzikoli Nlodwala Motani?
3, 4. Kodi ndimotani mmene kudwala kwa makhalidwe kukuwunikiridwira m’dzikoli ndi m’kachitidwe ka anthu?
3 Palibe chikaikiro kuti dzikoli nlodwala kwenikweni mwamakhalidwe. Ife timawona matenda akupha “m’ziŵalo” zonse za dziko iri—chipembedzo chake, dongosolo lake la ndale zadziko, magulu ake a zamalonda, zosangulutsa zake. Oŵerengeka ndi amene ali ndi ulemu wa Mulungu ndi malamulo amene iye wapereka chifukwa cha ubwino wa anthu. Ndipo monga mmene mbiri yakale ikusonyezera, kuwola kwa makhalidwe kumatsogolera mokhazikika ku kuwonjezereka kwa matenda akuthupi ndi mavuto. Mwaumbuli, ochulukira samafuna kuchita chirichonse ponena za kuchiritsa mkhalidwe wamatenda umenewu chifukwa chakuti amakonda zinthu zomwe zimachititsa iwo.
4 Nlodwala chotani nanga dziko limeneli! M’kufunafuna kusangulutsa kapena m’kuyesera kuthaŵa zenizeni, ambiri awononga miyoyo yawo kupyolera m’zakumwa zoledzeretsa ndi kugwiritsira ntchito molakwa anam’goneka. Chiwawa chiri paliponse, moyo uli wopepuka, ndipo ndende zadzazidwa ndi apandu kwadzawoneni. M’maiko ambiri, theka la maukwati onse amathera m’chisudzulo. Ana osoŵa kuyang’aniridwa kwabwino kwaukholo amakula ali opulupudza. Chifukwa chakuti chisembwere cha kugonana chiri chofalikira, AIDS ndi matenda ena opatsirana mwa kugonana akufalikira mofulumira.
5. Kodi ndimotani mmene Yesaya analogosolera mikhalidwe m’Yuda wakale?
5 Mulungu anganene za dziko lodwalali chimene anawuzira Yesaya kulengeza ponena za Yuda wopanduka kuti: “Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbewu yakuchita zoipa, ana amene achita mowononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israyeli, iwo adana naye nabwerera m’mbuyo. Nanga bwanji mukali chimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka. Kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu m’menemo mulibe changwiro.”—Yesaya 1:4-6.
6. M’Yuda wakale ndi m’tsiku lathu, kodi ndi kuyankha kotani komwe kwakhalapo ku kuchonderera kwa Yehova kwa kuphunzira kuchita chimene chiri chabwino?
6 Kuchonderera kwa Yehova kwa kulapa ndi “kuphunzira kuchita zabwino” mwachisawawa sikunalabadiridwe mu Yuda. (Yesaya 1:16-20) Potsirizira pake ichi chinatsogolera ku chiwonongeko cha Yerusalemu ndi kuikidwa mu ukapolo kwa Ayuda mu Babulo. Okhulupirika oŵerengeka okha ndi amene anakumana ndi dalitso ndi kusungiriridwa kwa Mulungu pakati pa mtundu wodwalawo. Mofananamo lerolino, m’dziko iri lomwe liri lodwala kuchokera kumutu kufika pansi pa phazi, kokha oŵerengeka ndi amene amalakalaka kuphunzira kuchita zabwino. Atumiki a Yehova okhulupirika amenewa akupanga kuyesayesa kwakhama kwa kusungirira chikhulupiriro ndi umoyo wauzimu tsopano, ndi chiyembekezo cha kupeza umoyo wangwiro wakuthupi ndi moyo wosatha m’dziko latsopano lolonjezedwa ndi Mulungu.—2 Petro 3:13; Chibvumbulutso 21:1-4.
Ngozi Zauzimu m’Dziko Lodwalali
7. (a) Kodi ndi ngozi zotani zimene zimawopsyeza chikhulupiriro ndi umoyo wathu wauzimu? (b) Kodi nchiyani chimene Malemba amanena ponena za kuchita ndi mbali zazikulu zitatu zoika pangozi umoyo wauzimu?
7 Kusungirira chikhulupiriro ndi umoyo wauzimu kuli chitokoso chifukwa chakuti makhalidwe odwala a dzikoli ali oyambukira koposa. Akristu ayeneranso kulimbana ndi kupanda ungwiro kobadwa nako. (Aroma 7:21-25) Kuwonjezerapo, Satana, “mkulu wa dziko lapansi,” amadziŵa zifooko za thupi ndipo ali katswiri wa kuyesa. (Yohane 14:30; 1 Yohane 5:19) Ngozi zazikulu zitatu zimenezi zowopsyeza chikhulupiriro ndi umoyo wauzimu—thupi, dziko, ndi Mdyerekezi—nzokhwethemula. Koma nchotheka kusakhala “mbali ya dziko,” ngakhale kuti tikukhala mu ilo. Tingakhoze ‘kuyendayenda ndi mzimu wa Mulungu ndi kusafitsa chilakolako cha thupi.’ Ndipo ndi thandizo laumulungu tingakhoze “kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.” (Yohane 17:15, 16; Agalatiya 5:16; Aefeso 6:11; 2 Akorinto 2:11) Koma tsopano tiyeni tilingalire mmene tingachitire ndi mbali zitatu zazikulu zimenezi zoika m’ngozi chikhulupiriro ndi umoyo wauzimu.
8. Kodi ndimotani mmene Yesu akulongosolera mphamvu za mkati mwathu zimene zimagwira ntchito molimbana ndi umoyo wauzimu?
8 Mkati mwa chibadwa chathu chaumunthu chopanda ungwiro muli mphamvu zomwe zingapangitse chimo ndi zomwe zingatidwalitse mwauzimu. (Yakobo 1:14, 15) Ichi chiridi chowona ponena za mtima wophiphiritsira. Yesu ananena kuti: “Pakuti mkati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituluka mkati, nizidetsa munthu.”—Marko 7:21-23.
9. (a) Kodi ndi zilakolako zotani zimene zazikidwa mumtima wophiphiritsira? (b) Mogwirizana ndi Miyambo 4:20-23, kodi ndimotani mmene tingachinjirizire mtima?
9 Ngakhale kuti mtima uli magwero a zilakolako zoipa, mwa anthu a Mulungu ulinso magwero a kuwopa Yehova ndi kukonda chimene chiri chabwino. (Mateyu 22:37; Aefeso 4:20-24) Kaya ngati zabwino kapena zoipa zidzafalikira kwa ife zimangodalira pa zimene timaika m’mitima yathu. Mawu a Mulungu akutilangiza kuti: “Mwananga, tamvera mawu anga; tcherera makutu ku zonena zanga. Asachoke ku maso ako; uwasunge mkati mwa mtima wako. Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lawo lonse. Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.”—Miyambo 4:20-23.
10. Kodi ndimotani mmene zifooko zathu zakuthupi zimayambukirira maganizo athu ndi zilakolako?
10 Zikoofo zathu zakuthupi zimayambukira zolinga ndi zilakolako zathu. Ndani yemwe samagweredwa kaŵirikaŵiri ndi kukhumudwitsidwa, kusaleza mtima, kubwezera? Ngati tiwongolera zikhoterero zakuthupi zimenezi mofulumira, umoyo wauzimu ungasungiriridwe. Koma kunyada ndi zikhumbo zingazike mizu mofulumira mumtima. Umbombo ndi zilakolako za zosangulutsa zopambanitsa ndi kupikisana zingatilake. Ndipo zilakolako za kugonana, pamene kuli kwakuti ziri zachibadwa chifukwa cha njira imene Mulungu anatipangira, zingatipatutse ife mochenjera. Kuti tichinjirize kudwala kwauzimu koteroko kusachitika kwa ife, tifunikira kukulitsa zipatso za mzimu wa Mulungu m’miyoyo yathu tsiku ndi tsiku, kudziphunzitsa ife eni “kudana nacho choipa” ndi “kumamatira ku chimene chiri chabwino.”—Aroma 12:9; Agalatiya 5:22, 23.
Magwero Akunja a Matenda Auzimu
11. (a) Kodi ndi makhalidwe ndi zochita zakudziko ziti zimene ziri zoyambukira koposa? (b) Mogwirizana ndi Yesu, kodi ndi m’mbali iti mmene tiyenera kupereka chisamaliro ku mitima yathu?
11 Kuyambukiridwa kwauzimu kungadzenso kuchokera ku magwero akunja. Iko kungafalikire kwa ife kuchokera kwa omwe ali akufa mwauzimu. (Aefeso 2:1-3) Ngati ndife oyandikana nawo kwenikweni, tingatengeko mikhalidwe yawo ndi njira ya moyo. Kupambana mwa kudziko, kukonda ndalama, kusangalala ndi chuma chabwino koposa, ndi kukhala ndi nthaŵi yabwino ziri zinthu zazikulu m’miyoyo ya anthu a dziko iri. Koma chilakolako cha zinthu zoterozo nchoyambukira koposa, ndipo kudziwunikira mocheperadi ku izo kungatifooketse mwauzimu. Yesu anachenjeza kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndikuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pa nkhope pa dziko lonse lapansi.”—Luka 21:34, 35.
12. Kodi ndimotani mmene malingaliro ndi ziphunzitso zolakwika zingakhalire zangozi ku umoyo wauzimu?
12 Zolingalira ndi ziphunzitso zolakwika za dzikoli zingatiyambukirenso. Paulo anachenjeza kuti: “Pakuti idzafika nthaŵi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m’khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha: ndipo adzalubza dala pachowonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zachabe.” (2 Timoteo 4:3, 4) Ziphunzitso zonyenga ziri ngati chironda chonyeka. (2 Timoteo 2:16, 17) Chitayambika, mbali ya thupi lanu imafa chifukwa chakuti mwazi wopereka moyo walekeka kupita kumbali imeneyo ya thupi.
13. Ngati matenda auzimu ayambika mofanana ndi chironda chonyeka, kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa?
13 Chironda chonyekacho chimafalikira mofulumira chotani nanga! Kuti achinjirize imfa, dokotala angafunikire kudula mbali ya thupilo. Chotero, ngati kukaikira, madandaulo, kapena mpatuko uwopsyeza kukuipitsani mwauzimu, ziduleni izo mofulumira! (Yerekezani ndi Mateyu 5:29, 30.) Pezani thandizo kuchokera kwa akulu a mu mpingo. Musakhale ngati awo amene Paulo anawalongosola kukhala ‘odwala maganizo ndi zofunsafunsa ndi makani a mawu’ chifukwa chakuti sanakhoze “kuvomerezana nawo mawu amoyo.”—1 Timoteo 6:3, 4.
14. Kodi nchiyani chimene akulu angachipeze kukhala choyenerera kuchita kuti achinjirize umoyo wauzimu wa mpingo?
14 Kuti achinjirize umoyo wauzimu wa mpingo, akulu afunikira ‘kuchenjeza ndi chiphunzitso chaumoyo ndi kudzudzula otsutsa.’ (Tito 1:9, 13, 16; 2:1) Mwinamwake anthu oterowo angabwezeretsedwe ku mkhalidwe waumoyo wauzimu. (2 Timoteo 2:23-26) Koma bwanji ngati iwo mosalapa achirikiza chiphunzitso chonyenga? Pamenepo, m’chenicheni, ayenera kulekanitsidwa. Iwo amachotsedwa, ndipo timadzipatula kwa iwo kotero kuti kuyambukira kwawo kwauzimu sikukufalikira kwa ife.—Aroma 16:17, 18; 1 Akorinto 5:9-13; Tito 3:9-11.
15. M’kuyesera kufooketsa umoyo wauzimu wa anthu a Mulungu, kodi ndi kufikira kuŵiri kwakukulu kotani kumene Mdyerekezi wagwiritsira ntchito?
15 Magwero achitatu a ngozi ku chikhulupiriro ndi umoyo wauzimu ali Mdyerekezi. (Aefeso 6:11, 12) M’tsiku lathu lenilenili, iye wayesera kufooketsa chikhulupiriro cha anthu a Yehova mwa chizunzo, kuphatikizapo kuwukira kwa timagulu, kumenya, kuika m’ndende, ndi ziwopsyezo za imfa. (Chibvumbulutso 2:10) Popeza kuti Satana kaŵirikaŵiri samapambana ndi machenjera amenewa a kuswa umphumphu wa mmodzi wa atumiki wa Mulungu, iye amagwiritsira ntchito kukopa kwa dziko iri, pa limene iye ali mulungu, m’kuyesayesa kugwetsa ena.—2 Akorinto 4:4; 11:3, 14.
16. Kodi ndi zochinjiriza zotani zimene tiri nazo m’kulimbana ndi kuwukira kwa Mdyerekezi pa chikhulupiriro chathu ndi umoyo wauzimu?
16 Kodi ndimotani mmene tingachirimikire ndi kuwukira kwa Mdyerekezi? Mwa kuvala zida zonse zauzimu za Mulungu. Ife tiyeneradi ‘kudzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene tidzakhoza kuzima nacho mivi yonse’ imene Satana akutiponyera. Tiyeneranso kupemphera mogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” (Aefeso 6:11-18; Mateyu 6:13) Ngati tipemphera mwanjirayo ndi kuchita mogwirizana ndi mapemphero athu, tingayembekezere thandizo la Atate wathu wakumwamba m’kuzima mivi yonse ya Satana.
Kukhalabe Waumoyo m’Chikhulupiriro
17. M’kusungirira umoyo wauzimu, kodi ndimotani mmene chiriri chofunika kudya “chakudya pa nthaŵi yake” ndi kugawanamo mokhazikika mu ntchito Yachikristu?
17 Kuchinjiriza kuli chinthu chachikulu m’kusungirira umoyo wabwino wakuthupi. Zakudya zomangirira thupi, maseŵera abwino, ndi chisamaliro chachisawawa cha maganizo ndi thupi ziri zofunika kwambiri. Zotetezera zachibadwa molimbana ndi matenda zimakhala zamphamvu m’thupi laumoyo. Mofananamo, kuti tisungirire umoyo wauzimu, chiri chofunika kutsatira kadyedwe kamene Mulungu amakatchula ndi kuyamikira “chakudya cha pa nthaŵi yake” chosungirira chauzimu choperekedwa kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Kuti tikane zakudya zosapatsa thanzi mwauzimu za dzikoli, tiyenera kuphunzira Baibulo ndi mabukhu Achikristu ndi kusonkhana ndi anthu a Mulungu mokhazikika. (Mateyu 24:45-47; Ahebri 10:24, 25) Tifunikiranso maseŵera omwe amatulukapo “kukhala ndi zambiri zochita m’ntchito ya Ambuye” mu utumiki ndi ntchito zina Zachikristu.—1 Akorinto 15:58.
18. Kodi nchiyani chimene chiri “chitsanzo cha mawu amoyo,” ndipo kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchisunga icho mumtima ndi m’maganizo?
18 Kuti mukhale aumoyo m’chikhulupiriro, gwiritsirani ntchito mokwanira mphatso zauzimu za Mulungu. Monga momwe Paulo anamuuzira Timoteo kuti: “Gwira chitsanzo cha mawu a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chiri mwa Kristu Yesu. Chosungitsa chokomacho udikire mwa mzimu woyera [u]mene [u]khalitsa mwa ife.” (2 Timoteo 1:13, 14) Chinenero chimakhala ndi chitsanzo cha mawu. Mofananamo, “chinenero choyera” cha chowonadi cha Baibulo chiri ndi mtundu wozikidwa kwakukulukulu pa mutu wa kulengezedwa kwa Yehova kupyolera mu Ufumu. (Zefaniya 3:9, NW) Tiyenera kusunga chitsanzo cha mawu amoyo chimenechi mu mtima ndi m’maganizo ngati titi tisungirire chikhulupiriro chathu ndi umoyo wauzimu. Apo phuluzi, chidzazimiririkiratu kwa ife. Motsimikizirika ichi chinachitika mu mpingo wa ku Korinto, kumene ena “anafooka, nadwala” chifukwa chakuti analibe kuzindikira kwauzimu.—1 Akorinto 11:29-32.
19. (a) Ngati matenda auzimu ayambika, kodi nchiyani chomwe chiyenera kuchitika? (b) Kodi nchiyani chimene akulu angachite ngati munthu ali wodwala mwauzimu?
19 Nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa ngati inu mwakhala ndi matenda auzimu? Motsimikizirika thandizo lachikondi limafunikira ndipo liripo, popeza kuti Yakobo akunena kuti: “Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a mpingo, ndipo apemphere pa iye atamudzoza ndi mafuta m’dzina la [Yehova].” (Yakobo 5:14) Inde, itanani akulu. Monga asing’anga auzimu, iwo angakuthandizeni kufika ku chochititsa cha matenda auzimu. Iwo mwa pang’onopang’ono koma mophulapo kanthu adzakudzozani mafuta ochiritsa a Mawu a Mulungu. Ngati inu mwachita zolakwa ndipo mwalapa, tsimikizirani kuti Yehova amakhululukiradi. (Salmo 103:8-14) Pamene akulu apemphera nanu ndi kukuimirani, kodi nchiyani chomwe chingayembekezeredwe? Yakobo akuyankha kuti: “Pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo [Yehova] adzamuukitsa; ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.”—Yakobo 5:15.
Umoyo Wauzimu Umatsogolera ku Moyo Wamuyaya
20. (a) Kodi ndi uphungu wotani umene bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba linapereka ponena za kusungirira umoyo wauzimu? (b) Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza ife pamene tikuyembekezera madalitso a dziko latsopano?
20 ‘Umoyo wabwino kwa inu!’ Ndi mawu amenewo, bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba la anthu a Yehova linamaliza kalata yake likumatchula “zinthu zoyenerera” zofunikira kwa Akristu. Iwo anafunikira “kusala nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.” (Machitidwe 15:28, 29) Mankhwala amenewo a umoyo wabwino wauzimu adakali ogwira ntchito. Ndipo pamene tikuyembekezera madalitso a dziko latsopano, tingasungirire chikhulupiriro chathu ndi umoyo wauzimu ngati mwachangu tipitirizabe kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu ndi kuchirikiza dzina la Yehova m’dziko lodwalali. Kukhala otanganitsidwa mwanjirayi kudzatisunga ife kusakhala osaleza mtima za madalitso a dziko latsopano lomwe liri pafupi kwenikweni. Zowonadi, “chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima; koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.”—Miyambo 13:12.
21. Kodi ndi madalitso otani amene ali kutsogolo kwa awo omwe amasungirira mwachipambano chikhulupiriro chawo ndi umoyo wauzimu m’dziko lodwalali?
21 Musaphonye pa madalitso okulira amene Yehova ali nawo kwa awo omwe amamukonda. Kutsutsa konse kwa zisonkhezero zakudziko, kulimbana konse ndi zifooko zanu zakuthupi, ndi kupatutsa konse kwa mivi yoyaka moto ya Mdyerekezi sikudzakhala kwachabe. M’dziko latsopano la Yehova, inu mudzawona ndi maso anu enieniwo nthaŵi imene “wokhalamo sadzanena ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Izi zidzakhala zenizeni chifukwa cha mphatso ya Mulungu kupyolera mu nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, yemwe “anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu.” (Mateyu 8:17; Yesaya 53:4) Mudzakhala okhoza kumwa madzi ophiphiritsira a “mtsinje wa madzi a moyo” ndi kudya ku ‘mitengo ya moyo’ yomwe iri ndi masamba “akuchiritsa nawo amitundu.” (Chibvumbulutso 22:1, 2) Moyo wosatha mu ungwiro ndi chimwemwe udzakhala mphotho yanu ya kusungirira chikhulupiriro chanu ndi umoyo wauzimu m’dziko lodwalali.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji kukhala aumoyo m’chikhulupiriro kuli kofunika kwenikweni kuposa kukhala aumoyo wabwino wakuthupi?
◻ Kodi ndi ngozi zitatu zazikulu ziti zimene zimawopsyeza chikhulupiriro ndi umoyo wauzimu?
◻ Kodi ndi unansi wotani umene umoyo wabwino wauzimu uli nawo ku mtima wophiphiritsira?
◻ Ngati winawake ali wodwala mwauzimu, kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa?
[Zithunzi patsamba 16]
Ngakhale m’dziko lodwala, nchotheka kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndi umoyo wabwino wauzimu
[Zithunzi patsamba 18]
Umoyo wabwino wauzimu umadalira pa ntchito yokangalika Yachikristu ndi kudya mokhazikika chakudya chauzimu pa nthaŵi yake