Kalata Yopita kwa Tito
2 Koma iwe pitiriza kulankhula zinthu zogwirizana ndi mfundo zolondola.+ 2 Amuna achikulire akhale osachita zinthu mopitirira malire, opanda chibwana, oganiza bwino, achikhulupiriro cholimba, achikondi chachikulu ndi opirira kwambiri. 3 Nawonso akazi achikulire akhale ndi khalidwe loyenera anthu opembedza. Asakhale amiseche, kapena akapolo a vinyo wambiri, koma akhale aphunzitsi a zinthu zabwino, 4 nʼcholinga choti azilangiza* akazi achitsikana kuti azikonda amuna awo, azikonda ana awo, 5 azikhala oganiza bwino, oyera, ogwira ntchito zapakhomo,* abwino ndiponso ogonjera amuna awo,+ kuti mawu a Mulungu asanyozedwe.
6 Komanso upitirize kulimbikitsa anyamata kuti akhale oganiza bwino.+ 7 Ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino mʼnjira iliyonse. Uziphunzitsa zolondola* ndipo uzisonyeza kuti ndiwe wopanda chibwana.+ 8 Mawu ako azikhala oyenera, omwe sangatsutsidwe,+ kuti otsutsa achite manyazi ndipo asapeze chifukwa chotinenera.+ 9 Akapolo azigonjera ambuye awo pa zinthu zonse+ ndipo aziwakondweretsa. Asamatsutsane nawo 10 kapena kuwabera,+ koma akhale okhulupirika pa chilichonse, kuti azikometsera zimene Mpulumutsi wathu Mulungu amatiphunzitsa.+
11 Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake kwakukulu kumene kumabweretsa chipulumutso kwa anthu, kaya akhale otani.+ 12 Zimenezi zimatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu. Zimatiphunzitsanso kuti tisamalakelake zinthu zoipa zamʼdzikoli,+ koma kuti tikhale oganiza bwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu mʼdzikoli*+ 13 pamene tikuyembekezera zinthu zosangalatsa+ ndiponso kuonekera kwaulemerero kwa Mulungu wamkulu komanso kwa Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, 14 amene anadzipereka mʼmalo mwa ife+ kuti atilanditse*+ ku moyo wochita zinthu zosamvera malamulo za mtundu uliwonse ndiponso kuti atiyeretse, kuti tikhale anthu ake apadera, odzipereka pa ntchito zabwino.+
15 Pitiriza kulankhula zimenezi, kulimbikitsa ndi kudzudzula anthu pogwiritsa ntchito ulamuliro wonse umene wapatsidwa.+ Usalole kuti munthu aliyense akuderere.