NKHANI YOPHUNZIRA 1
NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa
Mukamachita Mantha, Muzidalira Yehova
LEMBA LA CHAKA CHA 2024: “Ndikamachita mantha, ndimadalira inu.”—SAL. 56:3.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona zimene tingachite kuti tizidalira kwambiri Yehova komanso tisamachite mantha.
1. N’chifukwa chiyani nthawi zina tingamachite mantha?
TONSEFE nthawi zina timachita mantha. N’zoona kuti kuphunzira Baibulo kwatithandiza kuti tisamaope akufa, tisamaope ziwanda kapenanso zinthu zam’tsogolo. Koma tikukhala m’nthawi imene ‘kukuoneka zinthu zoopsa’ monga nkhondo, zachiwawa komanso matenda. (Luka 21:11) Tikhozanso kumaopa anthu kuphatikizapo maboma omwe amatipondereza kapena achibale amene amatsutsa kulambira koona. Enanso amada nkhawa kuti sangathe kupirira mavuto amene akukumana nawo panopa kapena omwe adzakumane nawo m’tsogolo.
2. Fotokozani zimene zinachitikira Davide atapita ku Gati.
2 Nthawi zina Davide ankachitanso mantha. Mwachitsanzo, pamene Mfumu Sauli inkafuna kumupha, iye anathawira mumzinda wa Afilisiti wa Gati. Posakhalitsa, Akisi yemwe anali mfumu ya ku Gati anamva kuti Davide anali msilikali wamphamvu yemwe ankatchulidwa mu nyimbo kuti anapha “masauzande ambirimbiri” a Afilisiti. Davide “anachita mantha kwambiri.” (1 Sam. 21:10-12) Iye ankaopa zimene Akisi angamuchitire. Ndiye kodi n’chiyani chinathandiza Davide kuti alimbe mtima?
3. Mogwirizana ndi Salimo 56:1-3, 11, kodi Davide anatani kuti asamachite mantha?
3 Mu Salimo 56, Davide anafotokoza mmene ankamvera pamene anali ku Gati. Salimoli limafotokoza bwino chimene chinamuchititsa mantha komanso zimene zinamuchititsa kuti asiye kuchita manthawo. Atayamba kuopa, Davide anadalira Yehova. (Werengani Salimo 56:1-3, 11.) Iye anali ndi zifukwa zabwino zomuchititsa kudalira Yehova. Mothandizidwa ndi Yehova, Davide anaganiza zochita zinthu zina zachilendo. Iye anayerekezera kukhala wamisala ndipo zimenezi zinamuthandiza. Tsopano Akisi sanaonenso Davide ngati munthu woopsa ndipo anamulola kuti azipita.—1 Sam. 21:13–22:1.
4. Kodi tingatani kuti tizidalira kwambiri Yehova? Perekani chitsanzo.
4 Ifenso tingasiye kuchita mantha ngati timadalira Yehova. Koma kodi tingatani kuti tizidalira kwambiri Yehova makamaka ngati tikuchita mantha? Taganizirani chitsanzo ichi: Mukadziwa kuti muli ndi matenda enaake, poyamba mungachite mantha. Komabe simungachite mantha kwambiri ngati mumadalira dokotala wanu. Mwina mungamve kuti anathandizapo odwala ena ambiri omwe anali ndi vuto ngati lanulo. Iye angakumvetsereni mosamala komanso kukutsimikizirani kuti akumvetsa mmene mukumvera ndipo angakupatseni mankhwala omwe athandizapo anthu ena. Mofanana ndi zimenezi, ifenso tingamadalire kwambiri Yehova tikamaganizira zimene wachitapo kale, zimene akuchita panopa komanso zimene atichitire posachedwapa. Izi ndi zimene Davide anachita. Tikamakambirana zina zomwe anauziridwa kulemba mu Salimo 56, muziganizira zimene zingakuthandizeni inunso kuti muzidalira kwambiri Yehova n’cholinga choti musamachite mantha.
KODI NDI ZINTHU ZITI ZIMENE YEHOVA WACHITA KALE?
5. Kuti asamachite mantha, kodi Davide ankaganizira za chiyani? (Salimo 56:12, 13)
5 Pamene moyo wake unali pangozi, Davide ankaganizira zimene Yehova anali atachita kale. (Werengani Salimo 56:12, 13.) Pa moyo wake wonse Davide ankaganiza mwa njira imeneyi. Mwachitsanzo, nthawi zina iye ankaganizira zimene Yehova analenga, zimene zinkamukumbutsa kuti Yehova ndi Wamphamvu Zonse komanso kuti amakonda kwambiri anthu. (Sal. 65:6-9) Ankaganiziranso zimene Yehova anali atachitira anthu ena. (Sal. 31:19; 37:25, 26) Ndiponso ankaganizira zimene Yehova anali atamuchitirapo kale iyeyo. Yehova anali atathandiza komanso kuteteza Davide kuyambira ali mwana. (Sal. 22:9, 10) Mosakayikira, kuganizira zimenezi ndi kumene kunamuthandiza Davide kuti azidalira kwambiri Yehova.
6. Tikamachita mantha, kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizidalira kwambiri Yehova?
6 Mukamachita mantha muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova wachita kale?’ Muziganizira zimene iye analenga. Mwachitsanzo, ‘mukamayang’anitsitsa’ mmene amasamalirira mbalame komanso maluwa, zomwe sizinalengedwe m’chifaniziro chake komanso sizingathe kumulambira, mungayambe kumudalira kwambiri kuti inunso adzakusamalirani. (Mat. 6:25-32) Muziganiziranso zimene Yehova wachitira atumiki ake. Mungathe kuwerenga za munthu wina wotchulidwa m’Baibulo yemwe anasonyeza chikhulupiriro cholimba kapenanso mungawerenge zimene zinachitikira mtumiki wa Yehova wa m’nthawi yathu ino.a Kuwonjezera apo, muziganiziranso zimene Yehova wachita kale pokusamalira inuyo. Kodi anakuthandizani bwanji kuti muphunzire choonadi? (Yoh. 6:44) Kodi wakhala akuyankha bwanji mapemphero anu? (1 Yoh. 5:14) Kodi nsembe ya Mwana wake wokondedwa imakuthandizani bwanji tsiku lililonse?—Aef. 1:7; Aheb. 4:14-16.
7. Kodi zimene zinachitikira Danieli zinathandiza bwanji Vanessa kuti asamachite mantha?
7 Mlongo wina wa ku Haiti dzina lake Vanessa,b anakumanapo ndi zinthu zochititsa mantha. Mwamuna wina wa m’dera limene ankakhala ankamuimbira foni komanso kumutumizira mameseji tsiku lililonse pomukakamiza kuti akhale naye pachibwenzi. Vanessa anamuuza momveka bwino kuti sangachite zimenezo. Koma mwamunayo anakwiya kwambiri ndipo anayamba kumuopseza. Vanessa anati: “Ndinkachita mantha.” Ndiye kodi anatani kuti asiye kuchita mantha? Iye anachita zimene akanatha kuti aziteteze. Mkulu wina anamuthandiza kuti akanene kupolisi. Koma iye ankaganiziranso mmene Yehova anathandizira atumiki ake akale. Vanessa ananena kuti: “Munthu woyambirira amene ndinaganizira anali mneneri Danieli. Iye anaponyedwa m’dzenje la mikango ngakhale kuti sanalakwe kanthu. Koma Yehova anamuteteza. Choncho ndinapemphera kwa Yehova ndipo ndinasiya nkhaniyo m’manja mwake. Nditachita zimenezi, ndinasiya kuchita mantha.”—Dan. 6:12-22.
KODI NDI ZINTHU ZITI ZIMENE YEHOVA AKUCHITA PANOPA?
8. Kodi Davide sankakayikira za chiyani? (Salimo 56:8)
8 Ngakhale kuti moyo wa Davide unali pangozi pamene anali ku Gati, iye sankaganizira kwambiri zinthu zimene zinkamuchititsa manthazo. M’malomwake, ankaganizira zimene Yehova ankamuchitira pa nthawiyo. Davide ankatha kuona kuti Yehova ankamutsogolera, kumuteteza komanso ankamvetsa mmene ankamvera. (Werengani Salimo 56:8.) Iye analinso ndi anzake okhulupirika monga Yonatani komanso Mkulu wa Ansembe Ahimeleki, omwe ankamuthandiza. (1 Sam. 20:41, 42; 21:6, 8, 9) Ndipo ngakhale kuti Mfumu Sauli inkafuna kumupha, Davide anapulumuka. Iye sankakayikira kuti Yehova ankadziwa bwino mavuto amene ankakumana nawo komanso mmene mavutowo ankamukhudzira.
9. Kodi tizikumbukira chiyani tikakumana ndi mayesero?
9 Mukamakumana ndi mayesero omwe akukuchititsani mantha, muzikumbukira kuti Yehova amaona zomwe zikukuchitikirani ndipo amadziwa mmene mukumvera. Mwachitsanzo, sikuti Yehova ankangoona nkhanza zomwe Aisiraeli ankachitiridwa ku Iguputo koma ankadziwanso ‘ululu umene ankamva.’ (Eks. 3:7) Davide anaimba kuti Yehova ankaona “kusautsika” kwake komanso ‘mavuto aakulu amene anali nawo.’ (Sal. 31:7) Ndipo pamene anthu a Mulungu ankavutika, ngakhale chifukwa choti asankha zinthu mopanda nzeru, “iye ankavutikanso.” (Yes. 63:9) Pamene mukuchita mantha, Yehova amadziwa mmene mukumvera ndipo amakhala wokonzeka kukuthandizani.
10. N’chiyani chikukutsimikizirani kuti Yehova amakukondani ndipo adzakuthandizani kupirira mayesero alionse?
10 Koma mwina simungadziwe mmene Yehova akukuthandizirani mukamachita mantha chifukwa cha mayesero enaake. Choncho muzimupempha kuti akuthandizeni kuona mmene akukuthandizirani. (2 Maf. 6:15-17) Kenako muziganizira izi: Kodi munamvetsera nkhani kapena ndemanga inayake pamisonkhano yomwe yakulimbikitsani? Kodi pali buku, vidiyo kapena nyimbo ya broadcasting yomwe yakulimbikitsani? Kodi pali wina yemwe wakulimbikitsani ndi mfundo inayake kapena lemba? Zingakhale zosavuta kuiwala mmene abale ndi alongo athu amatisonyezera chikondi komanso mmene zinthu zomwe Yehova amatipatsa zimatilimbikitsira. Komatu zimenezi ndi mphatso yapadera yochokera kwa Yehova. (Yes. 65:13; Maliko 10:29, 30) Mphatsozi zimasonyeza kuti Mulungu amatikonda. (Yes. 49:14-16) Zimasonyezanso kuti ndi woyenera kuti tizimudalira.
11. Kodi n’chiyani chinathandiza Aida kuti asamachite mantha?
11 Aida yemwe amakhala ku Senegal, anaona mmene Yehova anamuthandizira atakumana ndi mayesero. Popeza kuti iye ndi mwana wamkulu m’banja lawo, makolo ake ankayembekezera kuti azipeza ndalama zokwanira zothandiza iyeyo komanso makolowo. Koma iye atasintha zinthu zina pa moyo wake n’cholinga choti azichita upainiya, anayamba kukumana ndi mavuto azachuma. Anthu a m’banja lake anamukwiyira ndipo ankamuimba mlandu. Iye anati: “Ndinkaopa kuti sindizitha kuthandiza makolo anga ndiponso kuti aliyense sadzicheza nane. Ndinafika poimba mlandu Yehova chifukwa cholola kuti zinthu zifike poipa chonchi.” Kenako anamvetsera nkhani kumisonkhano. Ndipo anati: “Wokamba nkhani anatikumbutsa kuti Yehova amadziwa bwino mavuto amene tikukumana nawo. Pang’ono ndi pang’ono malangizo omwe akulu komanso anthu ena anandipatsa, anandithandiza kuona kuti Yehova amandikonda. Ndinayamba kupemphera kwa Yehova ndi mtima wonse ndipo ndinkakhala ndi mtendere wamumtima poona akuyankha mapemphero anga.” Patapita nthawi, Aida anapeza ntchito yomwe inkamuthandiza pa utumiki wake waupainiya komanso ankatha kusamalira makolo ake ndi anthu ena. Iye anati: “Ndaphunzira kudalira Yehova ndi mtima wanga wonse. Panopa, ndikapemphera sindichitanso mantha.”
KODI YEHOVA ADZACHITA CHIYANI M’TSOGOLO?
12. Mogwirizana ndi Salimo 56:9, kodi Davide sankakayikira za chiyani?
12 Werengani Salimo 56:9. Lembali likufotokoza chinthu chinanso chomwe chinathandiza Davide kuti asamachite mantha. Chinthu chake n’chakuti, ngakhale kuti moyo wake unali udakali pangozi, iye ankaganizira zimene Yehova adzamuchitire m’tsogolo. Davide ankadziwa kuti Yehova adzamupulumutsa pa nthawi yoyenera. Ndipotu iye anali atanena kale kuti Davideyo ndi amene adzakhale mfumu ya Isiraeli. (1 Sam. 16:1, 13) Kwa Davide, zinali ngati chilichonse chomwe Yehova analonjeza chinali chitachitika kale.
13. Kodi tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzachita chiyani?
13 Kodi Yehova walonjeza kuti adzakuchitirani chiyani inuyo? Sitimayembekezera kuti azititeteza ku mavuto onse.c Komabe kaya tikukumana ndi mayesero otani m’dziko loipali, tizikumbukira kuti Yehova adzawathetsa m’dziko latsopano. (Yes. 25:7-9) Mlengi wathu ndi wamphamvu kwambiri moti adzaukitsa akufa, kutichiritsa komanso adzaononga otsutsa onse.—1 Yoh. 4:4.
14. Kodi tiyenera kumaganizira za chiyani?
14 Mukamachita mantha, muziganizira zimene Yehova adzachite m’tsogolo. Taganizirani mmene mudzamvere Satana akadzachotsedwa, anthu oipa akadzalowedwa m’malo ndi anthu olungama komanso anthu akadzayamba kukhala angwiro pang’onopang’ono tsiku lililonse. Pamsonkhano wachigawo wa 2014, panali chitsanzo cha zimene tingachite poganizira za chiyembekezo chathu. Mu chitsanzocho, bambo ankakambirana ndi banja lake mmene lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 lingamvekere mosiyana mavesiwa atakhala kuti akufotokoza mmene zidzakhalire m’Paradaiso. Anawerenga kuti: “M’dziko latsopano, idzakhala nthawi yapadera komanso yosangalatsa. Pakuti anthu adzakhala okonda anzawo, okonda kulambira Mulungu, odzichepetsa, ofatsa, otamanda Mulungu, omvera makolo, oyamikira, okhulupirika, okonda achibale awo, ofuna kugwirizana ndi anzawo, onena zabwino za anzawo, odziletsa, odekha, okonda zabwino, odalirika, oganizira za ena, osadzitukumula ndiponso osanyada, okonda Mulungu, m’malo mokonda zosangalatsa, ndiponso odziperekadi kwa Mulungu. Anthu amenewa usasiyane nawo.” Kodi mumakambirana ndi anthu a m’banja lanu kapena anzanu mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano?
15. Ngakhale kuti Tanja ankachita mantha, kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti akhalebe wokhulupirika?
15 Kuganizira madalitso a m’tsogolo kunathandiza mlongo wina wa ku North Macedonia dzina lake Tanja kuti asamachite mantha. Makolo ake ankamutsutsa kwambiri atayamba kuphunzira Baibulo. Iye anati: “Zinthu zina zomwe ndinkaopa kuti zingachitike, zinachitikadi. Mayi anga ankandimenya nthawi iliyonse yomwe ndapita kumisonkhano. Makolo anga anandiopseza kuti andipha ndikakhala wa Mboni za Yehova.” Pamapeto pake, makolo a Tanja anamuthangitsa kunyumba kwawo. Ndiye kodi iye anatani? Iye anati: “Ndinkaganizira mmene ndidzasangalalire mpaka kalekale chifukwa chokhalabe wokhulupirika. Ndinaganiziranso madalitso omwe Yehova adzandipatse m’dziko latsopano chifukwa cha zimene ndataya panopa, komanso kuti sindidzakumbukiranso zoipa zonse zomwe zinandichitikira.” Tanja anakhaladi wokhulupirika ndipo mothandizidwa ndi Yehova anapeza malo okhala. Panopa Tanja anakwatiwa ndi m’bale wokhulupirika ndipo akusangalala kuchita utumiki wa nthawi zonse.
MUZIDALIRA KWAMBIRI YEHOVA PANOPA
16. Kodi n’chiyani chidzatithandize kukhalabe olimba mtima tikadzaona zinthu zimene zinaloseredwa pa Luka 21:26-28?
16 Pa nthawi ya chisautso chachikulu, anthu “adzakomoka chifukwa cha mantha.” Koma anthu a Mulungu sadzagwedezeka ndipo adzakhala olimba mtima. (Werengani Luka 21:26-28.) N’chifukwa chiyani sitidzachita mantha? Chifukwa tidzakhala titaphunzira kale kudalira Yehova. Tanja yemwe tamutchula kale uja ananena kuti zimene anakumana nazo pa moyo wake m’mbuyomu zimamuthandiza akakumana ndi mavuto. Iye anati: “Ndaphunzira kuti Yehova akhoza kutithandiza pa vuto lililonse lomwe takumana nalo komanso kutidalitsa. Nthawi zina zingaoneke ngati anthu ena ali ndi mphamvu, koma zoona n’zakuti Yehova ndi amene ali ndi mphamvu kuposa iwowo. Ndipo ngakhale mayesero atakhala aakulu bwanji, amafika pamapeto pake.”
17. Kodi lemba la chaka cha 2024 lingatithandize bwanji? (Onani chithunzi chapachikuto.)
17 Masiku ano pali zinthu zambiri zimene zingatichititse mantha. Koma mofanana ndi Davide, sitiyenera kulola kuti mantha atigonjetse. Lemba la chaka cha 2024, ndi pemphero la Davide kwa Yehova. Iye anati: “Ndikamachita mantha, ndimadalira inu.” (Sal. 56:3) Ponena za vesili, buku lina lofotokoza Baibulo linanena kuti Davide “sankangoganizira za zinthu zimene zinkamuchititsa mantha kapenanso mavuto ake. M’malomwake, ankaganizira kwambiri za Mpulumutsi wake.” M’miyezi ikubwerayi, muziganizira lemba la chakali makamaka pamene mwakumana ndi zinthu zochititsa mantha. Muzipeza nthawi yoganizira zimene Yehova wakhala akuchita m’mbuyomu, zimene akuchita panopa komanso zimene achite m’tsogolo. Mukatero, mofanana ndi Davide, mudzatha kunena kuti: “Ine ndimadalira Mulungu, sindikuopa.”—Sal. 56:4.
KODI MUNGATHETSE BWANJI MANTHA MUKAMAGANIZIRA . . .
zimene Yehova wachita kale?
zimene Yehova akuchita panopa?
zimene Yehova achite posachedwapa?
NYIMBO NA. 33 Umutulire Yehova Nkhawa Zako
a Mungapeze nkhani zolimbitsa chikhulupiriro pa jw.org polemba pamalo ofufuzira mawu akuti “tsanzirani chikhulupiriro chawo” kapena “zochitika pa moyo wa a Mboni za Yehova”. Pa JW Library, pitani pagawo lakuti Article Series kenako pamene alemba kuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” kapena “Mbiri ya Mboni za Yehova Zosiyanasiyana.”
b Mayina ena asinthidwa.
c Onani buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, mutu 7, ndime 13-22.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Davide akuganizira mmene Yehova anamupatsira mphamvu kuti aphe chimbalangondo, mmene ankamuthandizira kudzera mwa Ahimeleki komanso zimene amayembekezera kuchita pomupatsa ufumu.
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale yemwe ali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chake akuganizira mmene Yehova anamuthandizira kuti asiye kusuta, mmene akumulimbikitsira kudzera m’makalata ochokera kwa abale ndi alongo ake komanso moyo wosatha womwe adzamupatse m’Paradaiso.