Lingaliro la Baibulo
Kodi Nchiyani Chiyenera Kuchitidwa Minisitala Atachimwa?
KHALIDWE loipa la atsogoleri achipembedzo likukopa anthu ambiri lerolino kuposa ndi kale lonse. Aprotestanti achita manyazi ndi khalidwe lonyansa la aminisitala olalikira pa TV. Pamene pasitala wolalikira pa TV anagwidwa kachiŵiri m’zaka zitatu ndi mkazi wadama, anauza otsatira ake kuti Mulungu anamuuza kuti khalidwe lake siliyenera kudetsa nkhaŵa munthu wina koma iye yekha.
Posimba za kupenda kwa zaka 25, magazini a Time anati: “Yemwe kale anali mtsogoleri wachipembedzo wa gulu lotchedwa Benedictine . . . akuyerekezera kuti theka la ansembe a Roma Katolika okwanira 53,000 mu United States akuswa lumbiro lawo la umbeta.” Ndiponso, lipoti la nyuzi la mu 1990 lonena za ansembe angapo a ku Canada amene anapezedwa ndi mlandu wa nkhanza yakugona ana likuti: “Atsogoleri a Tchalitchi ananyalanyaza, kutsutsa kapena kusachitapo kanthu mokhutiritsa pa zidandaulo zonena za nkhanza yakugona ana, ngakhale kuti analandira zidandaulo zoterozo kuchokera kwa mikole, ziŵalo za matchalitchi, apolisi, ogwira ntchito zothandiza anthu ndi ansembe ena.”
Magazini a Time anati: “Kufikira posachedwapa, ansembe olakwa anali kungosamutsidwa kuchoka m’dera lina la tchalitchi kunka ku dera lina la tchalitchi.” Koma popeza kuti tsopano milandu yoperekedwa ku khoti ndi mikole ya khalidwe loipa la ansembe yafika $300 miliyoni mu United States, kaŵirikaŵiri ansembe amapatsidwa chithandizo cha odwala misala asanabwerere ku ntchito yachipembedzo.
Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa ngati minisitala, wansembe, kapena mkulu achimwa? Kodi nchitsogozo chotani chimene Baibulo limapereka ponena za mmene mkhalidwe womvetsa chisoni woterowo ungasamaliridwire? Tiyeni tisanthule malemba ofunika aŵiri a Baibulo—Tito 1:7, NW ndi 1 Timoteo 3:2, NW.
Ayenera Kukhala “Wopanda Chinenezo”
Baibulo limati: “Woyang’anira [“bishopu,” The New American Bible (matembenuzidwa Achikatolika)] ayenera kukhala wopanda chinenezo monga mdindo wa Mulungu.” (Tito 1:7, NW) Paulo anapereka lamulo limeneli kwa Tito pamene anamgaŵira kuika akulu m’mipingo ya ku Krete. Komabe, kodi mtumwiyo anatanthauzanji?
Mawu akuti “wopanda chinenezo” amasuliridwa kuchokera ku liwu Lachigiriki lakuti a·negʹkle·tos. Pothirira ndemanga pa liwuli, The New International Dictionary of New Testament Theology imafotokoza kuti: “Liwu lakuti anenklētos limagwira ntchito m’kuzenga mlandu kwa m’bwalo lamilandu, ndipo limasonyeza mkhalidwe womwe uli wosatonzeka, mkhalidwe umene sunganenezedwe.” Chotero, mbiri ya munthuyo iyenera kukhala yabwino asanaikidwe kukhala mkulu; sayenera kukhala wotonzeka, kapena kunenezedwa. Ndipo kokha ngati akhalabe wopanda chinenezo chenicheni mpamene mkulu angapitirize paudindowo.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 3:10.
Mkulu safunikira kupereka chitsogozo chokha mumpingo koma ayeneranso kutumikira mpingo. Ayenera kuvomereza thayo la udindo wake. Iye ali mdindo wa Mulungu; amaŵeta nkhosa za Mulungu. Chotero, ayenera kukhala ndi thayo lalikulu kwa Mwini wa nkhosazo, Yehova, ndiyeno kwa anthu amene Mulungu anampatsa thayo lakuwayang’anira.—1 Petro 5:2, 3.
Ayenera Kukhala “Wopanda Chifukwa”
Baibulo limati: “Chifukwa cha chimenecho woyang’anira [“bishopu,” NAB] ayenera kukhala wopanda chifukwa.” (1 Timoteo 3:2, NW) Liwu Lachigiriki lakuti a·ne·piʹlem·ptos lamasuliridwa “wopanda chifukwa” ndipo m’lingaliro lenileni limatanthauza “sayenera kugwidwa.” Kunena m’mawu ŵena moyo wa woyang’anira suyenera kupereka kalikonse kamene woneneza angasonyeko ndi kugwiritsira ntchito kumtsutsa. Pofutukula tanthauzo la liwu Lachigirikilo, Theological Dictionary of the New Testament imanena kuti woyang’anira “sangaukiridwe (ngakhale ndi anthu osakhala Akristu) chifukwa cha khalidwe lake labwino.”
Mulungu amakhazikitsa miyezo yapamwamba kwa awo amene amafuna kuyang’anira anthu ake ndi kuphunzitsa Mawu ake. Yakobo ananena motere ponena za iyemwini ndi akulu ena: “Tidzalangika koposa.” Ndipo Yesu anatchula lamulo lamakhalidwe lotsogoza ili: ‘Kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri.’—Yakobo 3:1; Luka 12:48.
Choncho, ngati woyang’anira Wachikristu achimwa poyera ndiyeno nalapa, angakhalebe chiŵalo cha mpingo, koma ayenera kuchotsedwa pa udindo wake wa woyang’anira. Salinso wopanda chifukwa. Kungatenge zaka zambiri kuti akhazikitsenso mbiri yake yabwino kotero kuti akhalenso wopanda chinenezo. Nkhani yake ingayerekezeredwe ndi ya Sebina, mdindo wa Hezekiya. Yehova anamdzudzula ndi mawu awa chifukwa cha khalidwe lake loipa: ‘Ndidzakutulutsa iwe mu ntchito yako, ndi kukutsitsa iwe pokhala pako.’ Koma mwina pambuyo pake Sebina anapezanso mbiri yake yabwino chifukwa timaŵerenga kuti anali kutumikiranso mfumu monga mlembi.—Yesaya 22:15-22; 36:3.
Bwanji Ngati Minisitala Salapa?
Zipembedzo zambiri za Chikristu Chadziko zalekerera aminisitala amene amachita tchimo. Mu 1459 kadinala Rodrigo Borgia anakhala wachiŵiri kwa papa, udindo wapamwamba kwambiri woyang’anira m’Bungwe Lachikatolika. Iye anadzudzulidwa ndi Papa Pius II chifukwa cha chisembwere chake. Komabe, chinkana kuti anali ndi ana anayi achigololo, mu 1492 bungwe la akadinala linamusankha kukhala papa! Anapitiriza ndi ntchito yake yochititsa manyazi monga Papa Alexander VI. Mosakaikira kulekerera aminisitala osalapa, achiwerewere m’mbiri yonse ya Chikristu Chadziko kwachititsa kuipa komwe tikuwona lerolino. Pamenepo, kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa ngati minisitala salapa?
Minisitala Wachikristu amene amachita tchimo lalikulu ndi kulephera kupereka umboni wa kulapa ayenera kuchotsedwa mumpingo. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kudya naye wotere, iyayi . . . Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.’—1 Akorinto 5:11-13.
Kachitidwe kamphamvu kamachinjiriza mbiri ya mpingo ndi kuupatula kwa awo amene ‘avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana iye.’ Njira imene chipembedzo chimachitira ndi vuto la minisitala amene amachimwa idzakuthandizani kuzindikira ngati chipembedzocho chiridi Chachikristu.—Tito 1:16; Mateyu 7:15, 16.
[Chithunzi patsamba 22]
Papa Alexander VI
[Mawu a Chithunzi]
Alinari/Art Resource, N.Y.