Kukhala “Anzeru” Pamene Mapeto Ayandikira
“Chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru.”—1 PETRO 4:7.
1. Kodi kukhala “anzeru” kumaphatikizapo chiyani?
MAWU apamwambawo a mtumwi Petro ayenera kukhudza kwambiri mmene Akristu amakhalira moyo wawo. Komabe, Petro sanauze oŵerenga mawu ake kuti apeŵe maudindo awo akuthupi ndi nkhaŵa za moyo; ndiponso sanawasonkhezere kuti achite mantha osalamulirika ndi chiwonongeko choyandikiracho. M’malo mwake, anawalimbikitsa kuti: “Khalani anzeru.” Kukhala “anzeru” kumaphatikizapo kusonyeza kuona zinthu moyenera, kukhala atcheru, ochenjera, osamala kalankhulidwe ndi zochita zathu. Kumatanthauza kulola Mawu a Mulungu kulamulira maganizo ndi zochita zathu. (Aroma 12:2) Popeza tikukhala “pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka,” nzeru nzofunika kuti tipeŵe mavuto.—Afilipi 2:15.
2. Kodi kuleza mtima kwa Yehova kukuwapindulitsa motani Akristu lerolino?
2 “Nzeru” zimatithandizanso kudziganizira ife eni bwino ndiponso moona mtima. (Tito 2:12, NW; Aroma 12:3) Zimenezi nzofunika malinga ndi mawu a pa 2 Petro 3:9 akuti: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” Mwaonatu kuti Yehova aleza mtima, osati kwa osakhulupirira okha, komanso “kwa inu”—a mumpingo wachikristu. Chifukwa? Chifukwa “safuna kuti ena awonongeke.” Mwinamwake ena afunikirabe kusintha ndi kuwongolera pazinthu zina kuti ayenerere mphatso ya moyo wosatha. Motero tiyeni tione mbali zina zimene zingafunikire kuwongolera.
“Anzeru” Pamaunansi Athu
3. Kodi makolo angadzifunse mafunso otani ponena za ana awo?
3 Panyumba payenera kukhala pamtendere. Koma kwa ena pamakhala ‘panyumba podzala . . . makangano.’ (Miyambo 17:1) Bwanji ponena za banja lanu? Kodi panyumba panu sipamakhala “mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano”? (Aefeso 4:31) Bwanji nanga za ana anu? Kodi amaona kuti mumawakonda ndi kuwayamikira? (Yerekezerani ndi Luka 3:22.) Kodi mumapeza nthaŵi yowalanga ndi kuwaphunzitsa? Kodi ‘mumalangiza m’chilungamo’ m’malo molangiza mwachiwawa ndi mwaukali? (2 Timoteo 3:16) Popeza ana ndiwo “cholandira cha kwa Yehova,” iye amafunitsitsa kuona mmene mukuwasungira.—Salmo 127:3.
4. (a) Kodi pangatsatire zotani ngati mwamuna achitira mkazi wake nkhanza? (b) Kodi akazi okwatiwa angachirikize motani mtendere ndi Mulungu ndi chimwemwe cha banja lonse?
4 Bwanji za mnzathu wa muukwati? “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu Eklesia.” (Aefeso 5:28, 29) Mwamuna wamanyozo, wopondereza, kapena wosalolera samangosokoneza bata la nyumba yake koma amawononga unansi wake ndi Mulungu. (1 Petro 3:7) Bwanji nanga akazi? Iwonso ayenera ‘kumvera amuna awo a iwo eni, monga kumvera Ambuye.’ (Aefeso 5:22) Kulingalira zosangalatsa Mulungu kungathandize mkazi kunyalanyaza zophophonya za mwamuna wake ndi kumgonjerabe popanda kunyansidwa naye. Nthaŵi zina, mkazi angafune kufotokoza zakukhosi. Miyambo 31:26 imanena za mkazi wabwino kuti: “Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili palilime lake.” Mwa kutenga mwamuna wake mokoma mtima ndi mwaulemu, iye amasungabe mtendere ndi Mulungu, ndipo amachirikiza chimwemwe cha banja lonse.—Miyambo 14:1.
5. Kodi nchifukwa ninji achinyamata ayenera kutsatira uphungu wa Baibulo wonena za mmene ayenera kutengera makolo awo?
5 Ananu, kodi makolo anu mumawatenga bwanji? Kodi mumagwiritsira ntchito kalankhulidwe kotukwana, kopanda ulemu kamene dziko limaloleza? Kapena kodi mukulabadira lamulo la Baibulo lakuti: “Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko”?—Aefeso 6:1-3.
6. Kodi mtendere tingaufunefune motani ndi olambira anzathu?
6 Timasonyezanso “nzeru” pamene ‘tifunafuna mtendere ndi kuulondola’ ndi olambira anzathu. (1 Petro 3:11) Kusamvana ndi kumvana molakwa kumakhalapo nthaŵi ndi nthaŵi. (Yakobo 3:2) Ngati mulola udani kukula, mtendere wa mpingo wonse ungasokonezeke. (Agalatiya 5:15) Choncho thetsani mikangano mwamsanga; pezani zothetsera zamtendere.—Mateyu 5:23-25; Aefeso 4:26; Akolose 3:13, 14.
“Nzeru” ndi Maudindo a m’Banja
7. (a) Kodi Paulo analimbikitsa motani kusonyeza “nzeru” pazinthu zakuthupi? (b) Kodi amuna achikristu ndi akazi awo ayenera kuwaona motani maudindo awo apanyumba?
7 Mtumwi Paulo analangiza Akristu “kukhala ndi moyo ndi nzeru.” (Tito 2:12, NW) Chosangalatsa nchakuti m’nkhani imeneyo, Paulo akulimbikitsa akazi kuti “akonde amuna awo, akonde ana awo, akhale odziletsa, odekha, ochita m’nyumba mwawo.” (Tito 2:4, 5) Paulo analemba zimenezo m’zaka za 61-64 C.E., zaka zochepa dongosolo la zinthu lachiyuda lisanathe. Komatu zinthu zakuthupi, monga ntchito yapanyumba, zinali zofunikabe. Chotero amuna ndi akazi awo omwe ayenera kukhala ndi lingaliro labwino, lothandiza pa maudindo awo apanyumba kuti “mawu a Mulungu angachitidwe mwano.” Mutu wina wa banja unapepesa kwa mlendo kaamba ka kaonekedwe kochititsa manyazi ka nyumba yake. Iye anafotokoza kuti inali yosakonzeka bwino “chifukwa chakuti anali kuchita upainiya.” Kudzipereka kaamba ka Ufumu nkwabwinodi, koma tiyenera kusamala kuti sitikuika ubwino wa mabanja athu pangozi.
8. Kodi mitu ya mabanja ingasamale motani zosoŵa za mabanja awo moyenera?
8 Baibulo limalimbikitsa atate kusamalira mabanja awo choyamba, kuti amene alephera kusunga banja lake “wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Kakhalidwe kamasiyanasiyana padziko lonse lapansi, ndipo kuli bwino kusada nkhaŵa mopambanitsa ndi zinthu zakuthupi. “Musandipatse umphaŵi, ngakhale chuma,” anapemphera motero wolemba Miyambo 30:8. Komabe, makolo sayenera kunyalanyaza zofunika zakuthupi za ana awo. Mwachitsanzo, kodi kungakhale kwanzeru kumana dala banja lako zofunika zazikulu pamoyo kuti ulondole maudindo autumiki? Kodi zimenezi sizingakwiyitse ana ako? Miyambo 24:27, m’malo mwake, imati: “Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.” Inde, pamene kuli kwakuti tiyenera kudera nkhaŵa zinthu zakuthupi, ‘kumanga nyumba yako’—mwauzimu ndi mwamaganizo—nkofunika kwambiri.
9. Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kuti mitu ya mabanja ilingalire zakuti ikhoza kufa kapena kudwala?
9 Kodi mwapanga makonzedwe oti banja lanu likasamalidwe mutafa mosayembekezereka? Miyambo 13:22 imati: “Wabwino asiyira zidzukulu zake choloŵa chabwino.” Kuwonjezera pa choloŵa cha chidziŵitso cha Yehova ndi unansi wake, makolo amafuna kuchirikiza ana awo mwakuthupi. M’maiko ambiri mitu yosamala ya mabanja imayesa kusunga ndalama, kugaŵiratu katundu wake mwalamulo, ndi kukhala ndi inshuwalansi. Pajatu anthu a Mulungu nawonso amakumana ndi “nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika.” (Mlaliki 9:11, NW) Ndalama “zichinjiriza,” ndipo kulinganiza bwino nthaŵi zambiri kumapeŵetsa zovuta. (Mlaliki 7:12) Kumaiko kumene boma silimalipirira anthu zakuchipatala, ena angasankhe kupatula ndalama zogwiritsira ntchito pa zathanzi kapena kulinganiza zina zothandiza kusamalira thanzi.a
10. Kodi makolo achikristu ‘angaunjikire’ motani ana awo?
10 Malemba amanenanso kuti: “Ana sayenera kuunjikira atate ndi amayi, koma atate ndi amayi kuunjikira ana.” (2 Akorinto 12:14) Makolo ambiri akudziko amaunjikira ana awo ndalama za maphunziro a mtsogolo ndi ukwati kuti asakavutike pokayamba kudzikhalira okha. Kodi mwaganizapo zounjikira mwana wanu mtsogolo mwauzimu? Mwachitsanzo, tinene kuti mwana wosinkhuka ali mu utumiki wa nthaŵi zonse. Pamene kuli kwakuti atumiki a nthaŵi zonse sayenera kupempha kapena kuyembekezera thandizo la ena, makolo achikondi angasankhe ‘kumpatsa zosoŵa’ kuti amthandize kukhalabe mu utumiki wa nthaŵi zonse.—Aroma 12:13; 1 Samueli 2:18, 19; Afilipi 4:14-18.
11. Kodi kuziona moyenera ndalama kumasonyeza kusoŵa chikhulupiriro? Fotokozani.
11 Kuona ndalama moyenera sikumasonyeza kuti sitikhulupirira kuti mapeto a dongosolo loipa la Satana ali pafupi. Kwangokhala kusonyeza “nzeru yeniyeni” ndi kuona zinthu moyenera. (Miyambo 2:7; 3:21) Nthaŵi ina yake Yesu ananena kuti “ana a nthaŵi ya pansi pano ali anzeru . . . koposa ana a kuunika” mmene amagwiritsirira ntchito ndalama. (Luka 16:8) Ndiye chifukwa chake ena aona kufunika kwa kuwongolera mmene amagwiritsirira ntchito chuma chawo, kuti asamale bwino zosoŵa za mabanja awo.
“Nzeru” Pakaonedwe Kathu ka Maphunziro
12. Kodi Yesu anawaphunzitsa motani ophunzira ake kusintha malinga ndi mikhalidwe yatsopano?
12 “Mkhalidwe wa dzikoli ukusintha,” ndipo zachuma ndi tekinoloji zikusintha mwamsanga kulikonse. (1 Akorinto 7:31, NW) Komabe, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azisintha. Pamene anawatumiza nthaŵi yoyamba kukalalikira anawauza kuti: “Musadzitengere ndalama zagolidi, kapena zasiliva, kapena zakobiri m’malamba mwanu; kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya aŵiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.” (Mateyu 10:9, 10) Komano, nthaŵi ina pambuyo pake, Yesu anati: “Iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe.” (Luka 22:36) Kodi nchiyani chinasintha? Mikhalidwe. Nkhani yachipembedzo inakhala yodanitsa, ndipo iwo tsopano anayenera kudzikonzera zofunika zawo.
13. Kodi cholinga chachikulu cha maphunziro nchiyani, ndipo makolo angawachirikize motani ana awo pankhaniyi?
13 Leronso, mwina makolo angafunikire kulingalira za mkhalidwe weniweni walero wa zachuma. Mwachitsanzo, kodi mwatsimikiza kuti ana anu akulandira maphunziro okwanira? Chifuno chachikulu chamaphunziro chiyenera kukhala kukonzekeretsa wachinyamata kukhala mtumiki wogwira mtima wa Yehova. Ndipo maphunziro ofunika kwambiri pa onse ndiwo maphunziro auzimu. (Yesaya 54:13) Makolo amaderanso nkhaŵa kukhoza kwa ana awo kudzipezera okha ndalama. Choncho atsogozeni ana anu, athandizeni kusankha maphunziro oyenera ku sukulu, ndipo kambitsiranani nawo ngati kuli bwino kapena sikuli bwino kupezanso maphunziro ena owonjezereka. Ndi udindo wa banja kupanga zosankha zimenezi, ndipo ena sayenera kutsutsa njira imene atenga. (Miyambo 22:6) Bwanji za awo amene asankha kuphunzitsira ana awo panyumba?b Pamene kuli kwakuti ambiri achita bwino pamenepa, ena apeza kuti ntchitoyo njovuta kwambiri kuposa mmene ankaganizira, ndipo ana awo avutika. Choncho ngati mukulingalira za kuphunzirira panyumba, tsimikizani kuti mwaŵerengera mtengo wake, kufufuzadi zenizeni ngati maluso ake muli nawo ndipo ngati mukhoza kudzilanga kuti zonse ziyende bwino.—Luka 14:28.
‘Musafune Zinthu Zazikulu’
14, 15. (a) Kodi Baruki anasiya motani kusamala zauzimu? (b) Kodi nchifukwa ninji kunali kopusa kuti iye ‘afune zinthu zazikulu’?
14 Popeza mapeto a dongosolo lino sanafikebe, ena angayambe kumafuna zimene dziko limapereka—ntchito zolemekezeka ndi zopindulitsa kwambiri, ndi chuma. Talingalirani mlembi wa Yeremiya, Baruki. Iye anadandaula nati: “Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova wawonjezera chisoni pa zoŵaŵa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.” (Yeremiya 45:3) Baruki analema. Kutumikira monga mlembi wa Yeremiya kunali ntchito yovuta ndi yopanikiza. (Yeremiya 36:14-26) Ndipo analibe chiyembekezo choti zinthu zidzapepuka. Panali zaka 18 kuti Yerusalemu awonongedwe.
15 Yehova anauza Baruki kuti: “Taonani, chimene ndamanga ndidzapasula, ndi chimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m’dziko lonseli. Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune.” Baruki anasiya kusamala. Anayamba ‘kudzifunira yekha zinthu zazikulu,’ mwinamwake chuma, kutchuka, kapena kukundika katundu. Popeza kuti Yehova anali ‘kuzula m’dziko lonselo,’ kodi kufuna zinthu zimenezo kunali ndi phindu lanji? Motero Yehova anapatsa Baruki chikumbutso chopatsa maganizochi: “Pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, . . . koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati chofunkha m’malo monse mmene mupitamo.” Katundu wakuthupi sanali kudzapyola pachiwonongeko cha Yerusalemu! Yehova anangomtsimikiza za kupulumuka kwa ‘moyo wake monga chofunkha.’—Yeremiya 45:4, 5.
16. Kodi anthu a Yehova lerolino angaphunzirepo phunziro lotani pachokumana nacho cha Baruki?
16 Baruki analandira kuwongolera kwa Yehova, ndipo, mongadi mwa lonjezo la Yehova, Baruki anapulumuka. (Yeremiya 43:6, 7) Ndi phunziro lamphamvu chotani nanga kwa anthu a Yehova lero! Inoyi si nthaŵi ‘yodzifunira tokha zinthu zazikulu.’ Chifukwa? Chifukwa chakuti “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake.”—1 Yohane 2:17.
Kugwiritsira Ntchito Bwino Koposa Nthaŵi Yotsalayi
17, 18. (a) Kodi Yona anatani Anineve atalapa? (b) Kodi Yehova anamphunzitsa phunziro lotani Yona?
17 Ndiye ndi motani mmene tingagwiritsirire ntchito bwino koposa nthaŵi yotsalayi? Tengani phunziro pachokumana nacho cha mneneri Yona. Iye “[a]napita ku Nineve, . . . , nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anayi ndipo Nineve adzapasuka.” Koma Yona anadabwa kuona kuti Anineve analabadira uthenga wake nalapa! Yehova sanawononge mzindawo. Kodi Yona anatani? “Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ayi.”—Yona 3:3, 4; 4:3.
18 Kenako Yehova anaphunzitsa Yona phunziro lofunika kwambiri. Iye “anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake . . . Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo.” Komabe, chikondwerero cha Yona sichinakhalitse popeza chomeracho chinafota mwamsanga. Yona ‘anapsa mtima’ kuti sakupeza bwino. Yehova anagogomezera mfundo yake, nati: “Unachitira chifundo msatsiwo . . . Sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Nineve mudzi waukulu uwu; mmene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi aŵiri osadziŵa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere, ndi zoŵeta zambiri zomwe?”—Yona 4:6, 7, 9-11.
19. Kodi ndi malingaliro odzikonda otani amene tiyenera kupeŵa?
19 Kulingalira kwa Yona kunali kodzikonda chotani nanga! Iye anachitira chisoni chomera, koma sanawachitire chifundo mpang’ono pomwe anthu a ku Nineve—anthu amene, kunena mwauzimu, ‘sanadziŵe kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere.’ Ifenso tingafunitsitse kuti dziko loipali liwonongeke ndipotu pazifukwa zabwino! (2 Atesalonika 1:8) Komabe, pamene tikuyembekezera zimenezo tili ndi ntchito yothandiza anthu oona mtima amene, kunena mwauzimu, “sadziŵa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere.” (Mateyu 9:36; Aroma 10:13-15) Kodi panthaŵi yaifupi yotsalayi mudzathandiza ambiri amene mungathe kupeza chidziŵitso chamtengo wapatali cha Yehova? Kodi ndi ntchito yanji imene ingalingane ndi chimwemwe chopezeka mwa kuthandiza wina kupeza moyo?
Pitirizani Kukhala “Anzeru”
20, 21. (a) Kodi njira zina zimene tingasonyezere “nzeru” m’masiku akutsogolowa nziti? (b) Kodi tidzadalitsidwa motani ngati tikhala “anzeru”?
20 Pamene dongosolo la Satana liyandikirabe chiwonongeko chake, mosakayikira tidzakhala ndi zovuta zatsopano. Timoteo wachiŵiri 3:13 amalosera kuti: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire.” Koma ‘musaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.’ (Ahebri 12:3) Dalirani Yehova kuti akupatseni nyonga. (Afilipi 4:13) Phunzirani kusintha, kusintha malinga ndi mikhalidwe imene ikuipiraipirayi, m’malo moumirira zakale. (Mlaliki 7:10) Gwiritsirani ntchito nzeru yeniyeni, kutsatira mosamalitsa chitsogozo chimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akupereka.—Mateyu 24:45-47.
21 Sitikudziŵa utali wa nthaŵi yotsalayi. Komabe, tinganene mwachidaliro kuti “chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi.” Mpaka chitsirizirocho chitafika, tiyeni tikhale ndi moyo ndi “nzeru” pazimene tichita ndi ena, mmene tisamalirira mabanja athu, ndi pamaudindo athu akuthupi. Mwa kutero, tonsefe tingakhale ndi chidaliro chakuti pomalizira pake tidzapezedwa “mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema”!—2 Petro 3:14.
[Mawu a M’munsi]
a Mwachitsanzo, ku United States ambiri amakhala ndi inshuwalansi ya thanzi, ngakhale kuti imeneyi imadula. Mabanja ena a Mboni apeza kuti madokotala ena amakhala ofunitsitsa kupereka machiritso ena osaloŵetsapo mwazi ngati mabanja ali ndi inshuwalansi ya thanzi. Madokotala ambiri amalandira ndalama yolipidwira inshuwalansi ya machiritso akutiakuti kapena ndalama yolipiridwa ndi boma.
b Kaya wina afuna kumaphunzirira panyumba ili nkhani yaumwini. Onani nkhani yakuti “Kuphunzirira Panyumba—Kodi Kumakuyenererani?,” mu Galamukani! ya April 8, 1993 yachingelezi.
Mfundo Zobwereza
◻ Kodi tingasonyeze motani “nzeru” pamaunansi athu?
◻ Kodi tingasonyeze motani kulinganizika posamalira maudindo athu a m’banja?
◻ Kodi nchifukwa ninji makolo ayenera kusamala za maphunziro akusukulu a ana awo?
◻ Kodi tikutengapo maphunziro otani pa Baruki ndi Yona?
[Chithunzi patsamba 18]
Mwamuna ndi mkazi wake akamachitirana moipa, amawononga unansi wawo ndi Yehova
[Chithunzi patsamba 20]
Makolo ayenera kusamala za maphunziro a ana awo