Mkhalidwe Umene Umakometsera Chiphunzitso cha Mulungu
Posachedwapa, akulu a kampani mu Caracas, Venezuela, analembera kalata akulu ndi atumiki otumikira a mpingo wapafupi wa Mboni za Yehova. Mu iyo iwo analemba motere: “Talandira mapepala a ziyeneretso kwambiri abwino onena za anthu okhala m’chipembedzo chanu okhudza kusamalira kwawo mathayo ndi kuwona mtima. Ndi kaamba ka chifukwa chimenechi chimene takulemberani tsopano. Chifukwa cha kusowa kwathu antchito komwe tiri nako tsopano, tikufuna anthu aŵiri mofulumira kudzalowa ntchito zotsatirazi: mmodzi kudzakhala woyendetsa galimoto ndipo winayo kudzakhala manejala wa nkhokwe yathu yosungiramo zinthu. Tingayamikire kwambiri chidziŵitso chirichonse chimene mungatipatse chokhudza munthu wina wokhala mumpingo mwanu kapena umene uli pafupi nanu. Ife sitikufunadi kulemba ntchito anthu osakhala Mboni. Chonde, tidziŵitseni ngakhale ngati mulibe aliyense kwanuko, popeza kuti tidzayembekezera yankho lanu tisanapange chosankha chirichonse.”
Pamene anapeza kalatayo kunsi kwa chitseko cha Nyumba Yaufumu, mmodzi wa akulu a pampingopo anachezera mwini wa kampaniyo. Mwiniwakeyo anali anagwirapo ntchito ndi Mboni za Yehova kwa zaka 15 ndipo anakumbukira kusakhalapo ndi mavuto aakulu ndi antchito ake omwe anali Mboni. Iye anawatchula kukhala olama maganizo, athayo, owona mtima, ndi antchito akhama. Kenaka anawonjezera kuti: “Ndidziŵa kuti inu simumalekerera olakwa, ndipo mumawachotsa. Ichi chimasonyeza kuti mpingo wanu sumafuna kugwirizana ndi oterowo.”
Mkhalidwe woterowo umakometsera chiphunzitso cha Mulungu. (Tito 2:10) Ichi nchotulukapo cha chikhumbo chenicheni cha kumamatira mwathithithi ku malamulo amakhalidwe abwino ondandalitsidwa m’Baibulo.