Dziŵani Yehova Kupyolera M’mawu Ake
“Koma moyo wosatha ndiuwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—YOHANE 17:3.
1, 2. (a) Kodi ndiliti lomwe lili tanthauzo la “kudziŵa” ndi “chidziŵitso” monga momwe lagwiritsidwira ntchito m’Malemba? (b) Kodi ndizitsanzo zotani zimene zimamveketsa bwino lomwe tanthauzoli?
KUDZIŴA munthu wina monga mnansi chabe kapena kukhala ndi chidziŵitso wamba cha kanthu kena sikumapereka tanthauzo lenileni la mawu akuti “kudziŵa” ndi “chidziŵitso” monga momwe agwiritsiridwa ntchito m’Malemba. M’Baibulo kumeneku kumaloŵetsamo “kachitidwe ka kudziŵa kupyolera mwa chokumana nacho,” chidziŵitso chimene chimasonyeza “unansi wa kudalirana pakati pa anthu.” (The New International Dictionary of New Testament Theology) Zimenezi zimaphatikizapo kudziŵa Yehova kupyolera m’zochita zake zakutizakuti, monga ngati panthaŵi zambiri zolembedwa m’buku la Ezekieli pamene Mulungu anapereka ziweruzo pa anthu ochita zolakwa, akumalengeza kuti: ‘Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Yehova.’—Ezekieli 38:23.
2 Njira zosiyanasiyana zimene liwulo “kudziŵa” ndi “chidziŵitso” lingagwiritsidwiremo ntchito zingamveketsedwe bwino ndi zitsanzo zingapo. Pamene Yesu anati, “Sindinakudziŵani inu” kwa anthu ambiri odzinenera kukhala atachita ntchito m’dzina lake; anatanthauza kuti iye analibe nawo chochita. (Mateyu 7:23) Pa 2 Akorinto 5:21 pamati Kristu “sanadziŵa uchimo.” Kumeneku sikumatanthauza kuti sanadziŵe konse uchimo, koma kuti iye sanaloŵe muuchimo. Mofananamo, pamene Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndiuwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma,” zambiri zinaloŵetsedwamo kuposa chabe kudziŵa kanthu kena ponena za Mulungu ndi Kristu.—Yerekezerani ndi Mateyu 7:21.
3. Kodi nchiyani chimene chimatsimikiza kuti Yehova amasonyeza chizindikiro cha kukhala kwake Mulungu wowona?
3 Mikhalidwe yambiri ya Yehova ingadziŵidwe kupyolera m’Mawu ake, Baibulo. Umodzi wamkhalidwewo ndiwo kukhoza kwake kulosera molondola. Luso limeneli limadziŵikitsidwa kukhala chizindikiro cha Mulungu wowona: “Azitulutse, atitchulire ife, chimene chidzaoneka; tchulani inu zinthu zakale, zinali zotani, kuti ife tiganizire pamenepo, ndi kudziŵa mamaliziro awo; kapena tionetseni ife zinthu zimene zilinkudza. Tchulani zinthu zimene zilinkudza mtsogolo, kuti ife tidziŵe kuti inu ndinu milungu.” (Yesaya 41:22, 23) M’Mawu ake, Yehova amasimba za zinthu zoyambirira zonena za chilengedwe cha dziko lapansi ndi moyo pa ilo. Iye ananeneratu pasadakhale za zinthu zimene zidzachitika mtsogolo ndi zimene zinachitikadi. Ndipo ngakhale tsopano iye ‘amationetsa ife zinthu zimene zilinkudza,’ makamaka zinthu zoti zichitike ‘m’masiku ano otsiriza.’—2 Timoteo 3:1-5, 13; Genesis 1:1-30; Yesaya 53:1-12; Danieli 8:3-12, 20-25; Mateyu 24:3-21; Chivumbulutso 6:1-8; 11:18.
4. Kodi ndimotani mmene Yehova wagwiritsira ntchito mkhalidwe wake wa mphamvu, ndipo adzaugwiritsira ntchito motani?
4 Mkhalidwe wina wa Yehova ndiwo mphamvu. Njowonekera bwino kuthambo kumene nyenyezi zomachita monga ng’anjo zoyatsidwa zimatulutsa kuunika ndi kutentha. Pamene anthu kapena angelo opanduka anyoza ulamuliro wa Yehova, iye amagwiritsira ntchito mphamvu yake monga “wankhondo,” akumatetezera dzina lake labwino ndi miyezo yolungama. Pazochitika zotero samazengereza kutulutsa mphamvuyo mowononga, monga momwe zinaliri m’nthaŵi ya Chigumula cha Nowa, m’chiwonongeko cha Sodomu ndi Gomora, ndi pakulanditsidwa kwa Israyeli pa Nyanja Yofiira. (Eksodo 15:3-7; Genesis 7:11, 12, 24; 19:24, 25) Posachedwa, Mulungu adzagwiritsira ntchito mphamvu yake ‘kuphwanyira Satana pansi pa mapazi anu.’—Aroma 16:20.
5. Kuwonjezera pamphamvu yake, kodi ndimkhalidwe wotaninso umene Yehova ali nawo?
5 Komabe, ngakhale kuti ali ndi mphamvu yonseyi yopanda malire, pali kudzichepetsa. Pa Salmo 18:35, 36 (NW) pamati: “Kudzichepetsa kwa inu mwini kudzandikuza ine. Mudzakuza bwinobwino malo opondapo mapazi anga.” Kudzichepetsa kwa Mulungu kumamloleza ‘kudzitsitsa kuti apenye thambo ndi dziko lapansi, akumautsa wosauka kumchotsa kufumbi; amakweza waumphaŵi kumchotsa kudzala.’—Salmo 113:6, 7.
6. Kodi ndimikhalidwe yotani ya Yehova imene ili yopulumutsa moyo?
6 Chifundo cha Yehova pochita ndi anthu nchopulumutsa moyo. Ndichifundo chotani nanga chimene chinasonyezedwa kwa Manase pamene anakhululukidwa, ngakhale kuti anali atapalamula milandu yowopsa! Yehova amati: “Ndipo ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu: koma akabwerera iye kuleka tchimo lake, nakachita choyenera ndi cholungama; zoipa zake zilizonse anazichita sizidzakumbukika zimtsutse, anachita choyenera ndi cholungama, adzakhala ndi moyo ndithu.” (Ezekieli 33:14, 16; 2 Mbiri 33:1-6, 10-13) Yesu anali kusonyeza mkhalidwe wa Yehova pamene anafulumiza kukhululukira nthaŵi 77, ngakhaledi nthaŵi 7 patsiku limodzi!—Salmo 103:8-14; Mateyu 18:21, 22; Luka 17:4.
Mulungu Wokhudzidwa Mtima
7. Kodi Yehova ngwosiyana motani ndi milungu ya Agiriki, ndipo kodi ndimwaŵi wotani umene uli wotitsegukira?
7 Anthanthi Achigiriki, monga ngati Aepikureya, anakhulupirira milungu koma anaiwona kukhala yotalikirana kwambiri ndi dziko lapansi yosakondweretsedwa ndi anthu kapena kuyambukiridwa ndi malingaliro awo. Ngwosiyana chotani nanga unansi umene ulipo pakati pa Yehova ndi Mboni zake zokhulupirika! “Yehova akondwera nawo anthu ake.” (Salmo 149:4) Anthu oipa okhalapo Chigumula chisanadze anamumvetsa chisoni ndi ‘kuvutika mumtima mwake.’ Chifukwa cha kusakhulupirika kwake, Israyeli anavutitsa mtima wa Yehova. Chifukwa cha kusamvera kwawo, Akristu angamvetse chisoni mzimu wa Yehova; komabe, mwa kukhulupirika kwawo angamsangalatse. Nkodabwitsa chotani nanga kuganiza kuti munthu wochepa mphamvu padziko lapansi angachititse Mlengi wachilengedwe chonse kuvutika maganizo kapena kusangalala! Polingalira zinthu zonse zimene amatichitira, nkosangalatsa chotani nanga kuti ife tili ndi mwaŵi wa kumkondweretsa!—Genesis 6:6; Salmo 78:40, 41; Miyambo 27:11; Yesaya 63:10; Aefeso 4:30.
8. Kodi ndimotani mmene Abrahamu anagwiritsira ntchito ufulu wake wa kulankhula ndi Yehova?
8 Mawu a Mulungu amasonyeza kuti chikondi cha Yehova chimatipatsa “ufulu wa kulankhula.” (1 Yohane 4:17, NW) Tatengani nkhani ya Abrahamu pamene Yehova anadza kudzawononga Sodomu. Abrahamu anati kwa Yehova: “Kodi mudzawononga olungama pamodzi ndi oipa? Kapena alipo olungama makumi asanu mkati mwa mudzi; kodi mudzawononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo? . . . Musamatero ayi; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?” Ndimawu otani nanga amenewo kuti munthu anene kwa Mulungu! Komabe Yehova anavomereza kupulumutsa Sodomu ngati anthu olungama 50 anali mumzindawo. Abrahamu anapitirizabe kunena nafika pachiŵerengero chotsika kuchokera pa 50 kufika pa 20. Iye anayamba kukayikira kuti mwina angakhale anali kumuumiriza mopambanitsa. Iye anati: “Asakwiyetu [Yehova, NW], ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m’menemo?” Kachiŵirinso Yehova akuvomereza kuti: “Sindidzachita chifukwa cha khumi.”—Genesis 18:23-33.
9. Kodi nchifukwa ninji Yehova analola Abrahamu kulankhula monga momwe anachitiramo, ndipo kodi tingaphunzirenji pazimenezi?
9 Kodi nchifukwa ninji Yehova analola Abrahamu kukhala ndi ufulu wa kulankhula wakuti alankhule motere? Choyamba, Yehova anali kuzindikira mtima wa Abrahamu wovutikawo. Iye anadziŵa kuti Loti mwana wamphwake wa Abrahamu anali kukhala mu Sodomu, ndipo Abrahamu anadera nkhaŵa za kutetezereka kwake. Ndiponso, Abrahamu anali bwenzi la Mulungu. (Yakobo 2:23) Pamene munthu wina alankhula nafe mwaukali, kodi timayesa kudziŵa chochititsa kukalipako ndi kuchita kuti pakhale mtendere, makamaka ngati munthuyo ali bwenzi limene lapanikizika maganizo ndi kanthu kena? Kodi sikuli kotonthoza kudziŵa kuti Yehova amamvetsetsa kugwiritsira ntchito kwathu ufulu wa kulankhula monga momwe anachitira kwa Abrahamu?
10. Kodi ufulu wa kulankhula umatithandiza motani m’pemphero?
10 Makamaka pamene timfunafuna monga “Wakumva pemphero” wathu mpamene timakhumba ufulu wa kulankhula umenewu kuti timuuze zakukhosi kwathu, pamene tili achisoni kwambiri ndi opsinjika mtima. (Salmo 51:17; 65:2, 3) Ngakhale panthaŵi zimene timalephera kunena mawu, ‘mzimu . . . umatipempherera ndi zobuula zosatha kuneneka,’ ndipo Yehova amamvetsera. Iye amadziŵa malingaliro athu: “Muzindikira lingaliro langa muli kutali. Pakuti asanafike mawu palilime langa, tawonani, Yehova, muwadziŵa onse.” Ngakhale zili choncho, tiyenera kupitirizabe kupempha, kufunafuna, ndi kugogoda.—Aroma 8:26; Salmo 139:2, 4; Mateyu 7:7, 8.
11. Kodi timadziŵa motani kuti Yehova amatisamaladi?
11 Yehova amasamala. Amagaŵira zofunika za moyo umene analenga. “Maso a onse ayembekeza inu; ndipo muwapatsa chakudya chawo m’nyengo zawo. Muoloŵetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” (Salmo 145:15, 16) Tikupemphedwa kuwona mmene amadyetsera mbalame zakuthengo. Onani akakombowo m’munda, mmene amawavekera mokongola. Yesu anawonjezera kuti Mulungu adzatichitira zochuluka koposa zimene amachitira zinthu zimenezi. Chotero kodi nchifukwa ninji tiyenera kuda nkhaŵa? (Deuteronomo 32:10; Mateyu 6:26-32; 10:29-31) Lemba la 1 Petro 5:7 limakupemphani “kutaya pa iye nkhaŵa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.”
“Chizindikiro Chenicheni cha Chikhalidwe Chake”
12, 13. Kuwonjezera pakuwona Yehova kupyolera mwa chilengedwe chake ndi zochita zake zolembedwa m’Baibulo, kodi tingamuwonenso ndi kumumva motani?
12 Tikhoza kuwona Yehova Mulungu kupyolera m’chilengedwe chake; tingathe kumuwona mwa kuŵerenga zochita zake m’Baibulo; tingathenso kumuwona mwa mawu ndi ntchito zolembedwa zonena za Yesu Kristu. Yesu mwiniyo amatero, pa Yohane 12:45: “Ndipo wondiwona ine awona amene anandituma ine.” Kachiŵirinso, pa Yohane 14:9 iye amati: “Iye amene wandiwona ine wawona Atate.” Pa Akolose 1:15 pamati: “[Yesu] amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo.” Lemba la Ahebri 1:3 limalengeza kuti: “Ameneyo [Yesu], . . . ndichizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake.”
13 Yehova anatumiza Mwana wake osati kudzangopereka dipo komanso kudzapereka chitsanzo choti chitsanziridwe, ponse paŵiri m’mawu ndi m’zochita. Yesu analankhula Mawu a Mulungu. Pa Yohane 12:50 iye anati: “Zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi ine, momwemo ndilankhula.” Sanachite zinthu za iye mwini, koma anachita zinthu zimene Mulungu anamuuza kuchita. Pa Yohane 5:30 iye anati: “Sindikhoza kuchita kanthu kwa ine ndekha.”—Yohane 6:38.
14. (a) Kodi ndizinthu zotani zimene zinachititsa Yesu kusonkhezeredwa kuchita chifundo? (b) Kodi nchifukwa ninji njira ya Yesu yokambira zinthu inachititsa anthu kudzamumvetsera?
14 Yesu anawona anthu amene anali akhate, opunduka, ogontha, akhungu, ndi ogwidwa ndi ziŵanda ndi awo amene analira akufa awo. Posonkhezeredwa ndi chifundo, anachiritsa odwala ndi kuukitsa akufa. Iye anawona makamu okambululudwa ndi omwazikana mwauzimu, ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri. Anaphunzitsa osati ndi mawu okha oyenera komanso ndi mawu achisomo kuchokera mumtima mwake amene analoŵa mwachindunji m’mitima ya ena, anawakokera pafupi naye, anawachititsa kufika mwamsanga kukachisi kudzamumvetsera, anawachititsa kumtsatirabe, kumumvetsera mokondwa. Anasonkhana kudzamumva, akumalengeza kuti “palibe munthu analankhula chotero.” Ndipo anazizwa ndi njira yake yophunzitsira. (Yohane 7:46; Mateyu 7:28, 29; Marko 11:18; 12:37; Luka 4:22; 19:48; 21:38) Ndipo pamene adani ake anafunafuna kumkola ndi mafunso, anachititsa zinthu kuwatembenukira, akumawatontholetsa.—Mateyu 22:41-46; Marko 12:34; Luka 20:40.
15. Kodi mutu waukulu wa kulalikira kwa Yesu unali wotani, ndipo analoŵetsamo ena kuulengeza kufikira kuti?
15 Iye analengeza kuti “tembenukani mitima, pakuti ufumu wa kumwamba [unali utayandikira]” ndi kufulumiza ena kupitirizabe ‘kufunafuna ufumu choyamba.’ Anatumiza ena kukalalikira kuti “ufumu wa kumwamba [unali utayandikira],” ‘kukapanga ophunzira mwa anthu amitundu yonse,’ kukhala mboni za Kristu “kufikira kumadera akutali a dziko lapansi.” Lerolino Mboni za Yehova pafupifupi mamiliyoni anayi ndi theka zikuyenda m’mapazi ake, zikumachita zinthu zimenezo.—Mateyu 4:17; 6:33; 10:7; 28:19; Machitidwe 1:8, NW.
16. Kodi ndimotani mmene mkhalidwe wa Yehova wa chikondi unayesedwera koposa, koma kodi unatheketsa chiyani ku mtundu wa anthu?
16 “Mulungu ndiye chikondi,” timauzidwa motero pa 1 Yohane 4:8. Mkhalidwe wake wapadera umenewu unaikidwa pachiyeso chomvetsa ululu wosalingalirika konse pamene anatumiza Mwana wake wobadwa yekha padziko lapansi kudzafa. Ululu umene Mwana wokondedwa ameneyu anamva ndi madandaulo amene anapereka kwa Atate wake wakumwamba ziyenera kukhala zitampweteka ndi kumumvetsa chisoni Yehova, ngakhale kuti Yesu anatsimikizira chinenezo cha Satana chakuti Yehova sangakhale ndi anthu padziko lapansi amene angamamatire paumphumphu wawo kwa Iye pakuyesedwa kowopsa kukhala chonama. Tiyeneranso kuzindikira ukulu wa nsembe ya Yesu, pakuti Mulungu anamtumiza pansi pano kudzatifera. (Yohane 3:16) Imeneyitu sinali imfa yochitika mosavuta ndi mwamsanga. Kuti tizindikire bwino lomwe mmene Mulungu ndi Yesu yemwe anavutikira ndipo motero kuzindikira ukulu wa nsembe yake kaamba ka ife, tiyeni tipende cholembedwa cha Baibulo chonena za zimene zinachitika.
17-19. Kodi ndimotani mmene Yesu anafotokozera mavuto amene anali kumuyembekezera?
17 Yesu anafotokozera atumwi ake pafupifupi nthaŵi zinayi ponena za zimene zidzachitika. Masiku oŵerengeka okha zimenezo zisanachitike, iye anati: “Tawonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka iye kwa anthu a mitundu; ndipo adzamnyoza iye, nadzamthira malovu, nadzamkwapula iye, nadzamupha.”—Marko 10:33, 34.
18 Yesu anavutika mtima ndi zimene zinali kumuyembekezera, akumadziŵa bwino za kuopsa kwa mikwapulo Yachiroma. Timikwamba tachikopa ta chikoti chokwapuliracho tinasomekedwa ndi tizidutswa tachitsulo ndi tamafupa a nkhosa; chotero pamene kukwapulako kunali kuchitika, msana wa munthu ndi miyendo inali kutemekatemeka ndi kuchucha mwazi. Miyezi ingapo pasadakhale, Yesu anasonyeza kuvutika mtima kumene anali nako ndi zimene zinali kumuyembekezera, monga momwe timaŵerengera pa Luka 12:50 kuti: “Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nawo; ndipo ndikanikizidwa ine kufikira ukatsirizidwa!”
19 Kupanikizikako kunakula pamene nthaŵiyo inayandikira. Iye ananena za zimenezi kwa Atate wake wakumwamba kuti: “Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni ine kunthaŵi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthaŵi iyi.” (Yohane 12:27) Yehova ayenera kukhala atayambukiridwa kwambiri chotani nanga ndi kudandaula kumeneku kwa Mwana wake wobadwa yekha! Mu Getsemane, patatsala maola angapo imfa yake isanachitike, Yesu anavutika mtima kwambiri nati kwa Petro, Yakobo, ndi Yohane: “Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa.” Mphindi zoŵerengeka pambuyo pake anapereka pemphero lotsiriza pankhaniyo kwa Yehova kuti: “Atate, mukafuna inu, chotsani chikho ichi pa ine; koma sikufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike. Ndipo pokhala iye m’chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.” (Mateyu 26:38; Luka 22:42, 44) Mwinamwake kuchita thukuta kumeneku kungakhale kumene madokotala amadziŵa kukhala hematidrosis. Sikumachitika kaŵirikaŵiri koma kungachitike popsinjika mtima kwambiri.
20. Kodi nchiyani chimene chinathandiza Yesu kupirira mavuto ake?
20 Ponena za nthaŵi imeneyi mu Getsemane, lemba la Ahebri 5:7 limati: “M’masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu.” Popeza kuti sanapulumutsidwe muimfa ndi “Iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa,” kodi pemphero lake linamveka m’lingaliro lotani? Pa Luka 22:43 pamayankha kuti: “Ndipo anamuonekera iye mngelo wa kumwamba namlimbitsa iye.” Pempherolo linayankhidwa pamene mngelo amene Mulungu anatumiza analimbikitsa Yesu kupirira zovutazo.
21. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Yesu anapambana pamavutowo? (b) Pamene mayeso athu akula, kodi tidzafuna kulankhula motani?
21 Zimenezi zinaoneka bwino pazimene zinatsatirapo. Pamene kuvutika mtima kwake kunatha, Yesu ananyamuka, nabwerera kwa Petro, Yakobo, ndi Yohane, nanena kuti: “Ukani, tizimuka.” (Marko 14:42) Kwenikweni iye anali kunena kuti, ‘Ndilekeni ndimke kukaperekedwa mwa kumpsompsonedwa, kukagwidwa ndi khamu lachiwawa, kukaimbiwa mlandu mosayenera, kukaweruzidwa molakwa. Ndilekeni ndimke kukanyozedwa, kukalavuliridwa malovu, kukakwapulidwa, ndi kukhomeredwa pamtengo wozunzirapo.’ Kwa maola asanu ndi limodzi anali pachikike pamenepo, akumamva ululu waukulu, napirira kufikira mapeto. Pamene anali kufa, anafuula mwachipambano kuti: “Kwatha.” (Yohane 19:30) Anakhalabe wolimba nji ndipo anasonyeza umphumphu wake kuchilikiza ulamuliro wa Yehova. Kanthu kalikonse kamene Yehova anali atamtuma kukachita padziko lapansi anali atakachita. Pamene tifa kapena pamene Armagedo ikantha, kodi tidzakhala okhoza kunena kuti: “Kwatha” ponena za ntchito yathu ya kwa Yehova?
22. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza ukulu wa kufalikira kwa kudziŵa Yehova?
22 Mulimonse mmene zingakhalire, tingakhale otsimikiza kuti m’nthaŵi yokwanira ya Yehova imene ikuyandikira msanga, “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi kudziŵa ndi kukhala ndi chidziŵitso kumatanthauzanji?
◻ Kodi ndimotani mmene chifundo cha Yehova ndi chikhululukiro zasonyezedwera kwa ife m’Mawu ake?
◻ Kodi ndimotani mmene Abrahamu anagwiritsira ntchito ufulu wa kulankhula ndi Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji tingayang’ane kwa Yesu ndipo kupyolera mwa iye kuwona mikhalidwe ya Yehova?