Danieli
8 Mʼchaka chachitatu cha ulamuliro wa Mfumu Belisazara,+ ineyo Danieli ndinaona masomphenya pambuyo pa masomphenya amene ndinaona poyamba aja.+ 2 Ndikuona masomphenyawo ndinapezeka kuti ndili kunyumba yachifumu* ku Susani,+ imene ili mʼchigawo cha Elamu.+ Ndinaona masomphenyawa kuti ndinali mʼmphepete mwa mtsinje wa Ulai. 3 Nditayangʼana ndinaona nkhosa yamphongo+ itaima pafupi ndi mtsinjewo ndipo inali ndi nyanga ziwiri.+ Nyanga ziwirizi zinali zazitali koma imodzi, imene inamera pomalizira, inali yaitali kuposa inzake.+ 4 Ndinaona nkhosa yamphongoyo ikuukira adani ake kumadzulo, kumpoto ndi kumʼmwera ndipo palibe zilombo zakutchire zimene zinalimbana nayo komanso palibe amene akanakwanitsa kupulumutsa aliyense ku mphamvu zake.*+ Nkhosayo inkachita zofuna zake ndipo inkadzitama kwambiri.
5 Ndikupitiriza kuyangʼana, ndinaona mbuzi yamphongo+ ikuchokera kumadzulo* kudutsa padziko lonse lapansi koma sinkaponda pansi. Pakati pa maso a mbuziyo panali nyanga yoonekera patali.+ 6 Mbuziyo inkabwera kumene kunali nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri ija, imene ndinaiona itaima pafupi ndi mtsinje. Inkathamangira kumene kunali nkhosayo itakwiya kwambiri.
7 Ndinaona mbuziyo ikufika pafupi kwambiri ndi nkhosa yamphongoyo ndipo inakwiyira kwambiri nkhosayo. Kenako inagunda nkhosayo nʼkuthyola nyanga zake ziwiri, ndipo nkhosayo inalibe mphamvu zotha kulimbana nayo. Mbuziyo inagwetsera pansi nkhosayo nʼkuipondaponda ndipo panalibe woti aipulumutse ku mphamvu za* mbuziyo.
8 Kenako mbuzi yamphongoyo inayamba kudzitukumula mopitirira muyezo. Koma itangokhala yamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoledwa. Pamene panali nyangayo panamera nyanga 4 zoonekera patali ndipo zinaloza kumphepo 4 zakumwamba.+
9 Imodzi mwa nyanga zimenezi inatulutsa nyanga ina yaingʼono ndipo mphamvu zake zinachuluka kwambiri moti zinafika kumʼmwera, kumʼmawa* ndi ku Dziko Lokongola.+ 10 Inakula kwambiri mpaka inakafika kwa gulu lakumwamba, moti inachititsa kuti ena amʼgululi komanso nyenyezi zina zigwere padziko lapansi ndipo inazipondaponda. 11 Nyangayo inadzitukumula ngakhale pamaso pa Kalonga wa gululo. Inachititsa kuti nsembe imene inkaperekedwa nthawi zonse kwa Kalongayo isamaperekedwenso ndipo malo opatulika amene iye anakhazikitsa anagwetsedwa.+ 12 Chifukwa cha uchimo, gulu lakumwamba lija limodzi ndi nsembe imene inkaperekedwa nthawi zonse zinaperekedwa kwa nyangayo ndipo inapitiriza kugwetsera choonadi pansi. Nyangayo inkachita zofuna zake ndipo inapambana.
13 Ndiyeno ndinamva mngelo akulankhula ndipo mngelo wina anafunsa mngelo amene ankalankhulayo kuti: “Kodi masomphenya okhudza nsembe imene inkaperekedwa nthawi zonse komanso tchimo lobweretsa chiwonongeko apitiriza kuchitika kwa nthawi yaitali bwanji+ nʼkumachititsa kuti malo opatulika komanso gululo lizipondedwapondedwa?” 14 Iye anandiuza kuti: “Mpaka nsembe za tsiku ndi tsiku zokwana 2,300, zamadzulo ndi zamʼmawa, zitadutsa. Kenako malo opatulika adzakonzedwanso kuti akhale ngati mmene analili poyamba.”
15 Ndiyeno pamene ineyo Danieli ndinkaona masomphenyawo nʼkumawaganizira kuti ndiwamvetse, mwadzidzidzi ndinaona winawake wooneka ngati munthu ataima patsogolo panga. 16 Kenako ndinamva mawu a munthu kuchokera pakati pa mtsinje wa Ulai.+ Iye anaitana kuti: “Gabirieli,+ munthuyo umuthandize kuti amvetsetse zimene waona.”+ 17 Choncho iye anabwera pafupi ndi pamene ine ndinaima. Koma atafika, ndinachita mantha kwambiri ndipo ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi. Ndiyeno anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, dziwa kuti masomphenyawa ndi okhudza nthawi yamapeto.”+ 18 Koma akulankhula nane, ndinagona pansi chafufumimba nʼkugona tulo tofa nato. Ndiyeno iye anandigwira nʼkundiimiritsa pamalo omwe ndinaima aja.+ 19 Kenako anandiuza kuti: “Ine ndikudziwitsa zimene zidzachitike kumapeto kwa nthawi yopereka chiweruzo, chifukwa masomphenyawo adzakwaniritsidwa pa nthawi yoikidwiratu yamapeto.+
20 Nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri imene unaona, ikuimira mfumu ya Mediya ndi mfumu ya Perisiya.+ 21 Mbuzi yamphongo yaubweya wambiri ikuimira mfumu ya Girisi,+ ndipo nyanga yaikulu imene inali pakati pa maso ake ikuimira mfumu yoyamba.+ 22 Koma nyanga imene inathyoka ija ndipo mʼmalomwake nʼkumera zina 4,+ zikuimira maufumu 4 ochokera mu mtundu wake amene adzalamulire, koma sadzakhala ndi mphamvu ngati zake.
23 Kumapeto kwa ufumu wawo, zochita za anthu ochimwawo zikadzafika pachimake, mfumu yooneka mochititsa mantha ndiponso yomvetsa zinthu zovuta kumva idzayamba kulamulira. 24 Mphamvu za mfumuyo zidzachuluka, koma si iye amene adzachititse zimenezi. Idzawononga zinthu zambiri moti idzadabwitsa anthu. Chilichonse chimene mfumuyo izidzachita chizidzaiyendera bwino. Idzawononga anthu amphamvu ndi anthu oyera.+ 25 Mochenjera idzachita zinthu mwachinyengo kuti zinthu ziiyendere bwino ndipo idzadzitukumula kwambiri mumtima mwake. Pa nthawi yamtendere* idzawononga anthu ambiri. Mfumuyo idzalimbana ngakhale ndi Kalonga wa akalonga, koma idzathyoledwa osati ndi dzanja la munthu.
26 Zinthu zimene zanenedwa mʼmasomphenya zokhudza nsembe zamadzulo ndi zamʼmawa zija ndi zoona. Koma iweyo usunge masomphenyawo mwachinsinsi, chifukwa akunena zimene zidzachitike mʼtsogolo patapita masiku ambiri.”+
27 Ndiyeno ineyo Danieli ndinatopa kwambiri ndipo ndinadwala kwa masiku angapo.+ Kenako ndinadzuka nʼkugwira ntchito imene mfumu inandipatsa.+ Koma ndinadabwa kwambiri ndi zimene ndinaona ndipo palibe amene akanazimvetsa.+