Tsatirani Mfundo za M’Baibulo Kuti Mupeze Chimwemwe
INU mwaonapo mphaka ali mtulo, atadzipinda bwinobwino n’kumaliza nkonono. Mphakayo amachita kuonekeratu kuti akusangalala nawo moyo. Zingakhale bwino kwambiri ngati nafenso titadzipinda ngati mphakayo n’kumamva mmene iyeyo akumvera. Komano anthu ambiri amavutika kupeza chimwemwe, ndipo akachipeza sichichedwa kutha. N’chifukwa chiyani zili choncho?
N’chifukwa choti nthawi zambiri kupanda ungwiroku kumatichititsa zinthu zambiri zolakwika, ndipo timafunikiranso kupirira zophophonya za anthu ena. Komanso tikukhala m’nyengo imene Baibulo limaitcha kuti “masiku otsiriza,” yomwe ili yodziwika ndi “nthawi zowawitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Ngakhale kuti mwina tili ana timakumbukira kuti nthawi inayake tinkasangalala, ambirife timakumana ndi mavuto osaneneka chifukwa cha “nthawi zowawitsa” zimenezi. Kodi n’zotheka kupeza chimwemwe masiku ano?
Onani kuti Malemba sati nthawi zino ndi zosatheka kukhalamo koma amati ndi zowawitsa. Tingathe kupirira m’nthawi zino potsatira mfundo za m’Baibulo. Sikuti tikatero ndiye kuti mavuto athu tizithana nawo nthawi zonse, komabe tingathe kumakhala achimwemwe ndithu. Tiyeni tionepo mfundo zitatu.
Dziwani Kuti Pali Zinthu Zina Zimene Simungathe Kuchita
Kuti tikhale achimwemwe, tiyenera kudziwa kuti pali zinthu zina zimene ifeyo ndiponso anthu ena sangathe kuchita. M’kalata imene analembera Aroma, mtumwi Paulo anati: “Onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Zinthu zambiri zokhudza ulemerero wa Yehova n’zozama kwambiri moti sitingathe kuzimvetsa. Chitsanzo ndicho mfundo yotchulidwa pa Genesis 1:31, yakuti: “Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” Yehova akaganiza zoyang’ana chilichonse chimene anapangapo m’mbuyomu, nthawi zonse amati “zinali zabwino ndithu.” Koma palibe munthu amene anganene choncho nthawi zonse pa zochita zake. Motero njira yoyamba yokhalira achimwemwe ndiyo kudziwa kuti pali zinthu zina zimene ifeyo sitingathe. Koma si zokhazo ayi. Tiyeneranso kumvetsetsa ndi kuvomereza mmene Yehova amaonera nkhaniyi.
Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “tchimo” amachokera ku liwu limene limatanthauza “kuphonya.” (Aroma 3:9) Mwachitsanzo: Taganizirani za munthu amene akufuna kuwina mphoto polasa malo enaake ndi muvi. Iyeyu ali ndi mivi itatu. Akuponya muvi umodziwo ndipo akuphonya malowo ndi masentimita 100. Ndiye akupenda mosamala n’kuponya muvi wachiwiriwo koma akuphonyabe ndi masentimita 30. Kenaka akuchalira bwinobwino, ndipo akuponya muvi wotsirizawo n’kupezeka kuti wangophonya ndi masentimita awiri basi. Inde, anangotsala pang’ono kulasa malowo koma kuphonya n’kuphonya basi.
Tonsefe tili ngati munthu woponya miviyu. Nthawi zina zimaoneka kuti “taphonya” kwambiri. Nthawi zina timayesetsa ndithu, koma timaphonyabe basi. Timakhumudwa chifukwa choti tinayesetsa kwambiri, komabe sitinafikepo ayi. Tsopano tiyeni tibwerere ku chitsanzo cha woponya mivi uja.
Iye waphonya muvi wotsiriza uja ndiye akutembenuka pang’onopang’ono ali wokhumudwa chifukwa choti mphotoyo anaifunitsitsa kwambiri. Kenaka akudabwa kuti mkulu wa mpikisanowo akum’bweza mwadzidzidzi, n’kumupatsa mphoto ija, amvekere: “Ndikufuna ndikupatsebe mphotoyi chifukwa choti wandisangalatsa, ndipo ndaona kuti unachita khama kwambiri.” Pamenepa woponya mivi uja akusangalala zedi.
Chimwemwe chake chikuchita kusefukira. Munthu aliyense amene Mulungu adzam’patse “mphatso” ya moyo wosatha wangwiro adzamva chimodzimodzi. (Aroma 6:23) Kuchokera pamenepo, chilichonse chimene azidzachita chizidzakhala chabwino basi, sadzaphonyanso ayi. Nthawi zonse azidzakhala wachimwemwe chodzaza tsaya. Koma pakali pano kuona zinthu m’njira imeneyi kungatithandize kukhala osangalala ndi zochita zathu ndiponso za anzathu.
Zindikirani Kuti Chilichonse Chimatenga Nthawi
N’zosachita kufunsa kuti chilichonse chimatenga nthawi. Komabe, kodi munaona mmene zimavutira kukhala wachimwemwe chinachake chikamachedwa kuchitika kapena vuto linalake likamachedwa kutha? Komatu pali anthu ena amene akhalabe achimwemwe m’nthawi zoterezi. Taganizirani chitsanzo cha Yesu.
Asanabwere padziko lapansi pano, Yesu anali chitsanzo cha munthu womvera kwambiri. Komabe padziko pano m’pamene “anaphunzira kumvera.” Anatero motani? Anatero “ndi izi adamva kuwawa nazo.” Kumwambako ankangoona anthu akuvutika koma iyemwini anali asanavutikepo. Ali padziko lapansi, makamaka kuchokera pa ubatizo wake mu Yordano kufika pa imfa yake pa Gologota, iye anakumana ndi zovuta zambiri. Sitikudziwa mwatsatanetsatane kuti Yesu “anakonzeka wamphumphu” m’njira yotani kuti aphunzire kumvera, koma tikudziwa kuti zinatenga nthawi ndithu.—Ahebri 5:8, 9.
Yesu anakwanitsa kutero chifukwa choti ankasinkhasinkha za “chimwemwe choikidwacho pamaso pake,” kapena kuti mphoto ya kukhulupirika kwake. (Ahebri 12:2) Komabe, nthawi zina iye “anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi.” (Ahebri 5:7) Nthawi zina ifenso tingapezeke kuti tikupemphera choncho. Kodi Yehova amaona bwanji tikamatero? Vesi yomweyi imasonyeza kuti Yehova ‘anamva’ pemphero la Yesu. Mulungu adzamvanso pemphero lathulo. Chifukwa chiyani?
Chifukwa choti Yehova amadziwa zimene sitingathe kuchita ndipo amatithandiza. Aliyense ali ndi malire ake a kupirira. Anthu a ku Benin, ku Africa kuno, ali ndi mwambi wakuti: “Madzi akanyanya kuchuluka amamiza ngakhale chule amene.” Yehova amadziwa kuposa ifeyo kuti tatsala pang’ono kufika pa mapeto a malire athu a kupirira. Mwachikondi iye amatipatsa “chifundo ndi . . . chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa,” kapena kuti nthawi yoyenerera. (Ahebri 4:16) Anatero ndi Yesu ndiponso ndi anthu ena ambirimbiri. Taganizirani mmene Monica anathandizidwira m’njira imeneyi.
Monika anakulira moyo wopanda mavuto ambiri, ndipo anali mtsikana wathanzi labwino komanso wansangala. Koma mu 1968, asanakwanitse n’komwe zaka 25, anauzidwa nkhani yofoola kwambiri yoti amupeza ndi matenda enaake amene nthawi zambiri amapha ziwalo zina za thupi. Moyo wake unasinthiratu ndi matendawa ndipo anafunika kusintha zinthu zambiri pochita utumiki wake wa nthawi zonse. Monika anadziwa kuti matenda akewa akhala nawo kwa nthawi yaitali. Patatha zaka 16, iye anati: “Mankhwala a matenda angawa sanapezekebe ndipo n’zotheka kuti sapezeka mpaka pamene dongosolo latsopano la Mulungu lidzasinthe zinthu zonse n’kuzisandutsa zatsopano.” Iye ananena kuti wavutika kwambiri ndi matendawa: “Ngakhale kuti anzanga amanena kuti ndakhalabe wosangalala kwa nthawi yonseyi ndiponso kuti sindinasinthe ngakhale pang’ono, . . . anzanga apamtima amadziwa kuti nthawi zina ndimalira zedi, misozi kuchita kuti chuchuchu.”
Komabe iye anati: “Ndaphunzira kuleza mtima ndi kusangalala ngakhale ndikangoona kuti ndayamba kupezako bwino pang’ono chabe. Ubwenzi wanga ndi Yehova walimbikitsidwa chifukwa ndaona kuti anthu alephera pa ntchito yolimbana ndi matenda. Ndi Yehova yekha amene angachiritse anthu matenda awo onse.” Mothandizidwa ndi Yehova, Monika wakhalabe wosangalala ndipo tsopano wakhala akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 40.
N’zoona kuti kulimbana ndi vuto langati la Monika si nkhani ya masewera ayi. Komabe mumakhala achimwemwe pozindikira kuti zinthu zina zimatenga nthawi yaitali kuposa mmene mukuganizira. Monga Monika, nanunso musakayike kuti Yehova ‘adzakuthandizani pa nthawi yakusowa,’ kapena kuti yoyenera.
Musadziyerekezere ndi Ena, Zolinga Zanu Zikhale Zoti Mungazikwaniritse
Inuyo ndinu munthu panokha. Palibe aliyense amene ali ndendende ngati inuyo. Mwambi wina m’chinenero cha ku Africa kuno chotchedwa Chigani umatchula mfundo imeneyi m’njira yosavuta kumvetsa yakuti: “Zala sizifanana kutalika.” N’kupanda nzeru kuyerekezera chala chinachake ndi chinzake. Simungafune kuti Yehova azikuyerekezerani ndi munthu wina, ndipo iye satero ayi. Komabe, anthu amakonda kuyerekezerana ndipo zimenezi zingathe kulanda munthu chimwemwe chake. Powerenga lemba la Mateyu 20:1-16, taonani chitsanzo chogwira mtima kwambiri chimene Yesu anapereka pa mfundo imeneyi.
M’chitsanzochi Yesu anatchula kuti panali “mbuye” amene ankafuna antchito ku munda wake wa azitona. Ndiye anapeza anthu ena ofuna ntchito n’kuwalemba ntchito “mamawa,” mwina 6 koloko. Anagwirizana nawo kuti awapatsa malipiro a panthawiyo a tsiku limodzi, kapena kuti a maola 12. Malipiro ake anali lupiya la theka limodzi. N’zosakayikitsa kuti anthuwa anali osangalala kuti apeza ntchito ndiponso kuti alipidwa malipiro okwanira a panthawiyo. Kenaka, mbuyeyo anapeza magulu ena a anthu ofuna ntchito ndipo anawapatsanso ntchito, ena anayamba 9 koloko m’mawa, ena 12 koloko, ena 3 koloko masana ndipo enanso anayamba 5 koloko, tsiku litangotsala pang’ono kutha. Magulu onsewa sanagwire ntchito ya tsiku lonse lathunthu. Ndipo pa nkhani ya malipiro, mbuyeyo anawauza kuti awapatsa “chimene chili choyenera,” ndipo antchitowo anavomera.
Tsiku litatha, mbuyeyo anauza kapitawo wake kuti akalipire antchitowo. Anamuuza kuti aitane antchitowo ndipo ayambe kulipira amene anamalizira kulembedwa. Iwowa anali atagwira ntchito kwa ola limodzi lokha koma n’zodabwitsa kuti analandira malipiro a tsiku lonse. Ingoganizirani nkhani zosiyanasiyana zimenezi antchitowo anayamba kukambirana chifukwa cha zosayembekezekazi. Amene anali atagwira ntchito kwa maola onse 12 anaganiza kuti nawo alandira ndalama zochuluka kwambiri poyerekezera ndi nthawi imene akhala akugwira ntchito. Koma nawonso analandira ndalama zomwezo.
Ndiye kodi anatani? “Mmene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja, nati, omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing’ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake.”
Komatu umu si mmene mbuyeyo amaonera nkhaniyo. Iye anauza odandaulawo kuti malipiro amene wawapatsa ndi amene anagwirizana, sanawachotserepo chilichonse ayi. Anawauzanso kuti mwakufuna kwake anzawo aja anaganiza zowapatsa malipiro a tsiku lonse, ndipo n’zosakayikitsa kuti anali malipiro ambiri kuposa amene iwo anali kuyembekezera. Kwenikweni, palibe aliyense wa antchito onsewo amene analandira malipiro operewera pa malipiro amene anagwirizana, ndipo ambiri analandira malipiro ochuluka zedi kuyerekezera ndi malipiro amene anali kuyembekezera. Ndiyeno potsiriza pake mbuyeyo anafunsa kuti: “Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga?”
Tsopano taganizirani zimene zikanachitika kapitawo uja akanayamba kulipira gulu loyamba lija, gululo n’kuchoka nthawi yomweyo. Gululo likanakhutira ndi malipiro aja. Chinapangitsa kuti liderere malipirowo chinali chifukwa choona kuti anzawo alandira ndalama zomwezo ngakhale kuti anagwira ntchito yochepa chabe. Zimenezi zinawakwiyitsa mpaka kufika pom’dandaula mbuye uja, m’malo moti amuthokoze kwambiri monga mmene mwina anachitira pamene amawalemba ntchitoyo.
Nkhaniyi ikusonyeza bwino kwambiri zimene zimachitika tikamadziyerekezera ndi ena. Mukamaganizira za ubwenzi wa inu panokha ndi Yehova n’kuyamikira mmene akukudalitsirani inuyo, muzikhala achimwemwe. Osayerekezera moyo wanu ndi wa ena. Ngati zikuoneka kuti Yehova wadalitsa ena kwambiriko kuposa inuyo, sangalalani nawo.
Komabe, Yehova amafuna kuti inuyo muchite zinazake. Zotani? Lemba la Agalatiya 6:4 limati: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha.” Kapena tinene kuti, muzikhala ndi zolinga zoti mungazikwaniritse ndipo muzichita khama kuti muzikwaniritsedi. Ngati muli ndi cholinga choti mungathedi kuchikwaniritsa n’kupezeka kuti mwachikwaniritsadi, ndiye kuti ‘mudzakhala nako kudzitamandira.’ Mukatero mudzakhala ndi chimwemwe.
Mudzalandira Mphoto
Mfundo zitatu zimene taona zikusonyeza kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo kungathandize munthu kukhala wachimwemwe ngakhale m’masiku otsiriza ano ndiponso ngakhale kuti ndife opanda ungwiro. Mukamawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, muziyesetsa kuona mfundo zoterezi, zomwe mwina zachita kutchulidwa kapena zomwe zasonyezedwa m’nkhani kapena m’mafanizo enaake.
Ngati mukuona kuti chimwemwe chanu chikumka chichepa, yesetsani kupeza chifukwa chake. Kenaka fufuzani mfundo zimene mungagwiritse ntchito pothetsa vutolo. Mwachitsanzo, mungathe kuona tsamba 110 mpaka 111 m’buku la “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial.”a Masamba amenewa amafotokoza buku la Miyambo, ndipo mungapezemo malangizo ndi mfundo zambirimbiri zomwe zili m’mitu ing’onoing’ono yokwana 12. Tingadziwenso zambiri pogwiritsa ntchito Watch Tower Publications Indexb ndi Watchtower Library pa CD-ROM.c Pogwiritsa ntchito zinthu zimenezi kawirikawiri, mudzakhala katswiri popeza mfundo zoyenererana ndi nkhani inayake.
Anthu onse oyenerera, m’tsogolo muno Yehova awapatsa moyo wosatha wangwiro padziko lapansi m’paradaiso. Anthuwa adzakhala ndi chimwemwe chosefukira.
[Mawu a M’munsi]
a Zimafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
b Zimafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
c Zimafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 12]
“Onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 3:23
[Mawu Otsindika patsamba 13]
Yesu “anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo.”—Ahebri 5:8, 9
[Mawu Otsindika patsamba 15]
“Adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.”—Agalatiya 6:4