Kodi Nchiyani Chimapatsa Anthu Chimwemwe?
Pazaka makumi aŵiri gulu la ofufuza padziko lonse lakhala likufufuza za chimwemwe mwatsatanetsatane. Kodi anapeza zotani? “Zikuoneka kuti chimwemwe kwenikweni sichimadalira pa zinthu zakunja,” inatero magazini ya Scientific American.
Magazini ya sayansi imeneyi inanenanso kuti: “Chuma sindicho umboni wakuti munthu ali wachimwemwe. Anthu sanakhale ndi chimwemwe chochuluka pamene maiko awo atukuka kwambiri. . . . M’maiko ambiri palibe kugwirizana kwenikweni pakati pa ndalama ndi chimwemwe.”
Zofufuzazo zikusonyeza kuti pali mikhalidwe inayi imene anthu achimwemwe ali nayo: Amadzikonda ndipo amadziŵerengera, amakhulupirira kuti ali ndi ulamuliro pa moyo wawo, samataya mtima, ndipo amakonda kucheza ndi anthu anzawo. Ndiponso, maukwati abwino ndi maunansi abwino ndi ena zimathandizira chimwemwe m’moyo, ndipo zimenezo zimalimbitsa thanzi ndi kuwonjezera moyo wa munthu.
Zili bwinonso kudziŵa zimene Scientific American inanena kuti: “Anthu opembedza kwambiri alinso ndi chimwemwe chochuluka. Pambuyo pa kufufuza kotchedwa Gallup kofuna kudziŵa zolingalira za anthu kunapezeka kuti anthu opembedza kwambiri amakhala ndi chimwemwe chachikulu kuposa aja amene saali odzipereka kwambiri pa zauzimu. Kufufuza kwina, kuphatikizapo kwa maiko 16 ogwirizana, pa anthu 166,000 m’maiko 14, kunapeza kuti malinga ndi malipoti, chimwemwe ndiponso kukhutira ndi moyo zimawonjezeka ngati pali kudzipereka zolimba pa chipembedzo ndi kusaphonya mapemphero.”
Kalekale wamasalmo Davide anasonyeza kuti chimwemwe cha munthu chimakhalapo ngati pali kulambira Yehova Mulungu kogwirizana, nalemba kuti: “Ndinakondwera mmene ananena nane, Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”—Salmo 122:1.
Nzosadabwitsa kuti mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti: ‘Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi’! (Ahebri 10:24, 25) Inde, kusonkhana pamodzi ndi aja amene ali ndi chikhulupiriro chofanana ndi chathu polambira Mulungu kumasangalatsa amene amakonda choonadi cha Baibulo. Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri zatsimikiza kuti zimenezi nzoona ndipo zikukupemphani kuti mudzadzionere nokha mwa kulambira nawo limodzi pa Nyumba ya Ufumu pafupi ndi kwanu.