Nsembe Zotamanda Zimene Zimakondweretsa Yehova
“Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu.”—AROMA 12:1.
1. Kodi Baibulo limanenanji pa phindu losakhalitsa la nsembe zoperekedwa m’Chilamulo cha Mose?
“PAKUTI chilamulo, pokhala nawo mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.” (Ahebri 10:1) Pamenepa, m’chiganizo chimodzi chomveka bwino, mtumwi Paulo akutsimikiza kuti nsembe zonse zoperekedwa m’Chilamulo cha Mose zinalibe phindu lokhalitsa pa chipulumutso cha anthu.—Akolose 2:16, 17.
2. Kodi n’chifukwa chiyani sikuli kopanda phindu kuyesa kumvetsetsa nkhani zatsatanetsatane za m’Baibulo zokhudza zopereka ndi nsembe za Chilamulo?
2 Kodi izi zikutanthauza kuti nkhani za mu Pentatuke zokhudza zopereka ndi nsembe zilibe phindu kwa Akristu lerolino? Kwenikweni, kwa nthaŵi yoposa pang’ono chaka chimodzi, anthu amene analembetsa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase m’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi posachedwapa aŵerenga mabuku oyambirira asanu a m’Baibulo. Ena ayesetsa kuŵerenga ndi kumvetsetsa mfundo zonse. Kodi kuyesayesa kwawo konseko kwapita pachabe? Ndithudi sizingakhale tero, chifukwa “zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Choncho funso n’lakuti, Kodi ndi ‘malangizo’ ndi “chitonthozo” zotani zimene tingatolepo pa nkhani zonsezo za m’Chilamulo zokhudza zopereka ndi nsembe?
Kutilangiza ndi Kutitonthoza
3. Kodi tili ndi chofunika chachikulu chotani?
3 Ngakhale kuti sitikufunika kupereka nsembe zenizeni m’njira imene Chilamulo chinanena, tikufunikirabe kwambiri zimene nsembezo zinachitira Aisrayeli mochepera, ndiko kuti, kuti machimo athu akhululukidwe ndi kuyanjidwa ndi Mulungu. Popeza kuti sitikuperekanso nsembe zenizeni, kodi mapindu amenewo tingawalandire bwanji? Atatchula kupereŵera kwa nsembe za nyama, Paulo anati: “[Yesu] poloŵa m’dziko lapansi, anena, Nsembe ndi chopereka simunazifuna, koma thupi munandikonzera Ine. Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunakondwera nazo; pamenepo ndinati, Taonani, ndafika, (pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.”—Ahebri 10:5-7.
4. Kodi Paulo anagwiritsa ntchito motani Salmo 40:6-8 pa Yesu Kristu?
4 Pogwira mawu a Salmo 40:6-8, Paulo ananena kuti Yesu sanabwere kudzapitiriza “nsembe ndi chopereka,” “nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo,” zimene zonse sizinali kuvomerezedwanso ndi Mulungu pofika nthaŵi imene Paulo anali kulemba mawuŵa. M’malo mwake, Yesu anabwera ndi thupi lokonzedwa ndi Atate ake akumwamba, thupi limene linali lolingana m’kalikonseko ndi limene Mulungu anakonza pamene Iye analenga Adamu. (Genesis 2:7; Luka 1:35; 1 Akorinto 15:22, 45) Monga Mwana wangwiro wa Mulungu, Yesu anali ndi udindo wa “mbewu” ya mkazi, monga kunaloseredwa pa Genesis 3:15. Anachita zinthu kuti ‘alalire [“anzunzunde,” NW] mutu wa Satana,’ ngakhale kuti Yesu mwiniyo ‘analaliridwa [“ananzunzundidwa,” NW] chitende.’ Moteremu, Yesu anakhala njira imene Yehova anapereka kuti anthu apulumutsidwe, njira imene anthu achikhulupiriro anali kuyang’anako kuchokera m’masiku a Abele.
5, 6. Kodi ndi njira yopambana yotani yofikira kwa Mulungu imene Akristu ali nayo?
5 Ponena za ntchito yapadera imeneyi imene Yesu anachita, Paulo anati: “Ameneyo sanadziŵa uchimo [Mulungu] anamuyesera uchimo m’malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.” (2 Akorinto 5:21) Mawu akuti “anamuyesera uchimo” angatembenuzidwenso kuti ‘kumuyesa monga nsembe yauchimo.’ Mtumwi Yohane anati: “Iye ndiye chiwombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.” (1 Yohane 2:2) Motero, pamene kuli kwakuti Aisrayeli anali ndi njira yosakhalitsa yofikira kwa Mulungu mwa nsembe zawo, Akristu ali ndi maziko opambana ofikira kwa Mulungu, nsembe ya Yesu Kristu. (Yohane 14:6; 1 Petro 3:18) Ngati tikhulupirira nsembe ya dipo imene Mulungu anapereka ndi kumumvera Iye, ifenso machimo athu angakhululukidwe ndipo tingayanjidwe ndi Mulungu ndi kulandira madalitso ake. (Yohane 3:17, 18) Kodi sizotonthoza zimenezi? Komabe, kodi tingaonetse bwanji kuti timakhulupirira nsembe ya dipo?
6 Atalongosola kuti Akristu ali ndi maziko opambana ofikira kwa Mulungu, mtumwi Paulo anafotokoza, monga momwe timaŵerengera pa Ahebri 10:22-25, njira zitatu zimene tingasonyezere kuti timakhulupirira ndiponso kuyamikira makonzedwe achikondi a Mulungu ameneŵa. Ngakhale kuti Paulo anali kulimbikitsa kwenikweni awo amene ali ndi ‘[njira, NW] yoloŵera m’malo opatulika,’ ndiko kuti, Akristu odzozedwa okhala ndi chiyembekezo cha kumwamba, ndithudi anthu onse afunika kulabadira mawu ouziridwa a Paulo ngati akufuna kupindula ndi nsembe yowombola ya Yesu.—Ahebri 10:19.
Perekani Nsembe Zoyera ndi Zosadetsedwa
7. (a) Kodi Ahebri 10:22 amasonyeza motani zimene zinali kuchitika popereka nsembe? (b) N’chiyani chinafunika kuchitidwa kutsimikizira kuti nsembe inali yololeka kwa Mulungu?
7 Choyamba, Paulo akulimbikitsa Akristu kuti: “Tiyandikire ndi mtima woona, m’chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuchotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera.” (Ahebri 10:22) Mawu amene agwiritsidwa ntchito pano akusonyeza ndendende zimene zinali kuchitika popereka nsembe yeniyeni ya m’Chilamulo. Zimenezi n’zoyenera chifukwa kuti nsembe ikhale yololeka, inafunika kuperekedwa ndi zolinga zabwino ndiponso kukhala ya chinthu choyera ndi chosadetsedwa. Nyama yoperekedwa nsembe inali ng’ombe kapena nkhosa, ndiko kuti, ya nyama zoyera, ndipo inali “yopanda chirema.” Ngati nsembeyo inali ya mbalame, zinayenera kukhala njiwa kapena maunda. Atakwanitsa zimenezi, ‘inkalandiridwa m’malo mwake, imutetezere.’ (Levitiko 1:2-4, 10, 14; 22:19-25) Nsembe yaufa inalibe chotupitsa, chimene n’chizindikiro cha kuipitsa; ndipo sinalinso kukhala ndi uchi, kapena kutanthauza madzi ozuna a chipatso, amene amakonda kuchititsa zinthu kuŵira. Pamene nsembezo, kaya zanyama kapena zaufa, zinali kuperekedwa pa guwa la nsembe, anali kuthirako mchere, chosungitsira zinthu.—Levitiko 2:11-13.
8. (a) Kodi n’chiyani chimene chinkafunika kwa munthu amene akupereka nsembe? (b) Kodi tingatsimikize motani kuti kulambira kwathu n’kololeka kwa Yehova?
8 Nanga bwanji za munthu amene akupereka nsembeyo? Chilamulo chinali kunena kuti aliyense amene akudza pamaso pa Yehova anayenera kukhala waudongo ndi wosadetsedwa. Munthu amene pachifukwa china anali wodetsedwa choyamba anafunika kupereka nsembe yauchimo kapena yopalamula kuti abwezeretse mbiri yake yabwino pamaso pa Yehova kotero kuti nsembe yake yopsereza kapena yoyamika ikhale yololeka kwa Iye. (Levitiko 5:1-6, 15, 17) Motero, kodi ife timazindikira kufunika kwa kukhala ndi mbiri yabwino nthaŵi zonse pamaso pa Yehova? Ngati tikufuna kuti kulambira kwathu kukhale kololeka kwa Mulungu, tiyenera kukonza mofulumira zolakwa zilizonse pa malamulo a Mulungu. Tiyenera kugwiritsa ntchito mofulumira njira zimene Mulungu watipatsa zotithandizira, “akulu a Mpingo” ndiponso “chiwombolo cha machimo athu,” Yesu Kristu.—Yakobo 5:14; 1 Yohane 2:1, 2.
9. Kodi ndi kusiyana kwakukulu kuti kumene kuli pakati pa nsembe zoperekedwa kwa Yehova ndi zija zoperekedwa kwa milungu yonyenga?
9 Kugogomeza kukhala osadetsedwa mwa njira iliyonse kwenikweni ndiko kunali kusiyana kwakukulu pakati pa nsembe zoperekedwa kwa Yehova ndi zimene zinali kuperekedwa kwa milungu yonyenga ndi anthu a mitundu yozungulira Israyeli. Pothirira ndemanga pa mbali yapadera imeneyi ya nsembe za m’Chilamulo cha Mose, buku lina la maumboni limati: “Tingaone kuti palibe kugwirizana kulikonse ndi maula kapena kuwombeza; palibe kuyaluka kwachipembedzo, kudzidula ziwalo, kapena kuchita chigololo kopatulika, miyambo ya kubala yakuthupi ndi yonkitsa inali kuletsedwa kotheratu; palibe kupereka munthu nsembe; palibe kupereka nsembe kwa akufa.” Zonsezi zimatichititsa kuganiza za mfundo imodzi yokha yakuti: Yehova ndi woyera, ndipo salola kapena kuvomereza cholakwa kaya choipa cha mtundu uliwonse. (Habakuku 1:13) Kulambira komanso nsembe zoperekedwa kwa iye ziyenera kukhala zoyera ndi zosadetsedwa—mwakuthupi, mwamakhalidwe ndiponso mwauzimu.—Levitiko 19:2; 1 Petro 1:14-16.
10. Mogwirizana ndi uphungu wa Paulo wolembedwa pa Aroma 12:1, 2, kodi ndi kudzipenda kotani kumene tiyenera kuchita?
10 Polingalira zimenezi, tiyenera kudzipenda m’mbali zonse za moyo kuti tikhale otsimikiza kuti utumiki wathu kwa Yehova uli wololedwa. Tisalingaliretu kuti malinga ngati timapezeka pa misonkhano yachikristu ndi kumachita nawo utumiki, zilibe kanthu kuti timachita zotani kwatokha. Sitiyeneranso kuganiza kuti kuchita nawo ntchito zachikristu m’njira ina kumatipangitsa kuti m’mbali zina za moyo wathu sitifunika kwenikweni kumvera malamulo a Mulungu. (Aroma 2:21, 22) Sitingayembekeze kuti Mulungu atidalitsa ndi kutiyanja ngati tilola chinthu chilichonse chosayera ndi chodetsedwa m’maso mwake kuti chiipitse kaganizidwe kathu ndi zochita zathu. Kumbukirani mawu a Paulo aŵa: “Ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.”—Aroma 12:1, 2.
Perekani Nsembe Zotamanda ndi Mtima Wonse
11. Kodi n’chiyani chimene chikuphatikizidwa m’mawu akuti “chilengezo chapoyera,” otchulidwa pa Ahebri 10:23?
11 Polembera kalata Ahebri, Paulo kenaka akutchula mbali yofunika kwambiri ya kulambira koona kuti: “Tigwiritse chilengezo chapoyera cha chiyembekezo chathu mosagwedera, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika.” (Ahebri 10:23, NW) Mawu akuti “chilengezo chapoyera” kwenikweni amatanthauza kuti “kuvomereza,” ndipo Paulo ananenanso za “nsembe yakuyamika.” (Ahebri 13:15) Zimenezi zikutikumbutsa mtundu wa nsembe imene amuna onga Abele, Nowa, ndi Abrahamu anapereka.
12, 13. Kodi Mwisrayeli anali kuvomereza chiyani pamene anapereka nsembe yopsereza, ndipo n’chiyani chimene tingachite kuti tionetse mzimu wofananawo?
12 Pamene Mwisrayeli anapereka nsembe yopsereza, inaperekedwa “mwakufuna kwake pamaso pa Yehova.” (Levitiko 1:3, NW) Mwa nsembe yoteroyo, iye modzifunira anali kulengeza poyera, kapena kuti kuvomereza, madalitso ochuluka a Yehova ndiponso kukoma mtima kwake kwachikondi pa anthu ake. Kumbukirani kuti chinthu chapadera kwambiri ndi nsembe yopsereza chinali chakuti chopereka chonsecho chinali kutenthedwa pa guwa la nsembe, chizindikiro choyenerera cha kudzipereka ndi kudzipatulira kotheratu. Mofanana ndi zimenezo, timasonyeza kukhulupirira nsembe ya dipo ndiponso kuti timayamikira makonzedwe amenewo pamene modzifunira ndi mwa mtima wonse tipereka kwa Yehova ‘nsembe yoyamika, ndiyo, chipatso cha milomo.’
13 Ngakhale kuti Akristu sapereka nsembe zenizeni, za nyama kaya za zomera, ali ndi udindo wochitira umboni uthenga wabwino wa Ufumu ndiponso wopanga ophunzira a Yesu Kristu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kodi mumagwiritsa ntchito mipata imene mumakhala nayo kuti mulengeze nawo poyera uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kotero kuti anthu ena ambiri adziŵe zinthu zodabwitsa zimene Mulungu wasungira anthu omvera? Kodi modzifunira mumathera nthaŵi yanu ndi nyonga yanu pophunzitsa anthu ochita chidwi ndi kuwathandiza kukhala ophunzira a Yesu Kristu? Kuchita kwathu utumiki mwachangu kumakondweretsa Mulungu, monga fungo lokoma la nsembe yopsereza.—1 Akorinto 15:58.
Sangalalani Poyanjana ndi Mulungu ndi Anthu
14. Kodi mawu a Paulo pa Ahebri 10:24, 25 akufanana motani ndi lingaliro la nsembe yoyamika?
14 Pomaliza, Paulo akunena za unansi wathu ndi Akristu anzathu pamene tikulambira Mulungu. “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lili kuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Mawu akuti “kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,” “kusonkhana kwathu pamodzi,” ndi “tidandaulirane” onse amatikumbutsa zimene nsembe yoyamika mu Israyeli inali kuchita kwa anthu a Mulungu.
15. Kodi ndi kufanana kotani kumene kulipo pakati pa nsembe yoyamika ndi misonkhano yachikristu?
15 Nthaŵi zina mawu akuti “nsembe zoyamika” amatembenuzidwa kuti “nsembe zamtendere.” Panopa mawu achihebri a “mtendere” akunena za zinthu zambiri, mwinamwake kusonyeza kuti kupereka nawo nsembe zoterozo kumachititsa munthu kukhala pa mtendere ndi Mulungu ndiponso kukhala pa mtendere ndi olambira anzako. Ponena za nsembe yoyamika, katswiri wina anati: “Ndithudi, iyi inali nthaŵi yosangalatsa yoyanjana ndi Mulungu Wachipangano, pamene Iye anali kudzichepetsa nakhala Mlendo wa Israyeli pa chakudya cha nsembecho, ngakhale Iye nthaŵi zonse anali Wowachereza.” Zimenezi zikutikumbutsa lonjezo la Yesu lakuti: “Kumene kuli aŵiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndili komweko pakati pawo.” (Mateyu 18:20) Nthaŵi zonse pamene tifika pa msonkhano wachikristu, timapindula ndi mayanjano omangirira, malangizo olimbikitsa, ndiponso poganizira kuti Ambuye wathu Yesu Kristu ali limodzi nafe. Zimenezo zimapangitsa msonkhano wachikristu kukhaladi nthaŵi yosangalatsa ndi yolimbitsa chikhulupiriro.
16. Tikulingalira za nsembe yoyamika, kodi n’chiyani chimene chimachititsa misonkhano yachikristu kukhala yosangalatsa kwambiri?
16 Pa nsembe yoyamika, mafuta onse—okuta matumbo, impso, chokuta cha mphafa, ndi m’chuuno, komanso mchira wamafuta wa nkhosa—anali kuperekedwa kwa Yehova mwa kuwotchedwa, kutenthedwa pa guwa la nsembe. (Levitiko 3:3-16) Mafuta anali kuonedwa kuti ndiyo mbali ya nyama yopatsa thanzi kwambiri ndiponso yabwino kwabasi. Kuwapereka paguwa la nsembe kunasonyeza kupatsa Yehova zabwino koposa. Chimene chimachititsa misonkhano yachikristu kukhala yosangalatsa mwapadera n’chakuti sitingolangizidwa basi komanso timapereka chitamando kwa Yehova. Timachita zimenezi, tikuyesayesa modzichepetsa ndi mwakhama, mwa kuimba nawo nyimbo kuchokera pansi pa mtima, kumvetsera mosamalitsa, ndi kuyankha pamene kuli kotheka kutero. “Haleluya, muyimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake,” anafuula motero wamasalmo.—Salmo 149:1.
Madalitso Ochuluka Ochokera kwa Yehova Akutidikira
17, 18. (a) Kodi ndi nsembe yaikulu yotani imene Solomo anapereka potsegulira kachisi mu Yerusalemu? (b) Kodi ndi madalitso otani amene anthu analandira kuchokera pa mwambo wotsegulira kachisi?
17 Pamene anali kutsegulira kachisi mu Yerusalemu, m’mwezi wachisanu ndi chiŵiri wa chaka cha 1026 B.C.E., Mfumu Solomo anapereka “nsembe [yaikulu, NW] pamaso pa Yehova,” imene inaphatikizapo “nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.” Kuwonjezera pa zimene zinaperekedwa pa nsembe yaufa, ng’ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000 zinaperekedwa nsembe panthaŵiyo.—1 Mafumu 8:62-65.
18 Kodi mungalingalire za kuchuluka kwa zinthu zimene zinawonongedwa ndiponso kukula kwa ntchito imene inalipo pa mwambo waukulu umenewo? Komatu, madalitso amene Israyeli analandira mwachionekere anaposeratu mtengo wa zimene anachitazo. Pamapeto a mwambowo, Solomo “anawauza anthu apite; ndipo iwo anadalitsa mfumu, napita ku mahema awo osekera ndi okondwera mtima chifukwa cha zokoma zonse Yehova anachitira Davide mtumiki wake, ndi Israyeli anthu ake.” (1 Mafumu 8:66) Ndithudi, monga ananenera Solomo, “madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—Miyambo 10:22.
19. Kodi tingachitenji kuti tilandire madalitso ochuluka kuchokera kwa Yehova tsopano ndiponso kosatha?
19 Tikukhala ndi moyo panthaŵi imene “mthunzi wa zokoma zilinkudza” waloŵedwa m’malo ndi “chifaniziro chenicheni cha zinthuzo.” (Ahebri 10:1) Yesu Kristu, paudindo wake monga Mkulu wa Ansembe wamkulu wophiphiritsa, waloŵa kale m’mwamba mwenimwenimo ndi kupereka mtengo wa mwazi wake kuti atetezere onse amene akukhulupirira nsembe yake. (Ahebri 9:10, 11, 24-26) Pamaziko a nsembe yaikulu imeneyo ndi mwa kupereka ndi mtima wonse kwa Mulungu nsembe zathu zotamanda zimene zili zoyera ndi zosadetsedwa, ifenso tingapite patsogolo “osekera ndi okondwera mtima,” tikuyembekezera madalitso ochuluka ochokera kwa Yehova.—Malaki 3:10.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi ndi malangizo ndi chitonthozo chotani chimene tingachipeze mu nkhani za m’Chilamulo za nsembe ndi zopereka?
• Kodi chofunika choyamba n’chiyani kuti nsembe ikhale yovomerezeka, ndipo zimenezi zikutanthauzanji kwa ife?
• Kodi tingapereke chiyani chimene chikufanana ndi nsembe yopsereza yodzifunira?
• Kodi tingayerekeze misonkhano yachikristu ndi nsembe yoyamika m’njira zotani?
[Chithunzi patsamba 18]
Nsembe ya dipo ya Yesu inaperekedwa ndi Yehova kuti ipulumutse anthu
[Chithunzi patsamba 20]
Kuti utumiki wathu ukhale wololeka kwa Yehova, tiyenera kukhala osadetsedwa ndi chilichonse
[Chithunzi patsamba 21]
Timavomereza poyera ubwino wa Yehova pamene tichita utumiki