Labadirani Malonjezo a Mulungu mwa Kusonyeza Chikhulupiriro
“Adatipatsa [Yehova Mulungu] malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu.”—2 PETRO 1:4.
1. Kodi nchiyani chimene chimatikhozetsa kusonyeza chikhulupiriro chowona?
YEHOVA amafuna kuti tisonyeze chikhulupiriro m’malonjezo ake. Komabe, “sionse ali nacho chikhulupiriro.” (2 Atesalonika 3:2) Mkhalidwe umenewu ndiwo chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito. (Agalatiya 5:22, 23) Chifukwa chake, awo amene amatsogozedwa ndi mzimu wa Yehova ndiwo okha amene angasonyeze chikhulupiriro.
2. Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo amafotokozera liwulo “chikhulupiriro”?
2 Koma kodi chikhulupiriro nchiyani? Mtumwi Paulo amachitcha kuti “kusonyezedwa kwa umboni wa zenizeni ngakhale kuti zili zosawonedwa.” Umboni wa zenizeni zosawonedwa umenewu ngwamphamvu kwambiri kwakuti umafanana ndi chikhulupiriro. Chikhulupiriro chimanenedwanso kukhala “chiyembekezo chotsimikizirika cha zinthu zoyembekezeredwa” chifukwa chakuti anthu amene ali ndi mkhalidwe umenewu amatsimikiza kuti zinthu zonse zolonjezedwa ndi Yehova Mulungu nzotsimikizirika mofanana ndi kuti zachitika kale.—Ahebri 11:1, NW.
Chikhulupiriro ndi Malonjezo a Yehova
3. Kodi nchiyani chimene Akristu odzozedwa adzalandira ngati asonyeza chikhulupiriro?
3 Kuti tikondweretse Yehova, tiyenera kukhulupirira malonjezo ake. Mtumwi Petro anasonyeza zimenezi m’kalata yake yachiŵiri youziridwa, yolembedwa pafupifupi 64 C.E. Iye anasonyeza kuti ngati Akristu anzake odzozedwa anasonyeza chikhulupiriro, akaona kukwaniritsidwa kwa “malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu.” Monga chotulukapo chake, ‘akakhala oyanjana nawo umulungu wake’ monga oloŵa nyumba limodzi ndi Yesu Kristu mu Ufumu wakumwamba. Pokhala ndi chikhulupiriro ndi thandizo la Yehova Mulungu, iwo anali atapulumutsidwa muukapolo wa zizoloŵezi zoipa ndi ntchito za dziko lino. (2 Petro 1:2-4) Ndipo tangoyerekezerani! Anthu amene amasonyeza chikhulupiriro chowona, ali ndi ufulu wosayerekezereka wofananawo lerolino.
4. Kodi ndimikhalidwe iti imene tiyenera kuwonjezera pachikhulupiriro chathu?
4 Kukhulupirira malonjezo a Yehova ndi kuyamikira ufulu wathu wopatsidwa ndi Mulungu ziyenera kutisonkhezera kuchita zomwe tingathe kuti tikhale Akristu ochita bwino. Petro anati: “Pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pachikhulupiriro chanu, ndi paukoma [chidziŵitso, NW]; ndi [pachidziŵitso, NW] chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro [kudzipereka kwaumulungu, NW]; ndi [pakudzipereka kwamulungu, NW] chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi.” (2 Petro 1:5-7) Motero Petro amatipatsa mpambo umene tingachite bwino kuuloŵeza mumtima. Tiyeni tipende mikhalidwe imeneyi.
Mbali Zofunika Kwambiri za Chikhulupiriro
5, 6. Kodi ukoma nchiyani, ndipo tingauwonjezere motani pachikhulupiriro chathu?
5 Petro anati ukoma, chidziŵitso, kudziletsa, chipiriro, kudzipereka kwaumulungu, kukonda abale, ndi chikondi ziyenera kuwonjezeredwa pachinzake ndiponso pachikhulupiriro chathu. Tiyenera kugwira ntchito zolimba kuti tiumbe mikhalidwe imeneyi yofunika pachikhulupiriro chathu. Mwachitsanzo, ukoma sitingausonyeze popanda chikhulupiriro. Wolemba dikishonale W. E. Vine akunena kuti pa 2 Petro 1:5, “ukoma wawonjezeredwa kukhala mkhalidwe wofunika posonyeza chikhulupiriro.” Uliwonse wa mikhalidwe inayo wotchulidwa ndi Petro uyeneranso kukhala mbali ya chikhulupiriro chathu.
6 Choyamba, tiyenera kuwonjezera ukoma pachikhulupiriro chathu. Kukhala waukoma kumatanthauza kuchita zokoma m’maso mwa Mulungu. Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kuti “ukoma” panopa, limatembenuzidwa ndi ena kuti “ubwino.” (New International Version; The Jerusalem Bible; Today’s English Version) Ukoma umatisonkhezera kupeŵa kuchita choipa kapena kuvulaza anthu anzathu. (Salmo 97:10) Umasonkhezeranso kuchitapo kanthu molimba mtima pochita chabwino kaamba ka phindu lauzimu, lakuthupi, ndi la malingaliro la ena.
7. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuwonjezera chidziŵitso pachikhulupiriro chathu ndi ukoma?
7 Kodi nchifukwa ninji Petro akutifulumiza kuwonjezera chidziŵitso pachikhulupiriro chathu ndi ukoma? Eya, pamene tiyang’anizana ndi zitokoso zatsopano za chikhulupiriro chathu, timafunikira chidziŵitso ngati titi tisiyanitse chabwino ndi choipa. (Ahebri 5:14) Kupyolera mwaphunziro la Baibulo ndi kudziŵa kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu ndi kugwiritsira ntchito nzeru yothandiza tsiku ndi tsiku m’moyo wathu, timawonjezera chidziŵitso chathu. Zimenezi nazonso, zimatikhozetsa kusunga chikhulupiriro chathu ndi kupitirizabe kuchita chimene chili chabwino poyesedwa.—Miyambo 2:6-8; Yakobo 1:5-8.
8. Kodi kudziletsa nchiyani, ndipo kodi kumagwirizanitsidwa motani ndi chipiriro?
8 Kuti tithandizidwe kulaka mayeso ndi chikhulupiriro, tifunikira kuwonjezera kudziletsa pachidziŵitso chathu. Liwu Lachigiriki lotanthauza “kudziletsa” limapereka lingaliro la kukhoza kwathu kudzilamulira. Chipatso cha mzimu wa Mulungu chimenechi chimatithandiza kusonyeza kudziletsa m’lingaliro, mawu, ndi m’khalidwe. Mwakupitirizabe kusonyeza kudziletsa, timawonjezera chipiriro. Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “chipiriro” limatanthauza kukhala wosasunthika molimba mtima, kusakhala wamantha ndi kusathaŵa mavuto osapeŵeka. Yesu anapirira pamtengo wozunzirapo chifukwa cha chisangalalo chimene chinaikidwa patsogolo pake. (Ahebri 12:2) Nyonga yopatsidwa ndi Mulungu yogwirizanitsidwa ndi chipiriro imalimbitsa chikhulupiriro chathu ndipo imatithandiza kusangalala munsautso, kulaka chiyeso, ndi kupeŵa kulolera molakwa pamene tizunzidwa.—Afilipi 4:13.
9. (a) Kodi kudzipereka kwaumulungu nchiyani? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuwonjezera kukonda abale pakudzipereka kwathu kwaumulungu? (c) Kodi tingawonjezerepo motani kukonda kwathu abale?
9 Pachipiriro chathu, tiyenera kuwonjezeranso kudzipereka kwaumulungu—mantha a ulemu, kulambira, ndi kutumikira Yehova. Chikhulupiriro chathu chimakula pamene tichita kudzipereka kwaumulungu ndi kuona mmene Yehova amachitira ndi anthu ake. Komabe, kuti tisonyeze umulungu, tifunikira kukonda abale. Ndiiko komwe, “iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.” (1 Yohane 4:20) Mitima yathu iyenera kutisonkhezera kusonyeza chikondi chowona kwa atumiki ena a Yehova ndi kufuna kuwachitira zabwino nthaŵi zonse. (Yakobo 2:14-17) Koma kodi nchifukwa ninji tikuuzidwa kuwonjezera chikondi pakukonda kwathu abale? Mwachiwonekere Petro anatanthauza kuti tiyenera kusonyeza chikondi kwa anthu onse, osati abale athu okha. Makamaka chikondi chimenechi chimasonyezedwa mwa kulalikira mbiri yabwino ndi kuthandiza anthu mwauzimu.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Ziyambukiro Zosiyana
10. (a) Kodi tidzachita motani ngati ukoma, chidziŵitso, kudziletsa, chipiriro, kudzipereka kwaumulungu, kukonda abale, ndi chikondi zawonjezeredwa pachikhulupiriro chathu? (b) Kodi nchiyani chimene chimachitika ngati wina wodzitcha kuti Mkristu asoŵa mikhalidwe imeneyi?
10 Ngati tiwonjezera ukoma, chidziŵitso, kudziletsa, chipiriro, kudzipereka kwaumulungu, kukonda abale, ndi chikondi pachikhulupiriro chathu, tidzaganiza, kulankhula, ndi kuchita zinthu m’njira yovomerezedwa ndi Mulungu. Chomwechonso, ngati munthu wodzitcha Mkristu alephera kusonyeza mikhalidwe imeneyi, amakhala wakhungu mwauzimu. Iye ‘amatsekera maso ake kuŵala’ kochokera kwa Mulungu naiŵala kuti anatsukiridwa machimo ake. (2 Petro 1:8-10; 2:20-22) Tisalepheretu mwanjira imeneyo ndi kutaya chikhulupiriro m’malonjezo a Mulungu.
11. Kodi nchiyani chimene tingayembekezere moyenera kwa odzozedwa okhulupirika?
11 Akristu okhulupirika odzozedwa amakhulupirira malonjezo a Yehova ndipo amayesetsa mwamphamvu kuchititsa kuitanidwa ndi kusankhidwa kwawo ndi Mulungu kukhala kotsimikizirika. Mosasamala kanthu ndi zopinga m’njira yawo, tingathe kuwayembekezera kusonyeza mikhalidwe yaumulungu. Kwa odzozedwa okhulupirika ‘kwawonjezedwa kolemerera khomo loloŵera muufumu wa Yesu Kristu’ kupyolera mwa chiukiriro chawo kumka kumoyo wauzimu wakumwamba.—2 Petro 1:11.
12. Kodi tiyenera kumva motani mawu a pa 2 Petro 1:12-15?
12 Petro anazindikira kuti akafa mwamsanga, ndipo anayembekezera kuukitsidwira kumwamba m’kupita kwa nthaŵi. Koma pamene anali asanafe “m’msasa uwu”—thupi lake laumunthu—anayesa kukulitsa chikhulupiriro mwa okhulupirira anzake ndi kuwasonkhezera mitima mwa kuwakumbutsa zinthu zofunika kuti apeze chiyanjo cha Mulungu. Petro atachoka mwa imfa, abale ake ndi alongo auzimu anatha kulimbitsa chikhulupiriro chawo mwa kukumbukira mawu ake.—2 Petro 1:12-15.
Chikhulupiriro m’Mawu a Ulosi
13. Kodi ndimotani mmene Mulungu anaperekera umboni wolimbikitsa chikhulupiriro wonena za kudza kwa Kristu?
13 Mulungu mwiniyo anapereka umboni wolimbitsa chikhulupiriro wonena za kutsimikizirika kwa kudza kwa Yesu “ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mateyu 24:30; 2 Petro 1:16-18) Posoŵa umboni, ansembe achikunja anasimba nthano zonama ponena za milungu yawo, pamene kuli kwakuti Petro, Yakobo, ndi Yohane anali mboni zoona ndi maso za ulemerero wa Kristu wa kusandulika kwake. (Mateyu 17:1-5) Anamuona akulemekezedwa ndipo anamva liwu la Mulungu mwiniyo likumavomereza Yesu kukhala Mwana Wake wokondedwa. Kuvomerezedwa kumeneko ndi kuoneka konyezimira kopatsidwa kwa Kristu panthaŵiyo kunali kuperekedwa kwa ulemu ndi ulemerero pa iye. Chifukwa cha vumbulutso laumulungu limeneli, Petro anatcha malowo, mwinamwake pa phiri la Hermoni, “phiri lopatulika.”—Yerekezerani ndi Eksodo 3:4, 5.
14. Kodi chikhulupiriro chathu chiyenera kuyambukiridwa motani ndi kusandulika kwa Yesu?
14 Kodi kusandulika kwa Yesu kuyenera kuyambukira chikhulupiriro chathu motani? Petro anati: “Ndipo tiri nawo mawu a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pamtima yanu.” (2 Petro 1:19) Mwachiwonekere “mawu a chinenero” anaphatikizapo osati kokha Malemba Achihebri a ulosi wonena za Mesiya komanso mawu a Yesu akuti akadza “ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” Kodi ndimotani mmene mawuwo anapangidwira kukhala “okhazikika koposa” ndi kusandulikako? Chochitika chimenecho chinatsimikizira mawu a ulosi wonena za kudza kwaulemerero kwa Kristu mumphamvu ya Ufumu.
15. Kodi nchiyani chimene chimaloŵetsedwamo m’kusamalira mawu a ulosi?
15 Kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu, tiyenera kusamalira mawu a ulosi. Zimenezi zimaphatikizapo kuphunzira mawuwo, kukambitsirana za iwo pamisonkhano Yachikristu, ndi kugwiritsira ntchito uphungu wake. (Yakobo 1:22-27) Tiyenera kuwalola kuti akhale “nyali younikira m’malo a mdima,” akumaunikira mitima yathu. (Aefeso 1:18) Mpokhapo pamene adzatitsogolera kufikira pamene “nthanda” kapena, “nyenyezi yonyenzimira ya nthanda,” Yesu Kristu, idzivumbula muulemerero. (Chivumbulutso 22:16) Vumbulutso limenelo lidzatanthauza chiwonongeko kwa anthu opanda chikhulupiriro ndipo madalitso kwa awo amene amasonyeza chikhulupiriro.—2 Atesalonika 1:6-10.
16. Kodi nchifukwa ninji tingakhulupirire kuti malonjezo onse a ulosi a m’Mawu a Mulungu adzakwaniritsidwa?
16 Aneneri a Mulungu sanali anthu wamba ochenjera onyenga amene ananeneratu mawu molondola, pakuti Petro anati: “Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi mzimu woyera, analankhula.” (2 Petro 1:20, 21) Mwachitsanzo, Davide anati: “Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine.” (2 Samueli 23:1, 2) Ndipo Paulo analemba kuti: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu.” (2 Timoteo 3:16) Popeza kuti aneneri a Mulungu anauziridwa ndi mzimu wake, tingakhulupirire kuti malonjezo onse a m’Mawu ake adzakwaniritsidwa.
Anakhulupirira Malonjezo a Mulungu
17. Kodi chikhulupiriro cha Abele chinazikidwa palonjezo lotani?
17 Malonjezo a Yehova anali maziko a chikhulupiriro cha ‘mtambo waukulu’ wa mboni zake nthaŵi Yachikristu isanakhale. (Ahebri 11:1–12:1) Mwachitsanzo, Abele anakhulupirira lonjezo la Mulungu lonena za “mbewu” imene idzaphwanya mutu wa “njoka.” Panali umboni wa kukwaniritsidwa kwa chilango cha Mulungu pa makolo a Abele. Kunja kwa Edene, Adamu ndi banja lake anadya mkate mwa kutuluka thukuta chifukwa chakuti nthaka yotembereredwa inabala minga ndi mitula. Mwachiwonekere Abele anaona Hava akukhumba mwamuna wake ndipo anaona Adamu akumlamulira. Ndithudi Hava ayenera kuti anali kudandaula ndi zoŵaŵa za pathupi pake. Ndipo chipata cha munda wa Edene chinalondedwa ndi akerubi ndi lupanga la moto lozungulira. (Genesis 3:14-19, 24) Zonsezi zinali “kusonyezedwa kwa umboni” wotsimikizira Abele wakuti chilanditso chikadza kupyolera mwa Mbewu yolonjezedwa. Pochita mwa chikhulupiriro, Abele anapereka nsembe kwa Mulungu imene inasonyezadi kukhala yamtengo wake kuposa ya Kaini.—Ahebri 11:1, 4.
18, 19. Kodi Abrahamu ndi Sara anasonyeza chikhulupiriro m’njira zotani?
18 Makolowo Abrahamu, Isake, ndi Yakobo nawonso anakhulupirira malonjezo a Yehova. Abrahamu anasonyeza chikhulupiriro m’lonjezo la Mulungu lakuti mabanja onse a padziko akadzidalitsa mwa iye ndi kuti mbewu yake ikapatsidwa dziko. (Genesis 12:1-9; 15:18-21) Mwana wakeyo Isake, ndi mdzukulu wake Yakobo anali “oloŵa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano” limodzimodzilo. Ndi chikhulupiriro Abrahamu “anakhala mlendo kudziko la lonjezano” ndi kuyembekezera “mudzi wokhala nawo maziko” enieni, Ufumu wakumwamba wa Mulungu muumene akaukitsidwiramo kumoyo padziko lapansi. (Ahebri 11:8-10) Kodi muli ndi chikhulupiriro chofananacho?
19 Mkazi wa Abrahamu, Sara, anali pafupifupi wa zaka 90 ndi wopyola pausinkhu wa kubala ana pamene anasonyeza chikhulupiriro m’lonjezo la Mulungu ndipo anapatsidwa mphamvu “ya kukhala ndi pakati pa mbewu” ndi kubala Isake. Motero, kuchokera kwa Abrahamu wa zaka 100, “wonga ngati wakufa” ameneyo, ponena za kubala, potsirizira pake “kunabadwa ana ochuluka monga khamu la nyenyezi zakumwamba.”—Ahebri 11:11, 12, NW; Genesis 17:15-17; 18:11; 21:1-7.
20. Ngakhale kuti makolowo sanaone kukwaniritsidwa konse kwa malonjezo amene Mulungu anawapatsa, kodi iwo anachitanji?
20 Makolo okhulupirikawo anafa asanaone kukwaniritsidwa kotheratu kwa malonjezo a Mulungu kwa iwo. Komabe, “adawaona [zinthu zolonjezedwazo] ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.” Panapyola mibadwo yambiri Dziko Lolonjezedwalo lisanakhale la mbadwa za Abrahamu. Komabe, m’miyoyo yawo yonse, makolo owopa Mulungu amenewo anasonyeza chikhulupiriro m’malonjezo a Mulungu. Chifukwa chakuti sanataye konse chikhulupiriro, posachedwa adzaukitsidwira kumoyo muulamuliro wa padziko lapansi wa “mzinda” umene Mulungu anawalinganizira pasadakhale, Ufumu Waumesiya. (Ahebri 11:13-16) M’njira yofananayo, chikhulupiriro chingatipangitse kukhala okhulupirika kwa Yehova ngakhale ngati sitingaone kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake onse abwino kwanthaŵi yomweyo. Chikhulupiriro chathu chidzatisonkhezeranso kumvera Mulungu, monga momwedi Abrahamu anachitira. Ndipo monga momwe anaperekera choloŵa chauzimu kwa mbadwa zake, nafenso tingathandize ana athu kusonyeza chikhulupiriro m’malonjezo amtengo wapatali a Yehova.—Ahebri 11:17-21.
Chikhulupiriro Nchofunika Kwambiri kwa Akristu
21. Lerolino kuti tivomerezedwe ndi Mulungu, kodi nchiyani chimene chiyenera kuphatikizidwa pakusonyeza kwathu chikhulupiriro?
21 Zowonadi, pamafunikira zambiri zoti ziwonjezeredwe pachikhulupiriro koposa kukhala chabe ndi chidaliro cha kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova. M’mbiri yonse ya anthu, kwakhala kofunika kusonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu m’njira zosiyanasiyana ngati titi tiyanjidwe naye. Paulo anasonyeza kuti “wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa [Yehova Mulungu]; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akumfuna Iye.” (Ahebri 11:6) Kuti avomerezedwe ndi Yehova lerolino, munthu ayenera kukhulupirira Yesu Kristu ndi nsembe ya dipo imene Mulungu wapereka kupyolera mwa iye. (Aroma 5:8; Agalatiya 2:15, 16) Kuli monga momwe Yesu mwiniyo ananenera kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi [la mtundu wa anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha. Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.”—Yohane 3:16, 36.
22. Kodi ndikukwaniritsidwa kwa lonjezo lotani kumene Ufumu Waumesiya udzabweretsa?
22 Yesu amachita mbali yofunika kwambiri m’kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu onena za Ufumu umene Akristu amapempherera. (Yesaya 9:6, 7; Danieli 7:13, 14; Mateyu 6:9, 10) Monga momwe Petro anasonyezera, kusandulika kunatsimikizira mawu a ulosi wonena za kudza kwa Yesu mumphamvu Yaufumu ndi ulemerero. Ufumu Waumesiya udzakwaniritsa lonjezo lina la Mulungu pakuti, Petro analemba kuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Ulosi wofanana nawo unakwaniritsidwa pamene andende Achiyuda okhala m’Babulo anabwezeretsedwa kudziko lakwawo mu 537 B.C.E. pansi pa boma lotsogozedwa ndi Zerubabele monga kazembe ndi Yesuwa monga mkulu wa ansembe. (Yesaya 65:17) Koma Petro anasonyeza za nthaŵi imene inali mtsogolo pamene “miyamba yatsopano”—Ufumu Waumesiya wakumwamba—ikalamulira pa “dziko lapansi latsopano,” chitaganya cha anthu olungama okhala pambulunga ino.—Yerekezerani ndi Salmo 96:1.
23. Kodi kenako ndimafunso otani onena za ukoma amene tidzakambitsirana?
23 Monga atumiki a Yehova okhulupirika ndi otsatira a Mwana wake wokondedwayo, Yesu Kristu, timakhumba dziko latsopano lolonjezedwalo la Mulungu. Timadziŵa kuti layandikira, ndipo timakhulupirira kuti malonjezo onse a Yehova amtengo wapataliwo adzakwaniritsidwa. Kuti tiyende movomerezedwa ndi Mulungu wathu, tiyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa kuwonjezerapo ukoma, chidziŵitso, kudziletsa, chipiriro, kudzipereka kwaumulungu, kukonda abale, ndi chikondi.a Tsopano, tingafunse kuti, Kodi ndimotani mmene tingasonyezere ukoma? Ndipo kodi ndimotani mmene kukhala kwathu aukoma kudzatipindulitsira limodzinso ndi ena, makamaka mabwenzi athu Achikristu, amene alabadira malonjezo a Mulungu mwa kusonyeza chikhulupiriro?
[Mawu a M’munsi]
a Chikhulupiriro ndi ukoma ndiyo mikhalidwe imene yafotokozedwa m’kope lino la Nsanja ya Olonda. Chidziŵitso, kudziletsa, chipiriro, kudzipereka kwaumulungu, kukonda abale, ndi chikondi zidzapendedwa mokwanira m’makope amtsogolo.
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi ndimotani mmene “chikhulupiriro” chingafotokozedwere?
◻ Malinga ndi lemba la 2 Petro 1:5-7, kodi ndimikhalidwe yotani imene iyenera kuwonjezeredwa pachikhulupiriro chathu?
◻ Kodi kusandulizika kwa Yesu kuyenera kuyambukira motani chikhulupiriro chathu?
◻ Kodi ndizitsanzo zotani za chikhulupiriro zimene zinaperekedwa ndi Abele, Abrahamu, Sara, ndi ena a m’nthaŵi zakale?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi mumadziŵa mmene kusandulika kwa Yesu kungayambukire chikhulupiriro cha munthu?