2 Samueli
23 Awa ndi mawu omaliza a Davide:+
“Mawu a Davide mwana wa Jese,+
Mawu a munthu amene anakwezedwa mʼmwamba,+
Wodzozedwa+ wa Mulungu wa Yakobo,
Munthu woimba bwino nyimbo+ za Isiraeli.
‘Munthu wolamulira anthu akakhala wachilungamo,+
Nʼkumalamulira moopa Mulungu,+
4 Zimakhala ngati kuwala kwa mʼmawa pamene dzuwa lawala,+
Mʼmawa wopanda mitambo.
Zimakhala ngati mvula yakata ndipo kwawala,
Nʼkuchititsa msipu kumera padziko.’+
5 Kodi nyumba yanga siili choncho kwa Mulungu?
Chifukwa wachita nane pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+
Analikonza bwino ndipo ndi lotetezeka.
Chifukwa ndi chipulumutso changa ndipo limandisangalatsa,
Chimenechi ndiye chifukwa chake amakulitsa panganoli.+
6 Koma anthu onse opanda pake amawakankhira kutali+ ngati zitsamba zaminga,
Chifukwa zitsamba zamingazo sangazinyamule ndi manja pozichotsa.
7 Munthu akamazigwira,
Ayenera kukhala ndi zipangizo zachitsulo komanso mtengo wa mkondo,
Ndipo ziyenera kutenthedwa ndi moto nʼkupseratu pamene zinamera.”
8 Awa ndi mayina a asilikali amphamvu a Davide:+ Yosebu-basebete mbadwa ya Hakemoni, mtsogoleri wa amuna atatu.+ Iye anatenga mkondo wake nʼkupha anthu 800 nthawi imodzi. 9 Womutsatira anali Eliezara+ mwana wa Dodo+ mwana wa Ahohi. Iye anali mmodzi mwa asilikali atatu amphamvu amene anali ndi Davide pamene ankanyoza Afilisiti. Iwo anasonkhana kumeneko kuti amenye nkhondo. Ndipo amuna a Isiraeli atathawa, 10 Eliezara sanathawe ndipo anapitiriza kupha Afilisiti mpaka dzanja lake linatopa nʼkuchita dzanzi.+ Moti tsiku limenelo Yehova anawathandiza kuti apambane+ ndipo anthu ena onse ankabwera mʼmbuyo mwake nʼkumatenga zinthu za anthu ophedwawo.
11 Womutsatira anali Shama, mwana wamwamuna wa Age wa ku Harari. Afilisiti anasonkhana ku Lehi, kumene kunali munda wa mphodza ndipo kumeneko anthu anathawa Afilisitiwo. 12 Koma iye anaima pakati pa mundawo nʼkuuteteza ndipo anapitiriza kupha Afilisiti, moti Yehova anawathandiza kuti apambane.+
13 Atsogoleri atatu mwa atsogoleri 30 anapita kwa Davide kuphanga la Adulamu+ pa nthawi yokolola. Apa nʼkuti Afilisiti atamanga matenti mʼchigwa cha Arefai.+ 14 Pa nthawiyi nʼkuti Davide ali kumalo ovuta kufikako,+ ndipo mudzi wa asilikali a Afilisiti unali ku Betelehemu. 15 Ndiyeno Davide ananena zimene ankalakalaka kuti: “Ndikanakonda ndikanamwa madzi amʼchitsime chimene chili pageti la ku Betelehemu.” 16 Zitatero asilikali amphamvuwo analimbana ndi anthu mpaka kulowa mumsasa wa Afilisiti nʼkutunga madzi mʼchitsime chimene chinali pageti la ku Betelehemu ndipo anapita nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa madziwo. Mʼmalomwake anawapereka kwa Yehova powathira pansi.+ 17 Iye anati: “Sindingachite zimenezi inu Yehova! Kodi ndimwe magazi+ a amuna amene anaika moyo wawo pangozi kuti akatunge madziwa?” Choncho iye anakana kumwa madziwo. Izi nʼzimene asilikali atatu amphamvuwo anachita.
18 Abisai,+ mchimwene wake wa Yowabu mwana wa Zeruya+ anali mtsogoleri wa anthu ena atatu. Iye anatenga mkondo wake nʼkupha anthu 300. Abisai anali wotchuka ngati amuna atatu aja.+ 19 Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna ena atatuwo, ndipo anali mtsogoleri wawo, iye sankafanana ndi amuna atatu oyambirira aja.
20 Benaya+ mwana wa Yehoyada, anali munthu wolimba mtima* ndipo anachita zinthu zambiri ku Kabizeeli.+ Iye anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu komanso analowa mʼchitsime chopanda madzi pa tsiku lomwe kunagwa sinowo* nʼkupha mkango umene unali mʼchitsimemo.+ 21 Benaya anaphanso munthu wamkulu modabwitsa wa ku Iguputo. Ngakhale kuti munthuyu anali ndi mkondo mʼmanja mwake, Benaya anapita kukakumana naye atanyamula ndodo, ndipo analanda mkondowo nʼkumupha ndi mkondo wake womwewo. 22 Zimenezi nʼzimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iye anali wotchuka ngati asilikali atatu amphamvu aja. 23 Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna 30 aja, sankafanana ndi amuna atatu aja. Koma Davide anamuika kukhala mmodzi wa asilikali ake omulondera.
24 Asaheli+ mchimwene wake wa Yowabu anali mʼgulu la amuna 30 aja. Mʼgululi munalinso Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,+ 25 Shama wa ku Harodi, Elika wa ku Harodi, 26 Helezi+ wa ku Beti-peleti, Ira+ mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, 27 Abi-ezeri+ wa ku Anatoti,+ Mebunai wa ku Husa,* 28 Zalimoni wa ku Ahohi, Maharai+ wa ku Netofa, 29 Helebi mwana wa Bana wa ku Netofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya wa fuko la Benjamini, 30 Benaya+ wa ku Piratoni, Hidai wakuzigwa* za Gaasi,+ 31 Abi-aliboni wa ku Beti-araba, Azimaveti wa ku Bahurimu, 32 Eliyaba wa ku Saaliboni, ana a Yaseni, Yonatani, 33 Shama wa ku Harari, Ahiyamu mwana wa Sarari wa ku Harari, 34 Elifeleti mwana wa Ahasibai, mwana wa munthu wa ku Maaka, Eliyamu mwana wa Ahitofeli+ wa ku Gilo, 35 Heziro wa ku Karimeli, Paarai wa ku Arabu, 36 Igali mwana wa Natani wa ku Zoba, Bani wa fuko la Gadi, 37 Zeleki mbadwa ya Amoni, Naharai wa ku Beeroti wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya, 38 Ira mbadwa ya Itiri, Garebi mbadwa ya Itiri+ 39 ndi Uriya+ Muhiti, onse pamodzi analipo 37.