Mutu 26
Nkhondo ya Kuchita Chimene Chiri Chabwino
1. Kodi Akristu ayenera kumenyana ndi zinthu ziwiri zotani?
MALINGA ngati dziko la Satana liripobe, Akristu ayenera kumenya nkhondo kuti akhale opanda chiyambukiro chake choipa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Valani zovala zonse za zida zankhondo zochokera kwa Mulungu kuti mukakhale okhoza kuima zolimba motsutsa [machitidwe ochenjera] a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11-18, NW) Komabe, nkhondo yathu sili kokha yotsutsa Satana ndi dziko lake, njotsutsanso zikhumbo zathu za ife eni za kuchita chimene chiri choipa. Baibulo limati: “Chikhoterero cha mtima wa munthu nchoipa kuyambira pa ubwana wake.”—Genesis 8:21, NW; Aroma 5:12.
2. (a) Kodi nchifukwa ninji ife kawirikawiri timakhala ndi chikhumbo champhamvu chakuchita choipa? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kumenyana ndi zikhumbo zoipa?
2 Chifukwa cha uchimo wolandiridwa kuchokera kwa munthu woyamba Adamu, mitima yathu ingalakalake kuchita chimene chiri choipa. Ngati tigonjera ku chilakolako chimenecho, sitidzalandira moyo wosatha m’dongosolo latsopano la Mulungu. Motero tifunikira kumenya nkhondo kuchita chimene chiri chabwino. Ngakhale mtumwi Paulo anali ndi nkhondo yoteroyo, monga momwe anafotokozera: “Pamene ndifuna kuchita chimene chiri chabwino, chimene chiri choipa chimakhala ndi ine.” (Aroma 7:21-23, NW) Inu, nanunso, mungawone nkhondo imeneyi kukhala yovuta. Nthawi zina nkhondo yamphamvu ingakhale ikuchitika mkati mwanu. Kodino mudzasankha kuchitanji?
3. (a) Kodi anthu ambiri amakhala ndi nkhondo yamkati yotani? (b) Kodi ndichowonadi Chabaibulo chotani chimene chikusonyezedwa ndi chenicheni chakuti ambiri amachita choipa pamene iwo akufuna kuchita chabwino?
3 Mwafika pa kudziwa malonjezo abwino kwambiri a Mulungu onena za kukhala ndi moyo kosatha m’mikhalidwe yabwino kwambiri padziko lapansi. Mukukhulupirira malonjezo amenewa, ndipo mukufuna kulandira zinthu zabwino zimenezi. Motero mukudziwa kuti kuli kokukomerani kosatha kutumikira Mulungu. Koma mumtima mwanu mungakhumbe zinthu zimene mukudziwa kuti nzoipa. Nthawi zina mungakhale ndi chikhumbo champhamvu chakuchita dama, kuba, kapena kuchita cholakwa china. Anthu ena ophunzira bukhu lino angakhaledi akuchita machitidwe oipa oterowo, ngakhale kuli kwakuti iwo akudziwa kuti zinthu zimenezi zikutsutsidwa ndi Mulungu. Chenicheni chakuti iwo amachita choipa pamene iwo akufuna kuchita chabwino chimasonyeza chowonadi Chabaibulocho: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.”—Yeremiya 17:9.
NKHONDOYO INGAPAMBANIDWE
4. (a) Kaya nkhondoyo ikupambanidwa kapena kulepheredwa zimadalira pa yani? (b) Kodi nchiyani chimene chikufunika kuti tipambane nkhondo yakuchita chimene chiri chabwino?
4 Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti, munthu alibe ulamuliro pa zikhumbo zake zamphamvu zakuchita choipa. Ngati mukufunadi, mungalimbikitse mtima wanu kotero kuti udzakutsogozani m’njira yoyenera. Koma ziri kwa inu kuchita zimenezi. (Salmo 26:1, 11) Palibe aliyense amene angakupambanireni nkhondoyo. Motero, choyambirira, pitirizani kulandira chidziwitso Chabaibulo chopatsa moyo. (Yohane 17:3) Komabe zambiri zikufunika koposa kulowetsa chabe chidziwitso chimenecho m’mutu mwanu. Chiyeneranso kulowa mumtima mwanu. Muyenera kufika pa kukhala ndi lingaliro lozama ponena za zimene mukuphunzira kotero kuti mukufunadi kuchita kanthu pa izo.
5. Kodi mungapeze motani kuyamikira kwamtima malamulo a Mulungu?
5 Koma kodi mungapeze motani kuyamikira kwamtima malamulo a Mulungu? Mufunikira kusinkhasinkha, kapena kuganizira mozama, ponena za iwo. Mwa chitsanzo, dzifunseni kuti: Kodi kumvera Mulungu kumapanga kusiyana kotani kwenikweni? Ndiyeno wonani miyoyo ya anthu amene anyalanyalaza malamulo ake, monga ngati msungwana wa usinkhu wa zaka 19yo amene analemba kuti: “Ndinatenga nthenda zamwaamuna katatu konse. Ulendo wotsiriza inandichotsera kuyenera kwanga kwa kubala ana chifukwa chakuti ndinafunikira kuchotsedwa chibereko.” Nzomvetsadi chisoni kulingalira vuto lonse limene limachititsidwa pamene anthu samvera malamulo a Mulungu. (2 Samueli 13:1-19) Mkazi wina amene adachita dama mwachisoni anati: “Sikoyenererana konse ndi ululu ndi kuvutika malingaliro kumene kumadza ndi kusamvera. Ndikuvutika kaamba ka zimenezo tsopano.”
6. (a) Kodi nchifukwa ninji chikondwerero chimene chingachokere m’kuchita chimene chiri choipa sichiri chokuyenerera? (b) Kodi Mose akadasangalala ndi moyo wa mtundu wotani m’Igupto?
6 Komabe mudzamva anthu akunena kuti dama, kuphatikizapo kuledzera ndi kumeza mankhwala oledzeretsa, nkokondweretsa. Koma chotchedwa chikondwererocho nchakanthawi chabe. Musanyengedwe kulowa m’kachitidwe kamene kadzakuchotserani chimwemwe chenicheni ndi chosatha. Taganizirani Mose amene analeredwa monga “mwana wamwamuna wa mwana wamkazi wa Farao.” Iye anakhala m’chuma cha banja lachifumu kumeneko mu Igupto wakale. Komabe, Baibulo limanena kuti, pamene anakula, anasankha “kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi.” (Ahebri 11:24, 25) Motero payenera kukhala panali chikondwerero kapena zokondweretsa m’kakhalidwe koipa ndi kusadziletsa kamene mwachiwonekere kanali pakati pa banja lachifumu Lachiigupto. Pamenepa, kodi nchifukwa ninji Mose anafulatira zonsezo?
7. Kodi nchifukwa ninji Mose anafulatira ‘kusangalala ndi uchimo kwakanthawi’ m’banja lachifumu Lachiigupto?
7 Nchifukwa chakuti Mose anakhulupirira Yehova Mulungu. Ndipo iye anadziwa kanthu kena kabwino kwambiri koposa chikondwerero chirichonse chakanthawi cha uchimo chimene iye akanapeza m’banja lachifumu Lachiigupto. Baibulo limati: “Anapenyerera chobwezera cha mphoto.” Mose anasinkhasinkha, kapena anaganizira mozama, zinthu zimene Mulungu adalonjeza. Iye anali ndi chukhulupiriro m’chifuno cha Mulungu cha kulenga dongosolo latsopano lolungama. Mtima wake unakhudzidwa ndi chikondi chachikulu cha Yehova ndi chisamaliro kwa anthu. Sikunali chabe kuti Mose adamva kapena adawerenga ponena za Yehova. Baibulo likunena kuti “anapirira molimbika, monga ngati kuwona wosawonekayo.” (Ahebri 11:26, 27) Yehova anali weniweni kwa Mose, ndipo chomwechonso malonjezo ake a moyo wosatha.
8. (a) Kuti tipambane nkhondo yakuchita chabwino, kodi tikufunikiranji? (b) Kodi ndilingaliro lotani, monga momwe lasonyezeredwera ndi mnyamata wina, kukhala kwanzeru kukhala nalo?
8 Kodi ziri choncho ndi inu? Kodi mumawona Yehova kukhala Munthu weniweni, monga Atate amene amakukondani? Pamene muwerenga malonjezo ake a kupereka moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi, kodi mumadziwona m’chithunzithunzi mulimo mukusangalala ndi madalitso amenewa? (Wonani tsamba 156 kufikira 162.) Kuti tipambane nkhondo yomenyana ndi zitsenderezo zambiri za kuchita choipa, tifunikira kukhala ndi unansi weniweni ndi Yehova. Ndipo tifunikira kuyang’ana, monga momwe anachitira Mose, ‘dwii ku kuperekedwa kwa mphotho.’ Mnyamata wina wa usinkhu wa zaka 20, amene anayang’anizana ndi chiyeso cha kuchita dama, anali ndi lingaliro la Mose. Iye anati: “Chiyembekezo changa cha moyo wosatha chinali chamtengo wapatali kwambiri kosati nkuchitaya kaamba ka mphindi zowerengeka za chigololo.” Kodi limenelo silingaliro labwino kukhala nalo?
KUPHUNZIRA M’ZOLAKWA ZA ENA
9. Kodi Mfumu Davide analephera m’njira yotani yakuchita chimene chiri chabwino?
9 Simungalekerere kukhala kwanu maso m’nkhondo imeneyi, monga momwe anachitira Mfumu Davide pa nthawi ina. Tsiku lina iye ankayang’ana ali pamwamba pa denga lake, ndipo chauko anawona Bateseba wokongola akusamba. Koposa ndi kupotoloka malingaliro osayenera asanakule mumtima mwake, iye anayang’anabe. Chikhumbo chake chakugonana ndi Beteseba chinakhala champhamvu kwambiri chakuti iye anamuitanitsa kunyumba yake yachifumu. Pambuyo pake, popeza kuti mkaziyo adakhala ndi pakati, ndipo iye anali wosakhoza kuchititsa chigololo chawo kubisika, iye analiganiza kuti mwamuna wake aphedwe m’nkhondo.—2 Samueli 11:1-17.
10. (a) Kodi Davide analangidwa motani kaamba ka tchimo lake? (b) Kodi nchiyani chimene chikadapewetsa kulowa kwa Davide m’chigololo?
10 Limenelo linalidi tchimo lowopsa. Ndipo Davide anavutika nalodi. Osati kokha anasautsika kwambiri ndi zimene adachita, koma Yehova anamlanga ndi vuto m’banja lake kwa moyo wake wonse. (Salmo 51:3, 4; 2 Samueli 12:10-12) Mtima wa Davide unali wonyenga kwambiri koposa mmene iye anazindikirira; zikhumbo zake zoipa zinamgonjetsa. Pambuyo pake iye anati: “Wonani, ndinabadwa m’mphulupulu: ndipo mayi wanga anandilandira m’zoipa.” (Salmo 51:5) Koma chinthu choipa chimene Davide anachita ndi Bateseba sichinafunikire kuchitika. Vuto lake linali lakuti iye anapitiriza kuyang’ana; sanapewe mkhalidwe umene unachititsa chilakolako chake kukula kaamba ka mkazi wa munthu wina.
11. (a) Kodi tiyenera kuphunziranji m’chokumana nacho cha Davide? (b) Kodi nzochita zotani zimene munganene kuti zinganyandule “chilakolako”? (c) Monga momwe wachichepere wina anafotokozera, kodi munthu wanzeru amapewanji?
11 Tiyenera kuphunzira m’chokumana nacho cha Davide kuchenjerera mikhalidwe imene imanyandula zilakolako zosayenera zakugonana. Mwa chitsanzo, kodi chidzachitika nchiyani ngati muwerenga mabukhu ndi kuwonera maprogramu atelevizheni ndi akanema amene amaika chigogomezero pa kugonana? Mosakayikira zilakolako zakugonana zidzadzutsidwa. Motero pewani zochita ndi zosangalatsa zimene zimayambitsa “chilakolako.” (Akolose 3:5; 1 Atesalonika 4:3-5; Aefeso 5:3-5) Musadziike mu mkhalidwe wa munthu wina umene ungatsogolere ku dama. Wina wa usinkhu wa zaka 17 ananena mwanzeru kuti: “Aliyense anganene kuti, ‘tikudziwa polekezera.’ Zowona, munthu angadziwe polekezera, koma kodi ndi angati angatero? Kuli bwino kwambiri kupewa mkhalidwewo.”
12. Kodi ndichitsanzo cha Yosefe chotani chimene tiyenera kukumbukira?
12 Ngati Davide akadakumbikira chitsanzo cha Yosefe, iye sakadachitira Mulungu tchimo lalikulu limenelo. Ku Igupto, Yosefe adaikidwa kukhala woyang’anira banja la Potifala. Pamene Potifala anali atachoka, mkazi wake wanyereyo ankayesa kunyenga Yosefe wokongolayo, kuti: “Gona ndi ine.” Koma Yosefe anakana. Ndiyeno tsiku lina iye anamgwira nayesa kumpangitsa kugona naye. Koma Yosefe anapsatanguka nathawa. Iye analimbikitsabe mtima wake mwa kuganizira, osati kukhutiritsa chilakolako chake cha iye mwini, koma chimene chinali chabwino m’maso mwa Mulungu. “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” iye anatero.—Genesis 39:7-12.
CHITHANDIZO CHIMENE MUKUFUNIKIRA KUTI MUPAMBANE
13, 14. (a) Kodi nchiyani chimene chikufunika kuti tipambane nkhondo imeneyi? (b) Kodi awo amene anakhala Akristu m’Korinto anapanga kusintha kotani, ndipo limodzi ndi chithandizo chotani? (c) Kodi Paulo ndi Tito adali anthu a mtundu wotani?
13 Kuti mupambane nkhondo imeneyo muyenera kulola chidziwitso Chabaibulo kutsikira mumtima mwanu kotero kuti mukusonkhezeredwa kuchita kanthu pa icho. Koma mufunikiranso kusonkhana ndi anthu a Mulungu, kukhala mbali ya gulu lowoneka la Yehova. Mwachithandizo chake, ziribe kanthu mmene mungakhalire mutalowerera kwambiri m’kuchita cholakwa, mungasinthe. Ponena za anthu m’Korinto wakale amene anasintha, mtumwi Paulo analemba kuti: “Musasocheretsedwe, adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa.”—1 Akorinto 6:9-11.
14 Taganizirani zimenezo! Ena a Akristu oyambirira amenewo papitapo adali adama, achigololo, odziipsa ndi amuna, mbala ndi oledzera. Koma mothandizidwa ndi gulu Lachikristu iwo anasintha. Mtumwi Paulo mwiniyo adachitapo zinthu zoipa. (1 Timoteo 1:15) Kwa Mkristu mnzake, Tito, iye analemba kuti: “Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu.”—Tito 3:3.
15. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti sikunali kwapafupi kwa Paulo kuchita chimene chiri chabwino? (b) Kodi tingapindule motani ndi chitsanzo cha Paulo?
15 Pamene Paulo anakhala Mkristu, kodi kunali kofewa kwa iye kuchita chimene chiri chabwino? Ayi. Paulo anali ndi nkhondo yamoyo wonse yolimbana ndi zikhumbo zoipa ndi zokondweretsa ku zimene iye anali kapolo pa nthawi ina. Analemba kuti: “Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.” (1 Akorinto 9:27) Paulo ‘anadzilumira mano’. Iye ankadzikakamiza kuchita chimene chiri chabwino, ngakhale pamene thupi lake linafuna kuchita choipa. Ndipo ngati inu muchita monga momwe iye anachitira, inunso mungapambane nkhondo imeneyi.
16. Kodi ndizitsanzo zamakono zotani zimene zingatithandize kupambana nkhondo yakuchita chabwino?
16 Ngati mukuwona kukhala kovuta kugonjetsa chizolowezi china choipa, fikani pamsonkhano waukulu wotsatirapo wa Mboni za Yehova. Mosakayikire mudzagwidwa mtima ndi khalidwe loyera ndi chisangalalo cha awo ofikapo. Chikhalirechobe ambiri a anthu amenewa anali pa nthawi ina mbali ya dziko lino m’limene dama, chigololo, kuledzera, kudziipsa ndi amuna, kusuta fodya, kumwerekera ndi mankhwala oledzeretsa, kuba, chinyengo, kunama ndi kutchova juga ziri zofala kwambiri. Ambiri a iwo anachita zinthu zimenezi nthawi ina. (1 Petro 4:3, 4) Ndiponso, pamene mukusonkhana ndi Mboni za Yehova pamisonkhano yampingo yocheperapo, kumene kuyenera kuchitidwa mosazengereza, mudzakhala pakati pa anthu amene amenya nkhondo kuti alake machitidwe ndi zikhumbo zoipa zimodzimodzizo zimene inu tsopano mungakhale mukumenyana nazo. Motero limbani mtima! Iwo akupambana nkhondo ya kuchita chimene chiri chabwino. Inunso mungapambane mwa chithandizo cha Mulungu.
17. (a) Kodi ndikusonkhana kotani kumene kuli kofunika ngati titi tipambane nkhondoyo? (b) Kodi nkwayani kumene mungalandire chithandizo cha mavuto?
17 Ngati mwakhala mukuphunzira Baibulo kwa nthawi yaitali tsopano ndi Mboni za Yehova, mosakayikira mwafika pa Nyumba Yaufumu. Tonsefe timafuna chilimbikitso chauzimu cholandiridwa m’kusonkhana Kwachikristu koteroko. (Ahebri 10:24, 25) Fikani pa kudziwa “akulu,” kapena achikulire, a mpingo. Thayo lawo ndilo “kuweta gulu la Mulungu.” (1 Petro 5:1-3; Machitidwe 20:28) Motero musadodome kupita kwa iwo ngati mukufuna chithandizo kuti mulake chizolowezi china chimene chiri chosemphana ndi malamulo a Mulungu. Mudzawawona kukhala achikondi, okoma mtima ndi olingalira.—1 Atesalonika 2:7, 8.
18. Kodi ndichiyembekezo chamtsogolo chotani chimene chimapereka nyonga ya kupitirizabe m’nkhondoyo?
18 Chitsenderezo chakuchita choipa chimakhala pa ife, osati kokha chochokera kudziko la Satana koma kochokera mkati mwa thupi lathu lauchimo. Motero kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ndiko nkhondo yatsiku ndi tsiku. Ndipo kuli bwino chotani nanga kuti nkhondoyo sidzapitiriza kosatha! Posachedwa Satana adzachotsedwa ndipo dziko lake lonse loipa lidzawonongedwa. Ndiyeno, m’dongosolo latsopano la Mulungu loyandikiralo, mudzakhala mikhalidwe yolungama imene idzapangitsa njira yathu kukhala yosavuta kwambiri. Potsirizira pake zotsalirira zonse za uchimo zidzachoka, ndipo sikudzakhalanso nkhondo yaikulu imeneyi yakuchita chimene chiri chabwino.
19. Kodi nchifukwa ninji inu muyenera kukhala ofunitsitsa kupanga kuyesayesa kulikonse kuti mukondweretse Mulungu?
19 Ganizirani nthawi ndi nthawi madalitso a dongosolo latsopano limenelo. Inde, valani “monga chisoti chiyembekezo cha chipulumutso.” (1 Atesalonika 5:8, NW) Lingaliro lanu likhaletu lija la mkaziyo amene anati: “Ndimaganizira chirichonse chimene Yehova wandichitira ndi kundilonjeza. Iye sanandileke. Wandidalitsa m’njira zambirimbiri. Ndikudziwa kuti iye amafuna kokha zabwino koposa kwa ine, ndipo ndikufuna kumkondweretsa. Moyo wamuyaya ngwoyenerera kuyesayesa kulikonse.” Ngati tilondola chilungamo mokhulupirika, ‘malonjezo onse abwino amene Yehova wapanga’ kwa awo amene akumkonda adzakwaniritsidwa.—Yoswa 21:45.
[Chithunzi patsamba 219]
Popeza kuti munali chikondwerero m’kakhalidwe ka Igupto wakale, kodi nchifukwa ninji Mose anakakana?
[Zithunzi pamasamba 220, 221]
Davide anayang’anabe; sanapewe mkhalidwe umene unatsogolera ku choipa
[Chithunzi patsamba 222]
Yosefe anathawa zonyengerera zoipa za mkazi wa Potifala