Dalirani Yehova Kuti Adzakwaniritsa Chifuno Chake
“Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—SALMO 37:29.
1. Kodi chifuno cha Yehova nchotani kaamba ka anthu ndi dziko lapansi lino?
PAMENE Yehova analenga makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anawalenga angwiro. Ndipo anawalenga kuti akhale ndi moyo kosatha padziko lapansi lino,—akadamvera malamulo ake. (Genesis 1:26, 27; 2:17) Ndiponso, Mulungu anawaika m’malo aparadaiso. (Genesis 2:8, 9) Yehova anati kwa iwo: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28) Motero, mbadwa zawo m’kupita kwanthaŵi zikafalikira padziko lonse lapansi, ndipo pulaneti lino likakhala paradaiso wodzazidwa ndi fuko la anthu angwiro ndi achimwemwe. Ha, ndichiyambi chabwino chotani nanga chimene banja la anthu linali nacho! “Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.”—Genesis 1:31.
2. Kodi mkhalidwe wa zinthu wa anthu umabutsa mafunso otani?
2 Komabe, mkhalidwe wa zinthu wa anthu umene wakhalapo kwa zaka zikwizikwi sukusonyeza kufanana kulikonse ndi chifuno choyambirira cha Mulungu. Mtundu wa anthu watalikirana kwambiri ndi ungwiro ndipo suli wachimwemwe konse. Mikhalidwe ya dziko yakhala yosautsa, ndipo monga momwe kunaloseredwa, iyo yaipa chiipire m’nthaŵi yathu. (2 Timoteo 3:1-5, 13) Chotero kodi ndimotani mmene tingakhalire achidaliro kuti chifuno cha Mulungu kwa anthu chidzakwaniritsidwa posachedwapa? Kodi padzapitabe nyengo zazitali ndi mikhalidwe yosautsa yopitirizabe?
Kodi Chinalakwika Nchiyani?
3. Kodi nchifukwa ninji Yehova sanathetse chipanduko cha mtundu wa anthu poyamba penipenipo?
3 Awo amene ali ndi chidziŵitso cholongosoka cha Mawu ouziridwa a Mulungu amadziŵa chifukwa chake Yehova walola mikhalidwe yoipa imeneyi padziko lapansi. Amadziŵanso zimene adzachita pa iyo. Mwa cholembedwa cha Baibulo, iwo adziŵa kuti makolo athu oyamba anagwiritsira ntchito molakwa mphatso yabwino koposa ya ufulu wakudzisankhira imene Mulungu adapatsa anthu. (Yerekezerani ndi 1 Petro 2:16.) Iwo anasankha molakwa njira yosadalira Mulungu. (Genesis, chaputala 2 ndi 3) Chipanduko chawo chinadzutsa mafunso aakulu kwambiri, onga akuti: Kodi Mfumu Yachilengedwe Chonse ili ndi kuyenerera kwa kulamulira anthu? Kodi ulamuliro wake ndiwo wabwino koposa kwa iwo? Kodi ulamuliro wa anthu ungapambane popanda uyang’aniro wa Mulungu? Njira yotsimikizirika yopezera mayankho pamafunsoŵa inali kulola zaka mazana ambiri za ulamuliro wa munthu kupita. Zotulukapo zikasonyeza popanda chikayikiro chilichonse kuti kaya anthu akakhoza kupambana popanda Mpangi wawo kapena ayi.
4, 5. (a) Kodi nchiyani chakhala chotulukapo cha kukana kwa anthu ulamuliro wa Mulungu? (b) Kodi kupita kwanthaŵi kwasonyezanji popanda chikayikiro chilichonse?
4 Pamene Adamu ndi Hava anasiya Mulungu, iye sanawachirikizenso mwaungwiro. Popanda chichirikizo chake, iwo anafumuka. Chotsatirapo chinali kupanda ungwiro, ukalamba, ndiyeno imfa potsirizira pake. Kupyolera m’malamulo a choloŵa chachibadwa, makolo athu oyamba anayambukiritsa mikhalidwe yovulaza imeneyo kwa mbadwa zawo zonse, kuphatikizapo ifeyo. (Aroma 5:12) Ndipo bwanji ponena za chotulukapo cha zaka zikwi zambiri za ulamuliro waumunthu? Chakhala chatsoka, monga momwe lemba la Mlaliki 8:9 limanenera mowona kuti: “Wina apweteka mnzake pomlamulira.”
5 Kupita kwanthaŵi kwasonyeza motsimikizirika ndithu kuti sikuli kwa anthu kuyendetsa zinthu zawo mwachipambano popanda Mlengi wawo. Mlembi wa Baibulo wouziridwa Yeremiya analengeza kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23; Deuteronomo 32:4, 5; Mlaliki 7:29.
Chifuno cha Mulungu Sichinasinthe
6, 7. (a) Kodi zikwi za zaka za mbiri zasintha chifuno cha Yehova? (b) Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’chifuno cha Yehova?
6 Kodi zikwi za zaka za mbiri ya munthu zapitazo—zodzala ndi kuipa ndi kuvutika—zasintha chifuno cha Mulungu? Mawu ake amanena kuti: “Atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Motero Mulungu anaumba dziko lapansi kuti anthu akhalepo, ndipo chimenecho chidakali chifuniro chake.
7 Yehova sanalenge dziko lapansi kokha kuti likhale ndi anthu koma anafunanso kuti likhale paradaiso wa anthu angwiro, achimwemwe. Nchifukwa chake Baibulo linaneneratu kuti padzakhala “dziko latsopano,” chitaganya chatsopano cha anthu, mmene “mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Ndipo pa Chivumbulutso 21:4, Mawu a Mulungu amatiuza kuti m’dziko lake latsopanolo, “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo [anthu]; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” Ndicho chifukwa chake Yesu anakhoza kunena za dziko lapansi latsopano likudzalo monga “Paradaiso.”—Luka 23:43.
8. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzakwaniritsa chifuno chake?
8 Popeza kuti Yehova ali Mlengi wamphamvu zonse ndi wanzeru zonse wa chilengedwe chonse, palibe amene angalepheretse chifuno chake. “Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala.” (Yesaya 14:24) Chifukwa chake, pamene Mulungu anena kuti adzapangitsa dzikoli kukhala paradaiso wokhalamo anthu angwiro, zimenezo ndizo zidzachitikadi. Yesu anati: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5; yerekezerani ndi Salmo 37:29.) Tingathe kukhala ndi chidaliro cha kukwaniritsidwa kwa lonjezolo. Ndithudi, tikhoza kuikadi miyoyo yathu yeniyeniyo pachiswe kaamba ka ilo.
Iwo Anadalira Yehova
9. Kodi Abrahamu anachitanji chimene chinasonyeza chidaliro chake mwa Yehova?
9 Anthu ambiri owopa Mulungu m’mbiri yonse aika miyoyo yawo pachiswe kaamba ka chifuniro cha Mulungu cha dziko lapansi chifukwa chakuti anali okhutiritsidwa kuti iye akachikwaniritsa. Ngakhale kuti chidziŵitso chawo chingakhale chinali chochepa, iwo anadalira Mulungu ndipo anamanga miyoyo yawo pakuchita chifuniro cha Mulungu. Mwachitsanzo, panali Abrahamu, yemwe anakhalapo ndi moyo pafupifupi zaka 2,000 Yesu asanadze padziko lapansi—kale kwambiri Baibulo lisanayambe kulembedwa. Iye anadalira Yehova kuti akakwaniritsa malonjezo Ake. Mwachionekere, Abrahamu anaphunzira ponena za Mlengi kwa kholo lake lokhulupirika, Semu, amenenso anaphunzitsidwa ndi Nowa. Motero pamene Mulungu anauza Abrahamu kuchoka m’dziko lotukuka la Uri la Akaldayo kukaloŵa m’dziko losazoloŵereka ndi lowopsa la Kanani, khololo linadziŵa kuti likadalira Yehova, motero linapita. (Ahebri 11:8) M’kupita kwanthaŵi, Yehova analiuza kuti: “Ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu.”—Genesis 12:2.
10, 11. Kodi nchifukwa ninji Abrahamu anali wofunitsitsa kupereka mwana wake wobadwa yekha, Isake?
10 Kodi chinachitika nchiyani pambuyo poti Isake wabadwa kwa Abrahamu? Yehova anasonyeza Abrahamu kuti mbadwa zake zikakhala mtundu waukulu kudzera mwa Isake. (Genesis 21:12) Motero, kuyenera kuti kunaoneka kukhala kuwombana pamene Yehova anauza Abrahamu, monga chiyeso cha chikhulupiriro chake, kupereka nsembe mwana wake Isake. (Genesis 22:2) Komabe, ataika chidaliro chonse mwa Yehova, Abrahamu anachitapo kanthu ndi kulabadira, akumatengadi mpeni kuti aphe Isake. Pamphindi yotsirizira yeniyeni, Mulungu anatumiza mngelo kudzaletsa Abrahamu.—Genesis 22:9-14.
11 Kodi nchifukwa ninji Abrahamu anali womvera motero? Lemba la Ahebri 11:17-19 limavumbula kuti: “Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano anapereka mwana wake wayekha; amene kudanenedwa za iye, kuti Mwa Isake mbewu yako idzaitanidwa: poyesera iye kuti Mulungu ngokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso.” Mofananamo lemba la Aroma 4:20, 21 limati: “Ndipo poyang’anira lonjelo la Mulungu [Abrahamu] sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, . . . nakhazikikanso mumtima kuti, chimene [Mulungu] analonjeza, anali nayonso mphamvu ya kuchichita.”
12. Kodi Abrahamu anafupidwa motani kaamba ka chikhulupiriro chake?
12 Abrahamu anafupidwa chifukwa cha chikhulupiriro chake osati kokha mwa kupulumutsidwa kwa Isake ndi mwa kukhala ndi “mtundu waukulu” kudzera mwa iye komanso mwa njira ina. Mulungu anauza Abrahamu kuti: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mawu anga.” (Genesis 22:18) Motani? Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu ikadza kudzera mwa mzera wobadwira wa Abrahamu. Ufumuwo ukaphwanya ndi kuchotsa dziko loipali la Satana. (Danieli 2:44; Aroma 16:20; Chivumbulutso 19:11-21) Ndiyeno, m’dziko lapansi loyeretsedwa pansi paulamuliro wa Ufumuwo, Paradaiso akafutukulidwira pambulunga yonse, ndipo anthu ochita chifuniro cha Mulungu a “mitundu yonse” adzasangalala ndi thanzi langwiro ndi moyo wosatha. (1 Yohane 2:15-17) Ndipo ngakhale kuti Abrahamu anali chabe ndi chidziŵitso chochepa cha Ufumuwo, anadalira Mulungu ndipo anayembekezera kukhazikitsidwa kwake.—Ahebri 11:10.
13, 14. Kodi nchifukwa ninji Yobu anadalira Mulungu?
13 Pambuyo pa zaka mazana angapo, panali Yobu, yemwe anakhala ndi moyo pakati pa zaka za mazana a 17 ndi 16 B.C.E., m’dziko tsopano lotchedwa Arabia. Iyenso anakhalako Baibulo lisanayambe kulembedwa. Yobu “anali wangwiro ndi woongoka, wakuwopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.” (Yobu 1:1) Pamene Satana anakantha Yobu ndi nthenda yopweteka ndi yochititsa nseru, mwamuna wokhulupirika ameneyo “sanatchula ngakhale liwu limodzi lochimwa” m’kusautsika kwake konseko. (Yobu 2:10, The New English Bible) Yobu anadalira Mulungu. Ndipo ngakhale kuti sanadziŵe zonse zoloŵetsedwamo m’chimene anali kuvutikira motero, iye anangoyika moyo wake pachiswe kaamba ka Mulungu ndi malonjezo Ake.
14 Yobu anadziŵa kuti chinkana akafa, Mulungu akakhoza tsiku lina kumbwezereta ku moyo mwa chiukiriro. Iye anasonyeza chiyembekezo chimenechi pamene anati kwa Yehova Mulungu: “Ha! mukadandibisa kumanda, Mukadandisunga mtseri, . . . Mukadandiikira nthaŵi, ndi kundikumbukira. Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? . . . Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani.” (Yobu 14:13-15) Chinkana kuti anali paululu wa nsautso, Yobu anasonyeza chikhulupiriro pa uchifumu wa Yehova, akumati: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.”—Yobu 27:5.
15. Kodi ndimotani mmene Davide anasonyezera chidaliro chake m’chifuno cha Yehova?
15 Kwa zaka pafupifupi mazana asanu ndi limodzi pambuyo pa Yobu, ndipo pafupifupi zaka chikwi Yesu asanadze padziko lapansi, Davide anasonyeza chidaliro chake cha dziko latsopano. Iye anati m’salmo: “Iwo akuyembekeza Yehova, iwoŵa adzalandira dziko lapansi. Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Chifukwa cha chikhulupiriro chake chosagwedera, Davide analimbikitsa kuti: “Khulupirira Yehova, . . . Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.”—Salmo 37:3, 4, 9-11, 29.
16. Kodi ndichiyembekezo chotani chimene ‘mtambo waukulu wa mboni’ uli nacho?
16 M’zaka mazana onsewo, amuna ndi akazi okhulupirika akhala ndi chiyembekezo chimodzimodzichi cha moyo wosatha padziko lapansi. Kwenikweni, iwo amapanga ‘mtambo waukulu wa mboni’ zimene m’lingaliro lenileni zinaika pachiswe miyoyo yawo kaamba ka malonjezo a Yehova. Mboni za Yehova zochuluka zakalezo zinazunzidwa ndi kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, “kuti akalandire kuuka koposa.” Motani? M’dziko latsopano, Mulungu adzawafupa ndi chiukiriro choposa ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.—Yohane 5:28, 29; Ahebri 11:36; 12:1.
Mboni Zachikristu Zimadalira Mulungu
17. Kodi Akristu a m’zaka za zana loyamba anadalira Yehova mwamphamvu chotani?
17 M’zaka za zana loyamba C.E., Yehova anavumbulira mpingo Wachikristu wokhazikitsidwa chatsopanowo mbali zowonjezereka zonena za Ufumuwo ndi ulamuliro wake padziko lapansi. Mwachitsanzo, mzimu wake unauzira mtumwi Yohane kulemba kuti chiŵerengero cha awo amene akagwirizana ndi Yesu Kristu mu Ufumu wakumwamba chikakhala 144,000. Iwoŵa akakhala atumiki a Mulungu okhulupirika omwe ‘akagulidwa mwa mtundu wa anthu.’ (Chivumbulutso 7:4; 14:1-4) Iwo akalamulira dziko lapansi monga ‘mafumu’ limodzi ndi Kristu kumwamba. (Chivumbulutso 20:4-6) Motero Akristu a m’zaka za zana loyamba anadalira Yehova mwamphamvu kuti akakwaniritsa chifuno chake cha Ufumu wakumwamba ndi ulamuliro wake wa padziko lapansi kwakuti anali ofunitsitsa kupereka miyoyo yawo kaamba ka chikhulupiriro chawo. Ambiri a iwo anachita zimenezo kumene.
18. Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova lerolino zimatsanzirira zinzawo za m’nthaŵi zakale?
18 Lerolino, Mboni za Yehova pafupifupi mamiliyoni asanu zili ndi chidaliro chimodzimodzicho mwa Mulungu monga momwe zinachitira zinzawo zomwe zinakhalako zaka mazana ambiri izo zisanakhalepo. Mboni zamakono zimenezi zaikanso miyoyo yawo pachiswe chifukwa cha malonjezo a Mulungu. Izo zapatulira miyoyo yawo kwa iye ndipo zili ndi Baibulo lathunthu monga lolimbitsa chikhulupiriro chawo. (2 Timoteo 3:14-17) Mboni za Yehova zamakono zimenezi zimatsanzira otsatira a Yesu a m’zaka za zana loyamba omwe analengeza kuti ‘anayenera kumvera Mulungu koposa anthu.’ (Machitidwe 5:29) M’zaka za zana lino ambiri a Mboni Zachikristu zimenezi azunzidwa mwankhalwe. Ena ngakhale kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ena amwalira ndi matenda, ngozi, kapena ukalamba. Komabe, mofanana ndi mboni zokhulupirika za m’nthaŵi zakale, iwo adalira Mulungu chifukwa chakuti anadziŵa kuti iye akawabwezeretsa ku moyo m’dziko lake latsopano mwa chiukiriro.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15; Chivumbulutso 20:12, 13.
19, 20. Kodi timazindikiranji za ulosi wa Baibulo ponena za tsiku lathu?
19 Mboni za Yehova zimazindikira kuti kutengedwa kwawo m’mitundu yonse ndi kukhala gulu limodzi laubale wapadziko lonse kunanenedweratu kalekale muulosi wa Baibulo. (Yesaya 2:2-4; Chivumbulutso 7:4, 9-17) Ndipo Yehova akuwachititsa ntchito yolalikira ya padziko lonse kotero kuti asonkhanitsire enanso owona mtima ku chiyanjo ndi chitetezo chake. (Miyambo 18:10; Mateyu 24:14; Aroma 10:13) Onseŵa amaika chidaliro chawo chonse mwa Yehova, podziŵa kuti posachedwapa adzabweretsa dziko lake latsopano lodabwitsalo.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 15:58; Ahebri 6:10.
20 Maulosi a Baibulo amasonyeza kuti dziko la Satana lakhala m’masiku ake otsiriza kwa zaka pafupifupi 80 tsopano, chiyambire chaka chosinthirapo zinthucho cha 1914. Dzikoli likuyandikira mapeto ake. (Aroma 16:20; 2 Akorinto 4:4; 2 Timoteo 3:1-5) Motero Mboni za Yehova zili zolimbika mtima ndi zotsimikiza chifukwa zimadziŵa kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzatenga ulamuliro wonse wa zinthu padziko lonse lapansi. Mwa kuchotsapo dziko loipali ndi kubweretsa dziko lake latsopano lolungama, Mulungu adzafafaniza kotheratu mkhalidwe woipa umene wakhala padziko lapansi kwa zaka mazana ambiri.—Miyambo 2:21, 22.
21. Kodi nchifukwa ninji tingakhale osangalala mosasamala kanthu za mavuto amakono?
21 Ndiyeno, kwa umuyaya wonse, Mulungu adzasonyeza chisamaliro chake chachikulu kwa ife mwa kutitsanulira madalitso amene adzaloŵa m’malo choŵaŵitsa chilichonse chakale. Motero, padzachitika zinthu zabwino zambiri kwa ife m’dziko latsopano kwakuti mavuto athu akumbuyo adzafafanizika kotheratu m’chikumbukiro chathu. Kuli kotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti Yehova panthaŵiyo ‘adzatambasula dzanja lake ndi kukwaniritsa zamoyo zonse chokhumba chawo.’—Salmo 145:16; Yesaya 65:17, 18.
22. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuika chidaliro chathu mwa Yehova?
22 M’dziko latsopano, mtundu wa anthu okhulupirika udzaona kukwaniritsidwa kwa Aroma 8:21: “Cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” Adzaona kukwaniritsidwa kwa pemphero limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake lakuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Motero ikani chidaliro chanu chonse mwa Yehova chifukwa chakuti lonjezo lake losalephereka nlakuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi chifuno cha Yehova nchotani kaamba ka anthu ndi dziko lapansi lino?
◻ Kodi nchifukwa ninji Mulungu walola mikhalidwe yoipa padziko lapansi?
◻ Kodi ndimotani mmene anthu okhulupirika akale anasonyezera chidaliro chawo mwa Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji atumiki a Mulungu lerolino amadalira Yehova?
[Chithunzi patsamba 16]
Mulungu analenga anthu kuti akhale ndi moyo kosatha mwachimwemwe padziko lapansi laparadaiso
[Chithunzi patsamba 18]
Abrahamu anaika chidaliro chake m’mphamvu ya Yehova ya kuukitsa akufa