-
Dziko Lapansi Silinayenera IwoNsanja ya Olonda—1987
-
-
13. (a) Ndi ndani amene anazunzidwa mwa “kusekedwa ndi kumangidwa zingwe”? (b) Ndani amene anakumana “ndi kumangidwa ndi kuikidwa m’ndende”?
13 Ngati tiri ndi chikhulupiriro, tidzakhoza kupirira chizunzo. (Werengani Ahebri 11:36-38.) Pamene tikuzunzidwa, chingakhale chathandizo kukumbukira chiyembekezo cha chiukiriro mwa kuzindikira kuti Mulungu adzatithandiza ife monga m’mene anachitira ndi “ena [omwe] analandira chiyeso chawo [kapena, chiyeso chachikhulupiriro] mwa kusekedwa ndi kumangidwa zingwe, indedi, koposa chimenecho, ndi zingwe ndi ndende.” Aisrayeli “mopitirira anali kuseka aneneri ake, kufikira pamene mkwiyo wa Yehova unabwera pa anthu ake.” (2 Mbiri 36:15, 16) Ndi chikhulupiriro Mikaya, Elisa, ndi atumiki ena a Mulungu anapirira “kusekedwa.” (1 Mafumu 22:24; 2 Mafumu 2: 23, 24; Masalmo 42:3) “Kumangidwa zingwe” kunali kodziwika mu masiku a mafumu a Israyeli ndi aneneri, ndipo otsutsa “anamenya” Yeremiya, osati kokha kungomumenya monga woukira. “Zingwe ndi ndende” zingatikumbutse ife za zokumana nazo zake limodzi ndi za aneneri ena monga Mikaya ndi Hananiya. (Yere miya 20:l, 2; 37:15 1 Mafumu 12:11; 22:26, 27;2 Mbiri 16:7, 10) Chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro chofananacho, Mboni zaYehova zamakono zakhala zokhoza kupirira kuzunzika kofananako “kaamba ka chilungamo.”—1 Petro3:14.
-
-
Dziko Lapansi Silinayenera IwoNsanja ya Olonda—1987
-
-
15. Kodi ndani amene “anachitidwa zoipa” ndi “kuyendayenda m’zipululu”?
15 Ena “anafa ndi lupanga,” monga, mwachitsanzo, aneneri a Mulungu anzake a Eliya “anaphedwa ndi lupanga” masiku a Mfumu yoyipa Ahabu. (1 Mafumu 19:9, 10) Eliya ndi Elisa anali pakati pa awo omwe anali ndi chikhulupiriro omwe “anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa za mbuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa.” (1 Mafumu 19:5-8, 19; 2 Mafumu 1:8; 2:13; yerekezani ndi Yeremiya 38:6. ) Awo amene “anasokerera mumapululu ndi m’mapiri ndi m’mapanga ndim’mauna adziko” monga nkhole za chizunzo ayenera kuphatikiza osati kokha Eliya ndi Elisa komanso aneneri 100 omwe Obadiya anawabisa mu unyinji wa 50 m’mapanga, akumawapatsa iwo mkate ndi madzi pamene Mfumukazi Yezebeli wolambira mafano anayamba “kudula aneneri a Yehova.” (1 Mafumu 18:4, 13; 2 Mafumu2:13; 6:13, 30, 31) Ndi asungiriri aumphumphu a mtundu wotani nanga! Chosadabwitsa kuti Paulo akunena kuti: “Dziko lapansi [sosaite ya mtundu wa anthu osalungama] silinayenera iwo”!
-