Chikondi Chanu cha pa Abale Chikhalebe!
“Chikondi [chanu, NW] cha pa abale chikhalebe.”—AHEBRI 13:1.
1. Kodi mungachitenji kuti moto usazime usiku kutazizira, ndipo ndi ntchito iti yofanana imene tonse tili nayo?
KUNJA nkozizira kwambiri moti nkupha munthu, ndipo kuzizirako kukuwonjezeka. Chipinda chokha chotentha m’nyumba mwanu ndi chija chimene muli moto wothetheka. Kuti mukhale amoyo, mufunika kumasonkhezera motowo. Kodi mudzangokhala ndi kumaupenya motowo ukuzima mpaka makala ake ofiira atazirala? Kutalitali! Mudzalimbikira kusonkhezapo nkhuni kuti usazime. Tingati ifenso tili ndi ntchito yonga imeneyo pa “moto” wofunika koposa—umene uyenera kumayaka m’mitima mwathu—chikondi.
2. (a) Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti chikondi chazirala masiku ano otsiriza? (b) Kodi chikondi nchofunika motani kwa Akristu oona?
2 Tili m’nthaŵi imene, malinga ndi ulosi wa Yesu kalelo, chikondi chikuzirala pakati pa odzitcha Akristu kuzungulira dziko lonse. (Mateyu 24:12) Yesu anali kunena za chikondi chofunika kwambiri, kukonda Yehova Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo. Mitundu inayo ya chikondi ikuziralanso. Baibulo linalosera kuti “masiku otsiriza,” ambiri adzakhala “opanda chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:1-5) Zimenezo nzoonadi! M’banja muyenera kukhala chikondi chachibadwidwe, koma ngakhale mmenemo, chiwawa ndi nkhanza—nthaŵi zina zoopsa kwambiri—zilimo kwambiri. Komabe, m’nyengo yozizira ya dzikoli, Akristu amalamulidwa osati chabe kukondana wina ndi mnzake komanso kukhala ndi chikondi chodzimana, kuika ena patsogolo pako. Tiyenera kusonyeza chikondi chimenechi bwino lomwe kuti chionekere kwa onse, kukhala chizindikiro chodziŵitsa mpingo woona wachikristu.—Yohane 13:34, 35.
3. Kodi chikondi cha pa abale nchiyani, ndipo kunena kuti chikhalebe kutanthauzanji?
3 Mtumwi Paulo anauziridwa kulamula kuti: “Chikondi [chanu] cha pa abale chikhalebe.” (Ahebri 13:1) Malinga ndi buku lina la maphunziro, liwu lachigiriki lotembenuzidwa panopa kuti “chikondi cha pa abale” (phi·la·del·phiʹa) “limanena za chikondi cha m’mtima, kukoma mtima, chifundo, kufuna kuthandiza.” Ndipo kodi Paulo anatanthauzanji pamene anati chikondi chotero chikhalebe? “Sichiyenera kuzirala,” buku limodzimodzilo likutero. Choncho sikokwanira kungokhala ndi chikondi pa abale athu; tiyenera kuchionetsera. Ndiponso, tiyenera kuchititsa chikondi chimenechi kukhalitsa, osachilola kuzirala. Mukuti nzovuta? Inde, koma mzimu wa Yehova ungatithandize kukhala ndi chikondi cha pa abale ndi kuchisunga. Tiyeni tipende njira zitatu zosonkhezerera moto wa chikondi m’mitima yathu.
Khalani Achifundo
4. Kodi chifundo nchiyani?
4 Ngati mukufuna kukhala ndi chikondi chachikulu pa abale anu ndi alongo achikristu, choyamba mufunika kuwamvera chifundo pa mayesero ndi zovuta zawo m’moyo. Mtumwi Petro ananena zimenezo pamene analemba kuti: “Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa.” (1 Petro 3:8) Liwu lachigiriki logwiritsiridwa ntchito panopa kunena kukhala ‘wachifundo’ limatanthauza “kuvutikira limodzi.” Katswiri wina pa Chigiriki cha m’Baibulo anati za liwulo: “Limanena za mzimu wa maganizo umene timakhala nawo pamene tiona kuvutika kwa ena ngati kwathu.” Ndiye chifukwa chake, chifundo nchofunika. Mtumiki wina wa Yehova wachikulire ndiponso wokhulupirika nthaŵi ina anati: “Chifundo ndiwo ululu wanu womwe ndimamva mumtima wanga.”
5. Kodi tidziŵa bwanji kuti Yehova ali ndi chifundo?
5 Kodi Yehova ali ndi chifundo chotero? Ntheradi. Mwachitsanzo, timaŵerenga za kuvutika kwa anthu ake Aisrayeli kuti: “M’mazunzo awo onse Iye anazunzidwa.” (Yesaya 63:9) Yehova sanangoona mavuto awo chabe; anawachitira chifundo anthuwo. Mawu ake Yehova, olembedwa pa Zekariya 2:8, NW, amasonyeza mmene iye amalasidwiradi mtima kwambiri: “Iye wokhudza inu akhudza mwana wa m’diso langa.”a Wokambapo pa vesi limeneli akuti: “Diso ndi chiŵalo chocholoŵana kwambiri ndi chosalimba m’thupi la munthu; ndipo mwana wa m’diso—khomo lomwe kuunika kwa kumwamba kumaloŵerapo kuti munthu aone—ndiyo mbali ya chiŵalocho yomwe imapweteka kwambiri, ndiponso yofunika kwambiri. Palibe chimene chingasonyeze bwino lomwe lingaliro la chisamaliro chachikulu kwambiri chimene Yehova amapereka kwa iwo omwe awakonda kusiyapo zimenezo.”
6. Kodi Yesu Kristu wasonyeza motani chifundo?
6 Nayenso Yesu wasonyeza chifundo chachikulu nthaŵi zonse. Kaŵirikaŵiri “anagwidwa chifundo” chifukwa cha nsautso ya anthu anzake omwe anali kudwala kapena kuvutika. (Marko 1:41; 6:34) Iye anasonyeza kuti pamene wina alephera kukomera mtima otsatira ake odzozedwa, Yesu amamva ngati kuti ndiye amene akuchitidwa zimenezo. (Mateyu 25:41-46) Ndipo lero monga “mkulu [wathu] wa ansembe” wakumwamba, ‘amamva chifundo ndi zofooka zathu.’—Ahebri 4:15.
7. Kodi chifundo chingatithandize bwanji pamene mbale kapena mlongo watiputa?
7 “Kumva chifundo ndi zofooka zathu”—kodi si lingaliro lotonthoza limenelo? Inde, ndiye nafenso tiyenera kuchita chimodzimodzi kwa wina ndi mnzake. Zoona, nkwapafupi kwambiri kuyang’ana pa zofooka za wina. (Mateyu 7:3-5) Koma pamene mbale kapena mlongo adzakuputani mtsogolo, bwanji osayesa izi? Tayerekezerani kuti ndinu amene mwachita zimene iye wachitazo, munali ndi makulidwe ake, umunthu wake, zolakwa zake zoti mulimbane nazo. Kodi mukutsimikiza kuti simukanaphonya chimodzimodzi—kapena mwina ngakhale kuposerapo? M’malo mofuna zopambanitsa kwa ena, tiyenera kusonyeza chifundo, chimene chidzatithandiza kukhala ololera ngati Yehova, amene “akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:14; Yakobo 3:17) Amadziŵa kulephera kwathu. Samafuna zambiri kuposa zomwe tikhoza kuchita. (Yerekezerani ndi 1 Mafumu 19:5-7.) Tonsefe tisonyezetu chifundo chotero kwa ena.
8. Kodi tiyenera kutani pamene mbale kapena mlongo akuvutika?
8 Paulo analemba kuti mpingo uli ngati thupi lokhala ndi ziŵalo zosiyanasiyana zimene ziyenera kugwirira ntchito limodzi mogwirizana. Anawonjeza kuti: “Chingakhale chiŵalo chimodzi chimva choŵaŵa, ziŵalo zonse zimva pamodzi.” (1 Akorinto 12:12-26) Tiyenera kuvutikira limodzi, kapena kuti kuchitira chifundo aja amene akuvutika. Akulu ndiwo amatsogolera kuchita zimenezo. Paulo analembanso kuti: “Afooka ndani wosafooka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?” (2 Akorinto 11:29) Akulu ndi oyang’anira oyendayenda amatsanzira Paulo pankhaniyi. M’nkhani zawo, pantchito yawo yaubusa, ngakhale posamalira milandu, amayesayesa kusonyeza chifundo. Paulo analimbikitsa kuti: “Lirani nawo akulira.” (Aroma 12:15) Pamene nkhosa ziona kuti abusa amazichitiradi chifundo, kuzindikira kulephera kwawo, ndi kumvetsa mavuto omwe zikumana nawo, nthaŵi zambiri zimakonda kulandira uphungu, chitsogozo, ndi chilango. Zimakonda kupezeka pamisonkhano, pokhala ndi chidaliro chakuti kumenekoko zidzapeza ‘mpumulo wa miyoyo yawo.’—Mateyu 11:29.
Kuyamikira Ena
9. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amayamikira zabwino zomwe zili mwa ife?
9 Njira yachiŵiri yosonkhezera chikondi cha pa abale ndiyo kuyamikira ena. Kuti tiyamikire ena, tiyenera kusumika maganizo pa mikhalidwe yawo yabwino ndi khama lawo ndiponso kuzizindikira. Tikatero, timatsanzira Yehova mwiniyo. (Aefeso 5:1) Iye amatikhululukira machimo athu ambiri aang’ono masiku onse. Amakhululukira ndi machimo aakulu omwe malinga munthu walapadi. Kenako atatikhululukira machimo athu, samakhala akuwaganizira. (Ezekieli 33:14-16) Wamasalmo anafunsa kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chiriri ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) Zimene Yehova amasumikapo maganizo ndi zinthu zabwino zomwe timachita pomtumikira.—Ahebri 6:10.
10. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kwangozi ngati okwatirana sayamikirana? (b) Ngati wina akusiya kuyamikira mnzake, ayenera kuchitanji?
10 Chitsanzo chimenechi nchofunika kwambiri kuchitsatira m’banja. Pamene makolo asonyeza kuti amayamikirana, amaikira banja lawo chitsanzo. M’nyengo ino ya maukwati osakhalitsa, nkwapafupi kwambiri kusasamala za mnzako ndi kukuza zophophonya zake ndi kuchepsa mikhalidwe yake yabwino. Kalingaliridwe koipa kameneko kamawononga ukwati, kuusandutsa mtolo wosautsa. Ngati mwaona kuti kuyamikira kwanu mnzanu kukuchepa, tadzifunsani kuti, ‘Kodi mnzanga alibedi mikhalidwe yabwino?’ Talingalirani zakumbuyo ndi kuona zifukwa zomwe munakonderana ndi kukwatirirana. Kodi zifukwa zonse zimenezo zomwe munamkondera munthu wapadera ameneyu zathadi? Ayi; choncho limbikirani kuyamikira mikhalidwe yabwino yomwe mnzanu ali nayo, ndipo muuzeni kuti mumamuyamikira.—Miyambo 31:28.
11. Kuti chikondi muukwati chikhale chosanyenga, kodi ndi zinthu zotani ziyenera kupeŵedwa?
11 Kuyamikirana kumathandizanso mwamuna ndi mkazi wake kukhala ndi chikondi chosanyenga. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 6:6; 1 Petro 1:22.) Chikondi chotero, chosonkhezeredwa ndi kuyamikirana kochokera mumtima, sichidzalola nkhanza mseri, sichidzalola mawu opweteka ndi onyazitsa, sichidzalola kunyalanyazana dala masiku akumangopita popanda kulankhulana mokoma mtima kapena mwaulemu, ndipotu sichidzalola ndewu. (Aefeso 5:28, 29) Mwamuna ndi mkazi amene amayamikiranadi amalemekezana. Amatero osati chabe pamene ali ndi anthu ena koma nthaŵi iliyonse imene Yehova akuwaona—m’mawu ena, nthaŵi zonse.—Miyambo 5:21.
12. Kodi nchifukwa ninji makolo ayenera kuyamikira zabwino zomwe ana awo amachita?
12 Ananso amafuna kuwayamikira. Sikuti makolo ayenera kuwatama iwo pachabe, koma ayenera kuwathokoza ana pamikhalidwe yawo ndi zinthu zabwino zimene iwo amachitadi. Kumbukirani chitsanzo cha Yehova pamene ananena kuti anakondwera naye Yesu. (Marko 1:11) Kumbukiraninso chitsanzo cha Yesu monga “mbuye” m’fanizo lina. Anathokoza ‘akapolo aŵiri abwino ndi okhulupirika’ mofanana, ngakhale kuti aliyense anapatsidwa zosiyana ndiponso zimene aliyense anapindula zinasiyananso. (Mateyu 25:20-23; yerekezerani ndi Mateyu 13:23.) Momwemonso, makolo anzeru amapeza njira yoyamikira mikhalidwe yapadera ya mwana aliyense, maluso ake, ndi zimene amakhoza. Komanso, amapeŵa kugogomezera kwambiri zimene iwo akhoza moti ana awowo nkuona kuti akuwasonkhezera kupambana ena. Safuna kuti ana awo akakule okwiya kapena okhumudwa.—Aefeso 6:4; Akolose 3:21.
13. Kodi amatsogolera ndani kuyamikira munthu aliyense mumpingo?
13 Mumpingo wachikristu, akulu ndi oyang’anira oyendayenda amatsogolera kuyamikira aliyense wa nkhosa za Mulungu. Malo awo ngovuta, pakuti alinso ndi udindo waukulu wolanga mwachilungamo, kubweza olakwa mumzimu wa chifatso, ndi kupereka uphungu wamphamvu kwa amene aufunikira. Kodi amawasamala motani maudindo osiyana ameneŵa?—Agalatiya 6:1; 2 Timoteo 3:16.
14, 15. (a) Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti anasamala popereka uphungu wamphamvu? (b) Kodi oyang’anira achikristu angasamale motani pamene pakufunika kuwongolera zolakwa ndi kuthokoza? Perekani chitsanzo.
14 Chitsanzo cha Paulo chimathandiza kwambiri. Anali mphunzitsi, mkulu, ndi mbusa waluso. Anali kusamalira mipingo imene inali ndi mavuto aakulu, ndipo iye sanalole mantha kumlepheretsa kupereka uphungu wamphamvu pamene unali kufunika. (2 Akorinto 7:8-11) Titapenda utumiki wa Paulo, tipeza kuti anali kudzudzula ena kamodzikamodzi—kokha pamene mkhalidwe unafuna zimenezo kapena pamene zinali zoyenera. Mwanjira imeneyi anasonyeza nzeru yaumulungu.
15 Ngati tingati utumiki wa mkulu mumpingo uli ngati nyimbo, ndiye kuti kutsutsa ndi kudzudzula kuli ngati noti imodzi imene ikugwirizana ndi nyimbo yonse. Noti imeneyo njoyenera pamalo ake. (Luka 17:3; 2 Timoteo 4:2) Talingalirani kuti nyimbo yonseyo ili ndi noti imodzi yokhayo, ndipo ikubwerezedwabwerezedwa. Maimbidwe ake posakhalitsa angamasokosere m’kutu. Momwemonso, akulu achikristu amayesa kukonza bwino chiphunzitso chawo ndi kuchikometsera mosiyanasiyana. Chiphunzitso chawo sichimangokhala chowongolera mavuto. M’malo mwake, kamvekedwe kake konse nkolimbikitsa. Monga Yesu Kristu, akulu achikondi choyamba amapeza chabwino chimene munthu angamthokozerepo, osati zifukwa kapena kusuliza. Amayamikira ntchito yaikulu imene Akristu anzawo akuchita. Ali ndi chidaliro chakuti kaŵirikaŵiri, aliyense amakhala akuchita zomwe angathe kuti atumikire Yehova. Ndipo akulu sazengereza kutchula zimene akuganiza.—Yerekezerani ndi 2 Atesalonika 3:4.
16. Kodi mzimu wa Paulo woyamikira ndi wachifundo unawakhudza motani Akristu anzake?
16 Mosakayikira, Akristu ochuluka omwe Paulo anatumikira anaona kuti anawayamikira ndipo anawachitira chifundo. Kodi tidziŵa bwanji zimenezi? Taonani mmene iwo anaonera Paulo. Sanamuope, ngakhale kuti anali ndi ukumu waukulu. Inde, anali wokondedwa ndi wofikirika. Ndiye chifukwa chake pamene anali kuchoka kudera lina, akulu ‘anamkupatira pakhosi pake, nampsompsona’! (Machitidwe 20:17, 37) Akulu—ndi ife tomwe—tiyenera kuyamikira chotani kuti tili ndi chitsanzo cha Paulo choti titsanzire! Inde, tiyamikirane wina ndi mnzake.
Ntchito Zokoma Mtima
17. Kodi ndi zabwino zotani zomwe zimatsatira ntchito zokoma mtima pampingo?
17 Imodzi ya nkhuni zoyaka kwambiri za chikondi cha pa abale ndiyo kuchita kanthu kena mokoma mtima. Monga ananenera Yesu, “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Kaya tampatsa munthu zauzimu, zakuthupi, kapena nthaŵi yathu ndi nyonga, sitimangokondweretsa chabe ena koma timadzikondweretsa ifenso. Mumpingo, kukoma mtima kumayambukira. Kuchita kanthu kena kokoma mtima kumasonkhezeranso ena kuchita mofanana. Posakhalitsa, chikondi cha pa abale chimasefukira!—Luka 6:38.
18. Kodi “kukoma mtima” kotchulidwa pa Mika 6:8, NW, kumatanthauzanji?
18 Yehova analimbikitsa anthu ake Aisrayeli kukhala okoma mtima. Pa Mika 6:8, timaŵerenga kuti: “Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo [“kukoma mtima,” NW] ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” Kodi “kukonda kukoma mtima” kumatanthauzanji? Liwu lachihebri logwiritsiridwa ntchito panopa kutanthauza “kukoma mtima” (cheʹsedh) latembenuzidwanso kuti “chifundo” m’Chingelezi ndi m’Chicheŵa momwe. Malinga ndi The Soncino Books of the Bible, liwu limeneli “limatanthauza chinthu chimene chimachita ntchito kwambiri kuposa liwu lachingelezi la chifundo longonena za mkhalidwe. Limatanthauza ‘chifundo chosonyezedwa ndi ntchito,’ kuchita zokoma mtima munthuwe, osati kwa osauka ndi osoŵa okha, koma kwa anthu anzako onse.” Ndiye chifukwa chake katswiri wina wa maphunziro anatero kuti cheʹsedh imatanthauza “chikondi chosonyezedwa ndi ntchito.”
19. (a) Kodi ndi motani momwe ife tingayambire kukomera mtima ena mumpingo? (b) Tchulani chitsanzo kuonetsa momwe ena anakusonyezerani chikondi cha pa abale.
19 Chikondi chathu cha pa abale si nthanthi. Ndi chenicheni. Chotero, funafunani njira zochitira zokoma kwa abale ndi alongo anu. Khalani monga Yesu, amene nthaŵi zonse sanali kungoyembekezera anthu kudza kwa iye kumpempha thandizo koma nthaŵi zambiri anayamba ndiye. (Luka 7:12-16) Makamaka talingalirani aja omwe ali osoŵa kwambiri. Kodi munthu wokalamba kapena wofooka akufuna kumchezera kapena mwina akufuna woti atume? Kodi “mwana wamasiye” akufuna nthaŵi yocheza naye ndiponso chisamaliro? Kodi munthu wopsinjika maganizo akufuna munthu womumvetsera kapena mawu otonthoza? Ngati tikhoza, tipezetu nthaŵi yochitira zinthu zokoma mtima ngati zimenezo. (Yobu 29:12; 1 Atesalonika 5:14; Yakobo 1:27) Musaiŵale kuti mumpingo wodzala anthu opanda ungwiro, mbali ina yofunika kwambiri ya kukoma mtima ndiyo chikhululukiro—kulekerera, ngakhale ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira. (Akolose 3:13) Kukhala okonzeka kukhululukirana kumathandizira kuti pampingo pasakhale magaŵano, chidani, ndi kutetana, zomwe zili monga mabulangeti onyowa omwe amazimitsa moto wa chikondi cha pa abale.
20. Kodi ife tonse tiyenera kupitiriza kudzipenda motani?
20 Tonsefe titsimikizetu kuti moto umenewu wofunika kwambiri sukuzima m’mitima yathu. Tipitirizetu kudzipenda ife eni. Kodi ena timawachitira chifundo? Kodi timawayamikira ena? Kodi timachitira ena zinthu zokoma mtima? Malinga ngati tipitiriza kutero, moto wa chikondi udzafunditsa ubale wathu kaya dzikoli likhale lozizira koŵaŵa ndi lankhanza motani. Choncho, mwanjira iliyonse “chikondi [chanu] cha pa abale chikhalebe”—tsopano ndi kunthaŵi zosatha!—Ahebri 13:1.
[Mawu a M’munsi]
a Ma Baibulo ena panopa amapereka lingaliro lakuti wokhudza anthu a Mulungu amakhudza, osati diso la Mulungu, koma la Israyeli kapena ngakhale lake iye mwini. Kuphonya kumeneku kunakhalako chifukwa alembi a m’nyengo zapakati amene, poyesa mosokera kukonza mavesi amene iwo anaganiza kuti sanali kupereka ulemu, anasintha vesili. Motero iwo anabisa mphamvu ya chifundo chake cha Yehova.
Kodi Mukuganizapo Bwanji?
◻ Kodi chikondi cha pa abale nchiyani, ndipo nchifukwa ninji tiyenera kuchilola kuti chikhalebe?
◻ Kodi kukhala kwathu ndi chifundo kumatithandiza motani kusunga chikondi chathu cha pa abale?
◻ Kodi kuyamikira kumathandizira motani chikondi cha pa abale?
◻ Kodi kuchita zokoma mtima kumawonjezera motani chikondi cha pa abale mumpingo wachikristu?
[Bokosi patsamba 16]
Chikondi Chigwira Ntchito
Zaka zingapo zapitazo, mwamuna wina yemwe anali kuphunzira Baibulo kwa nthaŵi ndi Mboni za Yehova anali kukayikirabe za chikondi cha pa abale. Anali kudziŵa kuti Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Koma zinamvuta kukhulupirira zimenezo. Tsiku lina, anaona chikondi chachikristu chikugwira ntchito.
Ngakhale kuti anali pa mpando wamawilo wa opunduka, mwamuna ameneyu anali paulendo kutali ndi kwawo. Ku Bethlehem, Israel, anapezeka pamsonkhano wa mpingo. Kumeneko, Mboni ina yachiluya inaumirira kuti Mboni ina imene inali mlendo igone kunyumba kwake, ndipo ngakhale wophunzira Baibulo ameneyu anamphatikizapo. Asanapite kukagona, wophunzirayo anapempha mwini nyumba ngati angamlole kutulukira kubwalo mmaŵa kuti akapenye dzuŵa potuluka. Mwini nyumbayo anamchenjeza zamphamvu kusachita zimenezo. Kutacha, mbale wachiluyayo anafotokoza chifukwa chake. Akumalankhula mwa womasulira, anatero kuti ngati anansi ake akanadziŵa kuti alendo akewo anali Ayuda—monganso wophunzira Baibulo ameneyo—akanatentha nyumba yake yonse, limodzi ndi iye ndi banja lake. Atazizwa, wophunzira Baibuloyo anamfunsa nati, “Nanga, munachitiranji zangozi chotere?” Popanda womasulira, Mbale wachiluyayo anamyang’ana m’maso nangoti, “Yohane 13:35.”
Wophunzira Baibuloyo anachitadi chidwi kuona chikondi cha pa abale. Posakhalitsa anabatizidwa.
[Chithunzi patsamba 18]
Mkhalidwe wa mtumwi Paulo wa ubwenzi ndi kuyamikira unamkhalitsa wofikirika