Kutsiriza Chiyero M’kuwopa Mulungu
“Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu.”—2 AKORINTO 7:1.
1. Ndimotani mmene timadziŵira kuti angelo okhala ndi malo apamwamba amazindikira chiyero cha Yehova?
YEHOVA ali Mulungu woyera. Angelo a malo apamwamba kumwamba amalengeza chiyero chake m’mawu osakaikirika. “Woyera, woyera, woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.” Koteroko kunali kuitana kodzutsa nthumanzi kwa aserafi owonedwa m’masomphenya ndi mneneri Yesaya m’zana lachisanu ndi chitatu B.C.E. Pamapeto pa zana loyamba C.E., mtumwi Yohane anawona masomphenya a chomwe chinayenera kudzawoneka “m’tsiku la Ambuye,” mmene ife tiri tsopano. Iye anawona zamoyo zinayi mozungulira mpando wachifumu wa Yehova ndipo anamva izo zikulengeza mosalekeza kuti: “Woyera, woyera, woyera, [Yehova, NW] Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.” Zilengezo za mbali zitatu zimenezi zochitidwa ndi zolengedwa zauzimu zakumwamba za Yehova zimagogomezera chiyero chopambana cha Mlengi.—Yesaya 6:2, 3; Chibvumbulutso 1:10; 4:6-8.
Chiyero ndi Kudzipatula
2. (a) Ndi mbali ziŵiri ziti zimene ziripo ku chiyero, ndipo ndimotani mmene Yehova aliri woyera m’mbali zonse ziŵiri zimenezi? (b) Ndimotani mmene Mose anagogomezera chiyero cha Yehova?
2 Chiyero chimatanthauza osati kokha udongo wa chipembedzo ndi kuyera komanso kudzipatula, kapena kudziyeretsa. Yehova ali waudongo koposa, kapena woyera; iye ali woikidwa pambali kotheratu kuchokera ku milungu yonse yauve ya mitundu. Mbali imeneyi ya chiyero chake, kapena kudziyeretsa, inasonyezedwa ndi Mose pamene anaimba mofuula kuti: “Afanana ndi inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi inu ndani, wolemekezedwa, [m’chiyero, NW]?”—Eksodo 15:11.
3. Ndi m’njira zotani mmene Aisrayeli onse anafunidwira kukhala oyera, ndipo ndimotani mmene Yehova anawathandizira iwo m’chigwirizano ndi ichi?
3 Mulungu woyera Yehova anafuna kuti Aisrayeli akale, anthu ake pa dziko lapansi, akayeneranso kukhala oyera. Ichi chinafunidwa osati kokha kwa ansembe ndi Alevi komanso kwa mtundu wonse. Yehova anati kwa Mose: “Nena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, nuti nawo, Muzikhala oyera; pakuti ine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.” (Levitiko 19:2) Kufika ku mapeto amenewo, Yehova anawapatsa iwo malamulo owathandiza iwo kukhalabe audongo mwauzimu, mwamakhalidwe, mwamaganizo, mwakuthupi, ndi mwamwambo, lomaliziralo likumakhala logwirizana ndi kulambira kwawo pa chihema ndipo, pambuyo pake, pa kachisi.
Anthu Oikidwa Pambali
4, 5. (a) Ndimotani mmene Israyeli wakuthupi analiri mtundu woyeretsedwa? (b) Nchiyani chimene chikufunidwa kwa Israyeli wauzimu, ndipo ndimotani mmene mtumwi Petro akutsimikizira ichi?
4 Ku ukulu umene Aisrayeli anatsatira malamulo a Mulungu, iwo anakhala osiyana ku mitundu yoipitsidwa yowazinga. Iwo analekanitsidwa monga anthu oikidwa pambali, kapena oyeretsedwa, kaamba ka utumiki wa Mulungu woyera Yehova. Mose anawawuza iwo kuti: “Inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko.”—Deuteronomo 7:6.
5 Udongo woterowo ndi kupatulika zikufunidwanso kwa Israyeli wauzimu. Mtumwi Petro analemba kwa awo osankhidwa kukhala Aisrayeli auzimu kuti: “Monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziŵa inu; komatu monga Iye wakuitana inu ali Woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti ine ndine woyera mtima.”—1 Petro 1:1, 14-16.
6, 7. (a) Ndimotani mmene ziŵalo za “khamu lalikulu” zikulongosoledwera mu Chibvumbulutso mutu 7, ndipo nchiyani chimene m’chenicheni chikufunika kwa iwo? (b) Kodi nchiyani chimene chidzalingaliridwa mu ndime zotsatira?
6 Mu Chibvumbulutso mutu 7, ziŵalo za “khamu lalikulu” zikulongosoledwa monga “akuimirira ku mpando wachifumu [wa Yehova] ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera,” pokhala “atatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” (Chibvumbulutso 7:9, 14) Zovala zawo zoyera zimaphiphiritsira kaimidwe kawo kaudongo, kolungama pamaso pa Yehova, kamene amawapatsa chifukwa cha chikhulupiriro chawo mu mwazi wowombola wa Kristu. Chotero, mwachiwonekere, osati Akristu odzozedwa okha koma “nkhosa zina” nazonso ziyenera kukhala zaudongo mwauzimu ndi mwa makhalidwe kotero kuti alambire Yehova molandirika.—Yohane 10:16.
7 Tiyeni tsopano tilingalire mmene anthu a Yehova m’nthaŵi zakale anafunidwira kudzitsimikizira iwo eni audongo ndi oyera ndi chifukwa chimene maprinsipulo ofananawo amagwira ntchito kwa anthu a Mulungu lerolino.
Udongo Wauzimu
8. Ndi kaamba ka zifukwa zotani zimene Aisrayeli anafunikira kudzisunga iwo eni opatuka kuchoka ku zipembedzo za ku Kanani?
8 Aisrayeli akuthupi anayenera kudzisunga iwo eni opatuka kotheratu kuchoka ku machitachita opanda udongo a chipembedzo a mitundu ina. Akumalankhula kupyolera mwa Mose, Yehova anawuza Israyeli kuti: “Dzipenyerere wekha kuti sukupanga pangano ndi nzika za dziko ku limene ukupita, kuwopera kuti chingatsimikizire kukhala msampha pakati pako. Koma maguwa awo ansembe anthu inu muyenera kuwagwetsa, ndipo mizati yawo yopatulika [yogwiritsidwa ntchito m’chigwirizano ndi kulambira konyansa kwa kugonana] muyenera kuiphwanya, ndipo mitengo yawo yopatulika muyenera kuigwetsa. Popeza kuti simuyenera kugwadira kwa mulungu wina, chifukwa Yehova, amene dzina lake liri Nsanje, ali Mulungu wansanje [kapena, “Mulungu wofuna kudzipereka kotheratu,” New World Translation Reference Bible, mawu a m’munsi]; kuwopera kuti mungapange pangano ndi nzika za dzikolo, popeza kuti motsimikizirika adzachita chigololo ndi milungu yawo ndi kupereka nsembe kwa milungu yawo.”—Eksodo 34:12-15, NW.
9. Ndi malangizo achindunji otani amene anaperekedwa kwa otsalira okhulupirika omwe anachoka ku Babulo mu 537 B.C.E.?
9 Mazana angapo pambuyo pake, Yehova anawuzira Yesaya kulankhula mawu aulosi awa kwa otsalira okhulupirika omwe akabwerera ku Yuda kuchokera ku Babulo: “Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova [zokagwiritsidwa ntchito kubwezeretsa kulambira koyera pa kachisi mu Yerusalemu].”—Yesaya 52:11.
10, 11. (a) Ndi malangizo ofanana otani amene anaperekedwa kwa Israyeli wauzimu m’zana loyamba C.E.? (b) Ndimotani mmene malangizo amenewa atsatiridwira makamaka chiyambire 1919 ndi 1935, ndipo ndi m’njira ina iti imene odzozedwa ndi atsamwali awo amadzisungira audongo mwauzimu?
10 Mofananamo, Aisrayeli auzimu ndi atsamwali awo ayenera kudzisunga iwo eni osadetsedwa ndi zipembedzo zolambira mafano za dziko lino. Akumalembera kwa Akristu odzozedwa mu mpingo wa Korinto, mtumwi Paulo analongosola kuti: “Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndi iwo adzakhala anthu anga. Chifukwa chake, tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati [Yehova, NW], ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo ine ndidzalandira inu.”—2 Akorinto 6:16, 17.
11 Chiyambire 1919 ziŵalo zoyeretsedwa ndipo zoyengedwa za otsalira odzozedwa zamasulidwa kuchoka ku zipembedzo zopanda udongo, zolambira mafano za Babulo Wamkulu. (Malaki 3:1-3) Iwo alabadira chiitano cha kumwamba chakuti: “Tulukani mwa iye, anthu anga, ngati simufuna kugawana naye machimo ake, ndipo ngati simufuna kulandira mbali ya miliri yake.” (Chibvumbulutso 18:4, NW) Chiyambire 1935 khamu lalikulu lomawonjezereka la “nkhosa zina” mofananamo lalabadira chiitano chimenechi ndipo laleka chipembedzo chopanda udongo Chachibabulo. Odzozedwa ndi atsamwali awo amakhalanso audongo mwauzimu mwa kupeŵa kugwirizana konse ndi malingaliro osakaza a ampatuko.—Yohane 10:16; 2 Yohane 9-11.
Udongo Wamakhalidwe
12. (a) Kodi ndi kupyolera mu malamulo ati mmene Yehova anakweza pamwamba kaimidwe ka mkhalidwe ka Aisrayeli kuposa kaja ka mitundu yowazinga? (b) Ndi malamulo otani amene mwapadera anali osamalitsa kwa ansembe?
12 Kupyolera mwa pangano la Chilamulo, Yehova anakweza kaimidwe ka makhalidwe ka Aisrayeli mokulira kuposa mkhalidwe wotsika wa mitundu yowazinga. Ukwati ndi moyo wa banja zinali zinthu zochinjirizidwa mu Israyeli. Lachisanu ndi chiŵiri la Malamulo Khumi linaletsa chigololo. Ponse paŵiri chigololo ndi dama zinali zodzetsa chilango mowopsya. (Deuteronomo 22:22-24) Anamwali anachinjirizidwa ndi Chilamulo. (Deuteronomo 22:28, 29) Malamulo kaamba ka ukwati anali osamalitsa kwenikweni makamaka kwa ansembe. Ponena za mkulu wansembe, iye anafunidwa kusankha namwali wosadetsedwa monga mkazi.—Levitiko 21:6, 7, 10, 13.
13. Ndi kwa ndani kumene ziŵalo za “mkwatibwi” wa Kristu zikuyerekezedwa, ndipo nchifukwa ninji?
13 Mofananamo, Mkulu Wansembe wamkulu, Yesu Kristu, ali ndi “mkwatibwi” wopangidwa ndi Akristu odzozedwa 144,000, omwe akufanizidwa ndi “anamwali.” (Chibvumbulutso 14:1-5; 21:9) Iwo amadzisunga iwo eni osadetsedwa ndi dziko la Satana ndi kukhala oyera mwa ziphunzitso ndi makhalidwe. Mtumwi Paulo analembera Akristu odzozedwa mu Korinto kuti: “Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Kristu.” (2 Akorinto 11:2) Paulo analembanso kuti: “Monganso Kristu anakonda [mpingo, NW] nadzipereka yekha mmalo mwake; kuti akaupatule, atauyeretsa ndi kuusambitsa ndi madzi ndi mawu; kuti iye akadziikire yekha [mpingo, NW] wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti ukhale woyera, ndi wopanda chirema.”—Aefeso 5:25-27.
14, 15. (a) Nchiyani chimene chiyenera kutsagana ndi kuyera kwauzimu kwa gulu la mkwatibwi, ndipo ndi lemba liti limene limasonyeza chimenechi? (b) Nchifukwa ninji chiri chachidziŵikire kuti zofunika zofananzo za kuyera kwa makhalidwe zimagwiranso ntchito kwa nkhosa zina?
14 Kuyera kwauzimu kumeneku kwa mkwatibwi wa Kristu kuyenera kutsagana ndi udongo wa makhalidwe ku mbali ya ziŵalo zake. Mtumwi Paulo analongosola kuti: “Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo . . . sadzaloŵa ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa.”—1 Akorinto 6:9-11.
15 Kunena kuti zofunikira zoterozo za kuyera kwa makhalidwe zimagwiranso ntchito kwa nkhosa zina kumakhala kowonekera pamene tikulingalira awo amene Yehova sadzawaphatikizapo m’mwamba mwake mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zolonjezedwa. Timaŵerenga kuti: “Koma . . . onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo . . . , cholandira chawo chidzakhala m’nyanja yotentha ndi moto ndi sulfure; ndiyo imfa yachiŵiri.”—Chibvumbulutso 21:1, 8.
Ukwati Wolemekezeka
16, 17. (a) Ndi malemba ati amene amasonyeza kuti kusakwatira sikuli chiyeneretso cha udongo wa makhalidwe? (b) Ndimotani mmene Mkristu angasonyezere kuwopa koyenera kwa Mulungu m’kusankha mnzake wa mu ukwati, ndipo nchifukwa ninji chingakhale chopanda nzeru kunyalanyaza chiletso cha utumwicho?
16 Kuti akhalebe audongo mwamakhalidwe, ziŵalo zodzozedwa za gulu la mkwatibwi ndi nkhosa zina sizikufunsidwa kukhala zosakwatira. Kukhala mbeta kokakamiza sikuli kwa m’malemba. (1 Timoteo 4:1-3) Kuyanjana kwa kugonana mkati mwa chomangira cha banja sikuli kodetsa. Mawu a Mulungu amalongosola kuti: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.”—Ahebri 13:4.
17 Ngakhale kuli tero, Mkristu wokhumba ‘kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu’ sayenera kudzimva womasuka kukwatira mwamuna kapena mkazi aliyense amene akondwera naye. Kokha kanthaŵi kochepa asanapereke uphungu kwa Akristu anzake ‘kudzikonzera okha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu,’ mtumwi Paulo analemba kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? . . . Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira?” (2 Akorinto 6:14, 15; 7:1) Monga chiŵalo cha anthu opatulika ndipo audongo a Yehova, mwamuna kapena mkazi Wachikristu yemwe akhumba kukwatira adzalandira chiletso cha utumwi cha kuchita tero “kokha mwa Ambuye,” uku ndiko kuti, mwa kusankha winawake yemwe ali mtumiki wa Yehova wodzipereka, wobatizidwa, ndipo wokhulupirika. (1 Akorinto 7:39) Mofanana ndi nthaŵi zakale, choteronso lerolino, chikakhala chopanda nzeru motsimikizirika kwa odzipereka pakati pa anthu a Mulungu kunyalanyaza uphungu wa m’Malemba umenewu. (Yerekezani ndi Deuteronomo 7:3, 4; Nehemiya 13:23-27.) Sichikakhala kusonyeza kuwopa koyenera kwa Ambuye Wamkulu, Yehova.—Malaki 1:6.
18. Kodi ndi m’njira ina yotani imene Akristu angasungire ukwati wawo kukhala wolemekezeka?
18 M’kuwonjezerepo, mu Israyeli, malamulo anaika polekezera machitachita a kugonana ngakhale mkati mwa chomangira cha ukwati. Mwamuna anayenera kuleka kukhala ndi kuyanjana kwa kugonana ndi mkazi wake mkati mwa kusamba kwake. (Levitiko 15:24; 18:19; 20:18) Ichi chinafunikira kulingalira kwachikondi ndi kudziletsa ku mbali ya gulu la amuna Achiisrayeli. Kodi Akristu ayenera kukhala olingalira mochepera ponena za akazi awo? Mtumwi Petro akunena kuti amuna Achikristu ayenera kukhala ndi akazi awo “monga mwa chidziŵitso,” uku ndiko kuti, chidziŵitso cha kapangidwe kawo monga “chotengera chochepa mphamvu, [chachikazi, NW].”—1 Petro 3:7.
Kuyenda pa “Njira Yopatulika”
19, 20. (a) Longosolani njira yaikulu yomwe ikutsatiridwa ndi unyinji wokulira wa mtundu wa anthu. (b) Ndimotani mmene anthu a Yehova ayenera kukhalira osiyana ndi dziko la Satana? (c) Kodi ndi njira yotani imene anthu a Mulungu akutsatira, ndi liti pamene inatsegulidwa, ndipo ndani okha amene akuloledwa pa iyo?
19 Zomwe zakambidwazo zikutsimikizira mpata womakulakulabe womwe umalekanitsa anthu a Yehova kuchoka ku dziko la Satana. Dongosolo la kachitidwe ka zinthu lakudziko lomwe liripoli liri lolekerera mowonjezereka ndipo lodzimwerekeretsa. Yesu analongosola kuti: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho.” (Mateyu 7:13) Njira yotakata imeneyo ikutsatiridwa ndi unyinji wokulira wa mtundu wa anthu. Kugwira mawu mtumwi Petro, iyo iri njira ya “kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, mamwaimwa ndi kupembedza mafano,” njira imene imatsogolera ku “kusefukira kwa chitaiko.” (1 Petro 4:3, 4) Mapeto ake ali chiwonongeko.
20 Anthu a Mulungu, ku mbali ina, akuyenda pa msewu wosiyanako, msewu waudongo wotsatiridwa ndi anthu audongo. Kutsegulidwa kwa msewu waudongo umenewu m’nthaŵi yamapeto kunanenedweratu ndi mneneri Yesaya, yemwe analemba kuti: “Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa Njira Yopatulika; audio sadzapita mmenemo.” (Yesaya 35:8) Kuchitira ndemanga pa ulosi umenewu, bukhu la Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere” likulongosola kuti: “Mu 1919 khwalala lophiphiritsira linatsegukira atumiki osangalala a Mulungu. Awo amene anafuna kukhala opatulika m’maso mwa Yehova ndiwo amene anayenda pa ‘khwalala’ limenelo, ‘Njira Yopatulika.’ . . . Lerolino, ngakhale kuli kwakuti taloŵa kwambiri mu ‘mapeto a dongosolo la zinthu,’ ‘khwalala’ loperekedwa ndi Mulungu likali chitsegukirebe. Makamu a anthu oyamikira . . . akuloŵa panjira yomka ku paradaiso wauzimu, ‘Njira Yopatulika.’”a
21. Ndimotani ndipo nchifukwa ninji atumiki a Yehova ayenera kukhala osiyanitsika ndi khamu la Mdyerekezi, ndipo nchiyani chimene chidzalingaliridwa mu nkhani yotsatira?
21 Inde, otsalira odzozedwa a Aisrayeli auzimu ndi atsamwali awo, nkhosa zina, amadzisiyanitsa iwo eni lerolino monga anthu oikidwa pambali kuchoka ku dziko la Satana, kwa amene mbali ya chiyero yataya tanthauzo lonse. Palibe chirichonse chimene chiri chopatulika ku khamu la Mdyerekezi lomwe likuyenda pa “msewu waukulu ndi wotakata . . . wotsogolera ku chiwonongeko.” Iwo sali kokha odetsedwa mwauzimu ndi mwa makhalidwe koma mu nkhani zambiri iwo ali odetsedwa mwakuthupi ndipo kawonekedwe kawo kali kosalongosoka, kunenako zochepera. Komabe, mtumwi Paulo akunena kuti: “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Njira m’zimene anthu a Mulungu ayenera kukhala osamala kukhala audongo m’maganizo ndi thupi zidzalingaliridwa mu nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Chaputala 16, masamba 134-5.
Nsonga kaamba ka Kubwereramo
◻ Ndi mbali ziŵiri ziti zimene ziripo za chiyero, ndipo nchifukwa ninji chinganenedwe kuti Yehova ali woyera kopambana?
◻ Ndi m’njira ziŵiri ziti m’zimene Aisrayeli anayenera kudzitsimikizira iwo eni kukhala mtundu woyera?
◻ Nchiyani chomwe chikufunikira kwa Aisrayeli auzimu ndi atsamwali awo, nkhosa zina?
◻ Ndimotani mmene kuwopa kwathu Mulungu kuyenera kuyambukirira kusankha kwathu mzathu wa mu ukwati?
◻ Kodi ndi misewu iŵiri iti yomwe ingatsatiridwe lerolino, ndipo nchifukwa ninji chosankha chowonekera bwino chiyenera kupangidwa?
[Chithunzi patsamba 13]
Mawu a Mulungu amanena kuti: “Ukwati uchitidwe ulemu”