Levitiko
20 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Munthu aliyense wa Chiisiraeli ndiponso mlendo aliyense wokhala mu Isiraeli amene wapereka mwana wake aliyense kwa Moleki, aziphedwa ndithu.+ Nzika zamʼdziko lanu zizimupha pomuponya miyala. 3 Ine ndidzamukana munthu ameneyo ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake, chifukwa wapereka mwana wake kwa Moleki ndipo wadetsa malo anga oyera+ komanso waipitsa dzina langa loyera. 4 Koma nzikazo zikanyalanyaza mwadala zimene munthuyo wachita popereka mwana wake kwa Moleki ndipo iwo sanamuphe,+ 5 ineyo ndidzadana ndi munthu ameneyo limodzi ndi banja lake.+ Ndidzapha munthu ameneyu limodzi ndi onse ogwirizana naye pochita uhule ndi Moleki, kuti asakhalenso pakati pa anthu awo.
6 Munthu amene wachita zosakhulupirika* podalira anthu olankhulana ndi mizimu+ komanso olosera zamʼtsogolo,+ ndidzadana naye ndithu ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+
7 Choncho mudzipatule ndipo mukhale oyera,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu. 8 Muzisunga malamulo anga ndipo muziwatsatira.+ Ine ndine Yehova amene ndikukupatulani kuti mukhale oyera.+
9 Munthu akatemberera* bambo kapena mayi ake, aziphedwa ndithu.+ Mlandu wa magazi ake ukhale pa iye chifukwa watemberera bambo ake kapena mayi ake.
10 Ili ndi lamulo lokhudza munthu amene wachita chigololo ndi mkazi wa munthu wina: Mwamuna amene wachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake aziphedwa ndithu. Mwamuna ndi mkazi amene achita chigololowo onse aziphedwa.+ 11 Mwamuna amene wagona ndi mkazi wa bambo ake, wachititsa manyazi* bambo akewo.+ Mwamuna ndi mkaziyo aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo. 12 Mwamuna akagona ndi mpongozi wake wamkazi, onse awiri aziphedwa ndithu. Iwo achita zinthu zosemphana ndi chibadwa. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo.+
13 Mwamuna akagona ndi mwamuna mnzake ngati mmene mwamuna amagonera ndi mkazi, onse awiri achita chinthu chonyansa.+ Iwo aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo.
14 Mwamuna akakwatira mkazi nʼkugonanso ndi mayi a mkaziyo, limenelo ndi khalidwe lonyansa.*+ Mwamunayo ndi akazi onsewo* aziphedwa kenako nʼkuwawotcha+ kuti anthu asapitirize kuchita khalidwe lonyansalo.
15 Mwamuna akagona ndi nyama, aziphedwa ndithu ndipo muziphanso nyamayo.+ 16 Mkazi akadzipereka kwa nyama kuti agone nayo,+ muzipha mkaziyo ndi nyamayo. Anthu ochita zimenezi aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo.
17 Mwamuna akagona ndi mchemwali wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake, chimenecho ndi chinthu chochititsa manyazi.+ Choncho onse awiri aziphedwa pamaso pa anthu a mtundu wawo. Iye wachititsa manyazi* mchemwali wake ndipo aziyankha mlandu wa kulakwa kwakeko.
18 Mwamuna akagona ndi mkazi amene akusamba, onse awiri sanalemekeze magazi a mkaziyo.+ Onse awiri aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wawo.
19 Usagone ndi mchemwali wa mayi ako kapena mchemwali wa bambo ako, chifukwa kuchita zimenezo nʼkuchititsa manyazi mʼbale wako.+ Iwo aziyankha mlandu wa kulakwa kwawo. 20 Ndipo mwamuna amene wagona ndi mkazi wa mchimwene wa bambo ake, wachititsa manyazi* mchimwene wa bambo akewo.+ Mwamuna ndi mkaziyo aziyankha mlandu wa tchimo lawolo. Iwo ayenera kufa kuti asabereke ana. 21 Mwamuna akakwatira mkazi wa mchimwene wake, wachita chinthu chonyansa.+ Iye wachititsa manyazi* mchimwene wake. Mwamuna ndi mkaziyo ayenera kufa kuti asabereke ana.
22 Muzisunga+ malamulo anga onse ndi zigamulo zanga zonse,+ kuti dziko limene ndikukulowetsani kuti mukhalemo lisadzakulavuleni.+ 23 Musamatsatire malamulo a mitundu imene ndikuithamangitsa pamaso panu,+ chifukwa iwo amachita zonsezi ndipo amandinyansa.+ 24 Nʼchifukwa chake ndinakuuzani kuti: “Inuyo mudzatenga dzikolo ndipo ine ndidzalipereka mʼmanja mwanu kuti likhale lanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndakupatulani kwa anthu a mitundu ina.”+ 25 Muzisiyanitsa nyama yoyera ndi yodetsedwa, mbalame yodetsedwa ndi yoyera.+ Musadziipitse ndi nyama, mbalame kapena chilichonse chokwawa padziko lapansi chimene ndanena kuti ndi chodetsedwa.+ 26 Mukhale oyera kwa ine, chifukwa ine Yehova ndine woyera.+ Ine ndikukusiyanitsani ndi anthu a mitundu ina kuti mukhale anthu anga.+
27 Mwamuna kapena mkazi aliyense amene amalankhula ndi mizimu kapena kulosera zamʼtsogolo* aziphedwa ndithu.+ Aziphedwa powaponya miyala. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo.’”