NKHANI YOPHUNZIRA 5
NYIMBO NA. 27 Ulemerero wa Ana a Mulungu Udzaonekera
‘Sindidzakutayani Ngakhale Pang’ono’
“Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’”—AHEB. 13:5b.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Cholinga cha Mulungu ndi kutsimikizira atumiki ake padziko lonse kuti iye sadzawasiya ngakhale pang’ono, Akhristu onse odzozedwa akadzapita kumwamba.
1. Kodi ndi pa nthawi iti pamene odzozedwa adzapite kumwamba?
ZAKA zambiri m’mbuyomu, anthu a Yehova ankadzifunsa kuti, ‘Kodi wodzozedwa womaliza adzatengedwa liti kupita kumwamba?’ Poyamba tinkaganiza kuti odzozedwa ena adzakhala m’Paradaiso padzikoli kwa kanthawi pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo. Koma mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2013, tinaphunzira kuti odzozedwa omwe ali padzikoli adzatengedwa kupita kumwamba nkhondo ya Aramagedo isanayambe.—Mat. 24:31.
2. Kodi ena angakhale ndi funso lotani, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Komabe funso lingakhale lakuti: Kodi n’chiyani chomwe chidzachitikire “nkhosa zina” za Khristu, zomwe zidzakhale zikutumikira Yehova mokhulupirika padzikoli pa nthawi ya “chisautso chachikulu?” (Yoh. 10:16; Mat. 24:21) Ena angamade nkhawa kuti angamadzaone ngati asiyidwa kapena ali okhaokha abale ndi alongo awo odzozedwa akadzapita kumwamba. Tiyeni tione nkhani ziwiri za m’Baibulo zomwe zingawachititse kuganiza zimenezi. Kenako tikambirana zifukwa zomwe zingachititse kuti tisamade nkhawa.
KODI N’CHIYANI CHOMWE SICHIDZACHITIKA?
3-4. Kodi ena angamaganize chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
3 Ena angamaganize kuti Akhristu ena adzasiya kutumikira Yehova, pakadzakhala kuti palibe abale odzozedwa a m’Bungwe Lolamulira oti aziwatsogolera. Iwo angamaganize choncho chifukwa cha nkhani zina zomwe zili m’Baibulo. Tiyeni tikambirane ziwiri mwa nkhanizi. Nkhani yoyamba ndi yokhudza Mkulu wa Ansembe Yehoyada. Iye anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu. Yehoyada ndi mkazi wake Yehosabati anateteza Yehoasi ali wamng’ono ndipo anamuthandiza kukhala mfumu yabwino ndi yokhulupirika. Pa nthawi yonse yomwe Yehoyada anali ndi moyo, Yehoasi ankachita zabwino. Koma atangomwalira, Yehoasi anayamba kuchita zoipa. Iye anamvera malangizo a akalonga oipa ndipo anasiya kutumikira Yehova.—2 Mbiri 24:2, 15-19.
4 Chitsanzo chachiwiri ndi cha Akhristu omwe anakhala ndi moyo pa nthawi yomwe atumwi anali atafa. Yohane, yemwe anali mtumwi womaliza, anali chitsanzo chabwino kwa Akhristu ambiri ndipo ankawathandiza kuti azitumikira Yehova mokhulupirika. (3 Yoh. 4) Mofanana ndi atumwi ena okhulupirika, kwa nthawi yaitali, Yohane anayesetsa kuteteza mpingo ku mpatuko womwe unkafala. (1 Yoh. 2:18; 2 Ates. 2:7) Komabe Yohane atamwalira, mpatukowo unafalikira kwambiri. Patangopita zaka zochepa, anthu ampatuko ankaphunzitsa zinthu zambiri zabodza komanso ankalola anthu amakhalidwe oipa mumpingo.
5. Kodi sitiyenera kuganiza chiyani tikamawerenga nkhani ziwirizi?
5 Kodi nkhani ziwiri za m’Baibulozi zikusonyeza kuti zofananazi zidzachitikiranso nkhosa zina za Khristu, odzozedwa akadzapita kumwamba? Pa nthawiyo, kodi Akhristu adzayamba kuchita zoipa ngati Yehoasi kapenanso kuyamba mpatuko ngati Akhristu omwe anakhalapo pa nthawi yomwe atumwi anali atafa? Yankho ndi loti Ayi. Tingakhale otsimikiza kuti odzozedwa akadzachoka padzikoli, a nkhosa zina adzapitiriza kutumikira Yehova m’njira yoyenera ndipo iye adzapitiriza kuwasamalira. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira zimenezi?
KULAMBIRA KOONA SIKUDZASOKONEZEDWA
6. Kodi tikambirana zokhudza nthawi zitatu ziti?
6 N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti kulambira koona sikudzasokonezedwa, ngakhale pa nthawi yovuta yomwe ikubwera kutsogoloku? Tikutero chifukwa Baibulo limafotokoza kuti nthawi yomwe tikukhalamoyi ndi yosiyana kwambiri ndi nthawi ya Aisiraeli komanso nthawi ya Akhristu omwe anakhala ndi moyo atumwi atafa. Tsopano tiyeni tikambirane zokhudza nthawi zitatuzi: (1) Nthawi ya Aisiraeli, (2) nthawi yomwe atumwi onse anali atafa, komanso (3) nthawi yathu ino, yomwe ndi “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse.”—Mac. 3:21.
7. M’nthawi ya Aisiraeli, n’chifukwa chiyani anthu okhulupirika sanataye mtima pamene mafumu ndi anthu ena ambiri anasankha kuchita zoipa?
7 Nthawi ya Aisiraeli. Atatsala pang’ono kumwalira, Mose anauza Aisiraeli kuti: “Ndikudziwa bwino kuti pambuyo pa imfa yanga, mosakayikira mudzachita zinthu zoipa n’kupatuka kusiya njira imene ndakulamulani.” (Deut. 31:29) Iye anawachenjezanso kuti akadzasiya kutumikira Mulungu, adzatengedwa kupita ku ukapolo. (Deut. 28:35, 36) Kodi zimenezi zinachitikadi? Inde. Kwa nthawi yaitali, mafumu ambiri ankachita zoipa ndipo ankachititsanso kuti anthu a Mulungu asiye kumutumikira. Zimenezi zinachititsa kuti Yehova alange anthu oipawo ndipo sanalole kuti mafumu a Chiisiraeli apitirize kulamulira anthu ake. (Ezek. 21:25-27) Koma Aisiraeli okhulupirika sanataye mtima, anapitirizabe kutumikira Mulungu ataona kuti zimene ananena zinakwaniritsidwa.—Yes. 55:10, 11.
8. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kuti atumwi onse atafa, mpatuko unalowa mumpingo? Fotokozani.
8 Nthawi yomwe atumwi anali atafa. Sitiyenera kudabwa poona kuti atumwi onse atafa, mumpingo wa Chikhristu munayamba mpatuko. Tikutero chifukwa Yesu anali ataneneratu kuti mpatuko waukulu udzayamba mumpingo. (Mat. 7:21-23; 13:24-30, 36-43) Nawonso atumwi monga Paulo, Petulo ndi Yohane anatsimikizira kuti ulosi wa Yesu unali utayamba kukwaniritsidwa munthawi yawo. (2 Ates. 2:3, 7; 2 Pet. 2:1; 1 Yoh. 2:18) Atumwiwo atafa, mpingo wa Chikhristu unasokonekera. Mpatuko unayamba ndipo unakhala mbali yaikulu ya Babulo Wamkulu, yemwe amaimira zipembedzo zonse zonyenga. Apanso zimene Yesu ananeratu, zinali zikukwaniritsidwa.
9. Kodi nthawi yomwe tikukhalayi ikusiyana bwanji ndi nthawi ya Aisiraeli komanso nthawi yomwe atumwi anali atafa?
9 “Nthawi yobwezeretsa zinthu zonse.” Nthawi yathu ino ndi yosiyana kwambiri ndi nthawi ya Aisiraeli komanso nthawi yomwe mpatuko unayamba atumwi onse atafa. Ndiye kodi nthawi yathuyi imatchedwa chiyani? Timangoitchula kuti “masiku otsiriza” a dziko loipali. (2 Tim. 3:1) Koma Baibulo limasonyezanso kuti chimenechi ndi chiyambi cha nthawi ina yapadera komanso yaitali. Nthawiyi idzapitirira mpaka pamene Ufumu wa Mesiya udzathandize anthu kukhalanso angwiro komanso kukonza dzikoli kukhala Paradaiso. Imeneyi imatchedwa “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse.” (Mac. 3:21) Nthawiyi inayamba mu 1914. Ndiye kodi n’chiyani chinabwezeretsedwa pa nthawiyi? Yesu anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba. Choncho Yehova anakhalanso ndi wolamulira womuimira, yemwe anali wolowa m’malo mwa Davide amene anali mfumu yokhulupirika. Koma sikuti Yehova anangobwezeretsa Ufumu wokhawu. Patangopita kanthawi, kulambira koona kunayambanso kubwezeretsedwa. (Yes. 2:2-4; Ezek. 11:17-20) Kodi kulambiraku kudzasokonezedwanso?
10. (a) Kodi Baibulo linaneneratu chiyani zokhudza kulambira koona munthawi yathu ino? (Yesaya 54:17) (b) N’chifukwa chiyani maulosi amenewa ali olimbikitsa?
10 Werengani Yesaya 54:17. Taganizirani zimene ulosiwu ukunena: “Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.” Ulosiwu ukukwaniritsidwa masiku ano. Mawu olimbikitsa otsatirawa, amafotokozanso za nthawi yathu ino: “Ana ako onse azidzaphunzitsidwa ndi Yehova, ndipo mtendere wa ana ako udzakhala wochuluka. Udzakhazikika molimba m’chilungamo. . . . Sudzaopa kanthu ndipo palibe chimene chidzakuchititse mantha, chifukwa palibe chilichonse choopsa chimene chidzakuyandikire.” (Yes. 54:13, 14) Ngakhale Satana, yemwe ndi “mulungu wa nthawi ino,” alibe mphamvu zoti n’kulepheretsa ntchito yophunzitsa ena, yomwe anthu a Yehova akugwira. (2 Akor. 4:4) Kulambira koona kunabwezeretsedwa ndipo sikudzasokonezedwanso, kudzakhalapo mpaka kalekale. Palibe chida chilichonse chomwe chidzapangidwe chimene chidzapambane.
KODI CHIDZACHITIKE N’CHIYANI?
11. N’chiyani chikutitsimikizira kuti a khamu lalikulu sadzakhala okha, odzozedwa akadzapita kumwamba?
11 Kodi chidzachitike n’chiyani odzozedwa akadzapita kumwamba? Tizikumbukira kuti Yesu ndi M’busa wathu. Iye ndi mutu wa mpingo wa Chikhristu. Yesu ananena momveka bwino kuti: “Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.” (Mat. 23:10) Yesu yemwe ndi Mfumu yomwe ikulamulira kumwamba, sadzasiya kusamalira otsatira ake padzikoli. Ndipo iwo sadzaopa chilichonse popeza azidzatsogoleredwa ndi Khristu. N’zoona kuti sitikudziwa zonse zokhudza mmene Khristu adzatsogolere anthu ake pa nthawiyo. Choncho, tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo za m’Baibulo zomwe zingatilimbikitse.
12. Kodi Yehova anasamalira bwanji anthu ake (a) Mose atamwalira? (b) Eliya atapatsidwa utumiki wina? (Onaninso chithunzi.)
12 Mose anamwalira Aisiraeli asanalowe m’Dziko Lolonjezedwa. Ndiye kodi n’chiyani chinachitikira anthu a Mulungu? Kodi Yehova anasiya kuthandiza anthu ake munthu wokhulupirikayu atamwalira? Ayi. Yehova ankawasamalira akapitiriza kukhala okhulupirika. Mose asanamwalire, Yehova anamuuza kuti asankhe Yoswa kuti adzatsogolere anthu ake. Mose anakhala akuphunzitsa Yoswa kwa zaka zambiri. (Eks. 33:11; Deut. 34:9) Kuwonjezera pamenepo, panali amuna ambiri omwe anali atsogoleri a anthu 1000, 100, 50 komanso ngakhale 10. (Deut. 1:15) Anthu a Mulungu anapitiriza kusamalidwa bwino. Ndi zomwenso zinachitika m’nthawi ya Eliya. Kwa zaka zambiri iye ankatsogolera kulambira koona ku Isiraeli. Koma nthawi ina Yehova anamusamutsira chakummwera ku Yuda kuti akachite utumiki wake kumeneko. (2 Maf. 2:1; 2 Mbiri 21:12) Kodi anthu okhulupirika a mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 anali atasiyidwa? Ayi. Eliya anali ataphunzitsa Elisa kwa zaka zambiri. Panalinso “ana a aneneri,” omwe ayenera kuti anali ataphunzitsidwa bwino. (2 Maf. 2:7) Choncho panali amuna ambiri okhulupirika omwe ankatsogolera anthu a Mulungu. Yehova anapitiriza kukwaniritsa cholinga chake ndipo ankasamalira atumiki ake okhulupirika.
13. Kodi pa Aheberi 13:5b, Yehova akutilonjeza chiyani? (Onaninso chithunzi.)
13 Tikaganizira zitsanzo zimene takambiranazi, kodi mukuganiza kuti n’chiyani chidzachitike wodzozedwa womaliza akadzatengedwa kupita kumwamba? Sitiyenera kuda nkhawa. Baibulo limafotokoza mfundo yomveka bwino ya choonadi, kuti: Yehova sadzataya anthu ake ngakhale pang’ono. (Werengani Aheberi 13:5b.) Mofanana ndi Mose komanso Eliya, Akhristu odzozedwa omwe akutsogolera masiku ano, omwe ndi ochepa, amadziwa kufunika kophunzitsa ena. Kwa zaka zambiri, abale a m’Bungwe Lolamulira akhala akuphunzitsa amuna a nkhosa zina kuti azitsogolera. Mwachitsanzo, iwo akonza masukulu ambiri ophunzitsa akulu, oyang’anira madera, abale a m’Makomiti a Nthambi, oyang’anira madipatimenti pa Beteli ndi ena. Akhalanso akuphunzitsa abale amene amathandiza makomiti osiyanasiyana a Bungwe Lolamulira. Panopa abale othandizawa akugwira mokhulupirika ntchito zambiri m’gulu la Yehova. Abalewa ndi okonzekeretsedwa kupitiriza kusamalira bwino nkhosa za Khristu.
14. Kodi mfundo yaikulu ya zomwe takambiranazi ndi iti?
14 Mfundo yaikulu ndi yakuti: Wodzozedwa womaliza akadzatengedwa kupita kumwamba kumapeto kwa chisautso chachikulu, kulambira koona kudzapitirizabe padzikoli. Choncho motsogoleredwa ndi Yesu Khristu, atumiki a Mulungu adzapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. N’zoona kuti pa nthawiyo tidzaukiridwa ndi Gogi wa ku Magogi, yemwe ndi mgwirizano wa mayiko. (Ezek. 38:18-20) Koma kuukiridwa kwa kanthawi kumeneku sikudzalepheretsa anthu a Mulungu kukhalabe okhulupirika. Iye adzawapulumutsa. M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona “khamu lalikulu” la nkhosa zina za Khristu. Yohane anauzidwa kulemba kuti “khamu lalikulu” limeneli ‘linatuluka m’chisautso chachikulu.’ (Chiv. 7:9, 14) Choncho sitikukayikira kuti Yehova adzawateteza.
15-16. Mogwirizana ndi Chivumbulutso 17:14, kodi Akhristu odzozedwa adzakhala akuchita chiyani pa nthawi yankhondo ya Aramagedo, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zolimbikitsa?
15 Komabe ena angafunse kuti: ‘N’chiyani chidzachitikire odzozedwa, nanga azidzachita chiyani akadzachoka padzikoli?’ Baibulo limayankha funsoli mosapita m’mbali. Limasonyeza kuti maboma a m’dzikoli “adzamenyana ndi Mwanawankhosa.” Komabe iwo sadzapambana. Timawerenga kuti: “Mwanawankhosayo adzawagonjetsa.” Kodi ndi ndani adzathandize Mwanawankhosayu? Vesili limayankha kuti ndi “oitanidwa,” “osankhidwa mwapadera” ndiponso “okhulupirika.” (Werengani Chivumbulutso 17:14.) Kodi anthu amenewa ndi ndani? Amenewa ndi odzozedwa onse. Choncho wodzozedwa womaliza akadzatengedwa kupita kumwamba pambuyo pa chisautso chachikulu, imodzi mwa ntchito yawo yoyamba idzakhala kumenya nkhondo. Imeneyitu idzakhala ntchito yapadera. Ena mwa Akhristu odzozedwa ankakonda ndewu asanakhale a Mboni za Yehova. Enanso anali asilikali ankhondo m’dzikoli. Koma kenako anakhala Akhristu ndipo anaphunzira njira yamtendere. (Agal. 5:22; 2 Ates. 3:16) Iwo anasiyiratu kumenya nkhondo kapenanso zachiwawa zilizonse. Komabe akadzaukitsidwa n’kupita kumwamba, iwo adzagwira ntchito limodzi ndi Khristu ndi angelo ake oyera pomenya nkhondo yomaliza yolimbana ndi adani a Mulungu.
16 Tangoganizani, ali padzikoli, Akhristu ena odzozedwa anali achikulire komanso opanda mphamvu. Koma iwo akadzangopita kumwamba adzakhala zolengedwa zauzimu zamphamvu zomwe sizingafe ndipo adzamenya nkhondo limodzi ndi Mfumu yankhondo Yesu Khristu. Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, iwo adzagwira ntchito limodzi ndi Yesu pothandiza anthu kuti akhale angwiro. Mosakayikira, iwo adzachitira zinthu zabwino kwambiri abale ndi alongo awo kuposa mmene akanachitira ali padzikoli.
17. Kodi tikudziwa bwanji kuti atumiki onse a Mulungu adzakhala otetezeka pankhondo ya Aramagedo?
17 Kodi muli m’gulu la nkhosa zina? Ndiye kodi inuyo muyenera kudzachita chiyani nkhondo yofunika ya Aramagedo ikamadzayamba? Mudzangoyenera kudalira Yehova ndi kutsatira malangizo ake. Kodi zimenezi zikuphatikizapo chiyani? Baibulo limanena kuti: “Pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati, ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Atumiki onse okhulupirika a Mulungu, kaya kumwamba kapena padzikoli, adzakhala otetezeka pa nthawiyi. Mofanana ndi mtumwi Paulo, ndife otsimikiza mtima kuti ngakhale “maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera . . . sizidzatha kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu.” (Aroma 8:38, 39) Nthawi zonse muzikumbukira kuti Yehova amakukondani, ndipo sadzakutayani ngakhale pang’ono.
PAMENE WODZOZEDWA WOMALIZA ADZATENGEDWE KUPITA KUMWAMBA,
n’chiyani chomwe sichidzachitika?
n’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti kulambira koona sikudzasokonezedwa?
n’chifukwa chiyani sitingakayikire kuti Yehova adzapitiriza kusamalira anthu ake?
NYIMBO NA. 8 Yehova Ndiye Pothawirapo Pathu