Ekisodo
33 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Nyamuka, uchoke pano limodzi ndi anthu amene unawatsogolera potuluka mʼdziko la Iguputo. Mupite kudziko limene ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzapereka dziko ili kwa mbadwa* zako.’+ 2 Ndidzatumiza mngelo patsogolo panu+ ndipo ndidzathamangitsa Akanani, Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ 3 Mupite kudziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Koma ine sindidzayenda pakati panu, chifukwa ndinu anthu okanika+ ndipo ndingakufafanizeni panjira.”+
4 Anthu atamva mawu odetsa nkhawa amenewa, anayamba kulira ndipo palibe aliyense amene anavala zodzikongoletsera. 5 Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aisiraeli kuti, ‘Inu ndinu anthu okanika.+ Ndingathe kulowa pakati panu nʼkukufafanizani mʼkanthawi kochepa.+ Choncho musavale zodzikongoletsera pamene ndikuganizira zoti ndikuchiteni.’” 6 Choncho Aisiraeli sanavalenso* zodzikongoletsera kuyambira pamene anachoka paphiri la Horebe nʼkumapitiriza ulendo wawo.
7 Ndiyeno Mose anatenga tenti yake nʼkukaimanga kunja kwa msasa, chapatali ndi msasawo ndipo tentiyo anaipatsa dzina lakuti chihema chokumanako. Aliyense amene ankafuna kufunsa malangizo kwa Yehova+ ankapita kuchihema chokumanako chimene chinali kunja kwa msasa. 8 Ndiyeno Mose akamapita kuchihemako, munthu aliyense ankaimirira pakhomo la tenti yake nʼkumayangʼanitsitsa Mose mpaka atalowa mʼchihemacho. 9 Mose akangolowa mʼchihema, chipilala cha mtambo+ chinkatsika nʼkuima pakhomo la chihemacho pa nthawi imene Mulungu akulankhula ndi Mose.+ 10 Anthu onse akaona chipilala cha mtambo chitaima pakhomo la chihema, aliyense ankagwada pakhomo la tenti yake. 11 Yehova ankalankhula ndi Mose pamasomʼpamaso,+ mmene munthu amalankhulira ndi munthu mnzake. Mose akabwerera kumsasa, mtumiki wake Yoswa,+ mwana wa Nuni, sankachoka kuchihemako.
12 Tsopano Mose anauza Yehova kuti: “Inu mukundiuza kuti, ‘Tsogolera anthuwa,’ koma simunandidziwitse amene mudzamʼtume kuti ndipite naye. Komanso mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino ndi dzina lako lomwe,* ndipo ndakukomera mtima.’ 13 Ndiye ngati mwandikomeradi mtima, chonde ndidziwitseni njira zanu+ kuti ndikudziweni komanso kuti mupitirize kundikomera mtima. Kumbukiraninso kuti mtundu uwu ndi anthu anu.”+ 14 Choncho Mulungu anati: “Ineyo ndipita nawe+ ndipo ndidzakupatsa mpumulo.”+ 15 Kenako Mose anati: “Ngati inuyo simupita nafe, ndiye musatiuze kuti tichoke pano. 16 Ngati simupita nafe, kodi anthu adziwa bwanji kuti ine ndi anthu anuwa mwatikomera mtima? Koma mukapita nafe+ zisonyeza kuti ine ndi anthu anuwa mwatisiyanitsa ndi anthu ena onse amene ali padziko lapansi.”+
17 Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: “Ndichitanso zimene wapemphazi, chifukwa ndakukomera mtima ndipo ndikukudziwa bwino, ndi dzina lako lomwe.” 18 Kenako Mose anati: “Chonde ndionetseni ulemerero wanu.” 19 Koma Mulungu anati: “Ineyo ndidzakuonetsa ubwino wanga wonse, ndipo ndidzalengeza dzina langa lakuti Yehova kwa iwe.+ Amene ndikufuna kumukomera mtima ndidzamukomera mtima, ndipo amene ndikufuna kumusonyeza chifundo, ndidzamusonyeza chifundo.”+ 20 Ndiyeno anawonjezera kuti: “Sungathe kuona nkhope yanga, chifukwa palibe munthu amene angandione nʼkukhalabe ndi moyo.”
21 Yehova ananenanso kuti: “Pali malo pafupi ndi ine, ndipo ukaime pathanthwe. 22 Ulemerero wanga ukamadzadutsa pafupi ndi iwe, ndidzakuika kuphanga la thanthwelo, ndipo ndidzakuphimba ndi dzanja langa mpaka nditadutsa. 23 Kenako ndidzachotsa dzanja langa, ndipo udzaona msana wanga, koma nkhope yanga sungaione.”+