MUTU 13
‘Anthu Inu, Lengezani Uthengawu Pakati Pa Mitundu Ina’
1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mmene Yehova analankhulira ndi mneneri wake n’zofanana ndi kubangula kwa mkango?
KODI munamvapo mkango ukubangula? Mkango umabangula mwamphamvu kwambiri moti umatha kumveka pa mtunda wa makilomita 8. Kodi mungatani mutamva mkango ukubangula pafupi ndi nyumba yanu pakati pa usiku? Mwina mungachite mantha kwambiri. Amosi, yemwe ndi mmodzi mwa aneneri 12 amene analemba mabuku amene tikukambiranawa, ananena kuti: “Mkango wabangula! Ndani sachita mantha? Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa walankhula! Ndani sanenera?” (Amosi 3:3-8) Kodi mutamva Yehova akulankhula, simungachite zimene Amosi anachita? Amosi atamva mawu a Yehova, nthawi yomweyo analosera kuti mtundu wa mafuko 10 wa Isiraeli udzawonongedwa.
2. (a) Kodi mungatsanzire bwanji Amosi pa nkhani yolengeza uthenga wabwino? (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutu uno?
2 Mwina inu munganene kuti, ‘Komatu ine si mneneri.’ Mungaone kuti simungakwanitse ntchito imeneyi chifukwa chakuti simunaphunzitsidwe ntchito ya uneneri. Koma kumbukirani mmene zinthu zinalili kwa Amosi. Polankhula ndi Amaziya, yemwe anali wansembe wolambira mwana wa ng’ombe, Amosi ananena kuti: “Ine sindinali mneneri kapena mwana wa mneneri, koma ndinali m’busa ndiponso woboola nkhuyu.” (Amosi 7:14) Ngakhale kuti Amosi ankachokera m’banja losauka, anali ndi mtima wofunitsitsa kutumikira Yehova, monga mneneri wake. Nanga bwanji inuyo? Kodi mukudziwa kuti mwapatsidwa ntchito yofanana ndi imene aneneri 12 aja ankagwira? Mukuyenera kulengeza uthenga umene Mulungu watipatsa masiku ano, komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Kodi mumaiona bwanji ntchito imeneyi? Kodi mukufunika kulengeza uthenga wotani kwa anthu a mitundu yonse? Kodi mukugwira ntchito imeneyi mwakhama? Kodi mungadziwe bwanji ngati utumiki wanu ukuyenda bwino kapena ayi? Tiyeni tikambirane mayankho a mafunso amenewa.
‘MAWU APAKAMWA PATHU ALI NGATI ANA AMPHONGO A NG’OMBE’
3. Kodi mungatani kuti muzigwira nawo ntchito yofanana ndi ya aneneri 12 aja?
3 Kodi ntchito imene inuyo mukugwira ndi yofananadi ndi ya aneneriwo? N’zoona kuti simunamvepo Yehova akulankhula nanu mwachindunji. Komabe, kuchokera m’Mawu ake Baibulo, mwamva uthenga wofunika kwambiri woti tsiku la Yehova lili pafupi. Monga tinaonera m’Mutu 1 wa buku lino, mawu akuti “mneneri” ali ndi matanthauzo osiyanasiyana. Ngakhale kuti si inu mneneri ngati mmene Amosi ndi aneneri ena analili, mungathebe kuuza ena za m’tsogolo. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Mungalengeze uthenga wa ulosi umene mwaphunzira m’Malemba Opatulika, kuphatikizapo uthenga umene aneneri 12 amenewa analemba. Ino ndi nthawi yabwino yoti muchite zimenezi.
4. Kodi ulosi wa pa Yoweli 2:28-32 ukukwaniritsidwa bwanji masiku ano?
4 Tiyeni tione mfundo zina pa nkhani imeneyi. Yehova Mulungu anauza mneneri Yoweli kuti nthawi ina anthu amitundu yonse adzanenera. Iye anati: “Zimenezi zikadzachitika ndidzatsanulira mzimu wanga pa chamoyo chilichonse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera. Amuna achikulire adzalota maloto ndipo anyamata adzaona masomphenya.” (Yoweli 2:28-32) Choncho mtumwi Petulo anasonyeza kuti ulosi umenewu unakwaniritsidwa pa Pentekosite m’chaka cha 33 C.E., pamene anthu omwe anasonkhana m’chipinda cham’mwamba ku Yerusalemu analandira mzimu woyera. Kenako anthuwo anayamba kulalikira “zinthu zazikulu za Mulungu.” (Machitidwe 1:12-14; 2:1-4, 11, 14-21) Ndiyeno ganizirani zimene zikuchitika m’nthawi yathu ino. Ulosi wa Yoweliwu wakhala ukukwaniritsidwa kwambiri kungoyambira kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Pa nthawiyo, Akhristu odzozedwa ndi mzimu, omwe ndi amuna, akazi, achikulire ndiponso achinyamata, anayamba ‘kunenera’ kapena kuti kulengeza “zinthu zazikulu za Mulungu,” kuphatikizapo uthenga wabwino wa Ufumu womwe tsopano unakhazikitsidwa kumwamba.
5. (a) Kodi tonsefe tili ndi mwayi wapadera wotani? (b) Kodi mungatani kuti ‘mawu apakamwa panu akhale ngati ana amphongo a ng’ombe amene mukuwapereka nsembe’?
5 Ngakhale kuti anthu amene ali ‘m’khamu lalikulu’ la “nkhosa zina” sanadzozedwe ndi mzimu woyera kuti akhale ana a Mulungu, iwo akuuza Akhristu odzozedwa kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16; Zekariya 8:23) Choncho kaya inuyo mukuyembekezera kudzalandira moyo wosatha kumwamba kapena padziko lapansi pompano, muli ndi mwayi wapadera wopereka ‘mawu apakamwa panu’ ngati nsembe ya “ana amphongo a ng’ombe.” (Hoseya 14:2) Kodi mawu a Hoseyawa akutanthauza chiyani? Katswiri wina wa nkhani za m’Baibulo, dzina lake C. F. Keil, ananena kuti: “Ana a ng’ombe . . . anali nyama zabwino zoyenera kuzipereka nsembe zoyamika.” Mtumwi Paulo anatchula mfundo imene ili palembali pamene analemba kuti: “Tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu, yomwe ndi chipatso cha milomo yathu. Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.” (Aheberi 13:15) Choncho “mawu apakamwa pathu” omwe ali ngati “ana amphongo a ng’ombe amene tikuwapereka nsembe,” akutanthauza mawu abwino amene timalankhula potamanda Yehova.
6. N’chifukwa chiyani tikufunika kuganizira mozama za nsembe zathu zotamanda Mulungu?
6 Inuyo mumapereka nsembe zotamanda Yehova mukamapemphera mochokera pansi pa mtima, mukamapereka ndemanga pamisonkhano yachikhristu, komanso mukamauza ena za iye mu utumiki wakumunda. Choncho aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimapereka nsembe zotani ndikamachita zinthu zimenezi?’ Popeza kuti mwaphunzira kuti ansembe achipongwe a m’nthawi ya Malaki ankapereka nsembe zolumala paguwa lansembe la Mulungu, mosakayikira mwayamba kudana ndi zimene iwo ankachitazo. Ndipo kudzera mwa Malaki, Yehova anawauza mosapita mbali kuti nsembe zimene ankaperekazo zinali zosayenera. Iye ankafunika kuchita zimenezi chifukwa anthuwo pawokha sankaona kuti akunyoza tebulo la Yehova. (Malaki 1:8) Choncho, ndi bwino kuti tiziganizira mozama za nsembe zathu kuti tione ngati tikupereka nsembe zabwino kwambiri zopanda chilema chilichonse.
KODI TIKUYENERA KULENGEZA UTHENGA WOTANI?
7. Kodi tikufunika kulimba mtima kuti tilengeze mbali iti ya uthenga wathu?
7 Inu mukudziwa kuti pamafunika kulimba mtima kuti “mawu apakamwa pathu akhale ngati ana amphongo a ng’ombe amene tikuwapereka nsembe” mu utumiki wathu. Izi zili choncho chifukwa chakuti uthenga umene tikulengeza uli ndi mbali ziwiri, ina yosangalatsa ndipo ina yosasangalatsa. Mwachitsanzo, mneneri Yoweli anauza anthu a Mulungu kuti: “Anthu inu, lengezani pakati pa mitundu ina kuti, ‘Konzekerani nkhondo! Konzekeretsani amuna amphamvu! Amuna onse ankhondo abwere!’” (Yoweli 3:9) Ulosi umenewu ukugwiranso ntchito masiku ano, ndipo ndi wosasangalatsa kwa anthu ambiri. Ulosiwu ukuneneratu kuti Yehova adzamenya nkhondo yolungama ndipo adzawononga anthu onse amene safuna kumumvera. Chotero pamene Yehova akuuza anthu ake kuti ‘asule malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo,’ akuuzanso adani ake kuti ‘asule makasu awo a pulawo kuti akhale malupanga, ndiponso zida zawo zosadzira mitengo kuti zikhale mikondo ing’onoing’ono.’ (Mika 4:3; Yoweli 3:10) Izi zikutanthauza kuti adani a Mulungu ayenera kukonzekera nkhondo yolimbana ndi Mlengi wa chilengedwe chonse. Kunena zoona kulengeza uthenga woterewu si chinthu chapafupi.
8. N’chifukwa chiyani “otsala a Yakobo” akuwayerekezera ndi mkango?
8 Mu uthenga wa mneneri Mika, anthu amene ‘mawu apakamwa pawo ali ngati ana amphongo a ng’ombe amene akuwapereka nsembe,’ akuwayerekezera ndi mkango. Iye analemba kuti: “Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu. Iwo adzakhala ngati mkango pakati pa nyama zakutchire. Adzakhala ngati mkango wamphamvu pakati pa magulu ankhosa, umene umati ukadutsa pakati pa nkhosazo, ndithu umazimbwandira ndi kuzikhadzula ndipo sipakhala wozipulumutsa.” (Mika 5:8) N’chifukwa chiyani anthuwo akuwayerekezera ndi mkango? Masiku ano anthu a Mulungu, amene akutsogoleredwa ndi Akhristu odzozedwa omwe adakali padziko lapansi, akufunikira kukhala olimba mtima ngati mkango polengeza uthenga wochenjeza anthu amitundu yonse.a
9. (a) Kodi mungafunike kulimba mtima ngati mkango pa nthawi ziti? (b) Kodi mungatani kuti mulimbe mtima mukakumana ndi anthu otsutsa kapena opanda chidwi?
9 Kodi mumakhala wolimba mtima ngati mkango mukamalengeza uthenga wochenjeza anthu? Mungafunike kukhala wolimba mtima ngati mukulankhula ndi anthu audindo, anzanu a kusukulu, a kuntchito komanso achibale anu amene si Mboni. (Mika 7:5-7; Mateyu 10:17-21) Kodi mungatani kuti mukhale wolimba mtima anthu akamakutsutsani kapena mukapeza anthu opanda chidwi? Tiyeni tione chimene chinathandiza Mika pamene ankagwira ntchito yovuta yochenjeza anthu za kuwonongedwa kwa mzinda wa Samariya ndiponso wa Yerusalemu. Iye anati: “Ine ndili ndi mphamvu zochuluka chifukwa cha mzimu wa Yehova. Ndine wokonzeka kuchita zachilungamo ndi kusonyeza mphamvu kuti ndiuze mbadwa za Yakobo za kupanduka kwawo, komanso kuti ndiuze Isiraeli za tchimo lake.” (Mika 1:1, 6; 3:8) Inunso mungakhale ndi “mphamvu zochuluka” chifukwa mzimu woyera wa Mulungu ungakupatseni mphamvu zimenezi. (Zekariya 4:6) Mukamadalira Mulungu n’kumapemphera nthawi zonse, mudzatha kulengeza uthenga umene udzadabwitse aliyense.—2 Mafumu 21:10-15.
10. Kodi tingatsanzire bwanji Zefaniya tikamalengeza uthenga wonena za “tsiku la Yehova”?
10 N’zoona kuti tikufunikira kukhala olimba mtima tikamauza anthu uthenga wochenjeza, komabe tikufunikiranso kukhala osamala. Tikufunika kukhala ‘odekha kwa onse,’ ngakhale pamene tikulengeza za “tsiku la Yehova” limene likubweralo. (2 Timoteyo 2:24; Yoweli 2:1, 11; Zefaniya 1:14) Pa nkhani imeneyi tingaphunzirenso zambiri kwa aneneri 12 aja. Iwo ankalengeza molimba mtima uthenga wa chiweruzo wochokera kwa Yehova, komabe ankalankhula mosamala kwa anthu amene anali ofunitsitsa kusintha. Mwachitsanzo, Zefaniya analankhula mosabisa Chichewa podzudzula akalonga ouma mtima a m’nthawi yake, koma podzudzulapo sanaphatikize Mfumu Yosiya, yomwe inali yokhulupirika. (Zefaniya 1:8) Ifenso tikamalengeza uthenga wochenjeza, tingachite bwino kumaona anthu kuti akhoza kusintha n’kukhala nkhosa, ndipo tizipewa kuwaweruza.—Mateyu 25:32-34.
11. (a) Kodi mbali yachiwiri ya uthenga wathu ndi iti? (b) Kodi tingatsanzire bwanji aneneri 12 tikamalengeza za tsiku la Yehova?
11 Kodi mbali yachiwiri ya uthenga umene timalengezawu ndi iti? Chaputala 5 cha buku la Mika chingatithandize kudziwa mbali imeneyi. Mika analemba kuti: “Otsala a Yakobo, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzakhala ngati mame ochokera kwa Yehova. Iwo adzakhala ngati mvula yamvumbi imene ikuwaza pazomera, yomwe sidalira munthu kapena kuyembekezera ana a anthu ochokera kufumbi.” (Mika 4:1; 5:7) Popeza kuti “otsala a Yakobo” wauzimu, kapena kuti Isiraeli wauzimu, pamodzi ndi anzawo akulengeza uthenga wabwino ku “mitundu yambiri ya anthu” masiku ano, iwo ali ngati “mame ochokera kwa Yehova” komanso ali ngati “mvula yamvumbi imene ikuwaza pazomera.” Pa mfundo yachiwiri imeneyi ya uthenga wathu, tingaphunzire zambiri m’mabuku 12 omalizira a m’Malemba Achiheberi. Tikutero chifukwa chakuti aneneri amene analemba mabukuwa sankalengeza uthenga wonena za kuwonongedwa kwa anthu wokha, koma ankalengezanso uthenga woti Ayuda ena adzapulumuka ndipo adzamanganso mzinda wawo. Choncho kodi inuyo mukakhala mu utumiki mumauza anthu mfundo zolimbikitsa zokhudza “tsiku la Yehova”?
KODI INUYO MUMALENGEZA BWANJI UTHENGAWU?
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani anthu a Mulungu amayerekezeredwa ndi tizilombo? (b) Kodi mumamva bwanji mumtima mukawerenga lemba la Yoweli 2:7, 8?
12 Koma kodi mukulengeza bwanji uthengawu? Ntchito imene anthu a Mulungu akugwira, mneneri Yoweli anaiyerekezera ndi miliri yobwera chifukwa cha tizilombo tosiyanasiyana, kuphatikizapo dzombe. (Yoweli 1:4) Koma n’chifukwa chiyani tikunena kuti anthu a Yehova ali ngati tizilombo tambirimbiri? Chifukwa chakuti malinga ndi lemba la Yoweli 2:11, Mulungu ananena kuti tizilombo timeneti ndi “asilikali ake ankhondo.” (Nalonso buku la Chivumbulutso limayerekezera anthu a Mulungu ndi dzombe. Onani Chivumbulutso 9:3, 4.) Tizilombo timene Yoweli anafotokoza tinkawononga zinthu ngati moto, moti malo amene ankaoneka ngati munda wa “Edeni” anasanduka “chipululu chowonongeka.” (Yoweli 2:2, 3) Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti mukudziwa kufunika kwa ulosi wa Yoweliwu?
13 Taganizirani mmene tizilombo timeneti timawonongera zinthu. Yoweli anafotokoza kuti: “Amathamanga ngati amuna amphamvu. Amakwera khoma ngati amuna ankhondo. Aliyense amayenda m’njira yake ndipo saphonya njira zawo. Iwo sakankhanakankhana ndipo amayendabe ngati mwamuna wamphamvu amene akuyenda panjira yake. Wina akalasidwa ndi kugwa enawo sabwerera m’mbuyo.” (Yoweli 2:7, 8) Palibe “khoma” limene lingatchinge njira ya tizilomboti kapena kutilepheretsa kuchita zofuna zake. N’chimodzimodzinso ndi Akhristu, chifukwa “wina akalasidwa ndi kugwa,” ngati mmene zinachitikira ndi Akhristu okhulupirika amene anaphedwa ndi adani ankhanza, Akhristu ena amapitiriza ntchito yawo ndipo amamalizitsa ntchito imene Yehova anawapatsa. Kodi mwatsimikiza ndi mtima wonse kugwira ntchito yolengeza za tsiku la Yehova mpaka Mulungu ataona kuti cholinga chake chakwaniritsidwa? Mwina nthawi zina mungafunikire kupitiriza ntchito imene Akhristu okhulupirika amene anamwalira ankagwira.
14. Kodi mungatani pothandizira kuti munthu aliyense amve uthenga wabwino?
14 Mfundo imene tikuphunzira pamenepa ndi yakuti tiyenera kulalikira kwa munthu aliyense. Kodi inuyo panokha mungatani pothandizira kuti munthu aliyense amve uthenga wabwino ngati mmene ulosi wa Yoweli ukunenera? Mungachite zimenezi pogwira nawo ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba komanso kubwerera kwa anthu amene anasonyeza chidwi kuti mukapitirize kuphunzira nawo. Kuwonjezera pamenepo, mungafunike kupitanso kunyumba zimene simunapezeko anthu. Mukamachita zimenezi mudzasonyeza kuti mukumvetsetsa tanthauzo la ulosi umenewu. Ndipotu mukamalalikira mumsewu, mungakumane ndi anthu amene simungathe kuwapeza panyumba. Zina zimene mungachite ndi izi: Mungathe kuthandiza anthu ochokera m’mayiko ena amene akukhala m’dera lanu.b Kodi mukuyesetsa kugwiritsira ntchito njira zolalikirira zimenezi n’cholinga choti aliyense amve uthenga wabwino?
KODI MUNGADZIWE BWANJI KUTI UTUMIKI WANU UKUYENDA BWINO?
15. Kodi anthu anachita chiyani atamva uthenga umene aneneri 12 aja ankalengeza?
15 Kodi anthu amatani akamva uthenga wonena za tsiku lochititsa mantha la Yehova? Sitiyenera kudabwa anthu ena akatitsutsa kapena akamaoneka kuti alibe chidwi ndi uthenga wathu. Zimenezi zinkachitikiranso aneneri ambiri a Mulungu, omwe ambiri a iwo ankafunika kulengeza uthenga wochenjeza anthu mosapita m’mbali. (Yeremiya 1:17-19; 7:27; 29:19) Ngakhale kuti aneneriwo ankakumana ndi zimenezi, ambiri zinthu zinawayendera bwino. Mwachitsanzo, aneneri asanu anathandiza anthu kuti alape komanso kusiya makhalidwe awo oipa. Aneneriwa ndi Yona, Mika, Zefaniya, Hagai ndi Zekariya.
16. Kodi ntchito imene mneneri Mika ankagwira inali ndi zotsatira zotani?
16 Zikuoneka kuti ntchito ya uneneri imene Zefaniya ankagwira ndi imene inachititsa Mfumu Yosiya kuti alimbikitse anthu kuyambiranso kulambira Mulungu woona. Mneneri Mika analengeza molimba mtima uthenga woti Mulungu adzaweruza atsogoleri a ku Yuda, ndipo zimene Mfumu Hezekiya anachita zinali zogwirizana ndi zimene mneneriyu ananena. (Mika 3:1-3) N’zochititsa chidwi kuti akulu ena a m’nthawi ya Yeremiya ananena kuti zimene Hezekiya anachita chinali chitsanzo chabwino. Iwo ananena kuti Hezekiya ‘anaopa Yehova ndi kukhazika pansi mtima wa Yehova.’ (Yeremiya 26:18, 19; 2 Mafumu 18:1-4) Mu ulamuliro wa Hezekiya, anthu a ku Yuda ndiponso ena a mu ufumu wa kumpoto amene ankafunitsitsa kutumikira Mulungu, anachita Pasika komanso Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa, ndipo anawonjezera nthawi ya chikondwererochi ndi mlungu umodzi. Kodi chinachitika n’chiyani anthuwa atayambiranso kulambira Mulungu woona? Baibulo limanena kuti: “Munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu.” (2 Mbiri 30:23-26) Mika anayamba pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Ahazi kulengeza uthenga wakuti Mulungu adzaweruza mtundu umene unasiya kumutumikira. Koma mneneriyu anayamba kuona zotsatira zabwino za ntchito yakeyi pamene Hezekiya, mwana wa Ahazi, anamvera uthenga wake.
17. Kodi Hagai ndi Zekariya anachita chiyani?
17 Ganiziraninso za mneneri Hagai ndi mneneri Zekariya. Aneneriwa anachita utumiki wawo Ayuda atabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo. Pa nthawiyo Ayudawo anali atayamba kudzikuza komanso ankachita zinthu mopanda chifundo. (Hagai 1:1, 2; Zekariya 1:1-3) Pa nthawi imene aneneriwa ankayamba utumiki wawo, panali patadutsa zaka 16 kuchokera pamene Ayudawo anamanga maziko a kachisi. Izi zikusonyeza kuti anthuwo ‘ankathamangathamanga kuti asamalire nyumba zawo’ koma ‘sanamalize kumanga nyumba’ ya Yehova. Hagai anauza Ayudawo kuti: “‘Limbani mtima anthu nonse a m’dzikoli ndipo gwirani ntchito,’ watero Yehova.” Kodi atatero chinachitika n’chiyani? “Yehova analimbikitsa” Bwanamkubwa Zerubabele, Mkulu wa Ansembe Yoswa, ndi “anthu ena onse.” Zimenezi zinachititsa kuti Ayudawo amalize ntchito yomanga kachisi.—Hagai 1:9, 12, 14; 2:4.
18, 19. (a) Kodi anthu a m’mayiko ena akuchita chiyani akamva uthenga wonena za tsiku la Yehova? (b) Kodi inuyo mungatani kuti mukhale m’gulu la anthu omwe akulengeza uthenga wochenjeza anthu a mitundu yonse za tsiku la Yehova?
18 Ambiri mwa aneneri 12 aja ankalengeza uthenga wawo kwa anthu a mtundu umene unali kale wodzipereka kwa Yehova. N’kutheka kuti ifeyo timalalikira kwa anthu amene sanamvepo za Mulungu woona, komabe tingaphunzire mfundo yofunika kwambiri tikaona mmene ntchito ya aneneriwa inayendera. Masiku anonso m’madera ambiri anthu akulabadira uthenga wochenjeza za tsiku la Yehova. Zomwe zikuchitika n’zofanana ndi zimene Zekariya analosera pamene anati: “Mitundu yambiri ya anthu idzadziphatika kwa Yehova pa tsikulo, choncho adzakhala anthu anga. Ine ndidzakhala mwa iwe.” (Zekariya 2:11) Izi zikusonyeza kuti masiku ano, “mitundu yambiri ya anthu” ikulabadira uthenga umene anthu a Mulungu akulengeza. (Chivumbulutso 7:9) Zekariya analosera kuti: “Anthu ambiri a mitundu ina ndiponso mitundu yamphamvu ya anthu idzabweradi kudzafunafuna Yehova wa makamu mu Yerusalemu. Idzabwera kudzakhazika pansi mtima wa Yehova.” Anthu amenewa akutchedwa “amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina” ndipo akugwira chovala cha Mwisiraeli wauzimu, n’kunena kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”—Zekariya 8:20-23.
19 Onani kuti lembali likunena za ‘zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina.’ Masiku ano, Baibulo komanso mabuku ofotokoza za m’Baibulo akumasuliridwa m’zinenero zambiri, ndipo a Mboni za Yehova akuphunzitsidwa kuti aziphunzitsa anthu a ‘zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina.’ (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8) Mwina inuyo munaphunzira chinenero china kuti muthandize anthu olankhula chinenero chimenecho m’dera lanu. Ndipotu pali ena ambiri amene adzipereka kuphunzira chinenero chimodzi kapena ziwiri zatsopano ndipo asamukira m’mayiko amene anthu ambiri amamvetsera uthenga wabwino. Kodi inuyo mungathe kusamukira kudera limene kuli anthu ambiri ofunitsitsa kumva uthenga wabwino kuti ‘mukalengeze uthengawo pakati pa anthu a mitundu ina’? Nkhani imeneyi muiganizire mofatsa ndi kuipempherera. Ngati muli ndi ana, muzikambirana nkhani imeneyi mobwerezabwereza n’cholinga choti ana anuwo adzakhale ndi mtima wofuna kudzachita utumiki umenewu akadzakula.
20. Kodi zimene Yehova anachita ndi anthu a ku Nineve zikusonyeza kuti ali ndi mtima wotani?
20 Mneneri Yona ankakayikira zoti anthu a ku Nineve, amene ankafunika kuti akawalalikire, angamvetsere uthenga wake. Koma anthuwo, kuphatikizapo mfumu yawo, anamvetsera uthenga wa Yona ndipo anakhulupirira Yehova. Choncho Mulungu anafunsa Yona kuti: “Kodi ine sindikuyenera kumvera chisoni mzinda waukulu wa Nineve, mmene muli anthu oposa 120,000, omwe sadziwa kusiyanitsa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere?” (Yona 4:11) Taganizirani mofatsa mawu amenewa, ndiyeno ganiziraninso cholinga chimene mumakhala nacho polengeza za tsiku loopsa la Yehova kwa anthu ena. Kodi mumaona kuti mukufunikira kugwira ntchito imeneyi chifukwa chakuti Yehova anapereka dipo n’cholinga choti mudzapulumuke? Kodi mumaona kuti muli ndi udindo wogwira ntchito imeneyi monga mtumiki wodzipereka kwa Yehova? (1 Akorinto 9:16, 17) Mafunso amenewa akutisonyeza zifukwa zomveka zotichititsa kulengeza za tsiku la Yehova. Kuwonjezera pamenepo ‘timamvera chisoni’ anthu amene tikuwachenjeza za tsiku la Yehovawo. Choncho timasangalala kwambiri tikamauza anthu za tsiku limeneli chifukwa chakuti, mofanana ndi Mulungu, tikuwamvera chifundo ndipo tikufuna adzapulumuke.
21. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Amosi amene ankatsutsidwa ndi Amaziya?
21 Sitikudziwa zonse zimene anthu anachita atamva uthenga wa Yoweli, Obadiya, Nahumu, Habakuku ndi Malaki.Koma tikudziwa zimene anachita atamva uthenga wa Amosi. Mwachitsanzo, Amaziya anatsutsa kwambiri Amosi, ndipo anamuneneza kuti wakonzera mfumu chiwembu ndipo ankafuna kuti Amosi aletsedwe kulalikira ku Beteli. (Amosi 7:10-13) Koma Amosi sanachite mantha ndi zimenezi. Masiku anonso anthu achipembedzo akhoza kuchititsa kuti anthu andale azizunza anthu a Yehova kapena kuti aletse ntchito yawo yolalikira. Kodi mungatsanzire Amosi polengeza uthenga wabwino ngakhale pamene anthu akukutsutsani?
22. N’chifukwa chiyani munganene kuti utumiki ukuyenda bwino m’dera lanu?
22 Ngakhale kuti anthu anachita zinthu zosiyanasiyana atamva uthenga umene aneneri 12 aja ankalengeza, aneneri onsewo anakwanitsa ntchito imene anapatsidwa. Mfundo yofunika kwambiri si yokhudza zimene anthu amachita akamva uthenga wathuwo, koma ndi yakuti ‘mawu apakamwa pathu amakhala ngati ana amphongo a ng’ombe amene tikuwapereka nsembe’ kwa Yehova, ndipo imeneyi ndi nsembe yabwino kwambiri ‘yotamanda Mulungu.’ (Hoseya 14:2; Aheberi 13:15) Choncho zotsatira za ntchito yathu tiyenera kungozisiya m’manja mwa Mulungu. Iye adzakoka anthu amene alidi ngati nkhosa. (Yohane 6:44) Komanso ntchito yanu yolengeza uthenga wochokera kwa Mulungu ingathe kuyenda bwino, kaya anthu akumvetsera uthengawo kapena ayi. Dziwani kuti ‘mapazi a munthu yemwe akubweretsa uthenga wabwino, munthu yemwe akulengeza za mtendere,’ ndi okongola kwabasi kwa anthu amene amamvetsera uthenga wabwino. Ndipotu mfundo yofunika kwambiri ndi yakuti mapazi a anthu amenewa ndi okongola kwambiri m’maso mwa Yehova. (Nahumu 1:15; Yesaya 52:7) Popeza kuti tsiku la Yehova layandikira kwambiri, khalani wotsimikiza ndi mtima wonse kuti mupitirize kuchita zimene Yoweli analosera kuti zidzachitika m’nthawi yathu ino. Iye anati: “Anthu inu, lengezani pakati pa mitundu ina kuti, ‘Konzekerani nkhondo! Konzekeretsani amuna amphamvu!’” Palembali akunena za nkhondo ya Mulungu yowononga anthu oipa.—Yoweli 3:9.
a Ulosi umenewu uyenera kuti unakwaniritsidwa koyamba pa nthawi ya Amakabeo. Pa nthawiyi Ayuda, motsogoleredwa ndi Amakabeo, anapirikitsa adani awo m’dziko la Yuda ndipo anapanganso mwambo wopereka kachisi kwa Mulungu. Zimenezi zinathandiza Ayuda ena kuti athe kulandira Mesiya pa nthawi imene anaonekera.—Danieli 9:25; Luka 3:15-22.
b Kabuku kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse n’kothandiza kwambiri polalikira kwa anthu amene salankhula chinenero chachikulu cha m’dera lanu.