Perekani Nsembe Zimene Zimakondweretsa Yehova
“Potero mwa iye [Yesu Kristu] tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.”—AHEBRI 13:15.
1. Kodi nchiyani chimene Yehova anachonderera Aisrayeli ochimwa kuchita?
YEHOVA ali Mthandizi kwa opereka nsembe zovomerezeka kwa iye. Chotero, chiyanjo chake pa nthaŵi ina chinali pa Aisrayeli omwe anapereka nsembe za nyama. Koma kodi nchiyani chimene chinachitika pamene anachimwa mobwerezabwereza? Kupyolera mwa mneneri Hoseya, iwo anachondereredwa kuti: “Israyeli, bwerera kumka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako. Mukani nawo mawu, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mawu milomo yathu ngati ng’ombe.”—Hoseya 14:1, 2.
2. Kodi nchiyani chomwe chinali ‘milomo ngati ng’ombe,’ ndipo kodi ndimotani mmene Paulo analozera ku ulosi wa Hoseya?
2 Zinali tero kuti anthu akale a Mulungu analimbikitsidwa kupereka kwa Yehova Mulungu ‘milomo yawo ngati ng’ombe.’ Kodi izi zinali chiyani? Nkulekeranji, popeza kuti zinali nsembe za chitamando chochokera mu mtima! Akumaloza ku ulosi umenewu, mtumwi Paulo anachonderera Akristu Achihebri “kupereka chiperekere nsembe ya kuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15) Kodi nchiyani chimene chingathandize Mboni za Yehova kupereka nsembe zoterozo lerolino?
“Mutsanze Chikhulupiriro Chawo”
3. Monga nsonga, kodi nchiyani chimene mtumwi Paulo ananena pa Ahebri 13:7, chikumadzutsa funso lotani?
3 Kugwiritsira ntchito uphungu umene Paulo anapereka kwa Ahebri kudzatitheketsa ife kupereka nsembe zolandirika kwa Mthandizi wathu Wamkulu, Yehova Mulungu. Mwachitsanzo, mtumwiyo analemba kuti: “Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mawu a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.” (Ahebri 13:7) Kodi ndi kwa yani kumene Paulo analozera pamene ananena kuti, “Kumbukirani atsogoleri anu,” kapena “abwanankubwa anu”?—New World Translation Reference Bible, mawu am’munsi.
4. (a) Mogwirizana ndi lemba Lachigriki, kodi nchiyani chimene awo ‘otsogolera’ akuchita? (b) Kodi ndani omwe ali ‘otsogolera’ pakati pa Mboni za Yehova?
4 Paulo analankhula za awo ‘otsogolera,’ kapena olamulira. (Mavesi 7, 17, 24) Liwu Lachingelezi la “kulamulira” latengedwa kupyolera m’Chilatin kuchokera ku Chigriki ky·ber·naʹo, kutanthauza “kuyendetsa chombo, kutsogoza, kulamulira.” Akulu Achikristu amalamulira mwa kugwiritsira ntchito “maluso [awo] kutsogolera” (Chigriki, ky·ber·neʹseis) m’kupereka utsogoleri ndi chitsogozo m’mipingo ya kumaloko. (1 Akorinto 12:28) Koma atumwiwo ndi akulu ena m’Yerusalemu anatumikira monga bungwe kupereka chitsogozo ndi uphungu ku mipingo yonse. (Machitidwe 15:1, 2, 27-29) Chotero, lerolino, bungwe lolamulira la akulu limapereka uyang’aniro wauzimu kwa Mboni za Yehova dziko lonse.
5. Kodi nchifukwa ninji ndipo ndimotani mmene tiyenera kupempherera akulu a mu mpingo ndi ziŵalo za Bungwe Lolamulira?
5 Akulu akumaloko ndi ziŵalo za Bungwe Lolamulira amatenga chitsogozo pakati pathu; chifukwa chake, tiyenera kuwalemekeza ndi kupemphera kuti Mulungu awapatse nzeru zofunikira kulamulira mpingo. (Yerekezerani ndi Aefeso 1:15-17.) Ndi choyenerera chotani nanga kuti tikumbukire aliyense yemwe ‘analankhula mawu a Mulungu kwa ife’! Timoteo anaphunzitsidwa osati kokha ndi amayi ndi agogo ake komanso pambuyo pake ndi Paulo ndi ena. (2 Timoteo 1:5, 6; 3:14) Chotero Timoteo akakhoza kupenyetsetsa mmene mikhalidwe ya otsogolera inakhalira ndipo anali wokhoza kutsanzira chikhulupiriro chawo.
6. Kodi ndi chikhulupiriro chayani chimene tiyenera kutsanzira, koma kodi ndani omwe tiyenera kutsatira?
6 Anthu oterowo onga Abele, Nowa, Abrahamu, Sara, Rahabi, ndi Mose anasonyeza chikhulupiriro. (Ahebri 11:1-40) Chotero, tingatsanzire chikhulupiriro chawo popanda kukaikira chifukwa chakuti iwo anafa okhulupirika kwa Mulungu. Komanso ‘tingatsanzire chikhulupiriro’ cha amuna okhulupirika omwe tsopano akutsogolera pakati pathu. Ndithudi, sitimatsanzira anthu opanda ungwiro, popeza kuti timalunjikitsa maso athu pa Kristu. Monga mmene wotembenuza Baibulo Edgar J. Goodspeed ananenera kuti: “Ngwazi zakale siziri chitsanzo cha m’khulupiriri, popeza kuti mwa Kristu iye ali ndi chitsanzo chabwino . . . Wothamanga Wachikristu ayenera kulunjikitsa maso ake pa Yesu.” Inde, ‘Kristu anamva zowawa chifukwa cha ife, natisiyira chitsanzo kuti tikalondole mapazi ake mosamalitsa.’—1 Petro 2:21; Ahebri 12:1-3.
7. Kodi ndimotani mmene Ahebri 13:8 ayenera kuyambukirira mkhalidwe wathu kulinga ku kuvutika chifukwa cha Yesu Kristu?
7 Akumalunjikitsa chisamaliro pa Mwana wa Mulungu, Paulo anawonjezera kuti: “Yesu Kristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi ku nthaŵi zonse.” (Ahebri 13:8) Mboni zokhulupirika zonga ngati Stefano ndi Yakobo zinasonyeza umphumphu wosasunthika, pambuyo pa chitsanzo chokhazikika cha Yesu. (Machitidwe 7:1-60; 12:1, 2) Popeza kuti anali ofunitsitsa kufa monga atsatiri a Kristu, chikhulupiriro chawo chiri choyenerera kwa ife kuchitsanzira. Kale, tsopano lino, ngakhale mtsogolo, anthu aumulungu samapempha chodzikhululukira kuthaŵa kuvutika ndi kuphedwera chikhulupiriro monga ophunzira a Yesu.
Peŵani Ziphunzitso Zonyenga
8. Kodi ndimotani mmene mukalongosolera mawu a Paulo pa Ahebri 13:9?
8 Kusasinthika kwaumunthu wa Yesu ndi ziphunzitso kuyenera kutipangitsa ife kumamatira ku chimene iye ndi atumwi ake anaphunzitsa. Ahebri anawuzidwa kuti: “Musatengedwe ndi maphunzitso amitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindula nazo.”—Ahebri 13:9.
9. Kodi ndi ku zinthu zokulira zotani zimene Paulo analozera m’kalata ya kwa Akristu Achihebri?
9 Ayuda analoza ku zinthu zonga ngati kuperekedwa kwa Chilamulo kozizwitsa pa Phiri la Sinai ndi ufumu wosatha wa Davide. Koma Paulo anasonyeza Akristu Achihebri kuti ngakhale kuti kuikidwa kwa pangano la Chilamulo kunali kopambana, Yehova anachitira umboni mwaukumu mwa zizindikiro, zozizwitsa, ntchito zamphamvu, ndi zogawira za mzimu woyera pamene pangano latsopano linayambitsidwa. (Machitidwe 2:1-4; Ahebri 2:2-4) Ufumu wakumwamba wa Kristu sungagwedezedwe, monga momwe kunachitira kulamulira kwaufumu wa Davide mu 607 B.C.E. (Ahebri 1:8, 9; 12:28) Ndiponso, Yehova akusonkhanitsa odzozedwa chinachake chozizwitsa koposa kuposa kusonyezedwa kozizwitsa pa Phiri la Sinai chisanachitike, popeza kuti iwo amafikira Phiri la Ziyoni lakumwamba.—Ahebri 12:18-27.
10. Mogwirizana ndi Ahebri 13:9, kodi mtima ukulimbikitsidwa ndi chiyani?
10 Chotero Ahebri anafunikira kupeŵa ‘kutengedwa ndi maphunzitso amitundumitundu ndi achilendo’ a Ayuda. (Agalatiya 5:1-6) Simwaziphunzitso zoterozo koma ‘mwa chisomo cha Mulungu ndi pamene mtima ungalimbitsidwe’ kotero kuti akhalebe okhazikika m’chowonadi. Mwachiwonekere ena anatsutsa ponena za zakudya ndi nsembe, popeza kuti Paulo ananena kuti mtima sunalimbitsidwe “ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindula nazo.” Mapindu auzimu amatuluka ku kudzipereka kwaumulungu ndi kuyamikira dipo, osati kuchokera ku kudera nkhaŵa kopambanitsa ponena za kudya zakudya zinazake ndi kusunga masiku ena. (Aroma 14:5-9) Ndiponso, nsembe ya Kristu inapangitsa nsembe za Alevi kusagwira ntchito.—Ahebri 9:9-14; 10:5-10.
Nsembe Zimene Zimakondweretsa Mulungu
11. (a) Kodi ndi chiyani chomwe chiri nsonga ya mawu a Paulo pa Ahebri 13:10, 11? (b) Kodi ndi guwa lansembe lophiphiritsira liti limene Akristu ali nalo?
11 Ansembe Achilevi anadya nyama ku nyama zoperekedwa nsembe, koma Paulo analemba kuti: “Tiri nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema [kachisi] alibe ulamuliro wa kudyako. Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa ndi mkulu wa ansembe kuloŵa m’malo opatulidwa, chifukwa cha zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa” pa Tsiku Lotetezera. (Ahebri 13:10, 11; Levitiko 16:27; 1 Akorinto 9:13) Akristu ali ndi guwa lansembe lophiphiritsira lotanthauza kufikira Mulungu pamaziko a nsembe ya Yesu yomwe imatetezera uchimo ndi kutulukapo kukhululukidwa ndi Yehova ndi chipulumutso ku moyo wosatha.
12. Pa Ahebri 13:12-14, kodi nchiyani chimene Akristu odzozedwa anachondereredwa kuchita?
12 Paulo sakugogomezera pa kufanana ndi Tsiku Lotetezera, komabe iye akuwonjezera kuti: “Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretsa anthuwo mwa mwazi wa iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata” cha Yerusalemu. Kumeneko Kristu anafa ndi kupereka nsembe yotetezera mokhutiritsa kotheratu. (Ahebri 13:12; Yohane 19:17; 1 Yohane 2:1, 2) Mtumwi Paulo anachonderera Akristu odzozedwa anzake kuti: “Chifukwa chake titulukire kwa iye [Kristu] kunja kwa tsasa osenza thonzo lake. Pakuti pano tiribe mudzi wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.” (Ahebri 13:13, 14; Levitiko 16:10) Ngakhale kuti timatonzedwa monga momwe Yesu anachitiridwa, timapirira monga Mboni za Yehova. Ife ‘timakana kupanda umulungu ndi zikhumbo za kudziko ndi kukhala ndi moyo ndi maganizo abwino ndi chilungamo ndi kudzipereka kwaumulungu pakati pa dongosolo lamakono iri lazinthu’ pamene tikuyang’ana ku dziko latsopano. (Tito 2:11-14; 2 Petro 3:13; 1 Yohane 2:15-17) Ndipo odzozedwa pakati pathu amafunafuna mofunitsitsa “mzinda,” Ufumu wakumwamba.—Ahebri 12:22.
13. Kodi nsembe zimene zimakondweretsa Mulungu sizimaphatikiza kokha chiyani?
13 Kenaka Paulo anatchula nsembe zimene zimakondweretsa Mulungu, akumalemba kuti: “Potero mwa iye [Yesu] tipereke chiperekere nsembe ya kuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake. Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” (Ahebri 13:15, 16) Nsembe Zachikristu siziri zodzala kokha ndi ntchito zaumunthu. Anthu mwachisawawa amachita zinthu zoterozo. Mwachitsanzo, ichi chinachitika pamene anthu amitundu yambiri anadzathandiza minkhole ya chivomezi mu Soviet Armenia kumapeto kwa 1988.
14. Kupereka kwa Mulungu nsembe zolandirika kumagogomezera pa ntchito yotani?
14 Utumiki wopatulika umene timapereka kwa Yehova “ndi mantha ndi chinthenthe chaumulungu” umazikidwa pa chikondi cha mtundu wodzipereka nsembe chimene Yesu anasonyeza. (Ahebri 12:28, NW; Yohane 13:34; 15:13) Utumiki umenewu umagogomezera ntchito yathu yolalikira, popeza kuti kupyolera mwa Kristu monga Wansembe Wamkulu ‘timapereka kwa Mulungu nsembe za chitamando, chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.’ (Hoseya 14:2; Aroma 10:10-15; Ahebri 7:26) Ndithudi, ife ‘sitimaiwala kuchitira chokoma ndi kugawira ena’ kuphatikizapodi enanso, osakhala “a pa banja lachikhulupiro.” (Agalatiya 6:10) Makamaka pamene Akristu anzathu akumana ndi tsoka kapena pamene ali m’kusoŵa kapena kutsenderezedwa, timapereka chithandizo chachikondi mwakuthupi ndi mwauzimu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti timakondana. Timafunanso iwo kukhala okhoza kugwiririra ku kulengeza kwapoyera kwa chiyembekezo chawo popanda kulobodoka, “pakuti ndi nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.”—Ahebri 10:23-25; Yakobo 1:27.
Khalani Ogonjera
15. (a) Kodi ndimotani mmene mukalongosolera uphungu wa Ahebri 13:17? (b) Kodi nchifukwa ninji muyenera kusonyeza ulemu kwa otsogolera?
15 Kuti tipereke nsembe zolandirika, tiyenera kugwirizana mokwanira ndi gulu la Mulungu. Popanda kupeputsa nkhani ya ulamuliro, Paulo analemba kuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.” (Ahebri 13:17) Tiyenera kulemekeza akulu oikidwa omwe amatsogolera mu mpingo, kotero kuti iwo sadzafunikira kudzikakamiza ndi kutsendereza chifukwa cha kusakhala ogwirizana kwathu. Kulephera kwathu kugonjera kukatsimikizira kukhala kolemetsa kwa oyang’anira ndipo kukatulukapo kuvulazidwa kwathu kwauzimu. Mzimu wogwirizana umachipangitsa kukhala chopepuka kwa akulu kupereka chithandizo ndi kuthandiza umodzi ndi kupita patsogolo kwa ntchito yolalikira ya Ufumu.—Salmo 133:1-3.
16. Kodi nchifukwa ninji chiri choyenerera kugonjera kwa otsogolera pakati pathu?
16 Ndi choyenerera chotani nanga kuti tikhale ogonjera kwa otsogolera! Iwo amaphunzitsa pa misonkhano yathu ndi kutithandiza mu utumiki. Monga abusa, iwo amafunafuna ubwino wathu. (1 Petro 5:2, 3) Iwo amatithandiza kusungabe unansi wabwino ndi Mulungu ndi mpingo. (Machitidwe 20:28-30) Mwa kugonjera ku uyang’aniro wanzeru ndi wachikondi, timasonyeza ulemu kwa Woyang’anira Wamkulu, Yehova Mulungu, ndi Woyang’anira Wothandizira wake, Yesu Kristu.—1 Petro 2:25; Chibvumbulutso 1:1; 2:1–3:22.
Khalani Opemphera
17. Kodi ndi mapemphero otani amene Paulo anapempha, ndipo kodi nchifukwa ninji iye molondola anawapempha iwo?
17 Popeza kuti Paulo ndi oyanjana nawo anzake analekanitsidwa kwa Ahebri, mwinamwake chifukwa cha chizunzo, iye ananena kuti: “Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tiri nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nawo makhalidwe abwino. Ndipo ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.” (Ahebri 13:18, 19) Ngati Paulo anali munthu woipa wokhala ndi chikumbumtima cha liŵongo, kodi ndi kuyenera kotani komwe iye akanakhala nako kwa kufunsa Ahebri kupemphera kuti agwirizane nawo? (Miyambo 3:32; 1 Timoteo 4:1, 2) Ndithudi, iye anali mtumiki wowona mtima, amene m’chikumbumtima chabwino anachirimika kwa Ayudawo. (Machitidwe 20:17-27) Paulo analinso ndi chidaliro chakuti iye akakhala wokhoza kugwirizananso ndi Ahebriwo mwamsanga ngati iwo anapempherera chimenecho kuchitika.
18. Ngati tiyembekezera ena kutipempherera, kodi ndi mafunso otani amene tiyenera kudzifunsa?
18 Pempho la Paulo la mapemphero a Ahebri limasonyeza kuti chiri cholondola kwa Akristu kupemphererana, ngakhale mwa kutchula maina. (Yerekezerani ndi Aefeso 6:17-20.) Koma ngati tiyembekezera ena kutipempherera, kodi sitiyenera kukhala ngati mtumwiyo ndi kutsimikizira kuti ‘tiri nacho chikumbumtima chokoma ndipo tikukhala nawo makhalidwe abwino m’zinthu zonse’? Kodi ndinu wowona mtima m’zochita zanu? Ndipo kodi muli ndi chidaliro chofananacho m’pemphero chimene Paulo anali nacho?—1 Yohane 5:14, 15.
Mawu Othera ndi Kudandaulira
19. (a) Kodi nchiyani chimene chinali chikhumbo cha pemphero cha Paulo kwa Ahebri? (b) Kodi nchifukwa ninji pangano latsopano liri pangano losatha?
19 Pokhala atafunafuna mapemphero a Ahebri, Paulo analongosola chikhumbo cha pemphero, akumanena kuti: “Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndi Ambuye wathu Yesu, akuyeseni inu opanda chirema m’chinthu chirichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Kristu; kwa iyeyu ukhale ulemerero ku nthaŵi za nthaŵi. Amen.” (Ahebri 13:20, 21) Pokhala ndi dziko lapansi la mtendere m’chiyang’aniro, “Mulungu wa mtendere” anaukitsira Kristu ku moyo wosafa kumwamba, kumene Yesu anapereka kuyenera kwa mwazi wake wokhetsedwa womwe unalimbitsa pangano latsopano. (Yesaya 9:6, 7; Luka 22:20) Liri pangano losatha chifukwa chakuti awo a pa dziko lapansi akulandira madalitso osatha kuchokera ku utumiki wa ana aamuna auzimu a Mulungu a 144,000 omwe akulamulira ndi Yesu m’mwamba ndi omwe ali m’pangano latsopano. (Chibvumbulutso 14:1-4; 20:4-6) Chiri kupyolera mwa Kristu kuti Mulungu, kwa amene timapereka ulemerero, ‘akutikonzereketsa ife ndi chinthu chirichonse chabwino chofunikira kuchita m’chifuniro chake ndi kukhala wokondweretsa pamaso pake.’
20. Kodi ndimotani mmene mungaikire ndi kulongosola kudandaulira kwa Paulo kwa Akristu Achihebri?
20 Pokhala wosatsimikiza za mmene Ahebri akayankhira ku kalata yake, Paulo ananena kuti: “Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mawu achidandauliro; [kumvetsera kwa Mwana wa Mulungu, osati Ayuda], pakutinso ndalembera inu mwachidule [polingalira kulemera kwa za mkati mwake]. Zindikirani kuti mbale wathu Timoteo wamasulidwa [m’ndende]; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga, ndidzakuwonani inu.” Mwinamwake polemba ali ku Roma, mtumwiyo anayembekeza kuti iye limodzi ndi Timoteo akachezera Ahebri m’Yerusalemu. Kenaka Paulo ananena kuti: “Lankhulani atsogoleri anu onse [monga akulu ogwira ntchito zolimba], ndi oyera mtima onse [okhala ndi chiyembekezo cha kumwamba]. Akulankhulani iwo a ku Italiya. Chisomo [cha Mulungu] chikhale ndi inu nonse.”—Ahebri 13:22-25.
Kalata ya Phindu Lokhalitsa
21. Kodi kalata ya kwa Ahebri imatithandiza ife kumvetsetsa mfundo zazikulu zotani?
21 Mwinamwake kuposa bukhu lina lirilonse la Malemba Oyera, kalata ya kwa Ahebri imatithandiza kumvetsetsa kufunika kwa nsembe zoperekedwa pansi pa Chilamulo. Kalatayo ikusonyeza mowonekera bwino kuti nsembe ya Yesu Kristu iri yokha imene imapereka dipo lofunikira kaamba ka mtundu wa anthu wochimwa. Ndipo uthenga wodziŵika wopezeka m’kalatayo uli wakuti tiyenera kumvetsera kwa Mwana wa Mulungu.
22. Kodi nzifukwa zina zotani zimene tifunikira kukhala oyamikira kaamba ka kalata ya kwa Ahebri?
22 Ndiponso, monga momwe tawonera mu nkhani ziŵiri zapitazo, tiri ndi zifukwa zina za kukhalira oyamikira kaamba ka kalata yowuziridwa mwaumulungu ya kwa Ahebri. Imatithandiza ife kusalema mu utumiki wathu, ndipo imatidzaza ndi kulimba mtima, popeza timadziŵa kuti Yehova ndiye Mthandizi wathu. Kuwonjezerapo, imatilimbikitsa ife kugwiritsira ntchito milomo yathu ndi nzeru zathu zamaganizo zonse mopanda dyera m’kupereka utumiki wopatulika usana ndi usiku ndi kupereka nsembe zochokera mu mtima zimene zimakondweretsa Mulungu wathu woyenera kutamandidwa ndi wachikondi, Yehova.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene kalata ya kwa Ahebri imatithandizira kupeŵa ziphunzitso zonyenga?
◻ Kodi nsembe zokondweretsa Mulungu zimalunjikitsa pa ntchito yofunika yotani?
◻ Kodi ndani amene ali “otsogolera,” ndipo nchifukwa ninji tifunikira kukhala ogonjera kwa iwo?
◻ Kodi ndimotani mmene kalata ya kwa Ahebri imagogomezerera pemphero?
◻ Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti kalata ya kwa Akristu Achihebri iri ya phindu losatha?
[Zithunzi patsamba 23]
Nsembe zokondweretsa za kwa Mulungu zimaphatikizapo kupanga maulendo a ubusa ndi kumangirira Akristu anzathu ndi uphungu wachikondi