Yehova Ndiye Mthandizi Wanga
“Tikhale olimba mtima kwambiri ndi kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga; sindidzawopa. Kodi munthu angandichitenji?’”—AHEBRI 13:6, “NW.”
1, 2. (a) Kodi onse aŵiri wamasalmo ndi mtumwi Paulo analongosola chidaliro chotani mwa Yehova? (b) Kodi ndi mafunso otani omwe amabuka?
YEHOVA MULUNGU ali magwero osalephera a chithandizo. Wamasalmo anadziŵa chimenechi kuchokera m’zokumana nazo ndipo anakhoza kunena kuti: “Yehova ndi wanga; sindidzawopa; adzandichitanji munthu?” (Salmo 118:6) Maganizo ofananawo analongosoledwa ndi mtumwi Paulo pamene analemba kalata yake yowuziridwa mwaumulungu kwa Akristu Achihebri.
2 Mwachiwonekere akumagwira mawu a wamasalmoyo kuchokera mu Septuagint Yachigriki, Paulo anawuza atsatiri Achihebri kuti: “Tikhale olimba mtima kwambiri ndi kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga; sindidzawopa. Kodi munthu angandichitenji?’” (Ahebri 13:6, NW) Kodi nchifukwa ninji mtumwiyo analemba m’njira imeneyi? Ndipo kodi nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera m’mawu ozungulira lembali?
Ofunikira Thandizo la Yehova
3. (a) Kodi ndi pansi pa mikhalidwe yotani imene Yehova anatsimikizira kukhala Mthandizi wa Paulo? (b) Kodi nchifukwa ninji Akristu Achihebri anafunadi Yehova monga Mthandizi wawo?
3 Paulo anali mboni yodzipereka nsembe yemwe anali ndi chitsimikizo chakuti Yehova anali Mthandizi wake. Mulungu anathandiza mtumwiyo kuyang’anizana ndi zipsyinjo zambiri. Paulo anaponyedwa m’ndende, kumenyedwa, ndi kuponyedwa miyala. M’maulendo ake monga mtumiki Wachikristu, iye anakumana ndi kusweka chombo limodzinso ndi ngozi zina zambiri. Iye anali wozoloŵerana bwino lomwe ndi zolemetsa, m’madikiro, njala, ludzu, ngakhale umaliseche. “Pambali pa zakunjazo,” iye akutero, “pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, chilabadiro cha mipingo yonse.” (2 Akorinto 11:24-29) Paulo anali ndi mtundu umenewo wa kudera nkhaŵa kwa Akristu Achihebri. Masiku a Yerusalemu anali oŵerengeka, ndipo abale ndi alongo Achiyuda a mtumwiyo m’Yudeya akayang’anizana ndi ziyeso zazikulu za chikhulupiriro. (Danieli 9:24-27; Luka 21:5-24) Chotero ankafunikira kukhala ndi Yehova monga Mthandizi wawo.
4. Kodi ndi kulangiza kwakukulu kotani kumene kukuperekedwa kupyolera m’kalata ya kwa Ahebri?
4 Potsegula kalata yake kwa Akristu Achihebri, Paulo anasonyeza kuti thandizo laumulungu likakumanizidwa kokha ngati iwo anamvetsera kwa Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu. (Ahebri 1:1, 2) Mfundo imeneyi inakulitsidwa m’kalatayo. Mwachitsanzo, kuti achirikize uphungu umenewo, mtumwiyo anakumbutsa aŵerengi ake kuti Aisrayeli analangidwa chifukwa chomvera m’chipululu. Ndi mochepera chotani nanga mmene Akristu Achihebri akathaŵira chilango choterocho ngati iwo anakana chimene Mulungu ananena kwa iwo kupyolera mwa Yesu ndi kukhala a mpatuko omamatira ku Chilamulo cha Mose chomwe chinaikidwa pambali ndi nsembe ya Kristu!—Ahebri 12:24-27.
Chikondi Chaubale pa Ntchito
5. (a) Kodi ndi uphungu wina uti umene kalata ya kwa Ahebri imapereka? (b) Kodi nchiyani chimene Paulo ananena ponena za chikondi?
5 Kalata ya kwa Ahebri inapereka kwa oloŵa m’nyumba a Ufumu wakumwamba woyembekezeredwa uphungu wa mmene angatsatirire Chitsanzo chawo, Yesu Kristu, ‘kupereka utumiki wopatulika limodzi ndi mantha ndi chinthenthe chaumulungu,’ ndi kukhala ndi Yehova monga Mthandizi wawo. (Ahebri 12:1-4, 28, 29) Paulo anachonderera akhulupirira anzake kukumana mokhazikika ndi ‘kufulumizana wina ndi mnzake ku chikondano ndi ntchito zabwino.’ (Ahebri 10:24, 25) Tsopano iye analangiza kuti: “Chikondi cha pa abale chikhalebe.”—Ahebri 13:1.
6. Kodi ndi m’lingaliro lotani limene Yesu anaperekera kwa atsatiri ake “lamulo latsopano” lonena za chikondi?
6 Yesu anafuna chikondi choterocho cha atsatiri ake, popeza iye ananena kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35) Ili linali “lamulo latsopano” m’chakuti linaitanira zoposa zimene Chilamulo cha Mose chinachita, chomwe chinati: “Uzikonda mnansi wako [kapena bwenzi] monga udzikonda wekha.” (Levitiko 19:18) “Lamulo latsopano” linachita zoposa pa kufuna kuti munthu akonde mnansi wake monga mmene adzikondera yekha. Ilo linaitanira chikondi chopereka nsembe ku mlingo wa kupereka moyo wanu kaamba ka winayo. Moyo wa Yesu ndi imfa inachitira chitsanzo mtundu umenewo wa chikondi. Tertullian analunjikitsa ku chizindikiro chozindikiritsa chimenechi pamene anagwira ndemanga za anthu a kudziko zonena za Akristu ndi kunena kuti: “‘Tawonani,’ iwo akutero, ‘mmene amakonderana . . . ndi mmene aliri okonzekera kuferana.’”—Apology, mutu XXXIX, 7.
7. Kodi ndimotani mmene chikondi chaubale chinali chowonekera pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E.?
7 Chikondi chaubale chinali chowonekera pakati pa ophunzira a Yesu pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E. Ndi cholinga chakuti akhulupiriri obatizidwa chatsopano kuchokera kumalekezero a dziko atalikitse kukhala kwawo m’Yerusalemu ndi kuphunzira zowonjezereka ponena za mphatso ya Mulungu ya chipulumutso kupyolera mwa Kristu, “onse akukhulupira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana. Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chawo, anazigulitsa monga momwe yense anasoŵera.”—Machitidwe 2:43-47; 4:32-37.
8. Kodi ndi chitsimikiziro chotani chimene chiripo chakuti chikondi chaubale chiripo pakati pa Mboni za Yehova lerolino?
8 Chikondi chaubale choterocho chiripo pakati pa Mboni za Yehova m’nthaŵi yathu. Mwachitsanzo, pambuyo pa Nkhondo ya Dziko ya II, chikondi choterocho chinafulumiza anthu a Mulungu kuchita ndawala ya ntchito ya zopereka zaufulu ya zaka ziŵiri ndi theka. Mboni mu Canada, Sweden, Switzerland, United States, ndi maiko ena zinasonkha zovala ndi ndalama zogulira zakudya kaamba ka akhulupiriri anzawo m’maiko okanthidwa ndi nkhondo a Austria, Belgium, Bulgaria, China, Czechoslovakia, Denmark, England, Finland, France, Germany, Greece, Hungary, Italy, Netherlands, Norway, Philippines, Poland, ndi Romania. Ichi chiri kokha chitsanzo, popeza kuti atumiki a Mulungu posachedwapa kwenikweni asonyeza chikondi choterocho kwa minkhole Yachikristu ya zivomezi mu Peru ndi mu Mexico, mphepo ya mkuntho mu Jamaica, ndi ngozi zofananazo kwinakwake. M’njira imeneyi ndi zina zambiri, anthu a Yehova ‘alola chikondi chawo chaubale kupitirizabe.’
Khalani Ochereza
9. (a) Kodi ndi mkhalidwe waumulungu wotani umene watchulidwa pa Ahebri 13:2? (b) Kodi ndimotani mmene ena mosadziŵa ‘anacherezera angelo’?
9 Paulo chotsatira anatchula mkhalidwe wina wowonetsedwa ndi awo otsatira Kristu, ‘kupereka utumiki wopatulika limodzi ndi mantha ndi chinthenthe chaumulungu,’ ndi omwe ali ndi Yehova monga Mthandizi wawo. Iye anachonderera kuti: “Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziŵa.” (Ahebri 13:2) Kodi ndani omwe mosachidziŵa “anachereza angelo”? Chabwino, kholo Abrahamu analandira angelo atatu. (Genesis 18:1-22) Aŵiri a iwo anapita, ndipo mphwake Loti anaitana alendo ameneŵa m’nyumba mwake mu Sodomu. Komabe, asanagone, nyumba ya Loti inazingidwa ndi gulu, “anyamata ndi okalamba.” Iwo anakakamiza kuti Loti atulutse alendo ake kaamba ka zifuno zachisembwere, koma iye anakana kwa mtu wa galu. Ngakhale kuti Loti sanachidziŵe icho poyamba, iye anali atachereza angelo, omwe kenaka anamthandiza iye ndi ana ake aakazi kuthaŵa imfa pamene ‘Yehova anavumbitsa mvula ya moto wa sulfure kuchokera kumwamba kudzera pa Sodomu ndi Gomora.’—Genesis 19:1-26.
10. Kodi ndi madalitso otani amene Akristu ochereza amasangalala nawo?
10 Akristu ochereza amasangalala ndi madalitso ambiri. Iwo amamva zokumana nazo zolemeretsa zikusimbidwa ndi alendo awo ndi kupindula ndi kuyanjana kwawo kwauzimu kodzetsa mphotho. Gayo anayamikiridwa chifukwa cholandira akhulupiriri anzake mochereza, “ndi kwa alendo,” mongadi mmene anthu a Yehova lerolino amacherezera oyang’anira oyendayenda. (3 Yohane 1, 5-8) Kukhala wochereza kuli ziyeneretso za kuikidwa monga mkulu. (1 Timoteo 3:2; Tito 1:7, 8) Chirinso chodziŵika kuti Yesu analonjeza madalitso Aufumu kwa anthu onga nkhosa omwe anachita zabwino mochereza kwa “abale” ake odzozedwa.—Mateyu 25:34-40.
Kumbukirani Ozunzidwa
11. Kodi nchifukwa ninji uphungu wa pa Ahebri 13:3 unali woyenerera?
11 Awo ofuna kukhala ndi thandizo la Yehova ndi ‘kupereka utumiki wopatulika kwa iye limodzi ndi mantha ndi chinthenthe chaumulungu’ sayenera kuiwala akhulupiriri anzawo amene akuvutika. Paulo anamvetsetsa kuvutika kopiriridwa ndi Akristu ochitidwa moipa. Nthaŵi zina poyambapo, ophunzira anali atamwazikana chifukwa cha chizunzo, ndipo wogwira ntchito mnzake Timoteo anali atangomasulidwa kuchoka m’ndende. (Ahebri 13:23; Machitidwe 11:19-21) Amishonale Achikristu ankayendayendanso kupanga mipingo yatsopano kapena kumangirira mwauzimu yomwe inalipo. Popeza kuti ambiri a abale ndi alongo omwe ankayendayenda panthaŵiyo anali Akunja, Akristu ena Achihebri angakhale anali osadera nkhaŵa mokwanira ponena za iwo. Kenaka, wa panthaŵi yake, unali uphungu wakuti: “Kumbukirani amsinga, monga amsinga anzawo; ochitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m’thupi.”—Ahebri 13:3.
12. Kodi ndimotani mmene tingagwiritsire ntchito uphungu wa kusunga m’maganizo akhulupiriri anzathu ochitidwa moipa?
12 Ahebri anali “anamva chifundo ndi am’ndende” koma sanafunikire kuiwala alambiri anzawo okhulupirika oterowo, kaya ngati iwo anali Ayuda kapena Akunja. (Ahebri 10:34) Koma bwanji ponena za ife? Kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuti timaganizira za Akristu ochitidwa moipa? M’nkhani zina chingakhale choyenerera kwa ife kuchitira apilu ku maulamuliro a boma mwa kalata m’kuyesayesa kuthandiza akhulupiriri anzathu oikidwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo m’maiko mmene ntchito yolalikira Ufumu yaletsedwa. Makamaka tifunikiranso kuwakumbukira iwo m’mapemphero athu, ngakhale kutchula ena ndi maina, ngati nkotheka. Chizunzo chawo chimatiyambukira ife mwakuya, ndipo Yehova amamvetsera mapembedzero athu ochokera mu mtima m’malo mwawo. (Salmo 65:2; Aefeso 6:17-20) Pamene kuli kwakuti sitiri mu nsinga zandende zofananazo, chiri monga ngati kuti tiri nawo ndipo ndife okhoza kupereka thandizo ndi chilimbikitso. Akristu obadwa ndi mzimu motsimikizirika amamva chifundo ndi odzozedwa ochitiridwa moipa. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 12:19-26.) Awa ali ndi kudera nkhaŵa kofananako kwa mabwenzi awo ozunzidwa okhala ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi, omwe amavutikanso ndi kuchitiridwa moipa kwa mitundu yambiri pamanja a ozunza. Chifundo choterocho chiri choyenerera, popeza kuti tonsefe tidakali m’thupi laumunthu ndipo tiri okhoza kuvutika ndi kuzunzidwa monga alambiri a Yehova.—1 Petro 5:6-11.
Ukwati Uchitidwe Ulemu
13. Monga nsonga, kodi nchiyani chimene Paulo ananena pa Ahebri 13:4?
13 Kutsatira chitsanzo cha Kristu ndi ‘kupereka utumiki wopatulika kwa Yehova limodzi ndi mantha ndi chinthenthe chaumulungu’ kuyenera kuyambukira kudera nkhaŵa kwathu ena m’njira zambiri. Pokhala atanena kuti “monga ngati inunso adatero nanu m’thupi,” Paulo anatchula unansi wokhala ndi mbali yakuthupi, yomwe inapereka mwaŵi wa kusonyeza kusamalira ena moyenera. (Ahebri 13:3) Iye anapereka kwa Akristu Achihebri chilangizo ichi: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” (Ahebri 13:4) Ndi woyenerera chotani nanga uphungu umenewu, popeza kuti chisembwere cha kugonana chinali chofala mu Ulamuliro wa Roma! Akristu amakono afunikiranso kulabadira mawu ameneŵa chifukwa cha miyezo yomazimiririka ya dziko ndi chenicheni chakuti chaka chirichonse zikwizikwi zimachotsedwa mu mpingo chifukwa cha chisembwere cha kugonana.
14. Kodi nchifukwa ninji munganene kuti ukwati uli wolemekezeka?
14 Pakati pa awo omwe sanasunge ukwati mu mkhalidwe wabwino anali Aesene a m’nthaŵi ya Paulo. Iwo kaŵirikaŵiri anali mbeta, ofanana ndi ena okhala m’magawo achipembedzo lerolino omwe molakwika amalingalira umbeta kukhala wopatulikitsa kupambana ukwati. Komabe, ndi chimene Paulo anawuza Akristu Achihebri, iye anasonyeza momvekera bwino kuti ukwati uli wolemekezeka. Kawonedwe kapamwamba ka iwo kanali kowonekera pamene Naomi analongosola chikhumbo chimenechi kwa apongozi ake oferedwa, Rute ndi Olipa: “Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m’nyumba ya mwamuna wake.” (Rute 1:9) Kwinakwake, Paulo iyemwini anasonyeza kuti ‘m’nthaŵi yotsiriza ena adzataya chikhulupiriro, akuletsa ukwati.’—1 Timoteo 4:1-5.
15. Kodi ndani omwe anatchulidwa kukhala adama ndi achigololo pa Ahebri 13:4, ndipo kodi ndimotani mmene Mulungu akawaweruzira iwo?
15 Ahebri omwe pa nthaŵi imodzi anali pansi pa Chilamulo koma adaikidwa m’pangano latsopano anadziŵa lamulo lakuti: “Usachite chigololo.” (Eksodo 20:14) Koma iwo anali m’dziko lachisembwere ndipo anafunikira chenjezo lakuti: “Pogona pakhale posadetsedwa, pakuti adama ndi achigololo Mulungu adzawaweruza.” Pakati pa adama pali anthu osakwatira omwe amadziloŵetsa mu unansi wa kugonana. Achigololo ali makamaka anthu okwatira omwe amayanjana ndi aja omwe sali anzawo a mu ukwati, akumadetsa kama lawo laukwati. Popeza kuti ochimwa osalapa adama ndi achigololo amayenera chiweruzo choipa cha Mulungu, iwo sadzaloledwa konse kuloŵa m’Yerusalemu Watsopano wakumwamba kapena kusangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi pansi pa kulamulira kwa Ufumu. (Chibvumbulutso 21:1, 2, 8; 1 Akorinto 6:9, 10) Chenjezo limeneli la kusadetsa kama la ukwati liyeneranso kupangitsa Akristu okwatira kupeŵa mkhalidwe wa kugonana wodetsa anzawo a mu ukwati, ngakhale kuti palibe chirichonse chodetsedwa ponena za kuyanjana kwakuthupi koyenera mkati mwa ukwati.—Onani Nsanja ya Olonda, September 1, 1983, masamba 28-32.
Okwaniritsidwa ndi Zomwe Muli Nazo
16, 17. Kodi nchiyani chimene chinanenedwa pa Ahebri 13:5, ndipo kodi nchifukwa ninji Ahebri anafunikira uphunguwo?
16 Tidzakwaniritsidwa ngati titsanzira Chitsanzo chathu ndi ‘kupereka utumiki wopatulika limodzi ndi mantha ndi chinthenthe chaumulungu,’ achidaliro kuti Yehova ali Mthandizi wathu. Kudziloŵetsamo mwakuya m’zolondola zakuthupi kungakhale chiyeso. Koma Akristu sayenera kugonjera ku icho. Ahebri anawuzidwa kuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Kodi nchifukwa ninji Ahebri anafunikira uphungu umenewu?
17 Mwinamwake Ahebri anali odera nkhaŵa mopambanitsa ponena za chuma chifukwa chakuti iwo anakumbukira za “njala yaikulu” m’kulamulira kwa Klaudiyo Kaisara (41-54 C.E.). Njala imeneyo inali yoipa kwenikweni kotero kuti Akristu kwinakwake anatumiza zothandiza kwa abale awo m’Yudeya. (Machitidwe 11:28, 29) Mogwirizana ndi kunena kwa katswiri wa mbiri yakale Wachiyuda Josephus, njalayo inakhalapo kwa zaka zitatu kapena kuposerapo, ikumapangitsa kusauka kotsendereza m’Yudeya ndi Yerusalemu.—Antiquities of the Jews, XX, 2, 5; 5, 2.
18. Kodi uphungu wa pa Ahebri 13:5 umapereka phunziro lotani kwa ife?
18 Kodi pano pali phunziro kwa ife? Inde, popeza kuti mosasamala kanthu za mmene tingakhalire osauka, sitiyenera kukonda chuma kapena kukhala odera nkhaŵa mopambanitsa ponena za icho. M’malo mokhala odera nkhaŵa ponena za chisungiko chakuthupi, mwinamwake ngakhale kukhala osirira, tiyenera kukhala ‘okwaniritsidwa ndi zimene tiri nazo.’ Yesu ananena kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake [cha Mulungu], ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:25-34) Iye anasonyezanso kuti tiyenera kusumika pa kukhala “wokhala nacho chuma cha kwa Mulungu” chifukwa chakuti ‘miyoyo yathu simachokera m’zinthu zomwe tiri nazo.’ (Luka 12:13-21) Ngati chikondi cha chuma chiwopsyeza uzimu wathu, pamenepo, lolani kuti tilabadire uphungu wa Paulo kwa Ahebri ndiponso kukumbukira kuti ‘kudzipereka kwaumulungu limodzi ndi kukwaniritsidwa’ kuli ‘kopindulitsa kwakukulu.’—1 Timoteo 6:6-8.
Khulupirirani Yehova
19. Kodi ndi chitsimikiziro chotani chimene Mulungu anampatsa Yoswa, ndipo kodi ndimotani mmene ichi chiyenera kutiyambukirira?
19 Monga atsatiri a Yesu omwe akufunafuna ‘kupereka utumiki wopatulika limodzi ndi mantha ndi chinthenthe chaumulungu,’ tiyenera kuika chikhulupiriro chathu osati m’chuma koma mwa Atate wathu wakumwamba, yemwe thandizo lake liri lofunika. Mosasamala kanthu za mavuto aliwonse omwe timayang’anizana nawo, tiyenera kukumbukira chitsimikiziro chake chakuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Pano Paulo anagwirizanitsa mawu a Mulungu kwa Yoswa: “Sindidzakusoŵa, sindidzakusiya.” (Yoswa 1:5; yerekezerani ndi Deuteronomo 31:6, 8.) Yehova sanasiye konse Yoswa, ndipo Iye sadzatisiya ngati tikhulupirira mwa Iye.
20. (a) Kodi ndi liti lomwe liri lemba lachaka cha 1990? (b) Popanda mantha, kodi nchiyani chimene tiyenera kupitirizabe kuchita?
20 Thandizo losalephera la Mulungu lidzagogomezeredwa pakati pa Mboni za Yehova m’miyezi yomwe iri kutsogoloko, popeza kuti lemba lawo lachaka cha 1990 limaŵerenga kuti: “Tikhale olimba mtima kwambiri ndi kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga.’” Mawu ameneŵa amapezeka pa Ahebri 13:6, NW, pamene Paulo anagwira mawu wamasalmo ndi kuwuza Ahebri kuti: “Kuti tikakhale olimba mtima kwambiri ndi kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga; sindidzawopa. Kodi munthu angandichitenji?’” (Salmo 118:6) Ngakhale kuti timazunzidwa, sitimawopa, pakuti anthu sangachite chirichonse choposa chimene Mulungu amalola. (Salmo 27:1) Ngakhale titafa monga asungiriri aumphumphu, tiri ndi chiyembekezo cha chiukiriro. (Machitidwe 24:15) Chotero lolani kuti tipitirize kutsanzira Chitsanzo chathu ‘m’kupereka utumiki wopatulika limodzi ndi mantha ndi chinthenthe chaumulungu,’ achidaliro kuti Yehova ndiye Mthandizi wathu.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu Achihebri anafunadi thandizo la Yehova?
◻ Kodi ndimotani mmene anthu a Yehova ‘alolera chikondi chawo chaubale kupitirizabe’?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ochereza?
◻ Kodi nchiyani chimene tingachite kusonyeza kuti timakumbukira akhulupiriri anzathu ochitidwa moipa?
◻ Kodi nchifukwa ninji ukwati uyenera kulemekezedwa?