Gwiritsitsani Chikhulupiriro Chanu Mosasamala Kanthu za Ziyeso!
“Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, mmene mukugwa m’mayesero a mitundumitundu.”—YAKOBO 1:2.
1. Kodi anthu a Yehova amamtumikira mokhulupirika ndi “mokondwera mtima” mosasamala kanthu za chiyani?
ANTHU a Yehova akutumikira monga Mboni zake mokhulupirira iye ndi “mokondwera mtima.” (Deuteronomo 28:47; Yesaya 43:10) Amachita zimenezi ngakhale kuti amavutika ndi ziyeso zambiri. Mosasamala kanthu za mavuto awo, iwo amapeza mpumulo m’mawu akuti: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, mmene mukugwa m’mayesero a mitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.”—Yakobo 1:2, 3.
2. Kodi tikudziŵanji ponena za wolemba kalata ya Yakobo?
2 Mawu amenewo analembedwa cha mu 62 C.E. ndi wophunzira Yakobo, mbale wa Yesu Kristu. (Marko 6:3) Yakobo anali mkulu mumpingo wa ku Yerusalemu. Kwenikweni, iyeyo, Kefa (Petro), ndi Yohane “anayesedwa mizati”—ochirikiza mpingo amphamvu ndi olimba. (Agalatiya 2:9) Pamene nkhani ya mdulidwe inafika kwa “atumwi ndi akulu” cha mu 49 C.E., Yakobo anapereka lingaliro labwino lozikidwa pa Malemba limene linagwiritsiridwa ntchito ndi bungwe lolamulira limenelo la m’zaka za zana loyamba.—Machitidwe 15:6-29.
3. Kodi Akristu a m’zaka za zana loyamba anali pamavuto ena otani, ndipo kodi tingapindule kwambiri motani ndi kalata ya Yakobo?
3 Pokhala mbusa wauzimu wosamala, Yakobo ‘anadziŵa kuti zoŵeta zake zili bwanji.’ (Miyambo 27:23) Anadziŵa kuti Akristu nthaŵi imeneyo anali paziyeso zazikulu. Ena anafunikira kusintha maganizo awo, popeza anali kukondera achuma. Kwa enanso angapo, kulambira kunali mwambo wamba. Ena anali kuvulaza anzawo ndi lilime lawo losalamulirika. Mzimu wa dziko unali kuwononga zinthu, ndipo ambiri sanali oleza mtima kapena olimbikira kupemphera. Kwenikweni, Akristu ena anadwala matenda auzimu. Kalata ya Yakobo ikulongosola mavuto ameneŵa m’njira yolimbikitsa, ndipo uphungu wake ngwothandiza lerolino monga momwe unalili m’zaka za zana loyamba C.E. Tidzapindula kwambiri ngati tipenda kalata imeneyi monga kuti analembera ife.a
Pamene Tikumana ndi Ziyeso
4. Kodi ziyeso tiyenera kuziona motani?
4 Yakobo akutisonyeza mmene tiyenera kuonera ziyeso. (Yakobo 1:1-4) Popanda kutchula ubale wake wakuthupi ndi Mwana wa Mulungu, iye modzichepetsa akudzitcha “kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Kristu.” Yakobo akulembera “mafuko khumi ndi aŵiri” a Israyeli wauzimu ‘obalalika,’ makamaka chifukwa cha chizunzo. (Machitidwe 8:1; 11:19; Agalatiya 6:16; 1 Petro 1:1) Monga Akristu, ifenso timazunzidwa, ndipo ‘timagwa m’mayesero a mitundumitundu.’ Koma tikakumbukira kuti ziyeso zomwe tapirira zimalimbitsa chikhulupiriro chathu, ‘tidzachiyesa chimwemwe chokha’ pamene zitigwera. Tikakhalabe okhulupirika kwa Mulungu paziyeso, zimenezi zidzatidzetsera chimwemwe chokhalitsa.
5. Kodi ziyeso zathu zingaphatikizepo chiyani, ndipo chimachitika nchiyani titazipirira mwachipambano?
5 Ziyeso zathu zimaphatikizapo nsautso zimene zingagwere aliyense. Mwachitsanzo, tingazunzike ndi matenda. Mulungu tsopano sakuchiritsa anthu mozizwitsa, koma amayankha mapemphero athu opempha nzeru ndi nyonga yofunikira kuti tipirire matenda. (Salmo 41:1-3) Timavutikanso potizunza chifukwa cha chilungamo monga Mboni za Yehova. (2 Timoteo 3:12; 1 Petro 3:14) Pamene tapirira ziyeso zimenezi mwachipambano, chikhulupiriro chathu chimakhala chotsimikizika, ndipo chimakhala chija ‘choyesedwa.’ Ndiponso chikhulupiriro chathu chikapambana, zimenezi ‘zimachita chipiriro.’ Chikhulupiriro cholimbitsidwa ndi ziyeso chidzatithandiza kupirira ziyeso zamtsogolo.
6. Kodi ‘chipiriro chingamalizitse ntchito yake’ motani, ndipo tingachite zinthu zotani zotithandiza pamene tikuyesedwa?
6 “Koma,” Yakobo akutero, “chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro [“chimalizitse ntchito yake,” NW].” Tikalola chiyeso kufika polekezera pake popanda kuyesa kuchidukiza mwamsanga mwa njira zosakhala za m’malemba, chipiriro chidzachita “ntchito” imene idzatipanga kukhala Akristu enieni, osasoŵa chikhulupiriro. Komabe, ngati chiyeso chivumbula chofooka chinachake, tiyenera kupempha thandizo la Yehova kuti tichigonjetse. Bwanji ngati chiyesocho nchakuti muchite chisembwere? Tiyeni tilipempherere vuto limenelo ndi kuchitapo kanthu mogwirizana ndi mapemphero athu. Mwina tingafunikire kusintha malo athu a ntchito kapena kuchitapo kanthu kena kuti tikhalebe okhulupirika kwa Mulungu.—Genesis 39:7-9; 1 Akorinto 10:13.
Kufunafuna Nzeru
7. Kodi tingathandizidwe motani kupirira ziyeso?
7 Yakobo akutiuza zimene tingachite ngati tasoŵa chochita pamene tikuyesedwa. (Yakobo 1:5-8) Yehova sadzatitonza ngati tasoŵa nzeru ndipo tikuzipempherera mwachikhulupiriro. Adzatithandiza kuti tione chiyeso moyenerera ndiponso kuti tipirire. Okhulupirira anzathu angatitchulire Malemba kapena tingawaphunzire paphunziro la Baibulo. Zochitika zoyendetsedwa ndi Mulungu zingatichititse kuona zimene tiyenera kuchita. Mzimu wa Mulungu ungatitsogoze. (Luka 11:13) Kuti tipeze mapindu ameneŵa, ndithudi tiyenera kumamatira zedi kwa Mulungu ndi anthu ake.—Miyambo 18:1.
8. Kodi nchifukwa ninji wokayika sadzalandira kanthu kwa Yehova?
8 Yehova amatipatsa nzeru kuti tipirire ziyeso ngati ‘tipempha ndi chikhulupiriro, osakayika konse.’ Wokayika “afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuŵinduka nayo” mosadziŵa chimene chidzachitika. Ngati ndife osakhazikika motero mwauzimu, ‘tisayese kuti tidzalandira kanthu kwa Ambuye.’ Tisakhale a “mitima iŵiri” ndi ‘osinkhasinkha [“osatsimikiza,” NW]’ popemphera kapena pazinthu zinanso. M’malo mwake, tiyeni tikhulupirire Yehova, Wopereka nzeru.—Miyambo 3:5, 6.
Achuma ndi Aumphaŵi Ayenera Kukondwera
9. Kodi nchifukwa ninji tili ndi chifukwa chokhalira okondwera monga alambiri a Yehova?
9 Ngakhale kuti umphaŵi ndiwo china mwa ziyeso zathu, tiyeni tikumbukire kuti Akristu achuma ndi aumphaŵi omwe ayenera kukondwera. (Yakobo 1:9-11, NW) Asanakhale otsatira a Yesu, odzozedwa ambiri anali aumphaŵi ndipo dziko linali kuwanyoza. (1 Akorinto 1:26) Koma anakondwera chifukwa cha “kukwezedwa” kwawo kukhala oloŵa Ufumu. (Aroma 8:16, 17) Mosiyana ndi zimenezo, anthu achuma amene kale anali olemekezeka ‘amachepetsedwa’ monga otsatira a Kristu chifukwa cha kunyozedwa ndi dziko. (Yohane 7:47-52; 12:42, 43) Komabe, pokhala atumiki a Yehova, tonsefe tingakondwere chifukwa chakuti chuma chadziko ndi malo apamwamba sizili kanthu poziyerekezera ndi chuma chauzimu chimene tili nacho. Ndipo ndife oyamikira chotani nanga kuti pakati pathu sitimanyada chifukwa cha chuma chathu chakuthupi!—Miyambo 10:22; Machitidwe 10:34, 35.
10. Kodi Mkristu ayenera kuchiona motani chuma chakuthupi?
10 Yakobo akutithandiza kuona kuti moyo wathu sumadalira pa chuma kapena chipambano chakudziko. Monga momwe kukongola kwa duwa sikungalitetezere kuti lisafe m’dzuŵa ‘lotentha,’ momwemonso chuma cha munthu wachuma sichingawonjezere moyo wake. (Salmo 49:6-9; Mateyu 6:27) Akhoza kufa akulondola “mayendedwe ake,” mwinamwake ali pamalonda ake. Choncho, chofunika kwambiri ndicho kukhala ndi “chuma cha kwa Mulungu” ndi kuchita zonse zomwe tingathe pochirikiza zinthu za Ufumu.—Luka 12:13-21; Mateyu 6:33; 1 Timoteo 6:17-19.
Achimwemwe Ali Iwo Akupirira Chiyeso
11. Kodi amene amagwiritsitsa chikhulupiriro chawo pokumana ndi ziyeso ali ndi chiyembekezo chotani?
11 Kaya tikhale achuma kapena aumphaŵi, tingakhale achimwemwe kokha ngati tipirira ziyeso zathu. (Yakobo 1:12-15) Ngati tipirira ziyeso ndi chikhulupiriro chathu chosagwedera, tingatchedwe kuti achimwemwe, popeza kuchita zimene zili zoyenera pamaso pa Mulungu kumadzetsa chimwemwe. Mwa kusataya chikhulupiriro chawo mpaka imfa, Akristu obadwa ndi mzimu amalandira “korona wa moyo,” moyo wosakhoza kufa kumwamba. (Chivumbulutso 2:10; 1 Akorinto 15:50) Ngati tili ndi chiyembekezo cha padziko lapansi ndipo tikhalabe ndi chikhulupiriro mwa Mulungu, tingayembekezere moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. (Luka 23:43; Aroma 6:23) Yehova ndi wabwino chotani nanga kwa onse omkhulupirira!
12. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kunena kuti: “Ndiyesedwa ndi Mulungu” pamene tili m’nsautso?
12 Kodi nzotheka kuti Yehova iye mwini angatiyese ndi nsautso? Ayi, tisanene kuti: “Ndiyesedwa ndi Mulungu.” Yehova samafuna kutinyengerera kuti tichimwe koma ngwotsimikiza kuti adzatithandiza ndi kutipatsa nyonga yofunikira kuti tipirire ziyeso ngati tikhalabe olimba m’chikhulupiriro. (Afilipi 4:13) Mulungu ngwoyera, choncho samatiika m’mikhalidwe imene ingafooketse mphamvu yathu yokana kuchita choipa. Ngati tadziloŵetsa mumkhalidwe umene suli woyera ndipo tachimwa, sitiyenera kumuimba mlandu, “pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” Ngakhale kuti Yehova angalole chiyeso kutilanga kuti tipindule, iye samatiyesa ndi cholinga choipa. (Ahebri 12:7-11) Satana angatiyese kuti tilakwe, koma Mulungu angatipulumutse kwa woipayo.—Mateyu 6:13.
13. Kodi chingachitike nchiyani ngati sitiletsa chikhumbo choipa?
13 Tiyenera kulimbikira kupemphera chifukwa chakuti mkhalidwe winawake ungatichititse kukhala ndi chikhumbo choipa chimene chingatiloŵetse mu uchimo. Yakobo akuti: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga.” Sitingaimbe mlandu Mulungu patchimo lathu ngati talola mtima wathu kusinkhasinkha pa chikhumbo chauchimo. Ngati sitiletsa chikhumbo choipa, ‘icho chimaima,’ chimakula mumtima, ndipo “chibala uchimo.” Uchimo utakula msinkhu, “ubala imfa.” Ndithudi, tiyenera kutetezera mitima yathu ndi kuletsa maganizo auchimo. (Miyambo 4:23) Kaini anachenjezedwa kuti uchimo unali pafupi kumgonjetsa, koma sanautsekereze. (Genesis 4:4-8) Choncho, nanga bwanji ngati tayamba kulondola njira yosakhala ya malemba? Ndithudi tiyenera kuyamikira kwambiri ngati akulu achikristu ayesa kutiwongolera kuti tisachimwire Mulungu.—Agalatiya 6:1.
Mulungu—Kumene Zinthu Zabwino Zimachokera
14. Kodi tinganene kuti mphatso za Mulungu zili ‘zangwiro’ m’lingaliro lotani?
14 Tiyenera kukumbukira kuti Yehova ndiye Wogaŵira zinthu zabwino, osati ziyeso. (Yakobo 1:16-18) Yakobo akutcha okhulupirira anzake kuti “abale anga” nasonyeza kuti Mulungu ndiye Wopereka “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” Mphatso za Yehova zauzimu ndi zakuthupi zili ‘zangwiro,’ kapena kuti zokwanira, zosapereŵera kanthu. Izo zimachokera “kumwamba,” kumalo okhala a Mulungu. (1 Mafumu 8:39) Yehova ndiye “Atate wa mauniko”—dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi. Iye amatipatsanso kuunika kwauzimu ndi choonadi. (Salmo 43:3; Yeremiya 31:35; 2 Akorinto 4:6) Mosiyana ndi dzuŵa limene limachititsa mthunzi kusuntha pamene lisuntha ndipo limafika pachimake masana okha, Mulungu nthaŵi zonse amapereka zabwino zochuluka. Ndithudi adzatikonzekeretsa kuti tilimbane ndi ziyeso ngati timagwiritsira ntchito mokwanira zogaŵira zake zauzimu zoperekedwa kudzera mwa Mawu ake ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mateyu 24:45.
15. Kodi imodzi mwa mphatso za Yehova zabwino koposa nchiyani?
15 Kodi nchiyani chimene chili imodzi mwa mphatso zabwino koposa za Mulungu? Kubala ana auzimu mwa mzimu woyera, wogwira ntchito mogwirizana ndi uthenga wabwino, kapena kuti “mawu a choonadi.” Awo amene amabadwanso mwauzimu ndiwo “zipatso [“zina,” NW] zoundukula,” zosankhidwa mwa anthu kukakhala “ufumu ndi ansembe” a kumwamba. (Chivumbulutso 5:10; Aefeso 1:13, 14) Yakobo ayenera kuti anali kuganizira za barele woyamba kucha woperekedwa nsembe pa Nisani 16, tsiku limene Yesu anaukitsidwa, ndiponso za kupereka nsembe mikate iŵiri ya tirigu patsiku la Pentekoste, pamene mzimu woyera unatsanuliridwa. (Levitiko 23:4-11, 15-17) Pamenepo, Yesu anali zipatso zoundukula ndipo oloŵa nyumba anzake “zipatso zina zoundukula.” Nanga bwanji ngati tili ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi? Eya, kuchikumbukira kudzatithandiza kugwiritsitsa chikhulupiriro chathu mwa Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino,” amene walinganiza kuti tikakhale ndi moyo wosatha padziko lapansi mu ulamuliro wa Ufumu.
Khalani ‘Wakuchita Mawu’
16. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ‘otchera khutu koma odekha polankhula ndi pakupsa mtima’?
16 Kaya panopo chikhulupiriro chathu chikuyesedwa kapena sichikuyesedwa, tiyenera kukhala “akuchita mawu.” (Yakobo 1:19-25) Tiyenera kukhala ‘otchera khutu’ ku mawu a Mulungu, kuwatsatira molabadira. (Yohane 8:47) Komabe, tiyeni tikhale ‘odekha polankhula,’ kukhala osamala kwambiri ndi mawu athu. (Miyambo 15:28; 16:23) Mwina Yakobo akutilimbikitsa kusafulumira kunena kuti ziyeso zathu zachokera kwa Mulungu. Talangizidwanso kuti tikhale ‘odekha pakupsa mtima. Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.’ Ngati takwiya ndi zimene wina wanena, tiyeni ‘tiugwire mtima’ kuti tisayankhe monyoza. (Aefeso 4:26, 27) Kupsa mtima kumene kungatiloŵetse m’mavuto ndi kuika ena pachiyeso sikungatulutse zimene chikhulupiriro mwa Mulungu wathu wolungama chimafuna kwa ife. Ndiponso, ngati ‘tipambana kumvetsa,’ tidzakhala ‘osakwiya msanga,’ ndipo abale ndi alongo athu adzayandikana nafe.—Miyambo 14:29.
17. Kodi kuchotsa zoipa mumtima ndi m’maganizo kumatithandiza motani?
17 Ndithudi tifunikira ‘kuvula chinyanso chonse’—chilichonse chimene chimanyansa Mulungu ndiponso chokwiyitsa. Ndiponso, tiyenera ‘kuvula chisefukiro cha choipa.’ Tonsefe tiyenera kusiya chodetsa chilichonse cha thupi ndi mzimu m’moyo wathu. (2 Akorinto 7:1; 1 Petro 1:14-16; 1 Yohane 1:9) Kuchotsa zoipa mumtima ndi m’maganizo mwathu kunatithandiza ‘kulandira ndi chifatso mawu ookedwa’ a choonadi. (Machitidwe 17:11, 12) Kaya takhala Akristu kwa nthaŵi yaitali motani, tiyenera kulola choonadi cha Malemba chowonjezereka kuokedwa mwa ife. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mwa mzimu wa Mulungu, mawu ookedwa amabala “munthu watsopano” amene amapeza chipulumutso.—Aefeso 4:20-24.
18. Kodi munthu amene ali chabe wakumva mawu amasiyana motani ndi amene amawachitanso?
18 Kodi timasonyeza motani kuti mawuwo ndiwo chitsogozo chathu? Mwa kufunitsitsa kukhala “akuchita mawu, osati akumva okha.” (Luka 11:28) “Akuchita” ali ndi chikhulupiriro chimene chimabala ntchito monga kuchita utumiki wachikristu mwachangu ndiponso kutengamo mbali nthaŵi zonse m’misonkhano ya anthu a Mulungu. (Aroma 10:14, 15; Ahebri 10:24, 25) Wakumva mawu chabe “afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirole.” Amadziyang’ana, nachoka ndi kuiŵala chimene chingafunikire kuti akonze kaonekedwe kake. Pokhala “akuchita mawu,” timaphunzira ndi kutsatira mosamalitsa “lamulo langwiro” la Mulungu, lophatikizapo zonse zimene amafuna kwa ife. Choncho ufulu umene tili nawo ndi wosiyana kotheratu ndi ukapolo wa uchimo ndi imfa, popeza ufuluwu umatsogolera ku moyo. Chotero tiyeni tipenye ‘chipenyerere m’lamulo langwiro,’ nthaŵi zonse kulifufuza ndi kulitsatira. Ndipo tangolingalirani! Pokhala ‘akuchita ntchito, osati akumva akuiŵala,’ tili ndi chimwemwe chifukwa cha kuyanjidwa ndi Mulungu.—Salmo 19:7-11.
Zoposa Kungokhala Opembedza Mwamwambo
19, 20. (a) Malinga ndi Yakobo 1:26, 27, kodi kulambira koyera kumafunanji kwa ife? (b) Kodi zitsanzo zina za kulambira kosadetsedwa nziti?
19 Ngati tikufuna kuyanjidwa ndi Mulungu, tifunikira kukumbukira kuti kupembedza koona si mwambo wamba. (Yakobo 1:26, 27, NW) Tingaganize kuti ndife ‘opembedza mwamwambo’ ololeka a Yehova, koma kaonedwe kake ka aliyense wa ife ndiko kofunika kwambiri. (1 Akorinto 4:4) Cholakwa china chachikulu chingakhale kulephera ‘kumanga lilime.’ Tingakhale tikudzinyenga poganiza kuti Mulungu amakondwera ndi kulambira kwathu ngati timaneneza ena, kunama, kapena ngati sitigwiritsira ntchito bwino lilime m’njira zina. (Levitiko 19:16; Aefeso 4:25) Ndithudi, sitikufuna “mapembedzedwe” athu kukhala ‘opanda pake’ ndi osaloleka kwa Mulungu pachifukwa chilichonse.
20 Ngakhale kuti Yakobo sakutchula mbali zonse za kulambira koyera, iye akuti kumaphatikizapo “kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo.” (Agalatiya 2:10; 6:10; 1 Yohane 3:18) Mpingo wachikristu umasonyeza kufunitsitsa pochirikiza akazi amasiye. (Machitidwe 6:1-6; 1 Timoteo 5:8-10) Popeza Mulungu ndiye Wotetezera mkazi wamasiye ndi mwana wopanda atate, tiyeni tigwirizane Naye mwa kuchita zimene tingathe powathandiza mwauzimu ndi mwakuthupi. (Deuteronomo 10:17, 18) Kulambira koyera kumatanthauzanso “kudzisungira mwini wosachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi,” anthu osalungamawa olamuliridwa ndi Satana. (Yohane 17:16; 1 Yohane 5:19) Choncho, tisakhale ndi khalidwe losaopa Mulungu la dzikoli kuti tilemekeze Yehova ndi kukhala othandiza mu utumiki wake.—2 Timoteo 2:20-22.
21. Mogwirizana ndi kalata ya Yakobo, kodi tiyenera kukambirananso mafunso ati?
21 Uphungu wa Yakobo umene takambiranawu kudzafika pano uyenera kutithandiza kupirira ziyeso ndi kugwiritsitsa chikhulupiriro chathu. Uyenera kukulitsa kuyamikira kwathu Wopereka mphatso zabwino wachikondiyo. Ndipo mawu a Yakobo akutithandiza kutsata kulambira koyera. Kodi iye akutiuzanso chiyani? Kodi tingachitenso zinthu zotani kuti tisonyeze kuti tili ndi chikhulupiriro mwa Yehova?
[Mawu a M’munsi]
a Paphunziro laumwini kapena labanja la nkhaniyi ndi nkhani ziŵiri zotsatira, mudzapindula kwambiri mwa kuŵerenga lemba lililonse losonyezedwa la m’kalata yolimbitsa chikhulupiriro ya Yakobo.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchiyani chidzatithandiza kupirira ziyeso?
◻ Mosasamala kanthu za ziyeso, kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kukondwera?
◻ Kodi tingakhale motani akuchita mawu?
◻ Kodi kulambira koyera kumaphatikizapo chiyani?
[Chithunzi patsamba 9]
Pamene muli pachiyeso, dalirani mphamvu ya Yehova yoyankha mapemphero
[Zithunzi patsamba 10]
“Akuchita mawu,” akulengeza Ufumu wa Mulungu padziko lonse