‘Dzitsimikizireni Nokha’
“Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha.”—2 AKORINTO 13:5.
1, 2. (a) Kodi kukayikakayika pa zikhulupiriro zathu kungatikhudze bwanji? (b) M’zaka 100 zoyambirira ku Korinto, n’chiyani chomwe chikanachititsa ena kukhala osatsimikizira za njira yoyenera kutsatira?
MUNTHU wina amene anali paulendo, anafika pa mphambano. Pamenepo, sanadziwe kuti ndi njira iti imene angatsate kuti akafike kumene akupita, choncho anafunsa anthu ena odutsa. Koma zimene anthuwo anamuuza zinali zotsutsana. Posowa chochita, analephera kupitiriza ulendo wake. Izi zingatichitikirenso ifeyo ngati tikhala okayikakayika pa zikhulupiriro zathu. Kukayika kotero kungatilepheretse kusankha zoyenera kuchita. Tingakhale osatsimikizira za njira yoyenera kutsatira.
2 Zoterezi bwenzi zitachitikira anthu ena mumpingo wachikristu wa m’zaka 100 zoyambirira ku Korinto, m’dziko la Girisi. Anthu ena otchedwa ‘atumwi oposa’ anali kukayikira ngati mtumwi Paulo analidi woyenera kuwatsogolera. Iwo ankati: “Akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake n’ngofooka, ndi mawu ake n’ngachabe.” (2 Akorinto 10:7-12; 11:5, 6) Maganizo otere ayenera kuti anachititsa ena mumpingo wa Korinto kukayikira za njira yoyenera kutsatira.
3, 4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi malangizo amene Paulo anapereka kwa Akorinto?
3 Paulo anakhazikitsa mpingo ku Korinto pamene anapita kumeneko mu 50 C.E. Anakhala ku Korinto “chaka chimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsa mawu a Mulungu.” Inde, “Akorinto ambiri anamva, nakhulupira, nabatizidwa.” (Machitidwe 18:5-11) Paulo anali n’chidwi kwambiri ndi moyo wauzimu wa okhulupirira anzake a ku Korinto. Nawonso Akorinto anam’lemberapo kalata Paulo pofunsira malangizo pankhani zina. (1 Akorinto 7:1) Iye anawapatsa malangizo abwino kwambiri.
4 Paulo anawalembera kuti: “Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha.” (2 Akorinto 13:5) Kugwiritsa ntchito malangizo amenewa kukanateteza abale a ku Korintowo kuti asakayikire za njira yoyenera kutsatira. Malangizowa angatitetezenso ifeyo lerolino. Koma kodi tingatsatire bwanji malangizo a Paulowa? Tingadziyese motani ngati tili m’chikhulupiriro? Nanga kodi kudzitsimikizira tokha kumaphatikizapo kutani?
“Dziyeseni Nokha Ngati Muli M’chikhulupiriro”
5, 6. Kodi tili ndi muyeso uti wodziyesera ngati tili m’chikhulupiriro, ndipo n’chifukwa chiyani muyesowo uli wabwino kwambiri?
5 Pamayeso, kawirikawiri pamakhala munthu kapena chinthu choti chiyesedwe ndiponso muyeso wake. Koma pano, choyesedwacho si chikhulupiriro, kutanthauza mfundo zonse za choonadi zimene taziphunzira, koma ndi ifeyo aliyense payekha. Pamayesowa, tili ndi muyeso wangwiro woyesera. Nyimbo imene analemba wamasalmo Davide imati: “Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni [kapena zikumbutso] za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru; malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima: malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.” (Salmo 19:7, 8) Baibulo lili ndi malamulo angwiro a Yehova ndiponso malangizo ake olungama. Lilinso ndi zikumbutso zake zokhazikika ndi malamulo ake oyera. Choncho, uthenga wa m’Baibulo ndiwo muyeso wabwino kwambiri.
6 Pa uthenga wouziridwa ndi Mulungu umenewu, mtumwi Paulo anati: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) Inde, mawu a Mulungu angathe kuyesa mtima wathu, zimene ifeyo tili m’kati mwathu. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji uthenga wamphamvu ndi wakuthwa umenewu m’moyo wathu? Wamasalmo anatchula mosapita m’mbali mmene tingagwiritsire ntchito mawu a Mulungu kuyesera mtima wathu. Iye anaimba kuti: “Wodala munthuyo . . . [amene] m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.” (Salmo 1:1, 2) “Chilamulo cha Yehova” chimapezeka m’Baibulo, lomwe ndi buku la Mawu a Mulungu. Tizikonda kuwerenga Mawu a Yehova. Inde, tizipatula nthawi yowawerenga chapansipansi kapena kuti kusinkhasinkha zimene zili m’menemo. Pochita zimenezi, tizidziyesa ndi zimene tikuwerengazo.
7. Kodi njira yaikulu kwambiri yodziyesera ngati tili m’chikhulupiriro ndi iti?
7 Chotero, njira yaikulu kwambiri yodziyesera ngati tili m’chikhulupiriro, ndiyo kuwerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu, n’kumadziyesa kuti khalidwe lathu likugwirizana motani ndi zimene tikuphunzira. Tili ndi mwayi chifukwa tili ndi zinthu zambiri zotithandiza kumvetsetsa Mawu a Mulungu.
8. Kodi mabuku ofalitsidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” angatithandize bwanji kudziyesa ngati tili m’chikhulupiriro?
8 Yehova wapereka ziphunzitso ndi malangizo kudzera m’mabuku ofotokozera Malemba a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Mwachitsanzo, taganizirani bokosi lakuti “Mafunso Owasinkhasinkha” limene limapezeka kumapeto kwa mitu yambiri m’buku la Yandikirani kwa Yehova.a Bokosi limeneli, limatipatsa mpata wabwino kwambiri wosinkhasinkha. Nkhani zosiyanasiyana za m’magazini athu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, zimatithandizanso kudziyesa ngati tilidi m’chikhulupiriro. Pankhani zofotokoza buku la Miyambo zimene zatuluka posachedwapa m’magazini a Nsanja ya Olonda, mayi wina wachikristu anati: “Nkhani zimenezi n’zopindulitsa. Zimandithandiza kuona ngati zolankhula zanga, khalidwe langa, ndi maganizo anga ali ogwirizanadi ndi miyezo yolungama ya Yehova.”
9, 10. Kodi Yehova watipatsa njira zotani potithandiza kudziyesa tokha ngati tili m’chikhulupiriro?
9 Timalangizidwanso ndi kulimbikitsidwa kwambiri pamisonkhano yampingo, yadera ndi yachigawo. Izi ndi zina mwa njira zimene Mulungu akuthandizira mwauzimu anthu amene Yesaya anawalosera kuti: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, . . . ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” (Yesaya 2:2, 3) Ndi mwayi waukulu kwambiri kulangizidwa njira za Yehova motere.
10 Njira ina yodziyesera tokha ndiyo malangizo ochokera kwa amene ali oyenerera mwauzimu, kuphatikizapo akulu achikristu. Za iwo, Baibulo limati: “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.” (Agalatiya 6:1) Tiyeneratu kukhala oyamikira thandizo lotiwongolera limeneli.
11. Kodi kudziyesa ngati tili m’chikhulupiriro kumafuna kutani?
11 Mabuku athu, misonkhano yachikristu, ndiponso akulu oikidwa, ndi mphatso zabwino zimene Yehova watipatsa. Komabe, kudziyesa ngati tili m’chikhulupiriro kumafuna kudzipenda. Choncho, powerenga mabuku athu kapena pomvetsera malangizo a m’Malemba, tiyenera kumadzifunsa kuti: ‘Kodi nkhaniyi ikunena ine? Kodi ine ndimachita zimenezi? Kodi ine ndimatsatira zikhulupiriro zonse zachikristu?’ Mmene timaonera malangizo amene timalandira m’njira zimenezi, zimasonyeza ngati tili anthu auzimu kapena ayi. Baibulo limati: “Munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu; pakuti aziyesa zopusa. . . . Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse.” (1 Akorinto 2:14, 15) Kodi sitiyenera kuyesetsa kukhalabe ndi maganizo auzimu oyamikira zimene timawerenga m’mabuku athu, m’magazini, ndi m’zofalitsa zina, ndiponso zimene timamva pamisonkhano yathu ndi kwa akulu?
“Dzitsimikizeni Nokha”
12. Kodi kutsimikizira mmene ifeyo tilili kumaphatikizapo kutani?
12 Kudzitsimikizira tokha kumafuna kudziunika. Inde, tingakhale m’choonadi, koma kodi timatsatira choonadi mpaka pati? Kutsimikizira mmene ifeyo tilili kumaphatikizapo kuonetsa umboni wakuti ndife okhwima mwauzimu ndiponso oyamikira zinthu zauzimu kuchokera pansi pa mtima.
13. Malinga ndi Ahebri 5:14, kodi n’chiyani chimene chimaonetsa kuti ndife okhwima?
13 Kodi tingayang’ane umboni wotani mwa ife eni wotsimikizira ngati tili Mkristu wokhwima? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chakudya cholimba n’cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zawo, iwowa anadzizoloweretsa kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.” (Ahebri 5:14, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) Timaonetsa umboni wakuti ndife okhwima mwa kuzoloweretsa nzeru zathu. Kuti munthu wochita masewera olimbitsa thupi azitha kuchita bwino masewerawo, amafunika kuzoloweretsa minofu ina ya m’thupi lake mwa kuigwiritsa ntchito kawirikawiri. Ifenso tiyenera kuzoloweretsa nzeru zathu mwa kuzigwiritsa ntchito potsatira mfundo za m’Baibulo.
14, 15. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa mwakhama kuphunzira zinthu zakuya za m’Mawu a Mulungu?
14 Koma tisanazoloweretse nzeru zathu, tiyenera kuphunzira. Chotero, kuphunzira patokha mwakhama n’kofunika. Tikamaphunzira patokha nthawi zonse, makamaka zinthu zakuya za m’Mawu a Mulungu, nzeru zathu zimawonjezeka. M’mbuyomu, mu Nsanja ya Olonda mwakhala mukutuluka nkhani zambiri zozama zosiyanasiyana. Kodi timatani tikapeza nkhani zofotokoza choonadi chozama? Kodi timazipewa osaziwerenga chifukwa chakuti ‘muli zina zovuta kuzizindikira,’ kapena kuti kuzimvetsa? (2 Petro 3:16) M’malo mwake, tiyenera kuchita khama kwambiri kuti tizimvetsetse nkhanizo.—Aefeso 3:18.
15 Kodi tingatani ngati zimativuta kuphunzira patokha? M’pofunika kuti tiyesetse kuti tizikonda kuphunzira patokha.b (1 Petro 2:2) Kukhala okhwima kumafuna kuti tiphunzire kudya chakudya cholimba, kapena kuti choonadi chozama cha m’Mawu a Mulungu. Kupanda kutero, nzeru zathu zidzakhala zoperewera. Komatu kupeza nzeru kokha sikokwanira kuonetsa umboni wakuti ndife okhwima. Pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku tizigwiritsa ntchito zimene tadziwa pophunzira mwakhama patokha.
16, 17. Ndi malangizo otani amene wophunzira Yakobo anapereka pa kukhala “akuchita mawu”?
16 Umboni wina wotsimikizira mmene ifeyo tilili, umaonekera pa ntchito zathu zoyamikira choonadi, ntchito za chikhulupiriro. Wophunzira Yakobo anapereka fanizo lamphamvu lofotokozera mbali yofunika kudziunika tokha imeneyi kuti: “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mawu wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirole; pakuti wadziyang’anira yekha, nachoka, naiwala pom’paja anali wotani. Koma iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.”—Yakobo 1:22-25.
17 Yakobo akuti: ‘Dziyang’anire wekha m’kalirole wa mawu a Mulungu ndi kudzipenda. Usaleke kuchita zimenezi, ndipo uzidziunika wekha ndi zimene ukupeza m’mawu a Mulungu. Ndiyeno usaiwale mwamsanga zimene waona. Konza zofunika kukonza.’ Kutsatira malangizo amenewa kungakhale kovuta nthawi zina.
18. N’chifukwa chiyani kutsatira malangizo a Yakobo kumakhala kovuta?
18 Mwachitsanzo, taganizirani za lamulo lakuti tizilalikira nawo za Ufumu. “Pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo chilungamo; ndi m’kamwa avomereza kutengapo chipulumutso,” anatero Paulo. (Aroma 10:10) Kuvomereza poyera chipulumutso ndi m’kamwa mwathu kumafuna kuti tisinthe zinthu zingapo. Kulalikira si ntchito yophweka kwa ambiri a ife. Kuti tikhale alaliki achangu ndiponso kuti tiike ntchitoyi patsogolo m’moyo wathu monga mmene imafunikira, tifunika kusintha zinthu zambiri ndiponso kudzipereka. (Mateyu 6:33) Koma tikakhala akuchita ntchito yopatsidwa ndi Mulunguyi, tidzakhala achimwemwe chifukwa cha ulemerero umene ntchitoyi imapereka kwa Yehova. Ndiye, kodi ndife alaliki a Ufumu achangu?
19. Kodi ntchito zathu za chikhulupiriro ziyenera kuphatikizapo chiyani?
19 Kodi ntchito zathu za chikhulupiriro ziyenera kuphatikizapo chiyani? Paulo anati: ‘Zimene mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.’ (Afilipi 4:9) Umboni wotsimikizira mmene ifeyo tilili, umaonekera mwa kuchita zimene taphunzira, talandira, tazimva ndi kuziona; zonse zokhudza kudzipereka kwathu kwachikristu ndi kukhala ophunzira. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova akutilangiza kuti: “Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo.”—Yesaya 30:21.
20. Kodi ndi anthu otani amene amakhala dalitso pa mpingo?
20 Amuna ndi akazi amene amaphunzira mwakhama Mawu a Mulungu, amene amalalikira mwachangu uthenga wabwino, amene ali okhulupirika, ndiponso amene ali odalirika pochirikiza ntchito za Ufumu, ndi dalitso lalikulu pampingo. Amalimbikitsa mpingo wawo. Amakhala othandiza kwambiri makamaka chifukwa chakuti pali atsopano ambiri ofunika kuwathandiza. Tikatsatira malangizo a Paulo akuti ‘tizidziyesa tokha ngati tili m’chikhulupiriro,’ ndi ‘kudzitsimikizira tokha,’ ifenso tidzakhala olimbikitsa kwa ena.
Sangalalani ndi Kuchita Chifuniro cha Mulungu
21, 22. Kodi tingatani kuti tizikonda kuchita chifuniro cha Mulungu?
21 Davide, mfumu ya dziko lakale la Israyeli, anaimba kuti: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m’kati mwamtima mwanga.” (Salmo 40:8) Davide ankakonda kuchita chifuniro cha Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti chilamulo cha Yehova chinali mu mtima mwake. Davide sanali wokayikakayika za njira yoyenera kutsatira.
22 Chilamulo cha Mulungu chikakhala mu mtima mwathu, sitidzakayikakayika za njira yoyenera kutsatira. Tidzakonda kuchita chifuniro cha Mulungu. Ndiyetu tiyeni tiziyesetsa kutumikira Yehova kuchokera mu mtima.—Luka 13:24.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
b Njira zothandiza za mmene mungaphunzirire zikupezeka patsamba 27 mpaka 32 m’buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lakuti, Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi tingadziyese motani ngati tili m’chikhulupiriro?
• Kodi kudzitsimikizira tokha kumaphatikizapo kutani?
• Tingasonyeze motani kuti ndife Mkristu wokhwima?
• Kodi ntchito zathu za chikhulupiriro zimatithandiza motani kudziunika mmene tilili?
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi mukudziwa njira yaikulu kwambiri yodziyesera ngati muli m’chikhulupiriro?
[Chithunzi patsamba 24]
Timaonetsa kuti ndife Akristu okhwima mwa kugwiritsa ntchito nzeru zathu
[Zithunzi patsamba 25]
Timaonetsa mmene tilili mwa kukhala ‘akuchita mawu, osati akumva akuiwala’