Khalani Otetezereka m’Gulu Lolinganizidwa la Mulungu
“Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.”—MIYAMBO 18:10.
1. Malinga ndi pemphero la Yesu, kodi Akristu ali mumkhalidwe wovuta wotani?
ATAKHALA pang’ono kufa, Yesu anapemphera kwa Atate wake wakumwamba, kupempherera otsatira ake. Posonyeza chisamaliro chachikondi, iye anati: “Ine ndawapatsa iwo mawu anu; ndipo dziko lapansi linadana nawo, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi. Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.” (Yohane 17:14, 15) Yesu anadziŵa kuti dziko lapansi linali kudzakhala malo oopsa kwa Akristu. Linali kudzasonyeza udani wake mwa kuwanamizira ndi kuwazunza. (Mateyu 5:11, 12; 10:16, 17) Linali kudzakhalanso lodetsa.—2 Timoteo 4:10; 1 Yohane 2:15, 16.
2. Kodi nkuti kumene Akristu angapeze malo achisungiko chauzimu?
2 Dziko limene linali kudzadana ndi Akristu nlopangidwa ndi anthu olekanitsidwa ndi Mulungu amenenso akulamuliridwa ndi Satana. (1 Yohane 5:19) Dzikoli nlalikulu kwambiri kuposa mpingo wachikristu, ndipo Satana iyemwini ngwamphamvu kwambiri kuposa munthu aliyense. Choncho udani wa dzikoli ngwoopsadi. Kodi nkuti kumene otsatira a Yesu angapeze chisungiko chauzimu? Nsanja ya Olonda yachingelezi ya December 1, 1922 inapereka yankho kuti: “Tili m’tsiku loipa tsopano. Gulu la Satana likumenyana ndi gulu la Mulungu. Nkumenyana koopsa.” Gulu la Mulungu ndilo malo achisungiko chauzimu pakumenyana kumeneku. Mawuwo “gulu lolinganizidwa” mulibe m’Baibulo, ndipo kalelo mu ma 1920, mawu akuti “gulu lolinganizidwa la Mulungu” anali mawu achilendo. Ndiye kodi gulu limeneli nchiyani? Ndipo kodi tingakhale otetezereka motani mkati mwake?
Gulu Lolinganizidwa la Yehova
3, 4. (a) Malinga nkunena kwa dikishonale ina ndi Nsanja ya Olonda inayake, kodi liwu lachingelezi lotembenuzidwa kuti gulu lolinganizidwa nchiyani? (b) Kodi Mboni za Yehova za m’maiko osiyanasiyana tingazitche kuti gulu lolinganizidwa m’lingaliro lotani?
3 Liwu lachingelezi lotembenuzidwa kuti gulu lolinganizidwa limatanthauza “anthu olinganizidwa,” malinga nkunena kwa dikishonale yotchedwa Concise Oxford Dictionary. Poganizira zimenezo, tikudziŵa kuti chifukwa chakuti atumwi analinganiza Akristu a m’zaka za zana loyamba kukhala mipingo ya kwawo komweko yoyang’aniridwa ndi bungwe lolamulira ku Yerusalemu, tinganenedi kuti “abale” amenewo anali gulu lolinganizidwa. (1 Petro 2:17) Mboni za Yehova lerolino nzolinganizidwa mofananamo. Umodzi wa gulu la m’zaka za zana loyamba unalimbitsidwa ndi “mphatso mwa amuna,” monga ngati “abusa ndi aphunzitsi.” Ena mwa ameneŵa ankayendera mipingo, pamene kuli kwakuti ena anali akulu m’mipingo imeneyo. (Aefeso 4:8, 11, 12, NW; Machitidwe 20:28) “Mphatso” zofananazo zimalimbitsa umodzi wa Mboni za Yehova lerolino.
4 Ponena za mawu akuti “gulu lolinganizidwa,” Nsanja ya Olonda yachingelezi ya November 1, 1922, inati: “Gulu lolinganizidwa ndilo bungwe la anthu amene akufuna kuchita chinthu china cholinganizidwa.” Nsanja ya Olonda imeneyo inafotokozanso kuti kutcha Mboni za Yehova kuti gulu lolinganizidwa sikumawapanga kukhala “gulu lampatuko monga momwe ena amanenera, koma zimangotanthauza kuti Ophunzira Baibulowo [Mboni za Yehova] akufuna kuchita zolinga za Mulungu ndi kuzichita mmene Ambuye amachitira zinthu zonse, mwadongosolo.” (1 Akorinto 14:33) Mtumwi Paulo anasonyeza kuti Akristu a m’tsiku lake nawonso anali kuchita zinthu mwadongosolo. Iye anayerekezera gulu la Akristu odzozedwa ndi thupi la munthu, limene lili ndi ziŵalo zambiri, ndipo chiŵalo chilichonse chimachita ntchito yake yachibadwa kuti thupilo ligwire bwino ntchito. (1 Akorinto 12:12-26) Chimenecho nchitsanzo chabwino kwambiri cha gulu lolinganizidwa! Kodi nchifukwa chiyani Akristu anali olinganizidwa? Kuti atumikire “zofuna za Mulungu,” kuchita chifuniro cha Yehova.
5. Kodi gulu looneka la Mulungu ndilo chiyani?
5 Baibulo linaneneratu kuti Akristu oona lerolino adzakhala muumodzi, ndipo adzasonkhanitsidwa monga “mtundu” umodzi mu “dziko” limodzi, mmene anali ‘kudzaonekera monga mauniko m’dziko lapansi.’ (Yesaya 66:8; Afilipi 2:15) “Mtundu” wolinganizidwa umenewu uli ndi anthu oposa mamiliyoni asanu ndi theka tsopano. (Yesaya 60:8-10, 22) Komabe, gulu la Mulungu silimathera pomwepo. Angelonso ali m’gulu lomweli.
6. M’lingaliro lake lalikulu, kodi ndani akupanga gulu lolinganizidwa la Mulungu?
6 Pali nthaŵi zambiri pamene angelo agwira ntchito mogwirizana ndi atumiki aumunthu a Mulungu. (Genesis 28:12; Danieli 10:12-14; 12:1; Ahebri 1:13, 14; Chivumbulutso 14:14-16) Ndiye chifukwa chake Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 15, 1925, moyenerera inati: “Angelo onse oyera ali m’gulu lolinganizidwa la Mulungu.” Ndiponso inati: “Mutu wa gulu la Mulungu ndiye Ambuye Yesu Kristu, wokhala ndi mphamvu zonse ndi ulamuliro wonse.” (Mateyu 28:18) Choncho, m’lingaliro lake lalikulu, gulu lolinganizidwa la Mulungu limaphatikizapo onsewo omwe ali kumwamba ndi padziko lapansi amene akugwirira ntchito pamodzi kuti achite chifuniro cha Mulungu. (Onani bokosi.) Ndi mwayi waukulu chotani nanga kukhala m’gulu limeneli! Ndiponso nzosangalatsa chotani nanga kuyembekezera nthaŵi pamene zolengedwa zonse zamoyo, zakumwamba ndi za padziko lapansi, zidzakhala zolinganizidwa kutamanda Yehova Mulungu muumodzi! (Chivumbulutso 5:13, 14) Komano kodi chitetezo chimene gulu la Mulungu limapereka lerolino nchotani?
Otetezeka m’Gulu la Mulungu—Motani?
7. Kodi gulu la Mulungu limatiteteza motani?
7 Gulu lolinganizidwa la Mulungu lingatithandize kuti tidziteteze kwa Satana ndi machenjera ake. (Aefeso 6:11) Satana amatsendereza, kuzunza, ndi kuyesa alambiri a Yehova ncholinga chimodzi chokha: kuwapatutsa ‘panjira yoyenera iwo kupitamo.’ (Yesaya 48:17; yerekezerani ndi Mateyu 4:1-11.) Sitingapeŵeretu ziukiro zonse zimenezi m’dongosolo lino la zinthu. Komabe, unansi wathu wathithithi ndi Mulungu ndi gulu lake umatilimbitsa ndi kutiteteza nutithandiza kukhalabe “m’njira” imeneyi. Chotsatirapo chake nchakuti sititaya chiyembekezo chathu.
8. Kodi gulu losaoneka la Yehova limawachirikiza motani atumiki ake a padziko lapansi?
8 Kodi gulu la Mulungu limachipereka motani chitetezo chimenechi? Choyamba, tili ndi chichirikizo champhamvu cha atumiki auzimu a Yehova. Pamene Yesu anapsinjika maganizo kwambiri, mngelo anamlimbikitsa. (Luka 22:43) Atayang’anizana ndi imfa, Petro anapulumutsidwa mozizwitsa ndi mngelo. (Machitidwe 12:6-11) Ngakhale kuti lero zozizwitsa zotere sizikuchitika, anthu a Yehova akulonjezedwa kuti adzachirikizidwa ndi angelo m’ntchito yawo yolalikira. (Chivumbulutso 14:6, 7) Nthaŵi zambiri amakhala ndi mphamvu yoposa yachibadwa atayang’anizana ndi mavuto. (2 Akorinto 4:7) Ndiponso, iwo akudziŵa kuti ‘mngelo wa Yehova akuzinga kuwachinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.’—Salmo 34:7.
9, 10. Kodi tinganene motani kuti “dzina la Yehova ndilo linga lolimba,” ndipo kodi pulinsipulo limeneli likugwiranso ntchito motani pa gulu lonse la Mulungu?
9 Nalonso gulu looneka la Yehova nchitetezo china. Motani? Pa Miyambo 18:10, timaŵerenga kuti: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” Zimenezi sizikutanthauza kuti kungotchulatchula dzina la Mulungu kumateteza. M’malo mwake, kuthaŵira kwathu ku dzina la Mulungu kumatanthauza kuti tikukhulupirira Yehova iyemwini. (Salmo 20:1; 122:4) Kumatanthauza kuchirikiza uchifumu wake, kuchirikiza malamulo ndi mapulinsipulo ake, ndi kukhulupirira malonjezo ake. (Salmo 8:1-9; Yesaya 50:10; Ahebri 11:6) Kumaphatikizapo kudzipereka kwa Yehova mosagaŵanika. Okhawo amene akulambira Yehova m’njira imeneyi ndiwo anganene mogwirizana ndi wamasalmo kuti: “Mtima wathu udzakondwera mwa [Yehova], chifukwa takhulupirira dzina lake loyera.”—Salmo 33:21; 124:8.
10 Tsopano onse amene ali m’gulu la Mulungu looneka akugwirizana ndi Mika kunena kuti: “Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.” (Mika 4:5) Gulu lamakonoli lasonkhanitsidwa mozinga “Israyeli wa Mulungu,” amene m’Baibulo akutchedwa kuti “anthu a dzina lake.” (Agalatiya 6:16; Machitidwe 15:14; Yesaya 43:6, 7; 1 Petro 2:17) Choncho, kukhala m’gulu la Yehova kumatanthauza kukhala pakati pa anthu amene amafunafuna, ndiponso amalandira, chitetezo m’dzina la Mulungu.
11. Kodi ndi m’njira zachindunji zotani zimene gulu la Yehova limaperekera chitetezo kwa anthu ake?
11 Ndiponso, gulu lolinganizidwa la Mulungu looneka lili gulu lachikhulupiriro, gulu la anthu achikhulupiriro chimodzi amene amamangirirana ndi kulimbikitsana. (Miyambo 13:20; Aroma 1:12) M’gululi ndimo mmene abusa achikristu amasamalira nkhosa, kulimbikitsa odwala ndiponso ochita tondovi, mmenenso amafuna kubwezeretsa amene anagwa. (Yesaya 32:1, 2; 1 Petro 5:2-4) “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akupereka “zakudya panthaŵi yake” kudzera m’gululi. (Mateyu 24:45) “Kapolo” ameneyu, wopangidwa ndi Akristu odzozedwa, amapereka zinthu zauzimu zabwino koposa—chidziŵitso cholongosoka cha m’Baibulo chimene chingatsogolere munthu ku moyo wosatha. (Yohane 17:3) Chifukwa cha chitsogozo cha “kapolo” ameneyu, Akristu akuthandizidwa kusunga makhalidwe abwino kwambiri ndi kukhala “ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda” m’dziko loopsa lowazinga. (Mateyu 10:16) Ndipo nthaŵi zonse amathandizidwa kuti azikhala “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye,” imene ili chitetezo champhamvu mwa iyo yokha.—1 Akorinto 15:58.
Kodi Ndani Ali m’Gulu Lolinganizidwa la Mulungu?
12. Kodi ndani amene akudziŵidwa kuti ali m’gulu lolinganizidwa la Mulungu lakumwamba?
12 Popeza kuti chitetezo chimenechi chimaperekedwa kwa awo amene ali m’gulu lolinganizidwa la Mulungu, kodi iwo ndani? Ponena za gulu lakumwamba, yankho lake nlodziŵikiratu. Satana ndi ziŵanda zake salinso kumwamba. Koma angelo okhulupirika adakali komweko ‘mumsonkhano wa onse.’ Mtumwi Yohane anaona kuti m’masiku otsiriza, “Mwanawankhosa,” akerubi (“zamoyo zinayi”), ndi “angelo ambiri” adzakhala moyandikana kwambiri ndi mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo anali kudzakhala pamodzi ndi akulu 24—Akristu odzozedwa amene aloŵa kale m’choloŵa chawo chaulemerero chakumwamba. (Ahebri 12:22, 23; Chivumbulutso 5:6, 11; 12:7-12) Mosakayikira onsewo ali m’gulu la Mulungu. Koma ponena za anthu, mpovuta kungoloza.
13. Kodi Yesu anawafotokoza motani amene ali m’gulu la Mulungu ndi amene sali m’gululo?
13 Ponena za ena amene adzanena kuti akumtsatira, Yesu anati: “Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 7:22, 23) Ngati munthu akuchita zosayeruzika, ndithudi ameneyo sali m’gulu la Mulungu, kaya adzinenere kuti ndi wotani, ndiponso mosasamala kanthu za kumene amalambirira. Yesu anasonyezanso mmene tingadziŵire munthu amene ali m’gulu la Mulungu. Iye anati: “Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.”—Mateyu 7:21.
14. Kodi ndi mbali ziti za chifuniro cha Mulungu zimene tikudziŵa kuti awo amene ali m’gulu la Mulungu ayenera kuchita mosalephera?
14 Chotero kuti munthu akhale m’gulu la Mulungu—limene “Ufumu wa Kumwamba” ndiwo mbali yake yofunika koposa—munthu ayenera kumachita chifuniro cha Mulungu. Kodi chifuniro chake nchiyani? Paulo anatchula mbali yofunika kwambiri ya chifunirochi pamene anati: “Chifuniro chake [cha Mulungu] nchakuti anthu amtundu uliwonse apulumuke nafike pa chidziŵitso cholongosoka cha choonadi.” (1 Timoteo 2:4, NW) Ngati munthu amayesetsadi kupeza chidziŵitso cholongosoka m’Baibulo, kuchitsatira pamoyo wake, ndi kuchigaŵira “anthu amtundu uliwonse,” ndiye kuti akuchita chifuniro cha Mulungu. (Mateyu 28:19, 20; Aroma 10:13-15) Nchifunironso cha Mulungu kuti nkhosa za Yehova zidyetsedwe ndi kusamaliridwa. (Yohane 21:15-17) Misonkhano yachikristu njofunika kwambiri pankhaniyi. Munthu amene ali ndi mpata wofika pamisonkhano imeneyi koma anyalanyaza kutero sakuyamikira malo ake m’gulu la Mulungu.—Ahebri 10:23-25.
Ubwenzi ndi Dziko Lapansi
15. Kodi Yakobo anapereka chenjezo lotani ku mipingo ya m’tsiku lake?
15 Zaka ngati 30 pambuyo pa imfa ya Yesu, mbale wake mwa atate wina, Yakobo, anatchula zinthu zina zimene zingatayitse munthu malo ake m’gulu la Mulungu. Iye analemba kuti: “Akazi achigololo inu, kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4) Ndithudi mdani wa Mulungu sali m’gulu lake. Chotero, kodi ubwenzi ndi dziko lapansi nchiyani? Wafotokozedwa kuti umasiyanasiyana, monga kukulitsa kapena kukhala ndi mayanjano oipa. Koma Yakobo anasumikanso pa chinachake—malingaliro oipa oyambitsa khalidwe loipa.
16. Kodi Yakobo anali kunena za chiyani pamene anapereka chenjezo lakuti ubwenzi ndi dziko lapansi ndi udani ndi Mulungu?
16 Pa Yakobo 4:1-3, timaŵerenga kuti: “Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera ku zikhumbitso zanu zochita nkhondo m’ziŵalo zanu? Mulakalaka, ndipo zikusoŵani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha. Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.” Yakobo atalemba mawuwa mpamene anachenjeza za ubwenzi ndi dziko lapansi.
17. Kodi mumpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba munali “nkhondo” ndi “zolimbana” m’lingaliro lotani?
17 Zaka mazana ambiri Yakobo atamwalira, Akristu onyenga anathirana nkhondo naphana m’lingaliro lenileni. Komabe, Yakobo anali kulembera anthu a mu “Israyeli wa Mulungu” a m’zaka za zana loyamba, anthu oyembekezera kukhala ‘ansembe ndi mafumu’ akumwamba. (Chivumbulutso 20:6) Iwo sanaphane m’nkhondo zenizeni. Koma kodi nchifukwa ninji Yakobo ananena kuti zinthu zimenezi zinali kuchitika pakati pa Akristu? Eya, mtumwi Yohane anati aliyense wodana ndi mbale wake ali wakupha munthu. Ndiponso Paulo ananena za kusemphana malingaliro ndi mikangano yosatha m’mipingo kukhala “makani” ndi “ndewu.” (Tito 3:9; 2 Timoteo 2:14; 1 Yohane 3:15-17) Mofananamo, zikuoneka kuti Yakobo anali kunena za kulephera kukonda Akristu anzawo. Pakati pawo, Akristu anali kuchita zinthu monga momwe anthu akudziko amachitira kwa wina ndi mnzake.
18. Kodi nchiyani chingachititse Akristu kulingalira ndi kuchita zinthu mopanda chikondi?
18 Kodi nchifukwa chiyani zinthu zimenezi zinali kuchitika m’mipingo yachikristu? Chifukwa cha malingaliro oipa, monga kusirira ndi “zikhumbitso.” Kunyada, nsanje, ndi kufuna malo apamwamba zingasokonezenso mayanjano achikondi mumpingo wachikristu. (Yakobo 3:6, 14) Malingaliro ameneŵa amapangitsa munthu kukhala bwenzi la dziko lapansi ndi kukhala mdani wa Mulungu. Onse okhala ndi malingaliro ameneŵa sayenera kuganiza kuti adzakhalabe m’gulu la Mulungu.
19. (a) Kodi ndani kwenikweni amene Mkristu angaimbe mlandu atapeza kuti wayamba kukhala ndi malingaliro oipa mumtima mwake? (b) Kodi Mkristu angawalake motani malingaliro oipa?
19 Kodi ndani amene tingaimbe mlandu tikapeza kuti malingaliro oipa ayamba kukula m’mitima mwathu? Satana? Inde, pamlingo wina. Iye ndiye “mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga” wa dziko lino, mmene malingaliro ameneŵa ali ofala kwambiri. (Aefeso 2:1, 2; Tito 2:12) Komabe, nthaŵi zambiri timakhala ndi malingaliro oipa chifukwa cha thupi lathu lopanda ungwiro. Atachenjeza za ubwenzi ndi dziko lapansi, Yakobo analemba kuti: “Kodi muyesa . . . kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?” (Yakobo 4:5) Tonsefe tili ndi chibadwa chofuna kuchita zoipa. (Genesis 8:21; Aroma 7:18-20) Koma tikhoza kuwathetsa malingaliro amenewo ngati tizindikira zofooka zathu ndi kudalira thandizo la Yehova kuti tizilake. Yakobo anati: “[Mulungu] apatsa chisomo choposa [chibadwa chathu chosirira zinthu].” (Yakobo 4:6) Chifukwa cha thandizo la mzimu woyera wa Mulungu ndi chichirikizo cha abale okhulupirika achikristu, ndiponso kudzera mwa thandizo la nsembe ya dipo ya Yesu, Akristu okhulupirika samagonjera zofooka za thupi lawo. (Aroma 7:24, 25) Iwo ngosungika m’gulu la Mulungu, ali mabwenzi a Mulungu, osati mabwenzi a dziko lapansi.
20. Kodi awo amene ali m’gulu lolinganizidwa la Mulungu ali ndi madalitso ochuluka ati?
20 Baibulo limalonjeza kuti: “Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu: Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.” (Salmo 29:11) Ngati ndifedi a “mtundu” wamakono wa Yehova, gulu lake looneka, tidzapeza nawo nyonga imene iye amapereka ndi kukhala ndi mtendere umene amadalitsa nawo anthu ake. Nzoona kuti dziko la Satana nlalikulu kwambiri kuposa gulu looneka la Yehova, ndiponso Satana ngwamphamvu kwambiri kuposa ife. Koma Yehova ndiye Wamphamvuyonse. Mphamvu yake yogwira ntchito sigonjetseka. Angelo ake amphamvu nawonso akugwirizana nafe potumikira Mulungu. Chotero, mosasamala kanthu za udani umene tikuyang’anizana nawo, tikhoza kuchirimika. Monga Yesu, tingalilake dziko lapansi.—Yohane 16:33; 1 Yohane 4:4.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi gulu lolinganizidwa la Mulungu looneka nchiyani?
◻ Kodi gulu la Mulungu limapereka chitetezo m’njira ziti?
◻ Kodi ndani ali m’gulu lolinganizidwa la Mulungu?
◻ Kodi tingapeŵe motani kukhala mabwenzi a dziko lapansi?
[Bokosi patsamba 9]
Kodi Gulu Lolinganizidwa la Mulungu Nchiyani?
M’mabuku a Mboni za Yehova, mawu akuti “gulu la Mulungu” amagwiritsidwa ntchito m’njira zitatu.
1 Gulu lakumwamba la Yehova losaoneka la zolengedwa zokhulupirika zauzimu. Limeneli limatchedwa “Yerusalemu wokwezeka” m’Baibulo.—Agalatiya 4:26, NW.
2 Gulu la Yehova la anthu, looneka. Lerolino, gululi ndilo otsalira odzozedwa ogwirizana ndi khamu lalikulu.
3 Gulu lachilengedwe chonse la Yehova. Lerolino, gululi ndilo gulu lakumwamba la Yehova pamodzi ndi anthu odzozedwa, amene wawatenga kukhala ana ake padziko lapansi okhala ndi chiyembekezo chauzimu. M’kupita kwa nthaŵi, lidzaphatikizaponso anthu angwiro a padziko lapansi.
[Chithunzi patsamba 10]
Chakudya chauzimu chabwino koposa chimaperekedwa kudzera mwa gulu lolinganizidwa la Yehova