Kodi Chikumbumtima Chanu Mungachikhulupirire?
NTHAŴI zambiri, kampasi ndi chiŵiya chodalirika. Singano yake nthaŵi zonse imaloza kumpoto chifukwa cha mphamvu yokoka ya dziko lapansi. Choncho, apaulendo angadalire kampasi kuti iwatsogolere kumene kulibe zizindikiro zowatsogolera. Koma kodi chimachitika nchiyani pamene chinthu china chokhala ndi maginito (mphamvu yokoka) chiikidwa pafupi ndi kampasiyo? Singanoyo ingaloze kumene kuli chinthu chamaginitocho m’malo moloza kumpoto. Panthaŵiyi kampasiyo sikhalanso mlondoleranjira wodalirika.
Zinthu zofananazo zingachitikirenso chikumbumtima cha munthu. Mlengi anaika mphamvu imeneyi mwa ife kuti ikhale ngati mlondoleranjira wodalirika. Popeza kuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, chikumbumtima chimenechi nthaŵi zonse chimayenera kutitsogolera m’njira yolondola pamene tikupanga zosankha. Chiyenera kutisonkhezera kuchita zinthu mogwirizana ndi malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino. (Genesis 1:27) Kaŵirikaŵiri, chimaterodi. Mwachitsanzo, mtumwi wachikristuyo Paulo analemba kuti ngakhale anthu ena amene alibe lamulo la Mulungu lovumbulidwa “amachita mwa okha za lamulo.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo.”—Aroma 2:14, 15.
Ngakhale zili choncho, chikumbumtima sichilankhula nthaŵi zonse pamene chiyenera kutero. Chifukwa chakuti ndife anthu opanda ungwiro, timafuna kuchita zinthu zimene tikudziŵa kuti nzoipa. “Pakuti monga mwa munthu wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu,” anavomereza motero Paulo, “koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga.” (Aroma 7:22, 23) Ngati nthaŵi zambiri timalingalira zinthu zoipa, chikumbumtima chathu chingafooke pang’onopang’ono ndipo pomalizira pake chingasiye kutiuza kuti khalidwe limenelo nloipa.
Komabe, ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, tingapangitse chikumbumtima chathu kukhala chogwirizana ndi malamulo a Mulungu. Ndithudi, nkofunika kwambiri kutero. Chikumbumtima choyera, chophunzitsidwa bwino sichingotithandiza kuti tikhale paunansi wathithithi ndi Mulungu koma nchothandizanso kwambiri pachipulumutso chathu. (Ahebri 10:22; 1 Petro 1:15, 16) Chikumbumtima choyera chidzatithandizanso kupanga zosankha zanzeru m’moyo wathu, zimene zidzatidzetsera mtendere ndi chimwemwe. Ponena za munthu wokhala ndi chikumbumtima chotero, wamasalmo anati: “Malamulo a Mulungu wake ali mumtima mwake; pakuyenda pake sadzaterereka.”—Salmo 37:31.
Kuphunzitsa Chikumbumtima Chathu
Kuphunzitsa chikumbumtima kumaphatikizapo zambiri osati kungoloŵeza pamtima mpambo wa malamulo nkumawatsatira mosaphonya monga momwe ankachitira Afarisi a m’tsiku la Yesu. Atsogoleri achipembedzo ameneŵa ankadziŵa Chilamulo ndipo anapanga malamulo owonjezereka, mwinamwake pofuna kuthandiza anthu kuti azipeŵa kulakwira Chilamulo. Choncho, iwo anathamangira kutsutsa ophunzira a Yesu pamene anabudula ngala zatirigu nadya patsiku la Sabata. Ndipo iwo anatsutsa Yesu pamene anachiza munthu wadzanja lopuwala patsiku la Sabata. (Mateyu 12:1, 2, 9, 10) Zochitika ziŵirizi, malinga ndi mwambo wa Afarisi, zinaswa lamulo lachinayi.—Eksodo 20:8-11.
Mwachionekere, Afarisiwo anaphunzira Chilamulo. Koma kodi chikumbumtima chawo chinali chogwirizana ndi malamulo a Mulungu? Kutalitali! Taonani kuti atangotsutsa zochitikazo zimene anaganiza kuti zinaswa lamulo la Sabata, Afarisiwo anakhala upo kuti ‘awononge’ Yesu. (Mateyu 12:14) Tangolingalirani—atsogoleri achipembedzo odzilungamitsa ameneŵa anaumirira pamfundo yoti kudya ngala zongobudula kumene ndiponso kuchiritsa pa Sabata nkulakwa; sanakhudzidwe nkomwe ndi chiwembu chawo chofuna kupha Yesu!
Akulu a ansembe anasonyezanso malingaliro opotoka ofananawo. Anthu oipa ameneŵa anaona kuti sanalakwe mpang’ono pomwe pamene anatenga ndalama 30 zasiliva m’bokosi losungiramo ndalama za m’kachisi napatsa Yudase kuti apereke Yesu. Koma pamene Yudase mosayembekezereka anabweza ndalamazo naziponya m’kachisimo, chikumbumtima cha akulu a ansembewo chinakhudzidwa ndipo anasoŵa chochita chifukwa cha malamulo. “Sikuloledwa kuziika [ndalamazo] m’chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi,” iwo anatero. (Mateyu 27:3-6) Mwachionekere, akulu a ansembewo anali ndi nkhaŵa yakuti ndalama za Yudasezo tsopano zinali zodetsedwa. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 23:18.) Komatu amuna omwewa analingalira kuti sikunali kulakwa kupereka ndalama kwa munthu woti apereke Mwana wa Mulungu!
Kuchita Zinthu Mogwirizana ndi Malingaliro a Mulungu
Zitsanzo zili pamwambazo zikusonyeza kuti ngati tikufuna kuphunzitsa chikumbumtima chathu, tifunikira kuchita zambiri osati kungosunga malamulo chabe. Inde, kudziŵa malamulo a Mulungu nkopindulitsa, ndipo tiyenera kuwatsatira kuti tipulumuke. (Salmo 19:7-11) Komabe, kuwonjezera pa kuphunzira malamulo a Mulungu, tiyeneranso kukulitsa mtima wochita zinthu mogwirizana ndi malingaliro a Mulungu. Choncho, ulosi wa Yehova woperekedwa kudzera mwa Yesaya ungakwaniritsidwe kwa ife, Ulosiwo umati: “Maso ako adzaona aphunzitsi ako; ndipo makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.”—Yesaya 30:20, 21; 48:17.
Inde, zimenezi sizikutanthauza kuti tidzamvadi mawu enieni akutiuza chochita pamene tiyang’anizana ndi chosankha chachikulu. Komabe, ngati malingaliro athu agwirizana ndi malingaliro a Mulungu pankhani zosiyanasiyana, chikumbumtima chathu chidzakhoza kutithandiza kupanga zosankha zomwe zidzamkondweretsa.—Miyambo 27:11.
Talingalirani za Yosefe, amene anakhalapo m’zaka za zana la 18 B.C.E. Pamene mkazi wa Potifara anamkakamiza kuti achite naye chigololo, Yosefe anakana, ndipo anati: “Nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” (Genesis 39:9) M’tsiku la Yosefe, kunalibe lamulo lolembedwa lochokera kwa Mulungu loletsa chigololo. Ndiponso, Yosefe ankakhala ku Igupto, kumene kunalibe a m’banja lake omuuza za makhalidwe abwino ndi mwambo wa makolo. Choncho, kodi nchiyani chomwe chinapangitsa Yosefe kukana chiyesocho? Kuyankha mwachidule, chinali chikumbumtima chake chophunzitsidwa bwino. Yosefe anagwiritsira ntchito malingaliro a Mulungu akuti mwamuna ndi mkazi adzakhala “thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Choncho, iye anaona kuti nkulakwa kutenga mkazi wa munthu wina. Malingaliro a Yosefe anagwirizana ndi malingaliro a Mulungu pankhaniyi. Kuchita chigololo kunali kulakwira makhalidwe ake abwino.
Lerolino, pali anthu ochepa ofanana ndi Yosefe. Chisembwere nchofala, ndipo ambiri sadera nkhaŵa konse za Mlengi wawo, iwo eni, kapena anzawo a muukwati kuti ayenera kukhala amakhalidwe abwino. Zangokhala zofanana ndi zimene zinafotokozedwa m’buku la Yeremiya kuti: “Panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m’nkhondo.” (Yeremiya 8:6) Choncho, nkofunika kwambiri kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi malingaliro a Mulungu. Tinapatsidwa chinthu chabwino chotithandiza kuchita zimenezo.
Chothandizira Kuphunzitsa Chikumbumtima
Malemba ouziridwa ‘ngopindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ (2 Timoteo 3:16, 17) Phunziro la Baibulo lidzatithandiza kukulitsa chimene Baibulo limatcha “zizindikiritso,” kuti tizitha kusiyanitsa chabwino ndi choipa. (Ahebri 5:14) Lidzatithandiza kukulitsa mkhalidwe wa kukonda zinthu zimene Mulungu amakonda ndi kuda zinthu zimene iye amadana nazo.—Salmo 97:10; 139:21.
Choncho, cholinga cha phunziro la Baibulo ndicho kupeza mzimu wa choonadi ndi phindu lake m’malo mongodziŵa bwino nkhani zake. Nsanja ya Olonda yachingelezi ya September 1, 1976 inati: “Tikamaphunzira Malemba tiyenera kuyesetsa kuzindikira mmene Mulungu akusonyezera chikondi ndi chilungamo chake ndipo zimenezi tiyenera kuzikhomereza m’mitima mwathu kotero kuti zikhale mbali ya moyo wathu monga momwe kulili kudya ndi kupuma. Tiyenera kudziŵa kuti nkofunika kwambiri kukhala ndi makhalidwe abwino mwa kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Chachikulu kwambiri nchakuti tiyenera kuthandiza chikumbumtima chathu kuti chizitsatira mosamalitsa Wopereka Malamulo ndiponso Woweruza wangwiro. (Yesaya 33:22) Choncho, tikamaphunzira zinthu zokhudza Mulungu, tiyenera kumayesetsa kumtsanzira kotheratu pamoyo wathu wonse.”
Kukhala ndi “Mtima wa Kristu”
Phunziro la Baibulo lidzatithandizanso kukhala ndi “mtima wa Kristu,” mkhalidwe wa kumvera ndi kudzichepetsa umene Yesu anasonyeza. (1 Akorinto 2:16) Iye ankasangalala pochita chifuniro cha Atate wake. Sankachita zinthu mosalingalira bwino. Mzimu wake unafotokozedwa mwaulosi ndi Davide wamasalmo, yemwe analemba kuti: “Kuchita chikondwero [“chifuniro,” NW] chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali mkati mwamtima mwanga.”a—Salmo 40:8.
Kuti tiphunzitse chikumbumtima chathu, tifunikira kukhala ndi “mtima wa Kristu.” Pamene anali padziko lapansi monga munthu wangwiro, Yesu anasonyeza kotheratu mikhalidwe ndi umunthu wa Atate wake malinga ndi mmene akanathera monga munthu. Choncho, iye anayeneradi kunena kuti: “Iye amene wandiona Ine waona Atate.” (Yohane 14:9) Pachochitika chilichonse padziko lapansi, Yesu anachita zomwedi Atate wake anamuuza. Choncho, pamene tiphunzira za moyo wa Yesu, timakhala tikukulitsa chidziŵitso chathu cha mikhalidwe ya Yehova Mulungu.
Timaŵerenga kuti Yehova ali “wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka.” (Eksodo 34:6) Nthaŵi zonse, Yesu ankasonyeza mikhalidwe imeneyi kwa atumwi ake. Pamene iwo anali kukangana mobwerezabwereza ponena za munthu amene anali wamkulu pakati pawo, Yesu anawaphunzitsa moleza mtima mwa mawu ndi chitsanzo chake kuti “amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu.” (Mateyu 20:26, 27) Chimenechi nchitsanzo china chosonyeza kuti tingathe kukhala ndi khalidwe lochita zinthu mogwirizana ndi malingaliro a Mulungu mwa kuphunzira za moyo wa Yesu.
Ngati tiphunzira zowonjezereka zokhudza Yesu, tidzatha kutsanziradi Atate wathu wakumwamba, Yehova. (Aefeso 5:1, 2) Chikumbumtima chogwirizana ndi malingaliro a Mulungu chidzatitsogolera m’njira yolondola. Yehova akulonjeza amene amamkhulupirira kuti: “Ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.”—Salmo 32:8.
Kupindula ndi Chikumbumtima Chophunzitsidwa Bwino
Pozindikira za kupulupudza kwa anthu opanda ungwiro, Mose anachenjeza Aisrayeli kuti: “Ikani mitima yanu pamawu onse ndikuchitirani nawo mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mawu onse a chilamulo ichi.” (Deuteronomo 32:46) Ifenso tiyenera kulemba chilamulo cha Mulungu m’mitima mwathu. Tikatero, chikumbumtima chathu mosakayika konse chidzatitsogolera m’mayendedwe athu ndiponso chidzatithandiza kupanga zosankha zoyenera.
Komatu tiyenera kusamala. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yowongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.” (Miyambo 14:12) Kodi nchifukwa ninji zimakhala choncho nthaŵi zambiri? Nchifukwa chakuti, malinga nkunena kwa Baibulo: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziŵa?” (Yeremiya 17:9) Choncho, tonsefe tiyenera kutsatira uphungu wa pa Miyambo 3:5, 6 wakuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika paluntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”
[Mawu a M’munsi]
a M’kalata yake yolembera Ahebri, mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito mawu a m’Salmo 40 pofotokoza za Yesu Kristu.—Ahebri 10:5-10.
[Chithunzi patsamba 7]
Monga kampasi, chikumbumtima chophunzitsidwa ndi Baibulo chingatilozere njira yolondola
[Mawu a Chithunzi]
Kampasi: Courtesy, Peabody Essex Museum, Salem, Mass.