Dziko
Tanthauzo: Potembenuzidwa kuchokera m’liwu Lachigiriki koʹsmos, “dziko” lingatanthauze (1) anthu onse, kusiyapo mkhalidwe wawo wabwino kapena njira ya moyo, (2) mpangidwe wa mikhalidwe ya anthu mu umene munthu amabadwira ndi mu umene amakulira, kapena (3) unyinji wa anthu kupatulako atumiki ovomerezedwa a Yehova. Otembenuza Baibulo ena apereka malingaliro olakwika mwa kugwiritsira ntchito “dziko” kukhala ndi tanthauzo lofanana ndi mawu Achigiriki otanthauza “dziko lapansi,” “dziko lapansi lokhalidwa ndi anthu,” ndi “dongosolo la zinthu.” Nkhani yotsatirayi ikusumika chisamaliro chake chachikulu pa lachitatu la matanthauzo olembedwa manambala la “dziko” monga momwe laperekedwera pamwambapa.
Kodi dziko lidzawonongedwa ndi moto?
2 Pet. 3:7: “Miyamba ndi dziko la masiku ŵano ndi mawu omwewo [a Mulungu] zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku lachiŵeruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.” (Tawonani kuti sianthu onse, amene adzawonongedwa, koma “anthu osapembedza.” Mofananamo, vesi 6 limatchula za chiwonongeko cha “dziko” m’tsiku la Nowa. Anthu oipa anawonongedwa, koma dziko lapansi limodzi ndi Nowa wowopa Mulunguyo ndi banja lake anatsala. Kodi “moto” wa m’tsiku lirinkudza lachiŵeruzo udzakhala weniweni, kapena kodi ngophiphiritsira chiwonongeko chotheratu? Kodi nchiyambukiro chotani chimene moto weniweni ukakhala nacho pamakamu a zakumwamba zenizeni zotero popeza ziri kale dzuŵa ndi nyenyezi zotentha? Kaamba ka kukambitsirana kowonjezereka kwa lembali, wonani tsamba 132, 133, pamutu wakuti “Dziko Lapansi.”)
Miy. 2:21, 22: “Pakuti owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiŵembu azadzulidwamo.”
Kodi ndani amene amalamulira dzikoli—Mulungu kapena Satana?
Dan. 4:35: “[Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova,] achita mwachifuniro chake kukhamu lakumwamba ndi kwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?” (M’lingaliro lofananalo, Yeremiya 10:6, 7 akusonya kwa Yehova kukhala “Mfumu ya mitundu” chifukwa chakuti iye ali Mfumu Yoposa onse, iye amene angakhoze ndi amene adzaimba mlandu mafumu aumunthu ndi mitundu pa imene akulamulira. Monga Mlengi wa dziko lapansi, Yehova ndiye Wolamulira wake woyenerera; iye sanasiyepo konse malo antchito amenewo.)
Yoh. 14:30: “[Yesu anati:] mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa ine.” (Mwachiwonekere wolamulira uyu saali Yehova Mulungu, amene nthaŵi zonse Yesu amachita chifuniro chake mokhulupirika. “Wolamulira wa dziko” ameneyu ayenera kukhala “woipayo,” Satana Mdyerekezi, amene “dziko lonse lapansi ligona” m’mphamvu yake, monga momwe kwafotokozedwera pa 1 Yohane 5:19. Ngakhale kuli kwakuti anthu akukhala pa planeti la Mulungu, dzikoli lapangiwa ndi awo amene saali atumiki omvera a Yehova limene liri pansi pa ulamuliro wa Satana chifukwa chakuti anthu otero amammvera. Awo amene amagonjera ndi mtima wonse kuulamuliro wa Yehova saali mbali yadziko limenelo. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 4:4.)
Chiv. 13:2: “Chinjoka [Satana Mdyerekezi] chinampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.” (Kuyerekezera kwamalongosoledwe a “chirombo” ichi ndi Danieli 7 kumasonyeza kuti chimaimira boma la anthu, osati limodzi lokha koma dongosolo ladziko lonse la ulamuliro wandale zadziko. Kuti Satana ndiye wolamulira wake kukuvomerezana ndi Luka 4:5-7, ndiponso ndi Chivumbulutso 16:14, 16, chimene chimafotokoza mawu auchiwanda kukhala akutsogolera olamulira onse a dziko lapansi kunkhondo yomenyana ndi Mulungu pa Armagedo. Ulamuliro wa Satana wa dzikoli ukungolekereredwa ndi Mulungu kufikira nthaŵi Yake yoikidwiratu ifika ya kuthetsa mkangano waufumu wa chilengedwe chaponseponse.)
Chiv. 11:15: “Panakhala mawu aakulu m’mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko wayamba kukhala wa Ambuye [Yehova], ndi wa Kristu wake.” (Pamene izi zinachitika mu 1914, “masiku otsiriza” a dongosolo loipa la zinthuli anayamba. Chisonyezero chatsopano cha ukumu wa Yehova chinawonekera, panthaŵiyi kupyolera mwa Mwana wa iye yekha monga Wolamulira Waumesiya. Mwamsanga dziko loipa lidzawonongedwa, ndipo Satana, wolamulira wake woipa wauzimu, adzaikidwa kuphompho, wosakhoza kusonkhezera anthu.)
Kodi nchiyani chimene chiri maganizo a Akristu owona kulinga kudziko ndi kulinga kwa anthu amene ali mbali ya dziko?
Yoh. 15:19: “Simuli [otsatira a Yesu] adziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi.” (Motero Akristu owona saali mbali ya unyinji wa chimangidwe cha anthu amene ali otalikirana ndi Mulungu. Iwo amasamalira ntchito zawo zozoloŵereka zaumunthu, koma amakana malingaliro, malankhulidwe, ndi mkhalidwe zimene ziri zodziŵika kukhala zadziko ndi zimene ziri zotsutsana ndi njira zolungama za Yehova.) (Wonani tsamba 368-374, ndiponso 323-327.)
Yak. 4:4, NW: “Akazi achigololo, kodi simudziŵa kuti ubwenzi ndi dziko ndiwo udani ndi Mulungu? Chifukwa chake, yense wofuna kukhala bwenzi ladziko, akudziika kukhala mdani wa Mulungu.” (Chifukwa chakuti Akristu ali opanda ungwiro, panthaŵi zina iwo angaipitsidwe kupyolera mwa kuwonana ndi dziko. Koma pamene apatsidwa uphungu wa m’Mawu a Mulungu, iwo amalapa nawongolera njira zawo. Komabe, ngati ena, mosankha dala, adziika iwo eni kumodzi ndi dziko kapena kutsanzira mzimu wake, amasonyeza kuti iwo saalinso Akristu owona koma afikira kukhala mbali yadziko limene liri paudani ndi Mulungu.)
Aroma 13:1, NW: “Moyo uliwonse ukhaletu wogonjera maulamuliro aakulu, pakuti palibe ulamuliro wina kusiyapo wochokera kwa Mulungu; olamulira alipoŵa amakhala m’malo awo aang’ono mololedwa ndi Mulungu.” (Awo amene amalabadira uphungu uwu saali opanduka, oyesa kugubuduza maboma adziko. Iwo amadzigonjetsera kuulamuliro wa olamulira andale zadziko, akumawamvera malinga ngati zofunsira za olamulira otero sizikuwombana ndi malamulo a Mulungu. Maboma otero anawonedweratu ndi kunenedweratu ndi Mulungu. Amagwiritsira ntchito ulamuliro, osati iye anaŵapatsa ulamulirowo, koma amatero mwachilolezo chake. M’nthaŵi yake yokwanira iye adzawachotsanso.)
Agal. 6:10: “Monga tiri nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo apabanja lachikhulupiriro.” (Chotero, Akristu owona samaleka kuchitira zabwino anthu anzawo. Iwo amatsanzira Mulungu, amene amapangitsa dzuŵa kuŵalira ponse paŵiri anthu oipa ndi abwino.—Mat. 5:43-48.)
Mat. 5:14-16: “Ndinu kuunika kwa dziko. . . . Lolani kuunika kwanu kuŵale pamaso pa anthu, kuti akawone ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wakumwamba.” (Kuti ena apereke ulemerero kwa Mulungu chifukwa cha zimene Akristu amachita, kuli kwachiwonekere kuti awo amene ali Akristu ayenera kukhala mboni zokangalika kudziko ponena za dzina la Mulungu ndi chifuno. Iri ntchitoyi imene Akristu owona amagogomezera kwakukulu.)
Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la mikhalidwe yamakono yadziko?
Wonani mutu waukulu wakuti “Masiku Otsiriza.”