Chifukwa Chake Tifunikira Chikhulupiriro ndi Nzeru
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Kalata ya Yakobo
ATUMIKI a Yehova amafunikira chipiriro pamene akuyesedwa. Ayenera kupeŵa mayendedwe amene akatulukapo kusavomerezedwa ndi Mulungu. Mfundo zoterozo zagogomezeredwa m’kalata ya Yakobo, ndipo kuchitapo kanthu kabwino ponena za izo kumafunikiritsa chikhulupiriro champhamvu ndi nzeru yochokera kumwamba.
Wolemba kalatayi sakudzidziŵikitsa monga mmodzi wa atumwi aŵiri a Yesu wotchedwa Yakobo koma monga ‘kapolo wa Mulungu ndi wa Kristu.’ Mofananamo, mbale wa Yesu wopeza Yuda akunena kuti iye ali “kapolo wa Yesu Kristu, ndi mbale wa Yakobo.” (Yakobo 1:1; Yuda 1; Mateyu 10:2, 3) Chotero, mbale wa Yesu wongopeza Yakobo mosakaikira analemba kalata yokhala ndi dzina lake.—Marko 6:3.
Kalatayi sikutchula chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E., ndipo wolemba mbiri Josephus akusonyeza kuti Yakobo anaphedwera chikhulupiriro mwamsanga pambuyo pa imfa ya nduna Yachiroma Festo pafupifupi 62 C.E. Chotero mwachiwonekere, kalatayi inalembedwa 62 C.E. isanafike. Iyo inalembedwa kwa ‘mafuko khumi ndi aŵiri’ a Israyeli wauzimu, popeza kuti inalunjikitsidwa kwa anthu okhala nacho ‘chikhulupiriro cha Ambuye ŵathu Yesu Kristu.’—Yakobo 1:1; 2:1; Agalatiya 6:16.
Yakobo akugwiritsira ntchito mafanizo amene angatithandize kukumbukira uphungu wake. Mwachitsanzo, iye akusonyeza kuti munthu amene apempha Mulungu nzeru sayenera kukaikira, ‘pakuti wokaikirayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.’ (1:5-8) Lilime lathu liyenera kulamuliridwa chifukwa chakuti lingatsogolere kayendedwe kathu monga momwe tsikiro limatsogolera chombo. (3:1, 4) Ndipo kuti tilake ziyeso, tifunikira kusonyeza chipiriro choleza mtima monga momwe amachitira mlimi poyembekezera kukolola.—5:7, 8.
Chikhulupiriro, Ziyeso, ndi Ntchito
Choyamba Yakobo akusonyeza kuti tingakhale achimwemwe monga Akristu mosasamala kanthu za ziyeso zathu. (1:1-18) Zina za ziyeso zimenezi, monga ngati kudwala, nzofala kwa anthu onse, koma Akristu amavutikanso chifukwa chokhala akapolo a Mulungu ndi a Kristu. Yehova adzatipatsa nzeru yofunikira kuti tipirire ngati tipitirizabe kuipempha mwachikhulupiriro. Iye samatiyesa ndi zinthu zoipa, ndipo tingadalire pa iye kutipatsa zabwino.
Kuti tilandire thandizo la Mulungu, tiyenera kumlambira iye kupyolera m’ntchito zimene zimasonyeza chikhulupiriro chathu. (1:19–2:26) Ichi chimatifunikiritsa kukhala ‘akuchita mawu,’ osati akumva okha. Tiyenera kulamulira lilime, kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye, ndi kukhala osachititsidwa maŵanga ndi dziko. Ngati tiyanja achuma ndi kunyalanyaza amphaŵi, tikaswa ‘lamulo lachifumu’ la chikondi. Timafunikiranso kukumbukira kuti chikhulupiriro chimasonyezedwa ndi ntchito, monga momwe zitsanzo za Abrahamu ndi Rahabi zimasonyezera bwino lomwe. Ndithudi, ‘chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.’
Nzeru Yochokera Kumwamba ndi Pemphero
Aphunzitsi afunikira zonse ziŵiri chikhulupiriro ndi nzeru kuti achite ntchito zawo. (3:1-18) Iwo ali ndi thayo lolemera monga alangizi. Mofanana nawo, tiyenera kulamulira lilime—kanthu kena kamene nzeru yochokera kumwamba imatithandiza kuchita.
Nzeru imatikhozetsa kuzindikira kuti kugonjera ku zizoloŵezi zakudziko kukawononga unansi wathu ndi Mulungu. (4:1–5:12) Ngati timalimbika ndikupeza zonulirapo zadyera kapena tawakana abale athu, tiyenera kulapa. Ndipo nkofunika chotani nanga kupeŵa ubwenzi ndi dziko lino, popeza kuti uli chigololo chauzimu! Tisanyalanyaze konse chifuniro cha Mulungu mwakupanga makonzedwe okondetsa zinthu zakuthupi, ndipo tichenjeretu ndi mzimu wa kusaleza mtima ndi kuusirana moyo.
Aliyense wodwala mwauzimu ayenera kufunafuna thandizo la akulu mumpingo. (5:13-20) Ngati pakhala kuchimwa, mapemphero awo ndi uphungu wanzeru zidzathandiza kubwezeretsa thanzi lauzimu la wochimwayo. Kwenikweni, ‘amene abweza wochimwa ku njira yake yosokera adzapulumutsa munthu [wochimwayo] ku imfa [yauzimu kapena yamuyaya].’
[Bokosi patsamba 23]
Akuchita Mawu: Tiyenera kukhala ‘akuchita mawu, osati akumva okha.’ (Yakobo 1:22-25) Wakumva mawu okha ‘afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirole.’ Pambuyo podziyang’anira mwachidule, iye achoka ‘naiŵala pompaja anali wotani.’ Koma ‘wakuchita mawu’ amayang’ana mosamalitsa pa lamulo la Mulungu langwiro, kapena lachikwanekwane, akumalabadira zonse zofunikira kwa Mkristu. Iye ‘atero chipenyerere’ napitiriza kufufuza lamulolo ncholinga chakupanga kuwongolera kotero kuti agwirizane nalo mwathithithi. (Salmo 119:16) Kodi ‘wakuchita ntchito’ amasiyana motani ndi munthu amene apenya m’kalirole naiŵala chimene iye avumbula? Eya, wakuchitayo amagwiritsira ntchito mawu a Yehova nasangalala ndichiyanjo Chake!—Salmo 19:7-11.