Tchinjirizani Mtima Wanu
“Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.”—MIYAMBO 4:23.
1, 2. N’chifukwa chiyani tifunika kutchinjiriza mtima wathu?
MWAMUNA wina wachikulire wa pa chilumba cha Caribbean anatuluka m’nyumba yake mphepo yamkuntho itatha kuomba. Pomwazamwaza maso kuona zinthu zimene mphepoyo inawononga, anaona kuti mtengo waukulu kwambiri umene unakhala kwa zaka zambirimbiri pafupi ndi khomo lakutsogolo kwa nyumba yakeyo wagwa. Anadzifunsa kuti: ‘Zatheka bwanji kuti mtengo waukuluwu ugwe pamene mitengo yaing’ono imene inali pafupi yapulumuka?’ Atayang’ana chitsa cha mtengowo, anapeza yankho. Mtengo umene unali kuoneka ngati sungagwewo unali wowola m’kati, ndipo mphepoyo inangovumbula kuwolako kumene sikunali kuonekera.
2 Zimakhalatu zomvetsa chisoni kwambiri ngati wolambira woona amene anali kuoneka kuti akutsatira kwambiri moyo wachikristu wagonja pa chiyeso cha chikhulupiriro. Baibulo moyenerera linanena kuti “ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.” (Genesis 8:21) Zimenezi zikutanthauza kuti ngati osasamala, ngakhale mitima yabwino inganyengedwe kuchita zoipa. Popeza munthu aliyense wopanda ungwiro angathe kufooketsedwa, tifunika kumvera langizo ili mosamala: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga.” (Miyambo 4:23) Ndiyeno kodi tingautchinjirize bwanji mtima wathu wophiphiritsa?
Kudzipima Nthaŵi ndi Nthaŵi N’kofunika Kwambiri
3, 4. (a) Kodi ndi mafunso ati okhudza mtima weniweni amene tingafunse? (b) Kodi n’chiyani chingatithandize kuyesa mtima wathu?
3 Mukapita kwa dokotala kuti akakupimeni, mwachionekere adzapima mtima wanu. Kodi thanzi lanu, kuphatikizapo mtima wanu, zikusonyeza kuti mukudya mokwanira? Kodi magazi anu akuthamanga motani? Kodi mtima wanu ukugunda bwino ndiponso mwamphamvu? Kodi mukuchita masewera olimbitsa thupi mokwanira? Kodi mtima wanu ukuvutika ndi maganizo mosayenera?
4 Ngati mtima weniweni umafunika kuupima nthaŵi ndi nthaŵi, kuli bwanji nanga mtima wanu wophiphiritsa? Yehova amauyesa. (1 Mbiri 29:17) Ifenso tizichita chimodzimodzi. Motani? Mwakufunsa mafunso onga akuti: Kodi mtima wanga ukudya chakudya chauzimu chokwanira kudzera m’phunziro laumwini la nthaŵi zonse ndi kupezeka pamisonkhano? (Salmo 1:1, 2; Ahebri 10:24, 25) Kodi uthenga wa Yehova ndi nkhani yaikulu mumtima mwanga ngati “moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga,” zimene zimandichititsa kupita nawo kolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira? (Yeremiya 20:9; Mateyu 28:19, 20; Aroma 1:15, 16) Kodi zikundichititsa kufuna kudzipereka mwamphamvu, kuchita nawo utumiki winawake wanthaŵi zonse ngati n’kotheka? (Luka 13:24) Kodi mtima wanga wophiphiritsa ndimauika m’malo otani? Kodi ndimakonda kucheza ndi anthu amene mitima yawo ili yogwirizana pa kulambira koona? (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) Tiyeni tifulumire kuona mbali zimene tikufooka ndi kuchitapo kanthu mwamsanga kukonza vutolo.
5. Kodi kuyesedwa kwa chikhulupiriro kungakhale kothandiza motani?
5 Nthaŵi zambiri chikhulupiriro chathu chimayesedwa. Zimenezi zingatipatse mpata wozindikira mmene mtima wathu ulili. Mose anauza Aisrayeli amene anatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa kuti: “Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m’chipululu zaka izi makumi anayi, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziŵa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena ayi.” (Deuteronomo 8:2) Kodi nthaŵi zambiri sitimadabwa ndi malingaliro, zokhumba, ndi zochita zathu zimene zimaonekera tikakumana ndi zinthu zimene sitinali kuyembekezera kapena mayesero? Mayesero amene Yehova amalola kutichitikira angatithandizedi kuzindikira zofooka zathu ndi kutipatsa mpata woti tiwongolere. (Yakobo 1:2-4) Tiyenitu tisinkhesinkhe ndi kupempherera za mmene tingachitire tikakumana ndi mayesero.
Kodi Zimene Timalankhula Zimavumbula Chiyani?
6. Kodi nkhani zimene timakonda kulankhula zingavumbule chiyani za mtima wathu?
6 Kodi tingadziŵe bwanji zinthu zimene timaziona kuti n’zofunika kwambiri mumtima mwathu? Yesu anati: “Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m’choipa chake: pakuti mkamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.” (Luka 6:45) Zimene timakonda kulankhula zimasonyeza zimene mtima wathu ukufuna kuchita. Kodi nthaŵi zambiri timalankhula za zinthu zakuthupi ndi kukhala ndi moyo wotsogola? Kapena kodi timakonda kukambirana zinthu ndiponso zolinga zauzimu? M’malo molankhula zolakwa za anthu ena, kodi timayesetsa mwachikondi kukwirira zolakwazo? (Miyambo 10:11, 12) Kodi timakonda kulankhula kwambiri za anthu ena ndi zimene akuchita koma osalankhula kwambiri nkhani zauzimu ndi za makhalidwe? Kodi zimenezi sizingasonyeze kuti tikududukira nkhani za eni ake?—1 Petro 4:15.
7. Kodi tikuphunzira chiyani za kutchinjiriza mtima m’nkhani ya abale khumi a Yosefe?
7 Taganizani zimene zinachitika m’banja lina lalikulu. Ana aamuna khumi aakulu a Yakobo ‘sanali kulankhula mwamtendere’ ndi mng’ono wawo, Yosefe. Chifukwa chiyani? Anali ndi nsanje chifukwa chakuti atate wawo anali kum’konda kwambiri mng’ono wawoyo. Kenaka, Mulungu atadalitsa Yosefe ndi maloto kusonyeza kuti Yehova anali kukondwera naye, iwo “anamuda iye koposa.” (Genesis 37:4, 5, 11) Anamugulitsa mwankhanza mng’ono wawoyo ku ukapolo. Ndiyeno, pofuna kubisa kulakwa kwawoko, ananamiza atate awo kuti Yosefe anaphedwa ndi nyama yakuthengo. Abale a Yosefe khumiwo analephera kutchinjiriza mitima yawo pa nkhani imeneyi. Ngati timakonda kuweruza anthu ena, kodi sungakhale umboni wakuti tili ndi njiru kapena nsanje mumtima mwathu? Tifunika kusamala zimene timalankhula ndi kufulumira kuchotseratu malingaliro olakwika.
8. Kodi n’chiyani chingatithandize kupenda mtima wathu tikanama?
8 Ngakhale kuti “Mulungu sakhoza kunama,” anthu opanda ungwiro amanama. (Ahebri 6:18) Wamasalmo anadandaula kuti: “Anthu onse nga mabodza.” (Salmo 116:11) Ngakhale mtumwi Petro ananama kuti sakumudziŵa Yesu ndipo anatero katatu konse. (Mateyu 26:69-75) Inde, tisamale kuti tipeŵe kunama, chifukwa Yehova amadana ndi “lilime lonama.” (Miyambo 6:16-19) Ngati nthaŵi ina tinanamapo, kungakhale kwanzeru kupenda chimene chinachititsa. Kodi tinatero chifukwa choopa munthu? Kodi tinali kuopa chilango? Kodi chinali chifukwa chakuti timafuna kuti mbiri yathu isaipe kapena chifukwa cha kudzikonda basi? Kaya chifukwa chake chinali chotani, n’koyeneratu kusinkhasinkha za nkhaniyo, kuvomereza modzichepetsa kulakwa kwathu, ndi kupempha Yehova kuti atikhululukire. Ndipo timupemphenso Yehova kuti atithandize kugonjetsa chofooka chathucho. “Akulu a mpingo” angatithandize kwambiri kuchita zimenezo.—Yakobo 5:14.
9. Kodi mapemphero athu angavumbule chiyani za mtima wathu?
9 Yehova, poyankha zimene Mfumu Solomo wachinyamata anapempha zoti ampatse nzeru ndi chidziŵitso, anati: “Popeza chinali mumtima mwako ichi, osapempha chuma, akatundu, kapena ulemu, . . . nzeru ndi chidziŵitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu.” (2 Mbiri 1:11, 12) Yehova anadziŵa zimene Solomo anali kuziika patsogolo poona zimene iye anapempha ndi zimene sanapemphe. Kodi mapemphero athu kwa Mulungu amavumbula chiyani za mtima wathu? Kodi amavumbula kuti timafunafuna chidziŵitso, nzeru, ndi kuzindikira? (Miyambo 2:1-6; Mateyu 5:3) Kodi zinthu za Ufumu timaziika patsogolo? (Mateyu 6:9, 10) Ngati timangopemphera mwamwambo kapena mwachisawawa, zingasonyeze kuti tikufunikira kusinkhasinkha mosamala pa zimene Yehova amachita. (Salmo 103:2) Akristu onse afunika kukhala tcheru ndi kuzindikira zimene mapemphero awo amavumbula.
Kodi Zimene Timachita Zimavumbula Chiyani?
10, 11. (a) Kodi chigololo ndi dama zimachokera kuti? (b) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipeŵe ‘kuchita chigololo mumtima’?
10 Anthu amanena kuti zochita zimavumbula zambiri kuposa mawu. Zimene timachita zimavumbuladi zambiri za mmene tilili mumtima mwathu. Mwachitsanzo, pa nkhani ya makhalidwe, kutchinjiriza mtima kumaphatikizapo zambiri osati kungopeŵa chabe kuchita dama ndi chigololo. Yesu, pa Ulaliki wake wa pa Phiri, ananena kuti: “Koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) Kodi tingapeŵe bwanji kuchita chigololo mumtima mwathu?
11 Yobu, kholo lakale lokhulupirika, anapereka chitsanzo kwa amuna ndi akazi achikristu amene ali m’banja. Mosakayikira, Yobu anali kulankhula ndi atsikana ndipo mwinanso kuwathandiza mwachifundo ngati anafuna thandizo. Komatu mwamuna wokhulupirika ameneyu sanalakelake zoti agone nawo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anatsimikiza mumtima mwake kuti sadzayang’ana akazi mowakhumbira. Iye anati: “Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?” (Yobu 31:1) Tiyeni nafenso tipange pangano limeneli ndi maso athu ndi kutchinjiriza mtima wathu.
12. Kodi mungagwiritse ntchito motani Luka 16:10 pofuna kutchinjiriza mtima wanu?
12 Mwana wa Mulungu ananena kuti: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m’chaching’onong’ono alinso wosalungama m’chachikulu.” (Luka 16:10) Inde, tifunika kupenda makhalidwe athu m’nkhani za moyo watsiku ndi tsiku zimene zingaoneke ngati zazing’ono ngakhalenso makhalidwe athu tikakhala kunyumba patokha. (Salmo 101:2) Pamene tili m’nyumba mwathu, n’kumaonerera wailesi yakanema, kapena kugwiritsa ntchito Intaneti, kodi timaonetsetsa kuti tikutsatira langizo la m’Malemba ili: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera.” (Aefeso 5:3, 4) Ndipo bwanji za chiwawa chimene angaonetse pa wailesi yakanema kapena m’maseŵero a pa vidiyo? Wamasalmo ananena kuti: “Yehova ayesa wolungama mtima: koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.”—Salmo 11:5.
13. Kodi ndi chenjezo lotani limene lingatithandize popenda zimene zikuchokera mumtima mwathu?
13 Yeremiya anachenjeza kuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” (Yeremiya 17:9) Kunyenga kwa mtima kumeneku kungaonekere pamene tidzikhululukira tikalakwa, kuchepetsa zophophonya zathu, kulungamitsa zofooka zathu zazikulu, kapena kukokomeza zimene tachita bwino. Mtima wosachiritsika umatha kukhalanso wapaŵiri—kunena zina, zochita n’kukhala zinanso. (Salmo 12:2; Miyambo 23:7) Ndiyetu n’kofunika kuti tikhale oona mtima pamene tikupenda zimene zikuchokera mumtima mwathu.
Kodi Diso Lathu Ndi la Kumodzi?
14, 15. (a) Kodi diso “la kumodzi” n’lotani? (b) Kodi kukhala ndi diso la kumodzi kungatithandize bwanji kutchinjiriza mtima?
14 Yesu ananena kuti: “Diso ndilo nyali ya thupi.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Chifukwa chake ngati diso lako lili la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala loŵalitsidwa.” (Mateyu 6:22) Diso lakumodzi limayang’ana pa cholinga chimodzi, osalola chinachake kulidodometsa kapena kulipatutsa. Inde, diso lathu liziyang’ana pa ‘kuthanga tafuna Ufumu ndi chilungamo [cha Mulungu].’ (Mateyu 6:33) Kodi n’chiyani chingachitikire mtima wathu wophiphiritsa ngati diso lathu silili la kumodzi?
15 Taganizani nkhani ya kupeza zofunika pa moyo. Kupezera zosoŵa mabanja athu ndi udindo wachikristu. (1 Timoteo 5:8) Koma bwanji ngati tayesedwa ndi chikhumbo chofuna kukhala ndi mafashoni kapena zinthu zatsopano, zinthu zapamwamba, ndi zakudya, zovala, nyumba ndi zinthu zina zosiririka kwambiri? Kodi zimenezo sizingachititse mtima ndi maganizo athu kukhala paukapolo, ndi kutichititsa kukhala a mtima wapaŵiri pa kulambira kwathu? (Salmo 119:113; Aroma 16:18) N’chifukwa chiyani maganizo athu onse sayenera kungokhala pa kusamalira zofuna za thupi, za banja lathu, ndiponso ntchito yathu basi? Kumbukirani langizo louziridwa ndi Mulungu ili: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope padziko lonse lapansi.”—Luka 21:34, 35.
16. Kodi Yesu anachenjeza chiyani zokhudza diso, ndipo chifukwa chiyani?
16 Diso ndi njira yofunika kwambiri yotumizira mauthenga ku maganizo ndi mtima. Zimene limaona zingalimbikitse mwamphamvu maganizo athu, ndi zochita zathu? Yesu ananena za chiyeso cha maso mwafanizo kuti: “Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti n’kwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziŵalo zako chiwonongeke, losaponyedwa thupi lako lonse m’gehena.” (Mateyu 5:29) Diso tiyenera kuliletsa kuona zinthu zosayenera. Mwachitsanzo, tisaonere zinthu zimene zimalimbikitsa zilakolako ndi zikhumbo zonyansa.
17. Kodi kugwiritsa ntchito Akolose 3:5 kungatithandize bwanji kutchinjiriza mtima?
17 Inde, palinso mphamvu zina za thupi zimene zimatithandiza kudziŵa za kunja kwa thupi, osati kuona kokha. Mphamvu zina monga kukhudza ndi kumvetsera, zimachitanso ntchito yawo, ndipo tiyenera kusamala ndi ziwalo zimene zimagwiritsa ntchito mphamvu zimenezi. Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Chifukwa chake fetsani ziŵalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano.”—Akolose 3:5.
18. Kodi tingatani kuti tipeŵe kuganiza zoipa?
18 Chikhumbo choipa chingachokere m’kati mwa maganizo athu. Kumangoganizabe zomwezo nthaŵi zambiri kumakulitsa chikhumbo choipacho ndi kulimbikitsa mtima kuchichita. “Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo.” (Yakobo 1:14, 15) Anthu ambiri avomereza kuti kaŵirikaŵiri psotopsoto kapena kudzichita ndi chala kumachitika mwa njira imeneyi. Ndiyetu n’kofunika kuti tiziganiza zinthu zauzimu nthaŵi zonse. (Afilipi 4:8) Ndipo tikayamba kuganiza zinthu zoipa, tiziyesetsa mwamphamvu kuchotsa maganizo amenewo.
‘Tumikirani Yehova ndi Mtima Wangwiro’
19, 20. Kodi tingapambane bwanji potumikira Yehova ndi mtima wangwiro?
19 Mfumu Davide atakalamba anauza mwana wake kuti: “Solomo mwana wanga, umdziŵe Mulungu wa atate wako, um’tumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo.” (1 Mbiri 28:9) Ndiyeno Solomo anapempha “mtima womvera.” (1 Mafumu 3:9) Komabe, anavutika kuti akhalebe ndi mtima umenewo kwa moyo wake wonse.
20 Kuti tipambane pa nkhani imeneyi, tifunika kutchinjiriza mtima wathu osati kungokhala ndi mtima wovomerezeka kwa Yehova. Kuti tikwanitse zimenezi, tiyenera kusunga zomwe Mawu a Mulungu amatikumbutsa “m’kati mwa mtima” wathu. (Miyambo 4:20-22) Tizipendanso mtima wathu nthaŵi ndi nthaŵi ndi kusinkhasinkha mwapemphero pa zimene mawu athu ndi zochita zathu zimavumbula. Kodi kusinkhasinkha kumeneku kungakhale ndi phindu lanji ngati sitipempha Yehova kuti atithandize kuwongolera zofooka zathu zilizonse zimene taziona? Ndiponso n’kofunikatu kwambiri kuti tizisamala za zimene timaloŵetsa mumtima mwathu kudzera m’mphamvu zathu za thupi tatchula zija. Tikachita zimenezi, tidzatsimikiza kuti “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima [yathu] ndi maganizo [athu] mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Inde, tiyeni tiyesetse kutchinjiriza mtima koposa zonse tizisunga ndi kutumikira Yehova ndi mtima wangwiro.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani n’kofunika kutchinjiriza mtima?
• Kodi kupenda zimene timalankhula kungatithandize bwanji kutchinjiriza mtima wathu?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi diso “la kumodzi’?
[Zithunzi patsamba 23]
Kodi nthaŵi zambiri timalankhula za chiyani pamene tili mu utumiki wakumunda, pa misonkhano, ndi kunyumba?
[Zithunzi patsamba 25]
Diso la kumodzi silimapatutsidwa