1 Mafumu
3 Solomo anachita mgwirizano wa ukwati ndi Farao mfumu ya Iguputo. Anakwatira mwana wamkazi wa Farao+ nʼkubwera naye mu Mzinda wa Davide,+ kuti azikhala kaye kumeneko mpaka iye atamaliza kumanga nyumba yake,+ nyumba ya Yehova+ ndiponso mpanda wa Yerusalemu.+ 2 Koma anthu ankaperekabe nsembe pamalo okwezeka,+ chifukwa pa nthawiyi nyumba ya dzina la Yehova inali isanamangidwe.+ 3 Solomo anapitiriza kukonda Yehova ndipo ankatsatira malamulo a Davide bambo ake, kungoti ankapereka nsembe zopsereza pamalo okwezeka.+
4 Mfumu inapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe, chifukwa kumeneko nʼkumene kunali malo okwezeka otchuka* kwambiri.+ Solomo anapereka nsembe zopsereza zokwana 1,000 paguwa lansembe.+ 5 Ku Gibiyoniko, Yehova Mulungu anaonekera kwa Solomo mʼmaloto usiku ndipo anamuuza kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikupatse.”+ 6 Solomo atamva zimenezi anati: “Inu mwasonyeza kwambiri chikondi chokhulupirika kwa mtumiki wanu Davide bambo anga, chifukwa anali wokhulupirika, wachilungamo komanso wowongoka mtima pamaso panu. Mwapitiriza kumusonyeza chikondi chimenechi mpaka pano pomupatsa mwana kuti akhale pampando wake wachifumu.+ 7 Tsopano Yehova Mulungu wanga, mwandiika ine mtumiki wanu kukhala mfumu mʼmalo mwa Davide bambo anga, ngakhale kuti ndine wamngʼono ndipo sindikudziwa zambiri.+ 8 Ine mtumiki wanu ndili pakati pa anthu anu amene mwawasankha,+ anthu ambirimbiri osatheka kuwawerenga. 9 Mundipatse ine mtumiki wanu mtima womvera kuti ndiweruze anthu anu+ komanso ndizitha kusiyanitsa zabwino ndi zoipa.+ Ndani angathe kuweruza anthu anu ambirimbiriwa?”*
10 Yehova anasangalala ndi zimene Solomo anapemphazi.+ 11 Ndiyeno Mulungu anamuuza kuti: “Popeza wapempha zimenezi ndipo sunapemphe moyo wautali, chuma, kapena kuti adani ako afe, koma wapempha kuti ukhale womvetsa zinthu kuti uzitha kuweruza milandu,+ 12 ndikupatsa zimene wapempha.+ Ndikupatsa mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu+ kuposa anthu onse amene anakhalapo mʼmbuyomu komanso amene adzakhaleko mʼtsogolo.+ 13 Ndikupatsanso zomwe sunapemphe.+ Ndikupatsa chuma ndi ulemerero,+ moti sikudzakhalanso mfumu ngati iwe pa nthawi yonse ya moyo wako.+ 14 Ndipo ukamayenda mʼnjira zanga posunga malangizo ndi malamulo anga ngati mmene Davide bambo ako anachitira,+ ndidzakupatsanso moyo wautali.”+
15 Solomo atadzuka, anazindikira kuti waona masomphenya. Kenako anapita ku Yerusalemu nʼkukaima patsogolo pa likasa la pangano la Yehova. Ndiyeno anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano+ ndipo anakonzera phwando atumiki ake onse.
16 Kenako mahule awiri anapita kwa mfumu nʼkuima patsogolo pa mfumuyo. 17 Mkazi mmodzi anati: “Mbuyanga, ine ndi mayi uyu tikukhala mʼnyumba imodzi. Ndipo ine ndinabereka mwana wamwamuna iyeyu ali mʼnyumba momwemo. 18 Patapita masiku atatu kuchokera tsiku limene ine ndinabereka mwana, nayenso anabereka mwana wamwamuna. Tinali awiriwiri mʼnyumbamo ndipo munalibe munthu wina aliyense. 19 Usiku mwana wa mayiyu anamwalira chifukwa anamutsamira. 20 Ndiyeno ine kapolo wanu ndili mʼtulo, mayiyu anadzuka pakati pa usiku nʼkutenga mwana wanga amene anali pambali panga nʼkumuika pachifuwa pake. Ndipo anatenga mwana wake wakufayo nʼkumuika pachifuwa panga. 21 Nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga, ndinapeza kuti anali wakufa. Choncho ndinamuyangʼanitsitsa mʼmawa nʼkuona kuti si mwana wanga amene ndinabereka.” 22 Koma mayi winayo anati: “Ayi, mwana wanga ndi wamoyoyu, wako ndi wakufayo!” Ndipo mayi woyamba uja ankanena kuti: “Ayi, mwana wako ndi wakufayu, wanga ndi wamoyoyo.” Iwo anapitiriza kukangana chonchi pamaso pa mfumu.
23 Kenako mfumuyo inati: “Uyu akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu, wako ndi wakufayo!’ Ndipo uyo akuti, ‘Ayi, mwana wako ndi wakufayo, wanga ndi wamoyoyu!’” 24 Ndiyeno mfumuyo inati: “Tabweretsani lupanga.” Choncho anabweretsa lupanga kwa mfumu. 25 Mfumuyo inati: “Dulani mwana wamoyoyu pakati. Mupereke hafu kwa mayi mmodzi, hafu ina kwa mayi winayo.” 26 Nthawi yomweyo mayi yemwe mwana wake anali wamoyoyo anayamba kuchonderera mfumu chifukwa chochitira chifundo mwana wakeyo. Iye anauza mfumuyo kuti: “Chonde mbuyanga, mʼpatseni mayiyu mwana wamoyoyu. Musamuphe.” Koma mayi winayo ankanena kuti: “Mwana ameneyu sakhala wanga kapena wako. Amudule pakati basi!” 27 Mfumuyo itamva zimenezi inati: “Perekani mwana wamoyoyu kwa mayi woyambayo. Musamuphe. Mayi ake ndi amenewa.”
28 Aisiraeli onse anamva mmene mfumu inaweruzira nkhaniyo ndipo anachita mantha ndi mfumuyo+ chifukwa anaona kuti Mulungu wamupatsa nzeru kuti aziweruza mwachilungamo.+