“Mayendedwe Anu mwa Amitundu Akhale Okoma”
“Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale.”—1 PETRO 2:17.
1, 2. (a) Kodi mtolankhani wa nyuzipepala ina ananena chiyani za Mboni za Yehova? (b) N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimayesetsa kukhalabe ndi makhalidwe abwino?
ZAKA zingapo zapitazo, mtolankhani wa nyuzipepala ina ku Amarillo, Texas, ku U.S.A., anayendera matchalitchi osiyanasiyana m’deralo ndipo anafotokoza zimene anapeza. Gulu lina analiona kuti linali lapadera kwambiri. Iye anati: “Ndakhala ndikusonkhana ndi Mboni za Yehova pamisonkhano yawo yapachaka pa bwalo la Amarillo Civic Center kwa zaka zitatu. Pamene ndinali nawo limodzi, sindinaone munthu ndi m’modzi yemwe akuyatsa ndudu, kutsekula botolo la mowa, kapena kulankhula mwachipongwe. Anali anthu aukhondo kwambiri, a makhalidwe abwino, ovala bwino, achimwemwe kuposa ena alionse amene ndinakumanapo nawo.” Mawu ofanana ndi ameneŵa onena za Mboni za Yehova asindikizidwanso nthaŵi zambirimbiri. N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimayamikiridwa nthaŵi zambiri ndi anthu omwe si Mboni?
2 Nthaŵi zambiri, anthu a Mulungu amawayamikira chifukwa cha makhalidwe awo abwino. Nthaŵi ino pamene makhalidwe a anthu ambiri akuloŵa pansi, Mboni za Yehova zimaona kuti ndi udindo wawo kusunga makhalidwe abwino, ndiyo mbali ya kulambira kwawo. Zimadziŵa kuti zochita zawo zimakhudza mmene anthu angaonere Yehova ndi abale awo achikristu ndi kuti makhalidwe awo abwino amatsimikizira choonadi chimene amalalikira. (Yohane 15:8; Tito 2:7, 8) Motero, tiyeni tione mmene tingakhalirebe ndi makhalidwe abwino kuti tipitirize kusunga mbiri yabwino ya Yehova ndi Mboni zake ndi kuonanso mmene timapindulira tikamachita zimenezo.
Banja Lachikristu
3. Kodi mabanja achikristu afunika kutetezedwa ku chiyani?
3 Taganizirani za mmene timachitira m’banja. Buku lina lonena za ufulu wachipembedzo (Die Neuen Inquisitoren: Religionsfreiheit und Glaubensneid) limene analemba Gerhard Besier ndi Erwin K. Scheuch, limati: “Kwa [Mboni za Yehova] banja ndi chinthu chofunika kuchiteteza kwambiri.” Mfundo imeneyi ndi yoona, ndipo masiku ano pali zovulaza zambiri zimene zimachititsa kuti banja lifunikire kuliteteza kwambiri. Pali ana amene ‘samvera akuwabala’ ndiponso pali anthu akuluakulu “opanda chikondi chachibadwidwe” kapena “osakhoza kudziletsa.” (2 Timoteo 3:2, 3) M’mabanja ambiri okwatirana amamenyana, makolo amazunza kapena kunyalanyaza ana awo, ndipo ana amaukira, kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi kuchita chiwerewere, kapena kuthaŵa panyumba. Zonsezi zikuchitika chifukwa cha mphamvu yoipa ya ‘mzimu wa dziko lapansi lino.’ (Aefeso 2:1, 2) Tikufunika kuteteza mabanja athu ku mzimu umenewo. Kodi tingachite bwanji zimenezo? Tingatero mwa kumvera uphungu ndi malangizo a Yehova kwa makolo ndi ana.
4. Kodi anthu a m’banja lachikristu ali ndi udindo wotani kwa wina ndi mnzake?
4 Akristu okwatirana amazindikira kuti ayenera kukondana, ndi kusamalana mwauzimu ndiponso mwakuthupi. (1 Akorinto 7:3-5; Aefeso 5:21-23; 1 Petro 3:7) Makolo achikristu ali ndi udindo waukulu kwa ana awo. (Miyambo 22:6; 2 Akorinto 12:14; Aefeso 6:4) Ndipo ana a m’mabanja achikristu akamakula, amaphunzira kuti nawonso ali ndi udindo. (Miyambo 1:8, 9; 23:22; Aefeso 6:1; 1 Timoteo 5:3, 4, 8) Kukwaniritsa udindo wa m’banja kumafuna khama, kutsimikiza mtima, ndi mtima wachikondi ndi wodzipereka. Komabe, onse a m’banja akamakwaniritsa udindo wawo woperekedwa ndi Mulungu, amakhala opindulitsa kwa wina ndi mnzake ndiponso amapindulitsa mpingo. Koposa zonse, amalemekeza Woyambitsa ukwati, Yehova Mulungu.—Genesis 1:27, 28; Aefeso 3:15.
Ubale Wachikristu
5. Kodi timapindula chiyani tikamasonkhana ndi Akristu anzathu?
5 Ife monga Akristu, tilinso ndi udindo kwa okhulupirira anzathu mumpingo ndiponso kwa onse amene akupanga “gulu lonse la abale . . . m’dziko.” (1 Petro 5:9, NW) Kugwirizana kwathu ndi mpingo n’kofunika kwambiri kuti tikhale ndi thanzi labwino lauzimu. Tikamasonkhana ndi Akristu anzathu, timasangalala ndi mayanjano awo olimbikitsa ndiponso timadya chakudya chauzimu chochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Ngati tili ndi mavuto, tingapite kwa abale athu kuti atipatse malangizo abwino ozikidwa pa mfundo za m’Malemba. (Miyambo 17:17; Mlaliki 4:9; Yakobo 5:13-18) Tikamafuna thandizo, abale athu satithaŵa. Ndi dalitsotu lalikulu kukhala m’gulu la Mulungu!
6. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti tili ndi udindo kwa Akristu ena?
6 Komabe, mumpingo tisamangoyembekezera kulandira. Ifenso tifunika kupatsa. Ndipotu, Yesu anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Mtumwi Paulo anatsindika za mtima wopatsa pamene analemba kuti: “Tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika; ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.”—Ahebri 10:23-25.
7, 8. Kodi timasonyeza bwanji mtima wopatsa mumpingo mwathu ndiponso kwa Akristu a m’madera ena?
7 Mumpingo, ‘timavomereza chiyembekezo chathu’ tikamapereka ndemanga pamisonkhano kapena kutenga nawo mbali m’njira zina pa pulogalamu. Kuchita zimenezo mosakayika kumalimbikitsa abale athu. Timawalimbikitsanso mwa kulankhula nawo misonkhano isanayambe kapena itatha. Imeneyi ndi nthaŵi imene tingalimbikitse ofooka, ovutika maganizo ndiponso odwala. (1 Atesalonika 5:14) Akristu oona amaoloŵa manja popereka motero, ndipo zimenezi n’zimene zimachititsa ambiri amene amafika pa misonkhano yathu kwa nthaŵi yoyamba kuchita chidwi ndi chikondi chimene amachiona pakati pathu.—Salmo 37:21; Yohane 15:12; 1 Akorinto 14:25.
8 Komabe, sitimangokonda a mumpingo wathu okha ayi. Timakondanso abale athu padziko lonse. N’chifukwa chake, mwachitsanzo, timakhala ndi bokosi la Thumba la Nyumba za Ufumu m’Nyumba za Ufumu zambiri. Nyumba yathu ya Ufumu ingakhale yabwino, koma tikudziŵa kuti Akristu anzathu ambirimbiri akusoŵa malo abwino osonkhanira. Tikamapereka ndalama ku Thumba la Nyumba za Ufumu, timasonyeza kuwakonda abale oterowo ngakhale kuti sitikuwadziŵa.
9. Kodi Mboni za Yehova zimakondana pa chifukwa chachikulu chiti?
9 N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimakondana? Zimakondana chifukwa chakuti Yesu anawalamula kuti azitero. (Yohane 15:17) Ndiponso kukondana kwawo ndi umboni wakuti mzimu wa Mulungu ukugwira ntchito mwa iwo monga munthu payekha ndiponso monga gulu. Chikondi ndi mbali ya “chipatso cha Mzimu.” (Agalatiya 5:22, 23) Mboni za Yehova zikamaphunzira Baibulo, kupezeka pa misonkhano yachikristu, ndi kupemphera nthaŵi zonse kwa Mulungu, chikondi chimakhala chachibadwa kwa iwo ngakhale kuti akukhala m’dziko limene ‘chikondi cha aunyinji chazirala.’—Mateyu 24:12.
Kuchita Zinthu ndi Dzikoli
10. Kodi tili ndi udindo wotani ku dzikoli?
10 Zimene Paulo ananena za ‘kuvomereza chiyembekezo chathu’ zikutikumbutsa za udindo wina. Kuvomereza kumeneku kukuphatikizapo ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu amene panopa sali abale athu achikristu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Aroma 10:9, 10, 13-15) Kulalikira kumeneku nakonso n’kupatsa. Kugwira nawo ntchito yolalikirayi kumafuna nthaŵi, nyonga, kukonzekera, kuphunzira, ndi kugwiritsira ntchito zinthu zathu. Komabe, Paulo analembanso kuti: “Ine ndili wamangawa wa Ahelene ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa. Chotero, momwe ndingakhoze ine, ndilikufuna kulalikira uthenga wabwino kwa inunso a ku Roma.” (Aroma 1:14, 15) Mofanana ndi Paulo, tiyeni tisaumire pamene tikupereka ‘mangawa’ ameneŵa.
11. Kodi ndi mfundo ziŵiri ziti za m’Malemba zimene zimatitsogolera mmene tingachitire ndi dzikoli, koma ngakhale zili choncho kodi timazindikira chiyani?
11 Kodi tilinso ndi maudindo ena kwa anthu amene sali okhulupirira anzathu? Ee. N’zoona kuti timazindikira kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Timadziŵa kuti Yesu ananena za ophunzira ake kuti: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” Komabe, timakhala m’dzikoli, kupeza zofunika pamoyo wathu momwemu, ndiponso limatichitira zinthu zina. (Yohane 17:11, 15, 16) Motero tili ndi maudindo m’dzikoli. Maudindo otani? Mtumwi Petro anayankha funso limenelo. Mzinda wa Yerusalemu utangotsala pang’ono kuwonongedwa, iye analembera kalata Akristu a ku Asia Minor ndipo ndime ya m’kalata imeneyo imatithandiza kuchita zinthu moyenera ndi dzikoli.
12. Kodi Akristu ali “alendo ndi ogonera” m’njira yotani, ndipo popeza ali otere, ayenera kupeŵa chiyani?
12 Poyamba, Petro anati: “Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo.” (1 Petro 2:11) Mwauzimu, Akristu oona ali “alendo ndi ogonera” chifukwa iwo moyo wawo wonse wagona pa kuyembekezera moyo wosatha. Odzozedwa ndi mzimu akuyembekezera kupita kumwamba ndipo a “nkhosa zina” akuyembekezera kudzakhala m’dziko lapansi la paradaiso la m’tsogolo. (Yohane 10:16; Afilipi 3:20, 21; Ahebri 11:13; Chivumbulutso 7:9, 14-17) Nanga kodi zilakolako za thupi n’chiyani? Zimenezi ndi zinthu zonga kulakalaka kulemera, kufuna kutchuka, kulakalaka zachiwerewere, ndi chilakolako chimene achifotokoza kuti “njiru” ndi “chisiriro.”—Akolose 3:5; 1 Timoteo 6:4, 9; 1 Yohane 2:15, 16.
13. Kodi zilakolako za thupi ‘zimachita nkhondo pa moyo [wathu]’ motani?
13 Zilakolako zoterozo ‘zimachitadi nkhondo pa moyo [wathu].’ Zimawononga ubale wathu ndi Mulungu ndipo motero zimaika pangozi chiyembekezo chathu chachikristu (“moyo” wathu). Mwachitsanzo, ngati timakonda zinthu zoipa, tingadzipereke bwanji “nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu”? Ngati tikodwa mumsampha wokondetsa chuma, tingakhale bwanji ‘tikuthanga tafuna ufumu’? (Aroma 12:1, 2; Mateyu 6:33; 1 Timoteo 6:17-19) Njira yabwino ndiyo kutsatira chitsanzo cha Mose, kukana zonyengerera za dziko lapansi ndi kuika utumiki wathu kwa Yehova pamalo oyamba m’moyo wathu. (Mateyu 6:19, 20; Ahebri 11:24-26) Imeneyi ndiyo mfundo yofunika kwambiri kuti tichite zinthu moyenera ndi dzikoli.
‘Mayendedwe Anu Akhalebe Okoma’
14. N’chifukwa chiyani ife monga Akristu timayesetsa kukhalabe ndi khalidwe labwino?
14 Langizo lina lofunika kwambiri tikulipeza m’mawu otsatira a Petro. Iye anati: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m’mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.” (1 Petro 2:12) Ife monga Akristu, timayesetsa kupereka chitsanzo chabwino. Kusukulu timalimbikira. Kuntchito, timagwira ntchito molimbika ndiponso moona mtima, ngakhale bwana wathu akhale wovuta. M’banja limene wina si Mboni, mwamuna kapena mkazi wokhulupirirayo amayesetsa mwakhama kutsatira mfundo zachikristu. Nthaŵi zina zimenezi n’zovuta koma timadziŵa kuti khalidwe lathu labwino limasangalatsa Yehova ndiponso limakhudza anthu omwe si Mboni.—1 Petro 2:18-20; 3:1.
15. Kodi tikudziŵa bwanji kuti khalidwe labwino la Mboni za Yehova likudziŵika ponseponse?
15 Kukwanitsa kwa Mboni za Yehova kukhalabe ndi makhalidwe abwino kumaoneka m’mawu onena za iwo amene akhala akufalitsidwa m’zaka zonsezi. Mwachitsanzo, nyuzipepala ya ku Italy yakuti Il Tempo inafotokoza kuti: “Anthu amene amagwira ntchito limodzi ndi Mboni za Yehova amanena kuti Mboni n’zoona mtima, zimatsimikizira kwambiri zimene zimakhulupirira moti zingaoneke ngati zimatengeka nazo kwambiri; komabe izo n’zoyenera kuzilemekeza chifukwa cha makhalidwe awo abwino.” Nyuzipepala ya Herald ya ku Buenos Aires, m’dziko la Argentina inati: “Kwa zaka zonsezi, Mboni za Yehova zasonyeza kuti ndi nzika zolimbikira ntchito, zakhama, zosawononga zinthu, ndiponso zoopa Mulungu.” Katswiri wina wa ku Russia, Sergei Ivanenko, anati: “Mboni za Yehova zikudziŵika padziko lonse kuti ndi anthu otsatira mokhulupirika malamulo ndipo makamaka chifukwa cha kusachita ukamberembere pokhoma misonkho.” Mkulu wa malo ena amene Mboni za Yehova zimagwiritsira ntchito pochita misonkhano yaikulu ku Zimbabwe anati: “Ndimaona Mboni zina zikutola mapepala ndi kukonza zimbudzi. Zikamachoka zimasiya bwalolo lili laukhondo kuposa kale. Achinyamata anu ndi ophunzitsidwa bwino. Ndikanakonda dziko lonse litadzala ndi Mboni za Yehova.”
Kugonjera Kwachikristu
16. Kodi timachita bwanji ndi maulamuliro a dzikoli, ndipo chifukwa chiyani?
16 Petro ananenanso za mmene tingachitire ndi olamulira a dzikoli. Anati: “Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino. Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa.” (1 Petro 2:13-15) Timayamikira zabwino zimene timalandira kuchokera ku maboma olongosoka ndipo potsatira mawu a Petro, timamvera malamulo a boma ndi kukhoma misonkho. Ngakhale timazindikira kuti Mulungu wapatsa ufulu maboma wolanga anthu oswa malamulo, chifukwa chachikulu chimene timagonjera maulamuliro a dzikoli ndicho “chifukwa cha Ambuye.” Chimenechi n’chifuniro cha Mulungu. Ndiponso, sitifuna kunyozetsa dzina la Yehova mwa kulangidwa chifukwa cholakwa.—Aroma 13:1, 4-7; Tito 3:1; 1 Petro 3:17.
17. “Anthu opusa” akamadana nafe kodi tingakhale ndi chikhulupiriro chotani?
17 N’zomvetsa chisoni kuti “anthu opusa” ena aulamuliro amatizunza kapena kudana nafe m’njira zina, monga kuipitsa mbiri yathu mwa kufalitsa mphekesera zabodza. Komabe, m’nthaŵi yoikika ya Yehova, mabodza awowo nthaŵi zonse amaonekera poyera ndipo “chipulukiro” chawocho chimatontholetsedwa mogwira mtima. Mbiri yathu ya makhalidwe abwino achikristu imavumbula yokha amene akunena zoona. N’chifukwa chake akuluakulu aboma oona mtima nthaŵi zambiri amatiyamikira monga anthu ochita zabwino.—Aroma 13:3; Tito 2:7, 8.
Akapolo a Mulungu
18. Kodi ife monga Akristu tingapeŵe bwanji kugwiritsira ntchito molakwika ufulu wathu?
18 Petro kenako anachenjeza kuti: “[Khalani, NW] monga mfulu, koma osakhala nawo ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu.” (1 Petro 2:16; Agalatiya 5:13) Masiku ano, kudziŵa kwathu choonadi cha m’Baibulo kumatimasula ku ziphunzitso zonyenga zachipembedzo. (Yohane 8:32) Ndiponso tili ndi ufulu wosankha, ndipo tingachite zimene tikufuna. Komabe, sitigwiritsira ntchito molakwika ufulu wathu. Posankha anthu ocheza nawo, zovala, kudzikongoletsa, zosangalatsa, ngakhale zakudya ndi zakumwa, timakumbukira kuti Akristu oona ali akapolo a Mulungu, osati odzisangalatsa okha. Timasankha kutumikira Yehova osati kukhala akapolo a zilakolako zathu zathupi kapena mafashoni ndi masitayelo a dzikoli.—Agalatiya 5:24; 2 Timoteo 2:22; Tito 2:11, 12.
19-21. (a) Kodi anthu amene ali ndi maudindo aulamuliro m’dzikoli timawaona bwanji? (b) Kodi ena asonyeza bwanji ‘kukonda abale’? (c) Kodi udindo wathu waukulu ndi uti?
19 Petro anapitiriza kuti: “Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, chitirani mfumu ulemu.” (1 Petro 2:17) Popeza Mulungu walola anthu kukhala ndi maudindo olamulira osiyanasiyana, timawalemekeza moyenera anthu oterowo. Timatha kuwapempherera, n’cholinga choti atilole kupitiriza kuchita utumiki wathu mumtendere pamodzi ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu. (1 Timoteo 2:1-4) Komabe pochita zimenezo, ‘timakonda abale.’ Nthaŵi zonse timachita zinthu zoti zipindulitse abale athu achikristu osati kuwavulaza.
20 Mwachitsanzo, dziko lina la mu Africa muno litagaŵanika ndi nkhondo yapachiweniweni, khalidwe lachikristu la Mboni za Yehova linaonekera. Nyuzipepala ya ku Switzerland yakuti Reformierte Presse inati: “Mu 1995, bungwe la African Rights . . . linapeza kuti zipembedzo zonse zinaloŵerera nawo [mu nkhondoyo] kupatulapo Mboni za Yehova.” Pamene nkhani ya tsokali inamveka ku mayiko akunja, Mboni za Yehova za ku Ulaya zinatumiza mofulumira thandizo la chakudya ndi mankhwala kwa abale awo ndi anthu ena m’dziko limene munkachitika nkhondolo. (Agalatiya 6:10) Zinamvera mawu a pa Miyambo 3:27 akuti: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.”
21 Komabe tili ndi udindo wina wofunika kwambiri kuposa ulemu umene tiyenera kupereka kwa olamulira a dzikoli kapenanso chikondi chimene tiyenera kusonyeza kwa abale athu. Kodi ndi udindo wotani umenewo? Petro anati: “Opani Mulungu.” Tili ndi udindo waukulu kwa Yehova kuposa umene tili nawo kwa wina aliyense. Kodi zimenezi n’zoona motani? Ndipo tingagwirizanitse bwanji udindo wathu kwa Mulungu ndi udindo wathu kwa olamulira a dzikoli? Nkhani yotsatirayi iyankha mafunso ameneŵa.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi Akristu ali ndi udindo wotani m’banja?
• Kodi tingasonyeze bwanji mtima wopatsa mumpingo?
• Kodi tili ndi udindo wotani ku dzikoli?
• Kodi timapindula chiyani pokhalabe ndi makhalidwe abwino?
[Chithunzi patsamba 9]
Kodi banja lachikristu lingatani kuti likhale losangalala?
[Zithunzi patsamba 10]
N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimakondana?
[Zithunzi patsamba 10]
Kodi tingasonyeze chikondi kwa abale athu ngakhale sitikuwadziŵa?