Anthu Aufulu Koma Oŵerengeredwa Thayo
‘Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.’—YOHANE 8:32.
1, 2. (a) Kodi ufulu wakhala wotani m’mbiri ya anthu? (b) Kodi ndani yekha ali waufulu kwenikweni? Fotokozani.
UFULU. Ha, ndiliwu lamphamvu chotani nanga limenelo! Mtundu wa anthu wavutika ndi nkhondo ndi zipanduko limodzinso ndi chipolowe chifukwa cha chikhumbo cha anthu chakufuna chimasuko. The Encyclopedia Americana imanenadi kuti: ‘M’kusinthika kwa kutsungula, palibe lingaliro limene lakhala ndi mbali yofunika kwambiri kuposa la ufulu.’
2 Komabe, kodi ndianthu angati omwe alidi omasuka? Ndipotu ndiangati amene amaudziŵa nkomwe ufulu? The World Book Encyclopedia imati: “Kuti anthu akhale ndi ufulu wotheratu, sipayenera kukhala ziletso pa kulingalira kwawo, kulankhula, kapena kuchita zinthu. Ayenera kudziŵa zosankha zawo, ndipo ayenera kukhala ndi mphamvu yakudzisankhira zimenezo.” Chotero, kodi mumadziŵa munthu aliyense amene alidi waufulu mwanjira imeneyo? Kodi ndani amene anganene kuti “alibe ziletso pa kulingalira kwawo, kulankhula, kapena kuchita zinthu”? Kunena zowona, pali munthu mmodzi yekha m’chilengedwe chonse amene ali wotero—Yehova Mulungu. Iye yekha ali ndi ufulu wotheratu. Iye yekhayo ndiye angapange chosankha chirichonse chimene angakhumbe ndi kuchichita mosasamala kanthu ndi chitsutso chimene chingakhalepo. Iye ndiyetu “Wamphamvuyonse.”—Chivumbulutso 1:8; Yesaya 55:11.
3. Kodi anthu nthaŵi zonse amakhala ndi ufulu pamaziko otani?
3 Kwa anthufe, ufulu nthaŵi zonse umakhala ndi polekezera. Umaperekedwa ndi wolamulira ndipo umadalira pakugonjera kwathu kwa wolamulirayo. Ndithudi, pafupifupi m’chochitika chirichonse, munthu angakhale womasuka ngati alemekeza ulamuliro wa wopereka ufuluwo. Mwachitsanzo, anthu okhala mu “dziko laufulu” amakhala ndi mapindu ochuluka, monga ufulu wa kuyenda, ufulu wa kulankhula, ndi ufulu wa kulambira. Kodi nchiyani chimene chimatsimikiziritsa kukhalapo kwa maufulu amenewo? Malamulo a dzikolo. Munthu angakhale nawo maufuluwo kokha ngati amvera malamulowo. Ngati agwiritsira ntchito molakwa ufulu wake namaswa malamulowo, amakhala ndi mlandu kwa olamulira, ndipo ufulu wake ungachepetsedwe kwakukulu mwakuponyedwa m’ndende.—Aroma 13:1-4.
Ufulu Waumulungu—Woŵerengeredwa Thayo
4, 5. Kodi olambira a Yehova ali ndi ufulu wotani, ndipo kodi iye adzawaŵerengera thayo pachiyani?
4 M’zaka za zana loyamba, Yesu ananena za ufulu. Iye anati kwa Ayuda: ‘Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.’ (Yohane 8:31, 32) Iye sankanena za ufulu wa kulankhula kapena ufulu wa kulambira. Ndipotu iye sankalankhula za kumasuka ku chitsenderezo cha Roma, chimene Ayuda ambiri adalakalaka. Ayi, ichi chidali kanthu kamtengo wapatali, ufulu woperekedwa, osati ndi malamulo a anthu kapena zolingalira za wolamulira waumunthu, koma ndi Wolamulira wamkulukulu wa chilengedwe chonse, Yehova. Unali ufulu womasuka ku malaulo, ufulu womasuka ku umbuli wachipembedzo, ndi zina zotero zochuluka. Ufulu woperekedwa ndi Yehova ndiwo ufulu weniweni, ndipo udzakhalapobe ku nthaŵi zomka muyaya.
5 Mtumwi Paulo adati: “Koma [Yehova, NW] ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali mzimu wa [Yehova, NW] pali ufulu.” (2 Akorinto 3:17) Kwa zaka mazana ambiri, Yehova wakhala akuchita ndi mtundu wa anthu kotero kuti okhulupirika afikire pakukhala ndi ufulu waumunthu wabwino ndi waukulu koposa, “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Pakali pano, Yehova akutipatsa ufulu pamlingo winawake kupyolera m’chowonadi cha Baibulo, ndipo timakhala oŵerengeredwa thayo kwa iye ngati tiugwiritsira ntchito molakwa ufuluwo. Mtumwi Paulo adalemba kuti: ‘Palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake, koma zonse zikhala zapambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa iye amene tichita naye.’—Ahebri 4:13.
6-8. (a) Kodi ndimaufulu otani amene Adamu ndi Hava anali nawo, ndipo kodi maufuluwo anadalira pamaziko otani? (b) Kodi Adamu ndi Hava anadzitaira chiyani limodzinso ndi mbadwa zawo?
6 Kuŵerengeredwa thayo ndi Yehova kunawonekera kwenikweni pamene makolo athu oyamba aumunthu, Adamu ndi Hava, adakali amoyo. Yehova adawalenga ndi mphatso yamtengo wapatali ya ufulu wakusankha. Malinga ngati anagwiritsira ntchito ufuluwo mosamala, iwo anasangalala ndi madalitso enanso, monga ngati ufulu ku mantha, ufulu ku matenda, ufulu ku imfa, ndi ufulu wakufikira Atate wawo wakumwamba ndi chikumbumtima choyera. Koma pamene anagwiritsira ntchito molakwa ufulu wawo wakusankha, zonsezo zidasintha.
7 Yehova adaika Adamu ndi Hava m’munda wa Edene, ndipo pofuna kuti akhale achimwemwe, adawapatsa zipatso za mitengo yonse ya m’mundamo—napatulapo umodzi wokha. Umenewo udali wa iye yekha; “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 2:16, 17) Mwakupeŵa kudya zipatso za mtengowo, Adamu ndi Hava akasonyeza kuvomereza kwawo kuti Yehova yekha ndiye anali ndi ufulu wakukhazikitsa muyezo wa chabwino ndi choipa. Ngati iwo akadasamala ndi kupeŵa kudya chipatso choletsedwacho, Yehova akadapitirizabe kusungitsa maufulu awo enawo.
8 Mwachisoni, Hava anamvera lingaliro lachinyengo la Njokayo lakuti ‘akadziŵa zabwino ndi zoipa.’ (Genesis 3:1-5) Iye choyamba, kenako Adamu, anadya chipatso choletsedwa. Chotsatirapo, pamene Yehova Mulungu anadzalankhula nawo m’munda wa Edene, anachita manyazi nabisala. (Genesis 3:8, 9) Iwo tsopano adali ochimwa osakhalanso ndi ufulu wakumfikira Mulungu ndi chikumbumtima choyera. Chifukwa cha zimenezi, anatayanso ufulu ku matenda ndi imfa, ponse paŵiri wa iwo eni ndi wa mbadwa zawo. Paulo anati: ‘Monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.’—Aroma 5:12; Genesis 3:16, 19.
9. Kodi ndani amene akudziŵika kuti anagwiritsira ntchito ufulu wawo mwanzeru?
9 Komabe, anthu anali nawobe ufulu wakusankha, ndipo mkupita kwa nthaŵi, anthu ena opanda ungwiro anaugwiritsira ntchito mwanzeru kutumikira Yehova. Ena a maina awo asungidwa kaamba ka ife kuchokera ku nthaŵi za makedzana. Amuna onga Abele, Enoke, Nowa, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo (wotchedwanso Israyeli) ali zitsanzo za anthu amene anagwiritsira ntchito ufulu umene adali nawo kuchita chifuniro cha Mulungu. Ndipo iwo anadalitsika kwenikweni kaamba ka zimenezo.—Ahebri 11:4-21.
Ufulu wa Anthu a Mulungu Osankhidwa
10. Kodi pangano limene Yehova anapangana ndi anthu ake apadera linazikidwa pamiyezo yotani?
10 M’masiku a Mose, Yehova anamasula ana a Israyeli—panthaŵiyo ofika ku mamiliyoni—kuukapolo m’Igupto ndi kupangana nawo pangano mwa limene anakhala anthu ake apadera. Pansi pa pangano limeneli, Aisrayeli anali ndi ansembe ndi makonzedwe a kupereka nsembe za nyama zimene zinakwirira machimo awo mwanjira yophiphiritsira. Motero, anali ndi ufulu wakumfikira Mulungu m’kulambira kwawo. Analinso ndi malamulo ndi malangizo owasunga kukhalabe omasuka ku machitachita a malaulo ndi kulambira konyenga. Pambuyo pake, akalandira Dziko Lolonjezedwa monga choloŵa, ndi kupatsidwa chitsimikizo cha chithandizo cha Mulungu poyang’anizana ndi adani awo. Mbali yawo m’chipanganocho inali yakusunga chilamulo cha Yehova. Aisrayeli anavomereza mofunitsitsa thayo limeneli, akumati: ‘Zonse adazilankhula Yehova tidzachita.’—Eksodo 19:3-8; Deuteronomo 11:22-25.
11. Kodi chinatsatirapo nchiyani pamene Israyeli analephera kusunga mbali yake ya pangano ndi Yehova?
11 Aisrayeli anakhala muunansi wapadera umenewo ndi Yehova kwa zaka zoposa 1,500. Koma kaŵirikaŵiri, analephera kusunga chipangano. Iwo ananyengedwa mobwerezabwereza ndi kugwera m’kulambira konyenga nakhala muukapolo wa kulambira mafano ndi kukhulupirira malaulo, kotero kuti Mulungu analola kuti adani awo awachititse kukhala akapolo awo enieni. (Oweruza 2:11-19) Mmalo mwakupeza madalitso akumasulidwa omwe anakhalapo mwakusunga chipangano, iwo analangidwa chifukwa chakuswa chipanganocho. (Deuteronomo 28:1, 2, 15) Potsiziriza pake, mu 607 B.C.E., Yehova analola mtunduwo kutengedwa muukapolo ku Babulo.—2 Mbiri 36:15-21.
12. Kodi nchiyani chimene chinawonekera pomalizira pake ponena za pangano la Chilamulo cha Mose?
12 Ichi chidali chilango chovuta kuchita nacho. Adayenera kutengapo phunziro la kufunika kwa kusunga Chilamulo. Komabe, pambuyo pa zaka 70, pamene Aisrayeli anabwerera ku dziko lakwawo, adalepherabe kusunga pangano la Chilamulo. Pafupifupi zaka zana limodzi atabwerera kwawo, Yehova anati kwa ansembe a Israyeli: ‘Inu mwapambuka m’njira; mwakhumudwitsa ambiri m’chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi.’ (Malaki 2:8) Ndithudi, ngakhale owona mtima koposa pakati pa Aisrayeli sanathe kufikira muyezo wa Chilamulo changwirocho. Mmalo mokhala dalitso kwa iwo, malinga nkunena kwa mtumwi Paulo, chinakhala “temberero.” (Agalatiya 3:13) Momvekera bwino, panafunikira kanthu kena koposa pangano la Mose la Chilamulo kotero kuti anthu opanda ungwiro, okhulupirika akhale ndi ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.
Mkhalidwe wa Ufulu Wachikristu
13. Kodi ndimaziko abwinopo opezera ufulu otani omwe anaperekedwa pomalizira pake?
13 Kanthu kena koposako kanali nsembe yadipo ya Yesu Kristu. Pafupifupi chaka cha 50 C.E., Paulo analembera mpingo wa Akristu odzozedwa ku Galatiya. Anafotokoza mmene Yehova anawamasulira ku ukapolo wa pangano la Chilamulo nanenanso kuti: ‘Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chirimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.’ (Agalatiya 5:1) Kodi ndimotani mmene Yesu anawamasulira anthu?
14, 15. Kodi ndimwanjira zodabwitsa zotani zimene Yesu anamasulira Ayuda ndi okhulupirira osakhala Ayuda?
14 Pambuyo pa imfa ya Yesu, Ayuda amene anamlandira monga Mesiya ndi kukhala ophunzira ake anakhala pansi pa pangano latsopano, limene linaloŵa mmalo pangano lakale la Chilamulo. (Yeremiya 31:31-34; Ahebri 8:7-13) Pansi pa pangano latsopano limeneli, iwo—ndi okhulupirira osakhala Aisrayeli omwe pambuyo pake anakhala amodzi a iwo—anakhala mbali ya mtundu wauzimu watsopano, umene udaloŵa mmalo Israyeli wakuthupi monga anthu a Mulungu apadera. (Aroma 9:25, 26; Agalatiya 6:16) Motero, iwo anakhala ndi ufulu umene Yesu adalonjeza pamene anati: ‘Chowonadi chidzakumasulani.” Kuwonjezera pa kuwamasula ku temberero la Chilamulo cha Mose, chowonadi chinamasula Akristu Achiyuda ku miyambo yonse yothodwetsa imene atsogoleri achipembedzo anaikundika pa iwo. Ndipo chinawonjola Akristu osakhala Ayuda ku kukhulupirira mafano ndi malaulo kwa kulambira kwawo kwakale. (Mateyu 15:3, 6; 23:4; Machitidwe 14:11-13; 17:16) Ndipo panali zina zowonjezereka.
15 Yesu, polankhula za chowonadi chimene chimamasula, anati: ‘Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa chimolo.’ (Yohane 8:34) Popeza kuti Adamu ndi Hava anachimwa, anthu onse otsatirapo anakhala ochimwa ndi akapolo a uchimo. Wopatukapo ndiye Yesu yekha, ndipo nsembe ya Yesu inamasula okhulupirira ku ukapolo umenewo. Indedi, iwo adaakali opanda ungwiro ndi ochimwa mwachibadwa. Komabe, tsopano anakhoza kulapa machimo awo ndi kupempha chikhululukiro pamaziko a nsembe ya Yesu, ali ndi chidaliro chakuti zopempha zawo zidzamvedwa. (1 Yohane 2:1, 2) Pamaziko a nsembe yadipo ya Yesu, Mulungu adawalengeza olungama, ndipo anatha kumfikira ndi chikumbumtima choyera. (Aroma 8:33) Ndiponso, popeza kuti dipo linapereka chiyembekezo cha chiukiriro cha moyo wosatha, chowonadi chinawamasuladi ku mantha a kuwopa imfa.—Mateyu 10:28; Ahebri 2:15.
16. Kodi ndimotani mmene ufulu Wachikristu unaphatikiziramo ambiri koposa ufulu uliwonse woperekedwa ndi dziko?
16 Mwanjira yodabwitsa, ufulu Wachikristu udatsegulidwa kwa amuna ndi akazi mosasamala kanthu za malo awo, malinga ndi kalingaliridwe kaumunthu. Amphaŵi, a m’ndende, ngakhale akapolo, anakhoza kumasuka. Kumbali ina, apamwamba a mitundu omwe anakana uthenga wonena za Kristu anakhalabe muukapolo ku malaulo, uchimo, ndi mantha akuwopa imfa. Tisatope konse kumamuthokoza Yehova kaamba ka ufulu umene tikusangalala nawo umenewu. Palibe chimene dziko lingachipereke chofanana nawo.
Omasuka Koma Oŵerengeredwa Thayo
17. (a) Kodi ndimotani mmene ena m’zaka za zana loyamba anataira ufulu Wachikristu? (b) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kunyengedwa ndi wowonekera kukhala ufulu m’dziko la Satana?
17 M’zaka za zana loyamba, mwachiwonekere Akristu odzozedwa ochuluka anakondwa ndi ufulu wawo ndi kusunga umphumphu wawo mosasamala kanthu ndi kutaikiridwa kulikonse. Komabe, mwachisoni, ena adalaŵa ufulu Wachikristu ndi madalitso ake onse komanso nkuutaya pambuyo pake, nabwerera ku ukapolo m’dziko. Kodi chinachititsa nchiyani? Mosakaikira, chikhulupiriro cha ambiri chidafooka, ndipo ‘adangotengeka.’ (Ahebri 2:1) Ena ‘anachikankha chikhulupiriro ndi chikumbumtima chokoma, ndipo chikhulupiriro chawo chinataika.’ (1 Timoteo 1:19) Mwinamwake adagonja pakukondetsa zinthu zakuthupi kapena moyo wachisembwere. Nkofunika kwambiri chotani nanga kuti titetezere chikhulupiriro chathu ndi kuchikulitsa, tikukhala otanganitsidwa ndi phunziro laumwini, mayanjano abwino, pemphero ndi ntchito Zachikristu! (2 Petro 1:5-8) Eya, tisaleketu kuyamikira ufulu Wachikristu! Indedi, ena angakhumbire kumasuka kumene amakuwona kunja kwa mpingo, akumalingalira kuti aja okhala m’dziko ali ndi ufulu wokulirapo kutiposa. Koma kunena zowona, umene ungawoneke ngati ufulu m’dziko kaŵirikaŵiri umangokhala moyo wosasamala. Ngati sitikhala akapolo a Mulungu, tikhala akapolo a uchimo, ndipo ukapolo umenewo umapereka mphotho yoŵaŵa ndithu.—Aroma 6:23; Agalatiya 6:7, 8.
18-20. (a) Kodi ndimotani mmene ena anakhalira ‘adani a mtengo wozunzirapo’? (b) Kodi ndimotani mmene ena amayesera ‘ufulu wawo kukhala wobisira choipa’?
18 Ndiponso, m’kalata yake kwa Afilipi, Paulo analemba kuti: ‘Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kaŵirikaŵiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a [mtengo wozunzirapo] wa Kristu.’ (Afilipi 3:18) Inde, alipo amene kale anali Akristu omwe anakhala adani a chikhulupiriro, mwinamwake ampatuko. Ha, nkofunika chotani nanga kuti tisatsatire njira yawo! Kenako, Petro anawonjezera kuti: ‘Monga mfulu, koma osakhala nawo ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu.’ (1 Petro 2:16) Kodi ndimotani mmene munthu angakhalire nawo ufulu monga chobisira choipa? Mwakuchita machimo aakulu—mwina mobisa—pamene akugwirizanabe ndi mpingo.
19 Kumbukirani za Diotrefe. Yohane anati ponena za iye: ‘Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo [mumpingo], satilandira ife. . . . ndipo . . . salandira abale . . . , ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mumpingo.’ (3 Yohane 9, 10) Diotrefe anagwiritsira ntchito ufulu wake monga chobisira chikhumbo chake chadyera.
20 Mtumwi Yuda analemba kuti: ‘Pakuti pali anthu ena anakwaŵira m’tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina awo kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza mfumu Wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Kristu.’ (Yuda 4) Pamene anagwirizana ndi mpingo, anthu ameneŵa anapereka chisonkhezero choipa. (Yuda 8-10, 16) M’Chivumbulutso timaŵerenga kuti mu mipingo ya Pergamo ndi Tiyatira, munali mipatuko, kulambira mafano, ndi chisembwere. (Chivumbulutso 2:14, 15, 20-23) Ha, ndikuupotoza chotani nanga ufulu Wachikristu!
21. Kodi nchiyani chidzachitikira amene amapotoza ufulu wawo Wachikristu?
21 Kodi nchiyani chidzachitika kwa amene amapotoza ufulu wawo Wachikristu mwanjira imeneyi? Kumbukirani chimene chinachitika kwa Israyeli. Israyeli anali mtundu wosankhidwa wa Mulungu, koma pomalizira pake Yehova anaukana. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Aisrayeli anagwiritsira ntchito unansi wawo ndi Mulungu monga chobisira choipa. Iwo anadzitama kuti anali ana a Abrahamu koma anamkana Yesu, Mbewu ya Abrahamu ndi Mesiya wosankhidwa wa Yehova. (Mateyu 23:37-39; Yohane 8:39-47; Machitidwe 2:36; Agalatiya 3:16) “Israyeli wa Mulungu” kumtenga yense sadzakhala wosakhulupirika mofananamo. (Agalatiya 6:16) Koma Mkristu aliyense payekha amene aipitsa mwakuthupi kapena mwauzimu adzayang’anizana ndi chilango pomalizira pake, ngakhaletu chiweruzo choipitsitsa. Tonsefe timaŵerengeredwa thayo ponena za mmene timagwiritsirira ntchito ufulu wathu Wachikristu.
22. Kodi amene amagwiritsira ntchito ufulu wawo Wachikristu kukhala akapolo kwa Mulungu amapeza chimwemwe chotani?
22 Nkwabwino chotani nanga kukhala kapolo wa Mulungu ndi kukhala womasukadi. Yehova yekha ndiye amapereka ufulu umene umapinduladi. Miyambo imati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Tiyeni tigwiritsiretu ntchito ufulu Wachikristu kulemekeza Yehova. Tikatero, miyoyo yathu idzakhala ndi tanthauzo, tidzakondweretsa Atate wathu wakumwamba, ndipo pomalizira pake tidzakhala pakati pa awo osangalala ndi ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi ndani yekhayo ali womasuka kotheratu?
◻ Kodi ndimaufulu otani amene Adamu ndi Hava anali nawo, ndipo anawataya motani?
◻ Kodi Aisrayeli anakhala ndi maufulu otani pamene anasunga pangano lawo kwa Yehova?
◻ Kodi amene anamlandira Yesu anakhala ndi maufulu otani?
◻ Kodi ndimotani mmene ena m’zaka za zana loyamba anataira kapena kupotoza ufulu wawo Wachikristu?.
[Chithunzi patsamba 13]
Ufulu umene Yesu anapereka unali wabwinopo koposa ufulu uliwonse umene munthu angaupereke