Mmene Ubatizo Ungatipulumutsire Ife
“Kumizidwa . . . kumatipulumutsa ife.”—1 PETRO 3:21, The Emphatic Diaglott.
1, 2. Nchiyani chimene chimafunikira munthu asanapite ku ubatizo wa m’madzi?
YEHOVA ali ndi zofunika zachindunji kaamba ka awo ofunafuna chipulumutso. Iwo ayenera kupeza chidziŵitso cholongosoka, kusonyeza chikhulupiriro, kulapa machimo awo, kutembenuka, kupanga kudzipereka kwa Mulungu, ndi kubatizidwa monga akhulupiriri. (Yohane 3:16; 17:3; Machitidwe 3:19; 18:8) Opita ku ubatizo afunikira kuvomereza mwapoyera kuti pa maziko a nsembe ya Yesu iwo alapa machimo awo ndipo adzipereka iwo eni kwa Yehova. Iwo ayeneranso kumvetsetsa kuti kudzipereka ndi ubatizo kumawazindikiritsa iwo monga Mboni za Yehova.
2 Kakonzedwe konse ka ubatizo, kuphatikizapo kusonyeza kwapoyera kwa chikhulupiriro kumeneku, kuli kofunika kaamba ka chipulumutso. (Aroma 10:10) Ichi chinatsimikiziridwa pamene mtumwi Petro analemba kuti: “Kumizidwa . . . kumatipulumutsa ife.” (1 Petro 3:21, ED) Koma kwenikweni ndimotani mmene tiyenera kumvetsetsera mawu amenewa? Kodi nchiyani chimene mawu ozungulira lembalo amasonyeza?
Mmene Ubatizo Umapulumutsira
3. M’mawu anu anu, ndimotani mmene mukafupikitsira 1 Petro 3:18-21?
3 Petro anasonyeza kuti monga mzimu wowukitsidwa, Yesu analalikira uthenga wotsutsa kwa mizimu yoipa ya m’ndende, ziwanda zosungidwa m’ndende zosatha kaamba ka chiŵeruzo cha tsiku lalikulu la Yehova. Iwo sanamvere mwa kutenga matupi aumunthu ndi kukhala ndi akazi “pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira m’masiku a Nowa, pokhala m’kukonzeka chingalawa, mmenemo oŵerengeka [Nowa, mkazi wake, ana ake amuna, ndi akazi awo], ndiwo a moyo asanu ndi atatu anapulumutsidwa mwa madzi.” Petro anawonjezera kuti: “Chimenenso chifaniziro chake chakupulumutsani tsopano, ndicho, ubatizo, (kosati [kufunika kokha kwa] kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu,) mwa kuwuka kwa Yesu Kristu.”—1 Petro 3:18-21; Genesis 6:1, 2; 2 Petro 2:4; 2 Akorinto 7:1.
4. Ndi kuchiyani kumene Petro anali kulozera pamene ananena kuti, “Chimenenso chifaniziro chake”?
4 Nchiyani chimene Petro anatanthauza pamene ananena kuti, “Chimenenso chifaniziro chake”? Iye anatanthauza kuti ubatizo wozikidwa pa chikhulupiriro umalingana ndi kupulumutsidwa kwa Nowa ndi banja lake, omwe ananyamulidwa mwa chisungiko kupyola madzi a chigumula omwe anawononga aja omwe anali kunja kwa chingalawa. Monga mmene Nowa anafunikira chikhulupiriro kumanga chingalawa, onse omwe amakhala ophunzira obatizidwa a Yesu Kristu ndi mboni za Yehova afunikira kukhala ndi chikhulupiriro kulimbana ndi zididikizo zobweretsedwa molimbana nawo ndi dziko lino lopanda chikhulupiriro ndi mulungu wake, Satana Mdyerekezi.—Ahebri 11:6, 7; 1 Yohane 5:19.
5. Ndimotani mmene ziriri kuti chipulumutso chiri “kupyolera m’kuwukitsidwa kwa Yesu Kristu”?
5 Ubatizo weniweniwo si chimene chimapulumutsa. Ndipo ngakhale kuti tifunikira ‘kutaya kwa litsiro lake lathupi,’ chimenecho chokha sichimatipulumutsa ife. M’mwalomwake, chipulumutso chiri “kupyolera m’kuwukitsidwa kwa Yesu Kristu.” Opita ku ubatizo afunikira kukhala ndi chikhulupiriro chakuti chipulumutso chiri chothekera kokha chifukwa chakuti Mwana wa Mulungu anafa imfa ya nsembe ndipo anawukitsidwa. Afunikiranso kulandira Yesu monga Mbuye wawo wokhala ndi ulamuliro wa kuweruza amoyo ndi akufa. “Amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu,” anatero Petro, “atalowa m’mwamba; pali angelo ndi maulamuliro ndi zimphamvu zomugonjera.”—1 Petro 3:22.
6. Kuti apeze chikumbumtima chokoma, nchiyani chimene wopita ku ubatizo afunikira kukhala atachita?
6 Petro anagwirizanitsanso ubatizo ndi “funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu.” Kuti apeze chikumbumtima chokoma, wopita kukamizidwa afunikira kulapa machimo ake, kutembenuka kuchoka ku njira yolakwa, ndi kupanga kudzipereka kotheratu kwa Yehova Mulungu m’pemphero kupyolera mwa Yesu Kristu. Ngati munthu wobatizidwa asungirira chikumbumtima chimenecho mwa kukhalirira ku miyezo ya Mulungu, iye amakhala mu mkhalidwe wopulumutsidwa womwe sumaitanira kaamba ka chiŵeruzo chotsutsa cha Yehova.
Kuyeneretsedwa kaamba ka Ubatizo
7. Ponena za ubatizo, nchiyani chimene amishonale a Chikristu cha Dziko achita?
7 Pamene Yesu analamulira atsatiri ake kubatiza ophunzira, iye sanawauze iwo kuwaza madzi pa osakhulupirira omwe anali mu zikwi. Koma kodi nchiyani chimene amishonale a Chikristu cha Dziko achita? Ponena za India, Jesuit Francis Xavier analemba mu 1545 kuti: “Mu ufumu wa Travancore . . . m’nyengo ya miyezi yoŵerengeka ndabatiza amuna, akazi, ndi ana oposa zikwi khumi. . . . Ndinapita ku mudzi ndi mudzi ndi kupanga iwo Akristu.” Imeneyo si njira ya Yesu ya ‘kupanga Akristu.’ Anthu afunikira kuyeneretsedwa kaamba ka ubatizo.
8. Nchiyani chomwe chotchedwa chiphunzitso cha Paulo chimanena ponena za awo odzipereka iwo eni kaamba ka ubatizo?
8 Ngakhale ena odzinenera kukhala Akristu a m’nyengo ya pambuyo pa atumwi anakhulupirira kuti awo odzipereka iwo eni kaamba ka ubatizo anafunikira kufikira zofunika zosamalitsa. Ponena za opita ku ubatizo oterowo, ziphunzitso zosakhala za m’Baibulo, zogwirizanitsidwa molakwika kwa mtumwi Paulo, zimanena kuti: “Lolani makhalidwe awo ndi moyo zifufuzidwe . . . Ngati iwo ali osakwatira, aloleni iwo aphunzire kusachita dama, koma kulowa mu ukwati wa lamulo. . . . Ngati mkazi wachigololo adza, mloleni iye aleke kuchita chigololo, ngati sitero mloleni iye akanidwe. Ngati wopanga mafano adza, lolani kaya kuti iye asiye ntchito yake, kapena mloleni kuti akanidwe. . . . Yemwe ali ndi liwongo la machimo osatchulidwa, . . . wamatsenga, sing’anga, wopenda nyenyezi, ng’anga, wogwiritsira ntchito maversi a matsenga, . . . wopanga zithumwa, wa malodza, woneneratu za mtsogolo, wolosera mwaŵi, wopenda zikhato . . . , lolani awa atsimikiziridwe kwa nthaŵi ina . . . ndipo ngati asiya machitachita amenewo, aloleni alandiridwe; koma ngati sadzavomera ku icho, aloleni akanidwe.”
9. Nchifukwa ninji akulu a pa mpingo amakhala ndi kukambitsirana ndi munthu wokhumba kubatizidwa?
9 Mboni za Yehova sizimatsatira zolembedwa zosakhala za m’malemba, zonga ngati zogwidwa mawu pamwambazo, koma akulu amakhala ndi kukambitsirana ndi awo okhumba kubatizidwa. Nchifkuwa ninji? Kuti atsimikizire kuti anthu amenewa ali akhulupiriri omwe amafikira zofunika zaumulungu ndipo apanga kudzipereka kwa Yehova. (Machitidwe 4:4; 18:8; 2 Atesalonika 3:2) Kukambitsirana mafunso m’bukhu la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu kumathandiza kutsimikizira kaya ngati munthu ali woyeneretsedwa kaamba ka ubatizo. Ngati nsonga zina ziri zosamvetsetseka kwa iye, kapena ngati iye sanagwirizanitse moyo wake ndi miyezo yaumulungu, akuluwo ali osangalatsidwa kupereka thandizo lauzimu.
10. Ngati tikhumba kubatizidwa, ndi mkhalidwe wotani umene tifunikira kukhala nawo?
10 Ngati tiyamikira kukoma mtima kwa Mulungu m’kutithandiza ife kuphunzira ponena za zifuno zake, tidzakhala ngati anthu kwa amene Paulo analalikira mu Antiyokeya, Asia Minor. Mosasamala kanthu za chitsutso cha Chiyuda, “pakumva ichi [za mwaŵi wa kulandiridwa ndi Mulungu] amitundu [Akunja], anakondwera nalemekeza mawu a [Yehova, NW], ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwa ku moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48) Akhulupiriri oterowo anabatizidwa.
Ubatizo mu Uchichepere
11. Kodi chiri cholondola kupanga kudzipereka kwa Mulungu monga munthu wachichepere, ndipo nchifukwa ninji mukuyankha tero?
11 Awo “oikidwa ku moyo wosatha” amaphatikizapo anthu ena achichepere. Chingadziŵidwe kuti ngakhale kuti Samueli ndi Yohane Mbatizi anali odzipereka kwa Mulungu asanabadwe, makolo sangapange kudzipereka kaamba ka ana awo. (1 Samueli 1:11, 24-28; 2:11, 18, 19; Luka 1:15, 66) Koma monga chotulukapo cha kuphunzitsa kwabwino kwa Baibulo, anthu achichepere ambiri amapita patsogolo ku ubatizo. Mlongo wa chimishonale wobatizidwa ali wachichepere analemba kuti: “Chimawoneka kwa ine kuti ndinadzipereka kutumikira Mlengi wanga kuchokera ku msinkhu weniweni wa kuzindikira kuti iye analiko, koma ndi kupezedwa kwa chidziŵitso china cholongosoka cha iye ndi zifuno zake, ndinafuna kubatizidwa mu umboni wowonekera wa chenicheni chimenecho. Ngakhale ndi tero, Amayi anakaikira kuti ndinadziŵa chimene ndinali kuchita, chotero iwo analingalira kuti ndiyembekeze kufikira winawake anali wokonzekera kubatizidwa.” Mkazi wokhumba kubatizidwa anapezedwa, ndipo mlongoyo akuwonjezera kuti: “Panalibe makalasi a kulangizidwa kwapadera kaamba ka opita ku ubatizo m’masiku amenewo, ngakhale kuti Wotsogolera Utumuki woikidwa ndi Sosaite . . . analankhula kwa ine mokoma mtima ponena za kusamalitsa kwa sitepi lomwe ndinkatenga. Ndinavomereza mofunitsitsa ku miyezo yonse yokhazikitsidwa, ndipo pa Sande lowala m’mawa mu May 1921 [mkaziyo] ndi ine tinabatizidwa.”
12. Ndimotani mmene Mbale Russell anawonera kudzipereka kwa wachichepere?
12 Mu 1914, C. T. Russell (pa nthaŵiyo prezidenti wa Watch Tower Society) analandira kalata mu imene Mkristu mnzathu anafunsa ngati mwana wake wamwamuna wa zaka 12 zakubadwa anayenera kulimbikitsidwa kupanga kudzipereka kwa Mulungu. “Ngati ndinali inu,” Russell anayankha tero, “sindikanakakamiza kudzipatulitsa [kudzipereka] pa iye, koma ndikanaziika izo m’malingaliro ake monga njira yokha yolondola kaamba ka anthu onse anzeru omwe abwera ku chidziŵitso cha Mulungu ndi zifuno zake zachisomo . . . Popanda kudzipatulitsa palibe ndi mmodzi yense yemwe angapeze moyo wosatha . . . Mwana wamwamuna wanu sangavulazidwe ndi kudzipatulitsa, koma angathandizidwe mokulira. . . . Ndani yemwe adzanena kuti mwana wa zaka khumi sangadze kwenikweni ndipo kotheratu ku chiyamikiro cha kudzipatulitsa kokwanira m’malingaliro ndi mawu ndi kachitidwe? Nditayang’ana kumbuyo ndikhoza kuwona kuti kudzipatulitsa kwanga konse choyamba kunapangidwa pa kupita patsogolo kochepera—kupyola pa msinkhu wa zaka khumi ndi ziŵiri.”
13. Nchiyani chimene magazini iyi inanena kwa achichepere zaka 94 zapitazo?
13 Zion’s Watch Tower ya July 1, 1894, inanena kuti: “Kwa ana onse okondedwa ndi anthu achichepere omwe apereka mitima yawo kwa Mulungu, ndi omwe akuyesera tsiku ndi tsiku kutsatira Yesu, WATCH TOWER ikutumiza moni wake. Timadziŵa ena a ang’ono kwambiri omwe amakonda Yesu, ndipo omwe sali amanyazi kuimirira kaamba ka Yesu pakati pa ana ena omwe samamkonda iye kapena kuyesera kumkondweretsa iye; ndi omwe ali olimba mtima ndi owona kwa Mulungu, ngakhale atasekedwa ndi kulingaliridwa kukhala osiyana ndi anzawo a ku sukulu kwa amene amalankhula mbiri yabwino ya ufumu. Ndipo tiri osangalatsidwa kuwona anthu ena achichepere, omwe atsutsa dziko molimba mtima ndi zokhumba zake ndi zosangalatsa, pakati pa okhulupirira koposa a awo omwe [apereka] miyoyo yawo kwa Ambuye. Ena a othandizira a ofesi athu, limodzinso ndi akoputala achipambano ambiri, adakali achichepere m’zaka.” Ngakhale kuti mudakali wachichepere, bwanji osalankhula kwa makolo anu ponena za kudzipereka kwa Yehova Mulungu?
Mbali ya Makolo
14. Ndi mapindu otani omwe amasangalalidwa ndi anthu achichepere omwe amapanga kudzipereka kwa Yehova?
14 Lingalirani mapindu osangalalidwa ndi ana omwe amalandira chitsogozo cha ukholo chomwe chimatsogolera ku ubatizo. (Aefeso 6:4) Kulingalira pa zinthu zauzimu kumawathandiza iwo kuthawa misampha ya kudziko ndi zopinga. (1 Yohane 2:15-17) Iwo samakolola zotuta zowawa zomwe zimatulukapo ‘m’kufesa kuthupi.’ (Agalatiya 6:7, 8) Popeza kuti iwo aphunzitsidwa kukhala ndi moyo waumulungu, iwo amasonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Pokhala odzipereka kwa Mulungu, iwo amasangalala ndi unansi wathithithi ndi iye. Ndipo chifukwa chakuti iwo aphunzira “kukhulupirira mwa Yehova,” amatsogozedwa ndi nzeru ya kumwamba ndi kuyenda m’njira ya chisangalalo ndi mtendere.—Miyambo 3:5, 6, 13, 17.
15. Nchiyani chimene makolo Achikristu angachite kuwumba miyoyo ya ana awo?
15 Popeza kuti kudzipereka kwa Yehova kuli kopindulitsa chotero kwa anthu achichepere, makolo Achikristu ayenera kuchita zonse zimene angathe kuwumba miyoyo ya ana awo. Monga Timoteo, achichepere angaphunzitsidwe Malemba kuchokera ku ubwana kotero kuti angakhoze ‘kupitirizabe m’zimene aziphunzira natsimikiza mtima nazo.’ (2 Timoteo 3:14, 15) Makolo aumulungu angaike mozungulira ana awo chisonkhezero cha miyoyo yawo yopereka chitsanzo, kupereka kwa achichepere awo chidziŵitso choterecho chonga unansi wawo ndi Mulungu, chizolowezi, ndipo chiŵeruzo cha uchikulire chingapereke. Zitatsogozedwa molondola, zoyesayesazi sizimaiwalidwa ndi achichepere.—Miyambo 22:6.
16. Nchiyani chimene ana anu ayenera kuwona m’chitsanzo chanu ndi kuphunzitsa?
16 Mwachitsanzo ndi kuphunzitsa, thandizani ana anu kuwona mmene mzera umaikidwira mowonekera bwino pakati pa gulu la Yehova ndi la Satana. Asonyezeni iwo kuti sipangakhale kugonjera moyanjana ndi dziko iri, kuti Akristu afunikira kutsutsa zinthu zake zonyenga, zosangalatsa zopanda umulungu, zikhumbo, ndi mayanjano. (1 Akorinto 15:33; 2 Akorinto 4:2) Mwa mkhalidwe wanu, limodzinso ndi kuphunzitsa ndi chitsanzo, lolani achichepere anu kuwona kupanda pake kumene zosangulutsa za kudziko ziri nako, ndi kunyengedwa kumene anthu a kudziko ali nako atayerekezedwa ndi Mboni za Yehova. Longosolani mmene Mulungu wakutsogolerani inu kupyolera mwa mzimu wake woyera, wakusungani inu kuchoka ku kusokera kulowa njira zomwe zikanatsogolera ku kusautsidwa, wakusungirani inu m’nthaŵi za kukanthidwa ndi chisoni. Musayese kupanga kuphophonya kwa kulingalira kuti ngati achichepere anu aloledwa kuthamanga m’njira zakudziko za kunyada, zikhumbo, kupusa, ndi uchitsiru, iwo adzakhala akhulupiriri. Dziko iri lisanatchere msampha ana anu, achinjirizeni iwo kuchokera ku zisonkhezero zake zoipa ndipo athandizeni iwo kuzika zokonda ndi ziyembekezo zawo mwa Yehova.
Kuyang’ana Kupyora pa Ubatizo
17. (a) Nchifukwa ninji Akristu obatizidwa ena amavutika ndi kugwa kwauzimu? (b) Ndimotani mmene tiyenera kuwonera kudzipereka kwathu?
17 Kaya muli wachichepere kapena wachikulire, mosakaikira wophunzira wopita ku ubatizo amafuna kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Chotero nchifukwa ninji Akristu ena obatizidwa amakumana ndi kugwa kwauzimu? Ngakhale kuti nsonga zosiyanasiyana zingalowetsedwemo, pamawonekera kukhala chochititsa chenicheni chimodzi—kulephera kumvetsetsa zonse zomwe zimatanthauzidwa ndi kudzipereka. Sikuli nkhani ya kudzipereka ife eni ku ntchito. Chimenecho chingatisunge ife kukhala otanganitsidwa koma sichikatipanga ife kukhala anthu auzimu. Tifunikira kukumbukira kuti ndife odzipereka osati ku ntchito koma kwa Munthu—Yehova Mulungu. Ichi chimatithandiza ife kupewa kuphophonya kwa kuwona kudzipereka kwathu monga sitepi wamba lomwe tinafunikira kutenga tisanayambe ntchito. Kupanga kudzipereka kuyenera kuwonedwa monga kulowa mu unansi wofunika kwambiri womwe nthaŵi zonse umafunikira kutetezeredwa ndi kusungiriridwa. Mu kawonedweka, tiri ndi chitsanzo cha Yesu Kristu. Olongosola kachitidwe kake kochokera ku mtima pamene anadzipereka iyemwini kwa Yehova ali mawu a ulosi awa: “Ndadza . . . Kuchita chikondwero chanu, kundikonda, Mulungu wanga, ndipo malamulo anu ali mkati mwa mtima mwanga.”—Salmo 40:6-8; Ahebri 10:5-10.
18. Ndimotani mmene lamulo la Mulungu linaliri “mkati mwa mtima” wa Yesu?
18 Ndimotani mmene chinaliri kuti lamulo la Yehova linali “mkati mwa mtima” wa Yesu? Iye anauza mlembi Wachiyuda kuti Yehova Mulungu wathu ali mmodzi ndipo palibe wina, chotero kugogomezera ukulu wa Yehova. Kenaka Yesu anasonyeza kuti nsonga ya lamulo la Mulungu imaphatikizapo kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, kumvetsetsa, ndi mphamvu, pamene tikukonda mnansi wathu monga ife eni. (Marko 12:28-34) Chimenecho ndicho chifukwa chachikulu chimene Yesu anakhoza kunena kuti, ‘ndikonda kuchita chifuniro cha Mulungu.’ Iye anali wokhoza kumamatira ku njira yake mokhulupirika mosasamala kanthu za ziyeso zokulira ndi kuvutika, osati kokha chifukwa chakuti iye anawona chimenechi kukhala ntchito yabwino koma chifukwa cha unansi wake wathithithi ndi Yehova Mulungu. Ngati tivomereza mofananamo ukulu wa Yehova ndi kumkonda iye ndi kugwirizana kosasweka, tidzakhalirira ku kudzipereka kwathu ndi ubatizo.
19. Ndi kugwirizana kotani kumene kulipo pakati pa unansi wathu ndi Yehova ndi ntchito imene timachita?
19 Pali, ndithudi, kugwirizana pakati pa unansi wathu ndi Mulungu ndi ntchito imene timachita. Timasonyeza chikondi kaamba ka Yehova mwa kuchita ntchito yolalikira Ufumu. M’chiyang’aniro cha ichi, malemu Grant Suiter, yemwe kale anali chiwalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, pa nthaŵi imodzi analemba kuti: “Pamene ndinamvetsera kwa [woyang’anira wina woyendayenda] akulankhula za mwaŵi wa kutumikira Yehova ndi thayo la kuchita tero, ndinazindikira chimene ndinayenera kuchita ndi chimene ndinafuna kuchita. Chotero ndinapanga kudzipereka kwaumwini kwa Yehova, ndipo chifupifupi pa nthaŵi imodzimodziyo ziwalo zina za banja langa zinateronso. Pa October 10, 1926, mu San Jose, California, tonsefe pamodzi tinazindikiritsa kudzipereka kwathu kwa Yehova Mulungu mwa kumizidwa m’madzi. . . . Pambuyo pa ubatizowo . . . atate anga ananena kwa mkulu woyang’anira ubatizo kuti: ‘Anthu inu mumapita kunja ndi mabukhu, kodi simumatero? Tikufuna kuchita ntchito imeneyo, nafenso, tsopano.’ Chotero banja lathu linayamba kutulukira mu utumiki wa m’munda.” Lerolino, anthu oyeneretsedwa amayamba kukhala ndi kugawanamo kwatanthauzo mu utumiki wa m’munda asanabatizidwe.
Ubatizo Ungatipulumutse Ife
20, 21. (a) Ndi mwanjira yotani mmene akapolo a Yehova ‘amaikidwira chizindikiro’? (b) Kodi “chizindikiro” chimenechi nchiyani, ndipo kukhala nacho kumatanthauza chiyani?
20 Ndi ntchito zathu, tingasonyeze kuti “tiri a Yehova.” Nkulekeranji, popeza kuti chipulumutso chimadalira pa kugwira ntchito mokhulupirika monga akapolo ake odzipereka! (Aroma 6:20-23; 14:7, 8) Mu nthaŵi zakale, akapolo kaŵirikaŵiri anaikidwa zizindikiro pa mphumi. Mwa ntchito ya kulalikira lerolino, oimira ‘munthu wovala bafuta’—otsalira a atsatiri odzozedwa a Yesu—‘akuika chizindikiro’ awo omwe adzapulumuka mapeto a dongosolo lino. Mu ntchito imeneyi odzozedwa akuthandizidwa ndi oyanjana nawo awo, “nkhosa zina.” (Ezekieli 9:1-7; Yohane 10:16) Ndipo kodi nchiyani chimene chiri “chizindikiro”? Chiri umboni wakuti tiri odzipereka kwa Yehova ndipo ndife ophunzira obatizidwa a Yesu omwe ali ndi umunthu wonga wa Kristu.
21 Makamaka tsopano ndi pamene chiri chofunika kwambiri kuti tikhale ndi “chizindikiro” ndi kuchisungirira icho, popeza kuti tiri ozama mu “masiku otsiriza.” (Danieli 12:4) Kuti tipulumutsidwe tiyenera ‘kupirira kufikira ku mapeto’ a moyo wathu ulipowu kapena a dongosolo lino. (Mateyu 24:13) Kokha ngati ife chotero tikhalabe okhulupirika monga mboni za Yehova ndi pamene ubatizo udzatipulumutsa.
Mafunso kaamba ka Kubwereramo
◻ Kuti tipulumutsidwe, nchiyani chimene chikufunikira kwa ife?
◻ Nchifukwa ninji akulu amakhala ndi kukambitsirana ndi awo okhumba kubatizidwa?
◻ Nchiyani chimene makolo angachite kupatsa ana awo chitsogozo chauzimu chomwe chimatsogolera ku ubatizo?
◻ Kodi timapanga kudzipereka ku ntchito?
◻ Ndimotani mmene ubatizo ungatipulumutsire ife?
[Chithunzi patsamba 16]
Kodi mumadziŵa mmene ubatizo umafananira ndi kupulumutsidwa kwa Nowa ndi banja lake m’chingalawa?
[Chithunzi patsamba 18]
Kudzipereka ndi ubatizo kumapindulitsa anthu achichepere. Kodi mumadziŵa kuti ndimotani?