Machitidwe a Atumwi
18 Kenako Paulo anachoka ku Atene nʼkupita ku Korinto. 2 Kumeneko anapeza Myuda wina dzina lake Akula,+ wa ku Ponto. Iyeyu pamodzi ndi mkazi wake Purisila, anali atangofika kumene kuchokera ku Italy, chifukwa Kalaudiyo anali atalamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Choncho Paulo anapita kunyumba kwawo. 3 Popeza ntchito yawo inali imodzi, anakhala kunyumba kwawoko. Iwo ankagwirira ntchito limodzi,+ chifukwa onse anali opanga matenti. 4 Paulo ankakamba nkhani mʼsunagoge+ tsiku la sabata lililonse+ ndipo ankakopa Ayuda ndi Agiriki.
5 Sila+ ndi Timoteyo+ atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu. Iye ankachitira umboni kwa Ayuda ndiponso kuwatsimikizira kuti Yesu ndiyedi Khristu.+ 6 Koma iwo atapitiriza kumutsutsa ndiponso kumunyoza, iye anakutumula zovala zake+ nʼkuwauza kuti: “Magazi anu akhale pamutu panu.+ Ine ndilibe mlandu.+ Kuyambira panopa ndizipita kwa anthu a mitundu ina.”+ 7 Zitatero, iye anachoka kumeneko* nʼkupita kunyumba ya munthu wina dzina lake Titiyo Yusito. Munthuyu anali wolambira Mulungu ndipo nyumba yake inali moyandikana ndi sunagoge. 8 Kirisipo,+ mtsogoleri wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye pamodzi ndi anthu onse a mʼbanja lake. Ndipo anthu ambiri a ku Korinto, amene anamva uthenga wabwino, anayamba kukhulupirira nʼkubatizidwa. 9 Komanso usiku, Ambuye anauza Paulo mʼmasomphenya kuti: “Usaope, pitiriza kulankhula. Usakhale chete, 10 chifukwa ine ndili nawe.+ Palibe munthu amene adzakukhudze nʼkukuvulaza, popeza ndili ndi anthu ambiri mumzindawu.” 11 Choncho anakhala kumeneko chaka ndi miyezi 6, akuwaphunzitsa mawu a Mulungu.
12 Pamene Galiyo anali bwanamkubwa* wa Akaya, Ayuda ananyamuka mogwirizana nʼkuukira Paulo ndipo anamutengera kumpando woweruzira milandu. 13 Kumeneko iwo anati: “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mʼnjira yosemphana ndi chilamulo.” 14 Koma pamene Paulo ankati azitsegula pakamwa, Galiyo anauza Ayudawo kuti: “Ayuda inu, chikanakhala cholakwa china kapena mlandu waukulu, ndithu ndikanaleza mtima nʼkukumvetserani. 15 Koma ngati nkhani yake ili yokhudza mikangano pa mawu, mayina ndi chilamulo chanu,+ zimenezo muthane nazo nokha. Ine sindikufuna kuti ndikhale woweruza nkhani zoterezi.” 16 Atatero anawauza kuti achoke kumpando woweruzira milanduwo. 17 Zitatero, onse anagwira Sositene,+ mtsogoleri wa sunagoge nʼkuyamba kumumenya pafupi ndi mpando woweruzira milanduwo. Koma zimenezi sizinamukhudze Galiyo ngakhale pangʼono.
18 Paulo atakhala kumeneko kwa masiku ndithu, anatsanzikana ndi abalewo ndipo anapitiriza ulendo wake wapamadzi kulowera ku Siriya. Pa ulendowu anapita limodzi ndi Purisila ndi Akula. Paulo anameta tsitsi lake ku Kenkereya+ chifukwa cha lonjezo limene anachita. 19 Choncho onse anafika ku Efeso, ndipo anzakewo anawasiya kumeneko. Koma iye yekha analowa mʼsunagoge nʼkuyamba kukambirana ndi Ayuda.+ 20 Ngakhale kuti anamupempha mobwerezabwereza kuti akhale nawo kwa masiku ambiri, iye sanalole. 21 Mʼmalomwake, anatsanzikana nawo nʼkuwauza kuti: “Yehova* akalola ndidzabweranso kudzakuonani.” Choncho ananyamuka ku Efeso ulendo wapanyanja 22 ndipo anafika ku Kaisareya. Kenako anapita* kukapereka moni ku mpingo ndipo pambuyo pake anapita ku Antiokeya.+
23 Atakhala kumeneko kwa kanthawi, ananyamuka nʼkuyamba kuyenda malo osiyanasiyana mʼchigawo cha Galatiya ndi Fulugiya+ ndipo ankalimbikitsa ophunzira onse.+
24 Tsopano Myuda wina dzina lake Apolo,+ wa ku Alekizandiriya, amene ankalankhula mwaluso, anafika ku Efeso. Iyeyu ankadziwanso bwino Malemba. 25 Mwamuna ameneyu anaphunzitsidwa* njira ya Yehova.* Iye anali wodzipereka kwambiri chifukwa chakuti anali ndi mzimu woyera, ndipo ankalankhula ndi kuphunzitsa molondola za Yesu. Koma ankangodziwa za ubatizo wa Yohane wokha. 26 Munthu ameneyu anayamba kulankhula molimba mtima musunagoge. Ndiyeno Purisila ndi Akula+ atamumvetsera, anamutenga nʼkumufotokozera njira ya Mulungu molondola. 27 Ndiponso, popeza kuti ankafunitsitsa kupita ku Akaya, abalewo analembera ophunzira kumeneko. Anawalimbikitsa kuti amulandire ndi manja awiri. Choncho iye atafika kumeneko, anathandiza kwambiri anthu amene anali atakhulupirira chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. 28 Chifukwa iye anawatsimikizira Ayuda poyera komanso mwamphamvu kuti anali olakwa, ndipo anagwiritsa ntchito Malemba posonyeza kuti Yesu ndiyedi Khristu.+