NKHANI YOPHUNZIRA 47
Kodi Tingatani Kuti Tizikondana Kwambiri?
“Tiyeni tipitirize kukondana, chifukwa chikondi chimachokera kwa Mulungu.”—1 YOH. 4:7.
NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo ananena kuti chikondi ndi khalidwe ‘lalikulu’? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
PAMENE mtumwi Paulo ankafotokoza za chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi, anamaliza ndi mawu akuti “chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.” (1 Akor. 13:13) N’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Chifukwa m’tsogolomu sitidzafunikanso kukhulupirira malonjezo a Mulungu okhudza dziko lapansi latsopano, kapenanso kukhala ndi chiyembekezo chakuti malonjezowo adzakwaniritsidwa chifukwa zidzakhala zitakwaniritsidwa kale. Koma nthawi zonse tidzafunika kukonda Yehova ndiponso anthu. Ndipotu chikondichi chidzapitiriza kukula mpaka kalekale.
2 Popeza tidzafunika kukhala ndi chikondi chimenechi. Choyamba tiyeni tikambirane mafunso atatu. Loyamba, n’chifukwa chiyani tiyenera kumakondana? Lachiwiri, kodi tingasonyeze bwanji kuti timakondana? Ndipo lachitatu, kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri anzathu?
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUMAKONDANA?
3. Kodi ndi zifukwa ziti zomwe zimatichititsa kuti tizikondana?
3 N’chifukwa chiyani zili zofunika kuti tizikondana? Chifukwa chimodzi n’chakuti chikondi ndi chizindikiro cha Akhristu enieni. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Komanso chikondi chimathandiza kuti tizigwirizana. Paulo ananena kuti chikondi “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akol. 3:14) Koma pali chifukwa chinanso chachikulu kwambiri chotichititsa kuti tizikondana. Mtumwi Yohane anauza Akhristu anzake kuti: “Munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.” (1 Yoh. 4:21) Tikamakondana timasonyeza kuti timakondanso Mulungu.
4-5. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kukonda anzathu kumagwirizana ndi kukonda Mulungu.
4 Kodi kukonda Mulungu kumagwirizana bwanji ndi kukonda abale ndi alongo athu? Kuti timvetse, taganizirani kugwirizana komwe kumakhalapo pakati pa mtima wathu ndi mbali zina za thupi lathu. Dokotala akhoza kudziwa ngati mtima wathu uli bwino pogwira pamkono wathu kuti adziwe kagundidwe kake. Ndiye kodi zimenezi zikugwirizana bwanji ndi nkhani ya chikondi?
5 Mofanana ndi dokotala, yemwe amatha kudziwa zokhudza mtima wathu poona kagundidwe kake pamkono, ifenso tikhoza kudziwa ngati timakonda kwambiri Mulungu poona mmene timakondera anzathu. Ngati titaona kuti chikondi chathu kwa Akhristu anzathu chayamba kuchepa, chimenechi chingakhale chizindikiro chakuti chikondi chathu kwa Mulungu chayambanso kuchepa. Koma ngati nthawi zonse timawasonyeza chikondi, chingakhale chizindikiro chakuti timakondanso kwambiri Mulungu.
6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu akasiya kukonda abale ndi alongo limakhala vuto lalikulu? (1 Yohane 4:7-9, 11)
6 Ngati sitikukonda kwambiri abale ndi alongo athu ndiye kuti pali vuto lalikulu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa zingasonyeze kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu suli bwino. Mtumwi Yohane anafotokoza mfundo imeneyi pomwe ananena kuti: “Amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:20) Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Yehova amasangalala nafe pokhapokha ngati ‘timakondana.’—Werengani 1 Yohane 4:7-9, 11.
KODI TIMASONYEZA BWANJI KUTI TIMAKONDANA?
7-8. Kodi tingasonyeze m’njira ziti kuti timakondana?
7 Mawu a Mulungu amatilamula mobwerezabwereza kuti ‘tizikondana.’ (Yoh. 15:12, 17; Aroma 13:8; 1 Ates. 4:9; 1 Pet. 1:22; 1 Yoh. 4:11) Komabe chikondi chimakhala mumtima ndipo palibe munthu amene angaone mumtima mwathu. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda ena? Zolankhula komanso zochita zathu ndi zimene zingasonyeze.
8 Pali njira zosiyanasiyana zomwe tingasonyezere kuti timakonda abale ndi alongo athu. Mwachitsanzo, Malemba amatilimbikitsa kuti: “Muziuzana zoona.” (Zek. 8:16) “Sungani mtendere pakati panu.” (Maliko 9:50) “Pa nkhani yosonyezana ulemu, muziyamba ndi inuyo.” (Aroma 12:10) “Muzilandirana.” (Aroma 15:7) “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana.” (Akol. 3:13) “Pitirizani kunyamulirana zinthu zolemera.” (Agal. 6:2) “Pitirizani kulimbikitsana.” (1 Ates. 4:18) “Pitirizani kutonthozana.” (1 Ates. 5:11) ‘Muzipemphererana.’—Yak. 5:16.
9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kutonthoza ena ndi njira yofunika yosonyezera chikondi? (Onaninso chithunzi.)
9 Tiyeni tikambirane njira imodzi imene yatchulidwa m’ndime yapitayi, yomwe tingasonyezere kuti timakonda ena. Tikambirana zimene mtumwi Paulo ananena kuti: “Pitirizani kutonthozana.” N’chifukwa chiyani kutonthoza ena kumasonyeza kuti tili ndi chikondi? Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo linanena kuti mawu akuti “kutonthoza” omwe Paulo anagwiritsa ntchito amatanthauza “kuima pafupi ndi munthu kuti timulimbikitse pamene wakumana ndi vuto lalikulu.” Choncho tikatonthoza m’Khristu mnzathu yemwe wakumana ndi vuto, timamuthandiza kuti aimirire n’kupitiriza kuyenda panjira yokalandira moyo. Nthawi iliyonse yomwe tatonthoza m’bale kapena mlongo, timasonyeza kuti timakonda Akhristu anzathu.—2 Akor. 7:6, 7, 13.
10. Kodi chifundo chimagwirizana bwanji ndi kutonthoza ena?
10 Kutonthoza ena n’kogwirizana ndi chifundo. N’chifukwa chiyani tikutero? Mtima wachifundo ndi umene umalimbikitsa munthu kuti atonthoze ena komanso kuwathandiza. Choncho timayamba ndi kukhala ndi chifundo, kenako timatonthoza ena. Paulo anagwirizanitsa chifundo cha Yehova ndi zimene amachita potonthoza ena. Iye ananena kuti Yehova ndi “Bambo wachifundo chachikulu ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse.” (2 Akor. 1:3) Paulo anagwiritsa ntchito mawu akuti “chifundo chachikulu” pofotokoza mmene wina amamvera ponena za ena. Choncho “Mulungu amatchedwa Bambo, kapena kuti Mwiniwake wa chifundo chachikulu, chifukwa chifundocho chimachokera kwa iye.” Choncho chifundo chimenecho ndi chimene chimamuchititsa kuti azititonthoza “pa mayesero athu onse.” (2 Akor. 1:4) Mofanana ndi madzi a pakasupe omwe amatsitsimula anthu omwe ali ndi ludzu, Yehova amatsitsimula komanso kutonthoza anthu omwe akumana ndi mavuto. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova potonthoza ena komanso kusonyeza chifundo? Tingachite zimenezi poyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene angatithandize kuti titonthoze anthu ena. Tiyeni tione ena mwa makhalidwe amenewa.
11. Mogwirizana ndi Akolose 3:12 ndiponso 1 Petulo 3:8, kodi ndi makhalidwe ati omwe tiyenera kukhala nawo kuti tizikonda komanso kutonthoza ena?
11 N’chiyani chingatithandize kukhala ndi chikondi chimene chimafunika kuti tizitonthozana tsiku ndi tsiku? Tiyenera kukhala ndi makhalidwe monga kumvera ena chisoni, kukonda abale komanso kukoma mtima. (Werengani Akolose 3:12; 1 Petulo 3:8.) Kodi makhalidwe amenewa angatithandize bwanji? Tikamakhala ndi chifundo komanso makhalidwe amene tatchulawa, sitingachitire mwina koma kutonthoza ena. Paja Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chabwino chamumtima mwake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma choipa chamumtima mwake.” (Mat. 12:34, 35) Kutonthoza abale ndi alongo athu omwe akumana ndi mavuto ndi njira yofunika kwambiri yomwe tingasonyezere kuti timawakonda.
KODI TINGATANI KUTI TIZIKONDANA KWAMBIRI?
12. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala? (b) Kodi tsopano tikambirana funso liti?
12 Tonsefe tiyenera ‘kupitiriza kukondana.’ (1 Yoh. 4:7) Koma tiyenera kukumbukira kuti Yesu anachenjeza kuti “chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.” (Mat. 24:12) Yesu sankatanthauza kuti chikondi cha ophunzira ake ambiri chidzachepa. Ngakhale zili choncho, tiyenera kukhala osamala kuti tisatengere mtima wopanda chikondi womwe ndi wofala m’dzikoli. Poganizira mfundo imeneyi, tiyeni tikambirane funso lina lofunika. Kodi pali njira yodziwira ngati timakonda kwambiri abale athu?
13. Kodi tingadziwe bwanji ngati timakonda kwambiri abale athu?
13 Njira imodzi yodziwira ngati timakonda kwambiri abale athu ndi kuona zimene timachita pa moyo wathu. (2 Akor. 8:8) Mtumwi Petulo anatchula chimodzi mwa zinthuzi pomwe anati: “Koposa zonse, muzikondana kwambiri chifukwa chikondi chimakwirira machimo ochuluka.” (1 Pet. 4:8) Choncho zimene timachita abale athu akalakwitsa zinthu, zingasonyeze ngati timawakonda kwambiri kapena ayi.
14. Mogwirizana ndi 1 Petulo 4:8, kodi tiyenera kukhala ndi chikondi chiti? Perekani chitsanzo.
14 Tiyeni tiwaone bwinobwino mawu a Petulowa. Mbali yoyamba ya vesi 8 ikufotokoza mtundu wa chikondi chomwe tiyenera kukhala nacho. Yanena kuti tizikondana kwambiri. Mawu amene Petulo anagwiritsa ntchito akuti “muzikondana kwambiri,” angatanthauze “kutambasula.” Mbali yachiwiri ya vesili ikufotokoza zotsatira za chikondi chimenechi. Ikuti chimakwirira machimo ochuluka a abale athu. Zili ngati timagwira chikondichi ndi manja awiri ngati mmene tingagwirire nsalu, n’kuchitambasula kuti chiphimbe, osati machimo ochepa, koma “machimo ochuluka.” Mawu akuti kuphimba, kapena kuti “kukwirira,” akufotokoza za kukhululuka. Mofanana ndi nsalu yomwe ingaphimbe malo akuda pa chovala, chikondi chimaphimba zimene abale athu amalakwitsa.
15. Kodi kukonda kwambiri abale ndi alongo athu kungatithandize kuchita chiyani? (Akolose 3:13)
15 Tiyenera kumakonda kwambiri abale athu moti tikhoza kuwakhululukira zolakwa zawo, ngakhale pamene kuchita zimenezi kungakhale kovuta. (Werengani Akolose 3:13.) Tikakhululukira ena timasonyeza kuti timawakonda kwambiri komanso timafuna kusangalatsa Yehova. Kodi n’chiyaninso chingatithandize kuti tizinyalanyaza zinthu zing’onozing’ono zimene amalakwitsa kapenanso makhalidwe awo amene satisangalatsa?
16-17. Kodi n’chiyaninso chingatithandize kunyalanyaza zinthu zing’onozing’ono zimene ena amalakwitsa? Perekani chitsanzo. (Onaninso chithunzi.)
16 Muziganizira kwambiri makhalidwe abwino amene abale ndi alongo ali nawo osati zimene amalakwitsa. Tiyerekeze kuti muli pagulu limodzi ndi abale ndi alongo. Mukucheza mosangalala ndipo pamapeto pake mukujambulitsa chithunzi. Ndiye mukujambula zithunzi ziwiri kapena zitatu kuopera kuti mwina choyambacho sichinaoneke bwino. Apa tsopano muli ndi zithunzi zitatu. Ndiye pachithunzi chimodzicho m’bale wina sakumwetulira bwino. Kodi zikatero mumatani? Mumangochidilita chifukwa muli ndi zithunzi zina ziwiri pamene aliyense akumwetulira bwino.
17 Zithunzizi zili ngati zinthu zosiyanasiyana zomwe timakumbukira zokhudza anthu ena. Pali zabwino zambiri zimene timakumbukira zomwe tinachita ndi abale ndi alongo athu. Koma bwanji ngati pa nthawi ina m’bale kapena mlongo analankhula kapena kuchita zinthu mosaganizira ena? Kodi tiyenera kutani? Ndi bwino kungozichotsa m’maganizo mwathu ngati mmene tingachitire ndi zithunzi zija. (Miy. 19:11; Aef. 4:32) Tikhoza kuchotsa zimenezi m’maganizo mwathu chifukwa pali zabwino zambiri zokhudza m’bale wathuyo zomwe tingamazikumbukire. Zinthu zabwinozo ndi zimene tiyenera kuzisunga m’maganizo mwathu.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUMAKONDANA KWAMBIRI MASIKU ANO?
18. Kodi munkhaniyi takambirana mfundo zikuluzikulu ziti zokhudza chikondi?
18 N’chifukwa chiyani tiyenera kukondana kwambiri masiku ano? Taona kuti tikamakonda kwambiri abale ndi alongo athu, timasonyeza kuti timakonda Yehova. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale ndi alongo athu? Njira imodzi ndi kuwalimbikitsa kapena kuwatonthoza. Chifundo ndi chimene chingatilimbikitse kuti ‘tizipitiriza kutonthozana.’ Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri abale athu? Tingatero poyesetsa kuti tiziwakhululukira zimene amalakwitsa.
19. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tizikondana kwambiri masiku ano?
19 N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tizikondana kwambiri masiku ano? Petulo anapereka chifukwa chake pomwe ananena kuti: “Mapeto a zinthu zonse ayandikira. Choncho . . . muzikondana kwambiri.” (1 Pet. 4:7, 8) Kodi chichitike n’chiyani pamene mapeto akuyandikira kwambiri? Ponena za otsatira ake, Yesu ananena kuti: “Anthu a mitundu yonse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.” (Mat. 24:9) Kuti tithe kupirira tiyenera kumagwirizana kwambiri. Tikatero, Satana sadzatha kutigawanitsa chifukwa chakuti tili ndi chikondi chimene “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa china chilichonse.”—Akol. 3:14; Afil. 2:1, 2.
NYIMBO NA. 130 Muzikhululukirana
a Kuposa kale lonse, n’zofunika kwambiri kuti tizikonda abale ndi alongo athu. N’chifukwa chiyani tikutero, nanga tingatani kuti tizikondana kwambiri?