Yehova Amadziwa Kupulumutsa Anthu Ake
“Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.”—2 PET. 2:9.
N’CHIFUKWA CHIYANI SITIYENERA KUKAYIKIRA ZOTI YEHOVA:
Ali ndi mphamvu zokwaniritsa zolinga zake pa nthawi yoyenera?
Adzagwiritsa ntchito mphamvu zake kuti apulumutse anthu ake?
Amadziwa mmene zinthu zidzachitikire pa “chisautso chachikulu”?
1. Kodi chidzachitike n’chiyani pa “chisautso chachikulu”?
DZIKO la Satanali lidzawonongedwa modzidzimutsa kwambiri. (1 Ates. 5:2, 3) Pa “tsiku lalikulu la Yehova,” padziko lonse padzakhala chipwirikiti. (Zef. 1:14-17) Ndipo mavuto ndi nkhawa zidzangokhala zochitika za tsiku ndi tsiku. Idzakhala nthawi ya mavuto aakulu ndipo chisautso chake ndi choti “sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano.”—Werengani Mateyu 24:21, 22.
2, 3. (a) Kodi anthu a Mulungu adzakumana ndi zotani pa nthawi ya “chisautso chachikulu”? (b) N’chiyani chingatipatse mphamvu kuti tisaope zimene zili m’tsogolo?
2 “Chisautso chachikulu” chikamadzafika pachimake, “Gogi wa kudziko la Magogi” adzaukira koopsa anthu a Mulungu. Pa nthawi imeneyo, “chigulu chachikulu chankhondo” chidzaukira anthu a Mulungu ngati ‘mitambo yodzaphimba dziko.’ (Ezek. 38:2, 14-16) Palibe anthu amene adzateteze anthu a Yehova. Mulungu yekha ndi amene adzawapulumutse. Kodi anthu a Mulungu adzatani adani awo akadzabwera kuti awawononge?
3 Ngati ndinu mtumiki wa Yehova, kodi mumakhulupirira kuti Yehova adzapulumutsadi anthu ake pa “chisautso chachikulu”? Mtumwi Petulo analemba kuti: “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero. Koma anthu osalungama amawasungira tsiku loweruza kuti adzawawononge.” (2 Pet. 2:9) Kuganizira mmene Yehova anapulumutsira anthu m’mbuyomu kungatipatse mphamvu kuti tisaope zimene zili m’tsogolo. Tiyeni tione zitsanzo zitatu zimene zingatithandize kukhulupirira kwambiri kuti Yehova ali ndi mphamvu zopulumutsa anthu ake.
ANAPULUMUKA CHIGUMULA CHA PADZIKO LONSE
4. N’chiyani chinayenera kuchitika Chigumula chisanafike?
4 Choyamba, tiyeni tikambirane nkhani ya Chigumula cha m’masiku a Nowa. Chigumula chisanayambe, panali zinthu zina zimene zinayenera kuchitika. Panayenera kuchitika ntchito yovuta yomanga chingalawa ndi kulowetsamo zinyama. Nkhani ya m’buku la Genesis imasonyeza kuti Yehova anaikiratu nthawi yoti adzabweretse Chigumula. Sikuti anayembekezera kuti chingalawa chimangidwe kenako n’kumaganiza za tsiku loti Chigumula chiyambe kuopera kuti chidzafika chingalawa chisanathe. Mulungu anaikiratu nthawiyi kalekale asanauze Nowa zoti amange chingalawa. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?
5. Kodi Yehova analengeza uthenga wotani pa Genesis 6:3, ndipo anaulengeza liti?
5 Baibulo limatiuza kuti Yehova analengeza kumwamba zimene anasankha kuchita. Malinga ndi Genesis 6:3, Mulungu anati: “Mzimu wanga supitiriza mpaka kalekale kulezera mtima anthu, popeza alinso athupi. Choncho, masiku a moyo wawo adzangokhala zaka 120.” Ponena zimenezi sikuti ankatanthauza kuti amenewa ndi malire a zaka zimene anthu azikhala moyo. Apa ankalengeza nthawi imene adzachotsa onse osaopa Mulungu n’cholinga choti ayeretse dziko.a Popeza Chigumula chinayamba mu 2370 B.C.E., Mulungu ayenera kuti ananena mawu amenewa mu 2490 B.C.E. Apa n’kuti Nowa ali ndi zaka 480. (Gen. 7:6) Ndiyeno patapita zaka pafupifupi 20, mu 2470 B.C.E., Nowa anayamba kubereka ana. (Gen. 5:32) Pa nthawiyi panali patatsala pafupifupi zaka 100 kuti Chigumula chichitike koma Yehova anali asanauzebe Nowa ntchito yapadera imene anayenera kugwira kuti anthu apulumuke. Kodi Mulungu anadikira nthawi yaitali bwanji asanauze Nowa?
6. Kodi ndi liti pamene Yehova anauza Nowa kuti amange chingalawa?
6 Zikuoneka kuti Yehova anayembekeza zaka zambiri asanauze Nowa zimene Iye ankafuna kuchita. N’chifukwa chiyani tikutero? Baibulo limasonyeza kuti pa nthawi imene Mulungu ankalamula Nowa kuti amange chingalawa, ana ake anali atakula ndiponso kukwatira. Yehova anamuuza kuti: “Ndikupanga pangano ndi iwe. Iweyo udzalowe m’chingalawacho limodzi ndi ana ako, mkazi wako, ndi akazi a ana ako.” (Gen. 6:9-18) N’kutheka kuti pamene Nowa ankauzidwa zoti amange chingalawa kunali kutangotsala zaka 40 kapena 50 kuti Chigumula chichitike.
7. (a) Kodi Nowa ndi banja lake anasonyeza bwanji chikhulupiriro? (b) Kodi ndi liti pamene Mulungu anauza Nowa za tsiku limene Chigumula chiyambe?
7 Pamene ntchito yomanga chingalawa inkapitirira, Nowa ndi banja lake sankadziwa mmene Mulungu adzabweretsere Chigumula ndiponso nthawi imene chidzayambe. Koma ngakhale kuti sankadziwa zinthu zimenezi iwo sanasiye kumanga chingalawa. Pa nkhaniyi, Malemba amati: “Nowa anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.” (Gen. 6:22) Yehova anatchula tsiku limene Chigumula chiyambe kutangotsala masiku 7 koma masiku amenewa anali okwanira kuti Nowa ndi banja lake alowetse zinyama m’chingalawa. Ndiyeno “m’chaka cha 600 cha moyo wa Nowa, m’mwezi wachiwiri, pa tsiku la 17 la mweziwo” zotsekera madzi akumwamba zinatseguka ndipo pa nthawiyi Nowa anali atamaliza kukonzekera.—Gen. 7:1-5, 11.
8. Kodi nkhani ya Chigumula imatithandiza bwanji kuti tisamakayikire zoti Yehova amadziwa nthawi yabwino yopulumutsira anthu ake?
8 Nkhani ya Chigumula imasonyeza kuti Yehova amadziwa nthawi yoyenera kuchita zinthu komanso njira yabwino yopulumutsira anthu. Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, sitiyenera kukayikira kuti zolinga za Yehova zidzachitika pa ‘tsiku ndi ola lake’ lenileni kapena kuti pa nthawi yake yoikidwiratu.—Mat. 24:36; werengani Habakuku 2:3.
ANAPULUMUTSIDWA PA NYANJA YOFIIRA
9, 10. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji athu ake kuti akole gulu la asilikali a Iguputo?
9 Tafikapa, taona kuti Yehova ali ndi mphamvu zokwaniritsa zolinga zake pa nthawi yoyenera. Chitsanzo chachiwiri chimene tikambirane chitithandiza kuona chifukwa china chimene tiyenera kukhulupirira kuti Yehova adzapulumutsa anthu ake. Iye adzagwiritsa ntchito mphamvu zake kuti aonetsetse kuti chifuniro chake chachitika. Yehova alidi ndi mphamvu zopulumutsa atumiki ake moti nthawi zina amagwiritsa ntchito atumiki akewo kuti akole adani ake mu msampha. Izi ndi zimene zinachitika atapulumutsa Aisiraeli ku ukapolo wa ku Iguputo.
10 N’kutheka kuti Aisiraeli amene ananyamuka ku Iguputo anali pafupifupi 3 miliyoni. Yehova anagwiritsa ntchito Mose kuti atsogolere Aisiraeli m’njira yoti Farao aziganiza kuti iwo asokonezeka ndipo akungoyendayenda. (Werengani Ekisodo 14:1-4.) Farao ataona zimenezi, anakopeka n’kuyamba kuwatsatira ndi gulu la asilikali ake ndipo ankaganiza kuti asowa kothawira pa Nyanja Yofiira. Aisiraeli ankaoneka kuti alibiretu mtengo wogwira. (Eks. 14:5-10) Komatu umu si mmene zinthu zinalili. Tikutero chifukwa chakuti Yehova anali atatsala pang’ono kulowerera kuti awapulumutse.
11, 12. (a) Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu ake? (b) Kodi zotsatira zake zinali zotani ndipo zimenezi zikutiphunzitsa chiyani za Yehova?
11 Ndiyeno “mtambo woima njo ngati chipilala” umene unkatsogolera Aisiraeli unachoka kutsogolo n’kukaima kumbuyo kwawo. Mtambowu unachititsa kuti asilikali a Farao akhale mu mdima ndipo asapeze Aisiraeliwo. Koma unkaunikira Aisiraeli ngakhale usiku. (Werengani Ekisodo 14:19, 20.) Kenako Yehova anabweretsa mphepo yamphamvu yakum’mawa imene inayamba “kugawa nyanjayo . . . ndi kuumitsa pansi pake.” Zimenezi ziyenera kuti zinatenga nthawi ndithu chifukwa nkhaniyo imati: “Patapita nthawi ana a Isiraeli anadutsa pakati pa nyanja, panthaka youma.” Tikayerekezera ndi magaleta a asilikali a Farao, Aisiraeli ankayenda pang’onopang’ono kwambiri. Koma sizikanatheka kuti Aiguputowo apeze Aisiraeli chifukwa chakuti Yehova ankawamenyera nkhondo. Yehova “anachititsa Aiguputowo kusokonezeka. Iye anali kugulula mawilo a magaleta awo moti anali kuwayendetsa movutikira.”—Eks. 14:21-25.
12 Aisiraeli onse atadutsa bwinobwino, Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako ndi kuloza panyanja, kuti madzi abwerere ndi kumiza Aiguputo, magaleta awo ankhondo ndi asilikali awo apamahatchi.” Pamene iwo anayesa kuthawa madziwo, “Yehova anakutumulira Aiguputowo pakatikati pa nyanja. . . . Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.” (Eks. 14:26-28) Apa Yehova anasonyeza kuti ali ndi mphamvu zopulumutsa anthu ake pa vuto lina lililonse.
ANAPULUMUKA PAMENE YERUSALEMU ANKAWONONGEDWA
13. Kodi Yesu anapereka malangizo otani ndipo n’kutheka kuti otsatira ake ankadzifunsa kuti chiyani?
13 Yehova amadziwa mmene zinthu zichitikire pokwaniritsa cholinga chake. Zimene zinachitika powononga Yerusalemu zikusonyeza kuti iye amadziwadi zimenezi. Yehova anagwiritsa ntchito Mwana wake popereka malangizo kwa Akhristu amene ankakhala mu Yerusalemu ndi mu Yudeya. Iye anawauza zimene angachite kuti adzapulumuke mzindawu ukamadzawonongedwa mu 70 C.E. Yesu anati: “Mukadzaona chinthu chonyansa chowononga chimene chinanenedwa kudzera mwa mneneri Danieli chitaimirira m’malo oyera, . . . amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri.” (Mat. 24:15, 16) N’kutheka kuti otsatira a Yesu ankadzifunsa kuti, ‘Kodi ulosiwu ukamadzakwaniritsidwa tidzadziwa bwanji?’
14. N’chiyani chinachitika kuti Akhristu amvetse tanthauzo la zimene Yesu ananena?
14 Patapita zaka zambiri, Akhristu anayamba kuzindikira tanthauzo la zimene Yesu ananena. M’chaka cha 66 C.E., asilikali achiroma motsogoleredwa ndi Cestius Gallus anafika ku Yerusalemu kuti adzaletse Ayuda kupanduka. Pamene Ayuda opandukawo, omwe ankadziwika ndi dzina loti Azeloti, anabisala m’kachisi, asilikali achiroma anayamba kugwetsa kachisiyo. Akhristu omwe anali tcheru anatha kuzindikira mosavuta kuti “chinthu chonyansa” chaima “m’malo oyera” pamene asilikali osalambira Mulungu anafika pampanda wa kachisi ku Yerusalemu. Imeneyi inali nthawi yoti otsatira a Yesu ayambe “kuthawira kumapiri.” Koma kodi akanatha bwanji kutuluka mumzinda womwe unali utazunguliridwa ndi asilikali? Zinthu zinali zitangotsala pang’ono kusintha.
15, 16. (a) Kodi Yesu anapereka malangizo osapita m’mbali ati ndipo n’chifukwa chiyani otsatira ake anafunika kumvera? (b) N’chiyani chidzafunike kuti tipulumuke?
15 Mosayembekezereka, Cestius Gallus limodzi ndi gulu lake la asilikali anayamba kuchoka ku Yerusalemu n’kubwerera kwawo. Ndiyeno Azeloti anayamba kuwathamangitsa. Magulu a asilikaliwa atachoka ku Yerusalemu, otsatira a Yesu anapeza mpata wothawa. Yesu anawalangiza mosapita m’mbali kuti ayenera kusiya chuma chawo n’kunyamuka mwamsanga. (Werengani Mateyu 24:17, 18.) Kodi iwo anafunikadi kunyamuka nthawi yomweyo? Inde anafunikadi kuchita zimenezi. Patangopita masiku ochepa, Azeloti anabwerera n’kuyamba kukakamiza aliyense wokhala ku Yerusalemu ndi Yudeya kuti apandukire Aroma. Zinthu zinayamba kusokonekera kwambiri ku Yerusalemu pamene magulu a Ayuda opandukawo ankamenyana pofuna kulamulira. Mwayi wothawa unayamba kuvuta kwambiri. Ndiyeno pamene Aroma anabwerera mu 70 C.E., zinali zosatheka n’komwe kuti munthu athawe. (Luka 19:43) Aliyense amene anazengereza anasowa kothawira. Koma Akhristu amene anamvera malangizo a Yesu n’kuthawira kumapiri anapulumuka. Iwo anadzionera okha kuti Yehova amadziwa kupulumutsa anthu ake. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa?
16 Pa chisautso chachikulu, Akhristu adzafunika kutsatira malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu ndiponso m’gulu lake. Mwachitsanzo, lamulo la Yesu lakuti anthu adzayambe “kuthawira kumapiri” lili ndi tanthauzo masiku ano. Panopa sitikudziwa kuti kuthawa kwake kudzakhala kotani.b Koma tikudziwa kuti nthawi yotsatira malangizowa ikadzakwana, Yehova adzatifotokozera momveka bwino. Tidzafunika kukhala omvera kuti tipulumuke. Ndiye ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi panopa ndimamvera malangizo amene Yehova akupereka kwa anthu ake? Kodi ndimamvera mwamsanga kapena ndimazengereza?’—Yak. 3:17.
TAPATSIDWA MPHAMVU KUTI TISAOPE ZAM’TSOGOLO
17. Kodi ulosi wa Habakuku ukusonyeza chiyani za nthawi imene anthu a Mulungu adzaukiridwe?
17 Tsopano tiyeni tikambirane za kuukira koopsa kwa Gogi kumene tatchula poyamba kuja. Mu ulosi wogwirizana ndi nkhaniyi, Habakuku anati: “Nditamva mawu ake, m’mimba mwanga munayamba kubwadamuka ndipo milomo yanga inanjenjemera. Mafupa anga anayamba kuwola ndipo ndinanthunthumira chifukwa cha mmene zinthu zinalili. Choncho ndidzayembekezera mofatsa tsiku la nsautso. Tsiku [la Mulungu] limeneli lidzabwera kwa anthu ngati mmene munthu amabwerera kwa adani ake kuti awaukire.” (Hab. 3:16) Atamva kuti anthu a Mulungu adzaukiridwa, m’mimba mwake munapotokola, milomo yake inanjenjemera ndipo analefuka. Zimene Habakuku ananenazi zikusonyeza kuti zidzakhala zoopsa kwambiri pamene Gogi ndi asilikali ake adzatiukira. Koma mneneriyu ankayembekezera mofatsa tsiku lalikulu la Yehova popanda kukayikira kuti Yehova adzapulumutsa anthu ake. Nafenso tikhoza kukhala ndi chikhulupiriro ngati Habakuku.—Hab. 3:18, 19.
18. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa kuukira kwa Gogi? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
18 Nkhani zitatu zimene takambiranazi zikusonyeza bwino kuti Yehova amadziwadi kupulumutsa anthu ake. Cholinga chake sichingalephereke ndipo n’zosachita kufunsa kuti chidzakwaniritsidwa. Kuti tidzaone zimenezi, tiyenera kukhala okhulupirika mpaka mapeto. Kodi Yehova amatithandiza bwanji masiku ano kuti tikhalebe okhulupirika? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
b Werengani Nsanja ya Olonda ya May 1, 1999, tsamba 19.
[Chithunzi patsamba 24]
Kodi Aisiraeli akanaphedwadi ndi asilikali a Farao?