Chenjerani ndi Aphunzitsi Onama!
“Padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu.”—2 PETRO 2:1.
1. Kodi Yuda anafuna kulemba za chiyani, nanga anasinthiranji nkhani yake?
ZODABWITSA! Aphunzitsi onama mumpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba! (Mateyu 7:15; Machitidwe 20:29, 30) Yuda, mbale wa Yesu mwa tate womlera, anadziŵa zimenezo. Iye anati anafuna kulembera okhulupirira anzake “za chipulumutso cha ife tonse,” koma anafotokoza kuti: “Ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro.” Kodi Yuda anasinthiranji nkhani yake? Iye anati, chifukwa “anthu ena anakwaŵira [m’mipingo] m’tseri, . . . akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa.”—Yuda 3, 4.
2. Kodi nchifukwa ninji 2 Petro chaputala 2 akufanana ndi Yuda?
2 Mwachionekere, Yuda analemba kalata yake Petro atangomaliza kulemba kalata yake yachiŵiri. Mosakayikira Yuda anali kudziŵa za kalatayi. Inde, anatchula malingaliro ambiri ofanana m’kalata yake yochenjeza ndiponso yamphamvu. Chotero, pamene tipenda 2 Petro chaputala 2, tidzaona kufanana kwake ndi kalata ya Yuda.
Zotsatira Zake za Ziphunzitso Zonama
3. Kodi zinachitika kale nzotani zomwe Petro akuti zidzachitikanso?
3 Petro atalimbikitsa abale ake kusamalira ulosi, akuti: “Koma padakhalanso pakati pa anthuwo [m’Israyeli wakale] aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu.” (2 Petro 1:14–2:1) Anthu a Mulungu akale analandira ulosi woona, koma analimbananso ndi ziphunzitso zoipitsa za aneneri onama. (Yeremiya 6:13, 14; 28:1-3, 15) “Mwa aneneri a ku Yerusalemu,” analemba Yeremiya, “ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama.”—Yeremiya 23:14.
4. Kodi nchifukwa ninji aphunzitsi onama ayenera kuwonongedwa?
4 Pofotokoza zimene aphunzitsi onama adzachita mumpingo wachikristu, Petro akuti: “Amene adzaloŵa nayo m’tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye [Yesu Kristu] amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.” (2 Petro 2:1; Yuda 4) Zotsatira zake zomaliza za mpatuko umenewo wa m’zaka za zana loyamba ndi Dziko Lachikristu limene tikulidziŵa lero. Petro akusonyeza chifukwa chake aphunzitsi onama ayeneradi kuwonongedwa: “Ambiri adzatsata zonyansa zawo; chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.”—2 Petro 2:2.
5. Kodi aphunzitsi onama anali ndi mlandu wotani?
5 Tangoganizirani zimenezo! Chifukwa cha chisonkhezero cha aphunzitsi onama, ambiri m’mipingo adzachita zonyansa. Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “zonyansa” limatanthauza kusadzisunga, kusadziletsa, zamanyazi. Poyamba Petro ananena kuti Akristu ‘anapulumuka ku chivundi chili padziko lapansi m’chilakolako.’ (2 Petro 1:4) Koma ena anali kudzabwerera ku chivundi chomwecho, ndipo aphunzitsi onama m’mipingo ndiwo adzakhala ndi mlandu waukulu! Ndiye chifukwa chake njira ya choonadi idzachitidwa mwano. Nzachisoni! Inde, nkhani imeneyi Mboni za Yehova zonse lero ziyenera kuisamalira kwambiri. Tisaiŵaletu kuti, malinga ndi khalidwe lathu, tingadzetse thamo kwa Yehova Mulungu ndi anthu ake kapena chitonzo pa iwo.—Miyambo 27:11; Aroma 2:24.
Kuyambitsa Ziphunzitso Zonama
6. Kodi chimasonkhezera aphunzitsi onama nchiyani, ndipo amatani kuti apeze zomwe akufuna?
6 Mwanzeru, tikuona mmene aphunzitsi onama amayambira kalingaliridwe kopotoka. Choyamba, Petro akunena kuti amatero m’tseri, kapena mosaonekera, mwakabisira. Akuwonjezera kuti: “M’chisiriro adzakuyesani malonda ndi mawu onyenga.” Dyera ndilo limasonkhezera aphunzitsi onama, monga momwe kumasulira kwa The Jerusalem Bible kumagogomezera kuti: “Iwo adzayesetsa kukugulani ndi malankhulidwe ochenjera kuti mukhale awo.” Mofananamo, Baibulo la James Moffatt panopa limati: “M’chilakolako chawo adzakudyererani ndi zifukwa zaukathyali.” (2 Petro 2:1, 3) Zonena za aphunzitsi onama zingamveke zokoma kwa munthu amene sali wogalamuka mwauzimu, koma mawu awo amawakonza bwinobwino kuti ‘agule’ anthu, kuwanyengerera kuti ayambe kuchita zolinga zadyera za onyengawo.
7. Kodi ndi filosofi yotani yomwe inafala m’zaka za zana loyamba?
7 Mosakayikira, aphunzitsi onama a m’zaka za zana loyamba anatengera kalingaliridwe ka dziko panthaŵiyo. Panthaŵi imene Petro anali kulemba, filosofi yotchedwa Chinositisizimu inali kufalikira. Anositiki ankakhulupirira kuti zinthu zonse nzoipa ndi kuti zokhudza mzimu wa munthu zokha ndizo zabwino. Chotero, ena a iwo ankati zilibe kanthu zimene munthu achita ndi thupi lake. M’kupita kwa nthaŵi, iwo anatero, munthu sadzakhala ndi thupi limeneli. Choncho, iwo anatero, machimo a thupi—kuphatikizapo akugonana—sali nkhani yaikulu ayi. Mwachionekere, omwe amadzitcha Akristu anayamba kutengera malingaliro ngati amenewo.
8, 9. (a) Kodi ndi kalingaliridwe kopotoka kotani komwe kanakhudza Akristu ena oyambirira? (b) Malinga ndi Yuda, kodi ena m’mipingo ankatani?
8 Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo anatero kuti “analipo ena m’Tchalitchi omwe anapotoza chiphunzitso cha kukoma mtima,” kapena “chisomo.” (Aefeso 1:5-7) Malinga ndi iyeyu, zifukwa zimene ena ankapereka zinali zotere: “Kodi mukuti [kukoma mtima] kwa Mulungu nkwakukulu kwambiri moti nkukwirira tchimo lililonse? . . . Ndiye tipitirizetu kuchimwa, pakuti [kukoma mtima] kwa Mulungu kutha kufafaniza tchimo lililonse. Ndipotu tikamachimwa kwambiri mpamenenso [kukoma mtima] kwa Mulungu kudzakhala ndi mpata wabwino wogwira ntchito.” Kodi munamvapo kalingaliridwe kopotoka kwambiri ngati kameneko?
9 Mtumwi Paulo anatsutsa kalingaliridwe kolakwika ponena za chifundo cha Mulungu pamene anafunsa kuti: “Tidzakhalabe m’uchimo kodi, kuti chisomo chichuluke?” Anafunsanso kuti: “Tidzachimwa kodi chifukwa sitili a lamulo, koma a chisomo?” Pafunso lililonse Paulo anayankha motsimikiza kuti: “Msatero ayi.” (Aroma 6:1, 2, 15) Mwachionekere, malinga ndi kunena kwa Yuda, ena anali “kusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa.” Komabe, Petro akuti ‘chitayiko [“chiwonongeko,” NW] cha oterowo sichiodzera.’—Yuda 4; 2 Petro 2:3.
Zitsanzo Zotichenjeza
10, 11. Kodi Petro akupereka zitsanzo zitatu ziti kutichenjeza?
10 Pofuna kugogomezera kuti Mulungu adzalanga ochimwira dala, Petro akupereka zitsanzo zitatu za m’Malemba kutichenjeza. Choyamba, akulemba kuti: “Mulungu sanalekerera angelo adachimwawo.” Yuda akuti ameneŵa “sanasunga chikhalidwe chawo choyamba, komatu anasiya pokhala pawopawo” kumwamba. Anabwera padziko lapansi chisanafike Chigumula navala matupi a anthu kuti azigonana ndi ana aakazi a anthu. Polangidwa iwo chifukwa cha khalidwe lawo losayenera losiyana ndi chibadwa, anaponyedwa “kundende,” kapena malinga ndi zimene nkhani ya Yuda ikunena, “adawasunga m’ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.”—2 Petro 2:4; Yuda 6; Genesis 6:1-3.
11 Kenako, Petro akutchula anthu a m’tsiku la Nowa. (Genesis 7:17-24) Akutero kuti panthaŵi ya Nowa Mulungu “sanalekerera dziko lapansi lakale . . . pakulitengera dziko la osapembedza chigumula.” Pomaliza, Petro akulemba kuti Mulungu anaika “chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza” mwa “kuisandutsa makala midzi ya Sodoma ndi Gomora.” Yuda akutchula zinanso zowonjezera kuti anthu amenewo ‘adadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo.’ (2 Petro 2:5, 6; Yuda 7) Amuna sanali kungochita chisembwere ndi akazi okha komanso analakalaka matupi a amuna anzawo, mwina ngakhale a nyama.—Genesis 19:4, 5; Levitiko 18:22-25.
12. Malinga ndi Petro, kodi khalidwe lolungama limafupidwa motani?
12 Komabe, nthaŵi imodzimodziyo, Petro akutchula kuti Yehova amapereka mphotho kwa iwo akumtumikira mokhulupirika. Mwachitsanzo, akusimba mmene Mulungu ‘anasungira Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi aŵiri’ pamene Iye anadzetsa Chigumula. Akusimbanso kuti Yehova anapulumutsa “Loti wolungamayo” panthaŵi ya Sodomu, namaliza kuti: “Ambuye adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe.”—2 Petro 2:5, 7-9.
Ntchito Zoyenera Chilango
13. Kodi ndani makamaka omwe chiweruzo chikuwayembekezera, ndipo mwachionekere amalota zotani?
13 Petro akutchula makamaka amene chiweruzo cha Mulungu chikuwayembekezera, ndiwo, “akutsata zathupi, m’chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro.” Titha kuona kuipidwa kwa Petro pamene iye akunena kuti: “Osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu.” Yuda akulemba kuti “iwo m’kulota kwawo adetsa matupi awo, . . . nachitira mwano maulemerero.” (2 Petro 2:10; Yuda 8) Maloto awo angaphatikizepo kutengeka maganizo ndi zachisembwere kumene kumawalimbikitsa kuchita chisembwere kuti akhutiritse zilakolako zawo zoipa. Nanga kodi ‘amapeputsa motani ulamuliro’ ndi kuchitira “mwano maulemerero”?
14. Kodi aphunzitsi onama ‘amapeputsa motani ulamuliro’ ndi kuchitira “mwano maulemerero”?
14 Amatero mwa kunyozera ulamuliro woikidwa ndi Mulungu. Akulu achikristu amaimira Yehova Mulungu waulemerero ndi Mwana wake, choncho, ali nawo ulemerero wina wake woikidwa pa iwo. Inde, amalakwa, monganso anachitira Petro, koma Malemba amalimbikitsa mpingo kuwagonjera aulemerero amenewo. (Ahebri 13:17) Zophophonya zawo sindizo chifukwa chowachitira mwano iwo. Petro akunena kuti angelo “sawaneneza [aphunzitsi onama],” ngakhale kuti zimenezo zingayenerere kwambiri. “Koma awo,” akupitiriza Petro, “ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuwonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziŵa, adzawonongeka m’kuwononga kwawo.”—2 Petro 2:10-13.
“Pamene Akudya . . . Nanu”
15. Kodi njira zomwe aphunzitsi onama amagwiritsira ntchito nzotani, ndipo nkuti komwe amagwiritsira ntchito kunyengerera kwawo?
15 Ngakhale kuti anthu oipa ameneŵa “akuyesera chowakondweretsa kudyerera usana” ndipo “ndiwo mawanga ndi zilema,” alinso akavuŵevuŵe. Amachita zinthu “m’tseri,” kugwiritsira ntchito “mawu onyenga,” zimene Petro wanena poyamba. (2 Petro 2:1, 3, 13) Chotero iwo samatsutsa moonekera kuyesayesa kwa akulu kuchirikiza malamulo a Mulungu a makhalidwe kapena samachita moonekera zokhutiritsa zilakolako zawo za kugonana. M’malo mwake, Petro akuti iwo amamwerekera “ndi chimwemwe chosadziletsa paziphunzitso zawo zonama pamene akudya pamodzi nanu.” (NW) Ndipo Yuda akulemba kuti: “Ameneŵa ndiwo miyala yaikulu yobisika pansi pa madzi m’mapwando anu a chikondi.” (Yuda 12, NW) Inde, monga miyala yojenya pansi pa madzi ingaboolere bwato kunsi ndi kumiza amalinyero opanda tcheru, aphunzitsi onama anali kuipitsa osachenjera omwe mwachinyengo anawasonyeza chikondi pa ‘mapwando a chikondi.’
16. (a) Kodi ‘mapwando a chikondi’ anali chiyani, ndipo ndi pazochitika ziti zonga amenewo pomwe amphulupulu angapezeke lero? (b) Kodi aphunzitsi onama amasumika maganizo awo pa yani, choncho iwowo ayenera kuchitanji?
16 ‘Mapwando a chikondi’ ameneŵa mwachionekere anali macheza pamene Akristu a m’zaka za zana loyamba ankakumana, kudya ndi kuyanjana. Leronso Mboni za Yehova nthaŵi zina zimacheza, mwinamwake kumadyerero a ukwati, kumapikiniki, kapena kungocheza madzulo. Kodi anthu oipa angagwiritsire ntchito motani zochitika ngati zimenezo kunyengerera ena? Petro akulemba kuti: “Okhala nawo maso odzala ndi chigololo . . . , kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika.” Amasumika ‘mtima wawo wozoloŵera kusirira’ pa aja osakhazikika mwauzimu amene sanapange choonadi kukhaladi chawo. Chotero zimene zinachitika m’tsiku la Petro zikhaletu chenjezo kwa inu, ndipo khalani maso! Mkanizeni yense amene ayesa kukunyengererani kuchita zoipa, ndipotu musapusitsidwe ndi maonekedwe kapena kukongola kwa amene akukunyengererani kuchita chisembwere!—2 Petro 2:14.
“Njira ya Balamu”
17. Kodi “njira ya Balamu” inali chiyani, ndipo inawakhudza motani Aisrayeli 24,000?
17 Anthu “a temberero” ameneŵa adziŵa choonadi nthaŵi yaitali. Angaonekebe okangalika mumpingo. Koma Petro akuti: “Posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama.” (2 Petro 2:14, 15) Njira ya mneneri Balamu inali yopereka uphungu wonyengerera nawo ena kuchita chisembwere kuti iye mwini apindule. Anauza Mfumu Balaki ya Moabu kuti Mulungu adzatemberera Israyeli ngati anthuwo angawanyengerere kuchita chigololo. Chotero, anthu a Mulungu ambiri ananyengedwa ndi akazi achimoabu, ndipo 24,000 anaphedwa chifukwa cha khalidwe lawo loipa.—Numeri 25:1-9; 31:15, 16; Chivumbulutso 2:14.
18. Kodi Balamu anali waliuma motani, ndipo zimene zinamchitikira zimatanthauzanji kwa aneneri onama?
18 Petro akutchula kuti Balamu anali ndi chomletsa pamene bulu wake analankhula, koma Balamu “anakonda mphotho ya chosalungama” kwambiri koti ngakhale zimenezo zitachitika, sanachoke pa “kuyaluka” kwake. (2 Petro 2:15, 16) Anali woipa zedi! Tsoka kwa yense wonga Balamu amene amayesa kuipitsa anthu a Mulungu mwa kuwanyengerera kuchita chisembwere! Kuipa kwake Balamu kunamphetsa, chitsanzo cha zimene zidzachitika kwa onse otsata njira yake.—Numeri 31:8.
Kunyengerera Kwawo Kwausatana
19, 20. (a) Kodi anthu onga Balamu ali ngati chiyani, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi amakopa yani, ndipo motani? (c) Kodi tinganenerenji kuti kunyengerera kwawo nkwausatana, ndipo tingadziteteze motani ife eni ndi kutetezanso ena kwa iwo?
19 Pofotokoza onga Balamu, Petro akulemba kuti: “Iwo ndiwo akasupe [kapena, zitsime] opanda madzi, nkhungu [kapena, mitambo] yokankhika ndi mkuntho.” Kwa waulendo wofa ludzu m’chipululu, chitsime chouma chingatanthauze imfa. Ndiye chifukwa chake “mdima wakuda bii uwasungikira” iwo onga zinthuzo! “Pakuti polankhula mawu otukumuka opanda pake,” akupitiriza Petro, “anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe olakwawo.” Amanyengerera osadziŵa mwa “kuwalonjezera iwo ufulu,” akutero Petro, pamene “iwo okha ali akapolo a chivundi.”—2 Petro 2:17-19; Agalatiya 5:13.
20 Kunyengerera kwa aphunzitsi oipa amenewo nkwausatana. Mwachitsanzo, iwo anganene kuti: ‘Pajatu Mulungu adziŵa kuti ndife ofooka ndipo timakopeka ndi chilakolako. Choncho ngati timwerekera nitikhutiritsa zilakolako zathu za kugonana, Mulungu adzatichitira chifundo. Tikaulula machimo athu, adzatikhululukira muja anachitira titangobwera kumene m’choonadi.’ Kumbukirani kuti Mdyerekezi anagwiritsira ntchito njira yonga imeneyo kwa Hava, namlonjeza kuti angachimwe kosalangidwa. Kwa Hava, iye anati akachimwira Mulungu, adzapeza chidziŵitso ndi ufulu. (Genesis 3:4, 5) Tikakumana ndi munthu woipa ngati ameneyo woyanjana ndi mpingo, tiyenera kudziteteza ife eni limodzi ndi ena mwa kukamnenera munthuyo kwa audindo mumpingo wachikristu.—Levitiko 5:1.
Otetezeredwa ndi Chidziŵitso Cholongosoka
21-23. (a) Kodi zotsatira zake za kusagwiritsira ntchito chidziŵitso cholongosoka nzotani? (b) Kodi ndi vuto lina lotani lomwe Petro akufotokoza lomwe tidzalipendanso?
21 Petro akumaliza chigawo chimenechi cha kalata yake mwa kufotokoza zotsatira zake za kusagwiritsira ntchito chidziŵitso chimene poyamba anati nchofunika kwambiri “pamoyo ndi chipembedzo.” (2 Petro 1:2, 3, 8) Akulemba kuti: ‘Pakuti ngati, adatha kuthaŵa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso [“chidziŵitso cholongosoka,” NW] cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu, akodwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zawo zidzaipa koposa zoyambazo.’ (2 Petro 2:20) Mmene zilili zachisoni nanga! Oterowo m’tsiku la Petro anataya chiyembekezo chamtengo wapatali chokakhala ndi moyo wosafa kumwamba chifukwa chofuna kukhutiritsa chilakolako chawo cha kugonana kwa kanthaŵi.
22 Choncho Petro akuti: “Pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo. Chidawayenera iwo cha nthanthi yoona, Galu wabwerera ku masanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m’thope.”—2 Petro 2:21, 22; Miyambo 26:11.
23 Mwachionekere vuto lina limene linali litayamba kuwakhudza Akristu oyambirira linali lofanana ndi lija lomwe likukhudza ena lero. Kalelo, ena mwachionekere anali kudandaula chifukwa choona ngati kuti kukhalapo kwa Kristu kolonjezedwako sikukufika. Tiyeni tipende mmene Petro akusamalira nkhaniyi.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi zitsanzo zitatu zotani zomwe Petro akutchula kutichenjeza?
◻ Kodi aphunzitsi onama ‘amapeputsa motani ulamuliro’?
◻ Kodi njira ya Balamu nchiyani, ndipo amene akuitsatira angayese motani kunyengerera ena?
◻ Kodi zotsatira zake za kusagwiritsira ntchito chidziŵitso cholongosoka nzotani?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Balamu ndiye chitsanzo chotichenjeza