Odala Iwo Amene Adikira!
“Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake.”—CHIVUMBULUTSO 16:15.
1. Popeza kuti tsiku la Yehova lili pafupi, kodi tiyenera kuyembekezeranji?
TSIKU lalikulu la Yehova lili pafupi, ndipotu imeneyo ndi nkhondo! M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona “mizimu ya ziŵanda” yonga achule ikumka kwa “mafumu,” kapena olamulira onse a dziko lapansi. Kukatani? Eya, “kuwasonkhanitsira ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse”! Yohane anawonjezera nati: “Anawasonkhanitsira ku malo otchedwa m’Chihebri Harmagedo.”—Chivumbulutso 16:13-16.
2. Kodi Gogi wa ku Magogi ndani, ndipo nchiyani chidzachitika pamene adzaukira anthu a Yehova?
2 Posachedwapa, Yehova adzatuma andale a dongosolo ili kuwononga Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 17:1-5, 15-17) Ndiyeno Gogi wa ku Magogi, Satana Mdyerekezi woponyedwa kudziko lapansi, adzamemeza magulu ake ndi kuukira mwamphamvu anthu a Yehova a mtendere, ooneka ngati opanda chitetezo. (Ezekieli 38:1-12) Koma Mulungu adzachitapo kanthu kutetezera anthu ake. Ndipo padzayambira “tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.”—Yoweli 2:31; Ezekieli 38:18-20.
3. Kodi zochitika za pa Ezekieli 38:21-23 mungazifotokoze motani?
3 Inde, Yehova adzapulumutsa anthu ake ndi kuwononga zotsala zilizonse za dongosolo la Satana pamene tidzafika pamkhalidwe wa dziko lonse wotchedwa Harmagedo, kapena Armagedo. Ŵerengani mawu aulosi a Ezekieli 38:21-23, ndipo yerekezani kuti mukuchiona chochitikacho. Yehova akugwiritsira ntchito mphamvu yake kudzetsa mvumbi waukulu, matalala owononga, moto wovumba, mliri wakupha. Dziko lonse likutekeseka pamene magulu a Gogi asokonezeka, kumenyana iwo okha. Adani alionse opulumuka a Mulungu Wamphamvuyonse akuphedwa pamene Yehova akugwiritsira ntchito njira zaumulungu kupulumutsa anthu ake. Pamene ‘chisautso chachikulu’ chonenedweratucho chitha, palibe kalikonse ka dongosolo la Satana losaopa Mulungu komwe kadzatsala. (Mateyu 24:21) Komabe, ngakhale pakufa kwawo, oipa adzadziŵa amene wachititsa tsoka lawo. Mulungu wathu wachipambano iye mwini akuti: “Adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova.” Zochitika zodabwitsa zimenezi zidzachitika m’tsiku lathu, mkati mwa kukhalapo kwa Yesu.
Kudza Ngati Mbala
4. Kodi Yesu adzadza motani kudzawononga dongosolo la zinthu loipali?
4 Ambuye waulemerero Yesu Kristu anati: “Taonani, ndidza ngati mbala.” Kudza konga kwa mbala kumakhala kodzidzimutsa, panthaŵi yosayembekezereka, pamene anthu ochuluka ali mtulo. Pamene Yesu adza ngati mbala kudzawononga dongosolo loipali, adzasunga awo amene akudikiradi. Iye anauza Yohane kuti: “Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiŵa, nangapenye anthu usiŵa wake.” (Chivumbulutso 16:15) Kodi mawuwa amatanthauzanji? Ndipo tingadikire motani mwauzimu?
5. Kodi makonzedwe a utumiki wa pakachisi anali otani pamene Yesu anali padziko lapansi?
5 Kwenikweni, mlonda sangamvule zovala atagona pantchito. Koma zimenezo zinkachitika pakachisi ku Yerusalemu pamene Yesu anali padziko lapansi pamene ansembe ndi Alevi opatsidwa magawo anali kutumikira pakachisi ku Yerusalemu. Ndi m’zaka za zana la 11 B.C.E. pamene Mfumu Davide analinganiza mazana a ansembe a Israyeli ndi zikwi za othandiza awo achilevi kukhala gulu la magawo 24. (1 Mbiri 24:1-18) Gawo lililonse la antchito ophunzitsidwa oposa chikwi chimodzi linkatumikira mbali zosiyanasiyana za utumiki wa pakachisi panthaŵi yake kwenikweni kaŵiri pachaka kwa mlungu umodzi nthaŵi iliyonse. Komabe, pa Phwando la Misasa magawo onse 24 ankagwira ntchito pamodzi. Panali kufunikanso thandizo lapadera pamapwando a Paskha.
6. Kodi Yesu ayenera kuti ankanena za chiyani pomwe anati, “Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake”?
6 Pamene Yesu anati, “Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake,” ayenera kuti ankanena za mmene ankachitira ntchito ya ulonda pakachisi nthaŵiyo. Mishnah yachiyuda ikuti: “Ansembe ankalonda malo atatu m’Kachisi: pa Chipinda cha Abtinas, pa Chipinda cha Laŵi la Moto, ndi pa Chipinda cha Chiotho; ndi alevi malo makumi asanu ndi chimodzi: asanu pazipata zisanu za Phiri la Kachisi, anayi pangondya zake zinayi zamkati, asanu pazipata zisanu za Bwalo la Kachisi, anayi pangondya zake zinayi zakunja, ndi mmodzi pa Chipinda cha Zopereka, ndi mmodzi pa Chipinda cha Nsalu Yotchinga, ndi mmodzi kuseri kwa malo a Mpando Wachifundo [kunja kwa khoma lakumbuyo la Malo Opatulikitsa]. Mkulu wa Phiri la Kachisi ankapita kwa mlonda aliyense ndi miuni patsogolo pake, ndipo ngati mlonda aliyense sanaimirire ndi kunena kwa iye kuti, ‘Mkulunu wa Phiri la Kachisi, mtendere ukhale nanu!’ ndipo anaoneka kuti wagona, anali kummenya ndi ndondo yake, ndipo anali ndi mphamvu ya kutentha zovala zake.”—The Mishnah, Middoth (“Miyeso”), 1, ndime 1-2, yotembenuzidwa ndi Herbert Danby.
7. Kodi nchifukwa ninji ansembe ndi Alevi apaulonda pakachisi anafunikira kudikira?
7 Alevi ndi ansembe ambiriwo a m’chigawo chomwe akutumikira ankadikira usiku wonse kulonda ndi kuletsa aliyense wodetsedwa kuloŵa m’mabwalo a kachisi. Popeza kuti “mkulu wa Phiri la Kachisi,” kapena “mdindo wa kukachisi,” ankazungulira malo 24 onsewo paulonda wausiku, mlonda aliyense anayenera kudikira pamalo ake ngati sanafune kumgwira atagona.—Machitidwe 4:1.
8. Kodi zovala za Mkristu zophiphiritsira nchiyani?
8 Akristu odzozedwa ndi atumiki anzawo afunikira kudikira mwauzimu ndi kusunga zovala zawo zophiphiritsira. Ameneŵa ndi maumboni akunja akuti taikidwa pautumiki wa pakachisi wauzimu wa Yehova. Chifukwa cha zimenezi, tili ndi mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yake yogwira ntchito, yotithandiza kuchita ntchito zathu ndi kukwaniritsa mathayo athu monga olengeza Ufumu. Kugona pamalo athu monga atumiki a Mulungu kungatiike pangozi ya kugwidwa ndi Yesu Kristu, Mdindo wa kachisi wamkulu wauzimu. Ngati tili mtulo tauzimu panthaŵiyo, adzativula zovala mophiphiritsira ndi kutitenthera zovala zathu zophiphiritsira. Choncho kodi tingadikire motani mwauzimu?
Mmene Tingadikirire
9. Kodi nchifukwa ninji phunziro la Baibulo mothandizidwa ndi zofalitsa zachikristu lili lofunika kwambiri?
9 Phunziro lakhama la Malemba mothandizidwa ndi zofalitsa zachikristu limasonkhezera kudikira kwauzimu. Phunziro lotere lidzatikonzekeretsa utumiki, lidzatithandiza kulimbana ndi mavuto, ndipo lidzationetsa njira ya chimwemwe chosatha. (Miyambo 8:34, 35; Yakobo 1:5-8) Phunziro lathu liyenera kukhala losamalitsa ndi lopita patsogolo. (Ahebri 5:14–6:3) Chakudya chabwino chodyedwa nthaŵi zonse chingatithandize kukhala maso ndi atcheru. Chingaletse kuodzera kumene kungakhale chizindikiro cha matenda a njala. Tilibe chifukwa chokhalira anjala ndi omaodzera mwauzimu, popeza kuti Mulungu akupereka chakudya chauzimu chochuluka kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wodzozedwa. (Mateyu 24:45-47) Kudya chakudya chauzimu nthaŵi zonse mwa phunziro laumwini ndi phunziro la banja ndiko njira ina imene tingakhalire tikudikira ndi ‘kulama m’chikhulupiriro.’—Tito 1:13.
10. Kodi misonkhano yachikristu, misonkhano yadera, ndi misonkhano yachigawo imatithandiza motani kudikira mwauzimu?
10 Misonkhano yachikristu, misonkhano yadera, ndi misonkhano yachigawo imatithandiza kudikira mwauzimu. Imapereka chilimbikitso ndi mpata wa ‘kufulumizana kuchikondano ndi ntchito zabwino.’ Tiyenera kusonkhana nthaŵi zonse makamaka pamene ‘tiona tsiku lili kuyandikira.’ Tsikulo lili pafupi kwenikweni tsopano. Ndilo “tsiku la Ambuye,” pamene adzatsimikiza uchifumu wake. Ngati tsikulo nlofunikadi kwa ife—ndipotu liyenera—‘sitidzaleka kusonkhana kwathu pamodzi.’—Ahebri 10:24, 25; 2 Petro 3:10.
11. Nchifukwa ninji tinganene kuti utumiki wachikristu uli wofunika pakudikira kwauzimu?
11 Kuchita nawo utumiki wachikristu ndi mtima wonse nkofunika kuti tidikire mwauzimu. Kukhala ndi phande nthaŵi zonse ndipo mwachangu pakulalikira uthenga wabwino kumatikhalitsa atcheru. Utumiki wathu umatipatsa mpata waukulu wolankhula ndi anthu za Mawu a Mulungu, Ufumu wake, ndi zifuno zake. Nkokhutiritsa kulalikira kunyumba ndi nyumba, kupanga maulendo obwereza, ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba m’zofalitsa monga Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Akulu a ku Efeso wakale anavomereza kuti Paulo anawaphunzitsa “pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba.” (Machitidwe 20:20, 21) Komabe, Mboni zina za Yehova zokhulupirika zili ndi matenda aakulu amene amasokoneza utumiki wawo mwa njira ina, koma amapeza njira zouzira ena za Yehova ndi uchifumu wake ndi kupeza chimwemwe chachikulu pochita zimenezi.—Salmo 145:10-14.
12, 13. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kumwerekera ndi zakudya ndi zakumwa?
12 Kupeŵa kumwerekera kudzatithandiza kudikira mwauzimu. Polankhula za kukhalapo kwake, Yesu analimbikitsa atumwi ake kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi.” (Luka 21:7, 34, 35) Kususuka ndi kuledzera sizigwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo. (Deuteronomo 21:18-21) Miyambo 23:20, 21 imati: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.”—Miyambo 28:7.
13 Komabe, ngakhale ngati kudya ndi kumwa mopambanitsa sikunafike pamlingo umenewo, kungachititse munthu kuodzera, ngakhale kuchita ulesi ndi kunyalanyaza kuchita chifuniro cha Mulungu. Mwachibadwa, pamakhala nkhaŵa zokhudza moyo wa banja, thanzi, ndi zina zotero. Komabe, tidzakhala achimwemwe ngati tiika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo ndi kukhala ndi chidaliro chakuti Atate wathu wakumwamba adzatipatsa zofunika. (Mateyu 6:25-34) Tikachitira mwina, “tsiku ilo” lidzatigwera ngati “msampha,” mwinamwake monga msampha wosaoneka umene udzangotigwira mosadziŵa kapena monga msampha wokhala ndi nyambo, monga uja umene umakopa ndi kugwira nyama yosayembekezera kalikonse. Zimenezi sizidzachitika ngati tidikira, odziŵa bwino lomwe kuti tikukhala mu “nthaŵi ya chimaliziro.”—Danieli 12:4.
14. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupemphera mochokera mumtima?
14 Pemphero lochokera mumtima limathandizanso kudikira mwauzimu. Mu ulosi wake waukuluwo, Yesu analimbikitsanso kuti: “Dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:36) Inde, tiyenitu tizipemphera kuti nthaŵi zonse tikhale kumbali ya Yehova ndi kukhala ndi kaimidwe kovomerezeka pamene Yesu, Mwana wa munthu, adzadza kudzawononga dongosolo la zinthu loipali. Kuti ifeyo tipindule ndi kupindulitsa okhulupirira anzathu amene tikupempherera, tifunikira ‘kudikira m’pemphero.’—Akolose 4:2; Aefeso 6:18-20.
Nthaŵi Ili Kutha
15. Kodi utumiki wathu monga alaliki a chilungamo ukukwaniritsanji?
15 Pamene tikuyembekezera tsiku lalikulu la Yehova, ndithudi tikukhumba kuchita zonse zimene tingathe mu utumiki wake. Ngati timapemphera kwa iye mochokera mumtima pankhaniyi, ‘khomo lalikulu ndi lochititsa’ lingatitsegukire. (1 Akorinto 16:8, 9) Panthaŵi yoikika ya Mulungu, Yesu adzapereka chiweruzo ndi kulekanitsa “nkhosa” zolungama zoyenerera moyo wosatha ndi “mbuzi” zosaopa Mulungu zoyenerera kuwonongedwa kwamuyaya. (Yohane 5:22) Ife sindife amene tikulekanitsa nkhosa ndi mbuzi. Koma utumiki wathu monga alaliki a chilungamo tsopano ukupatsa anthu mpata wosankha moyo wotumikira Mulungu ndi kukhalano ndi chiyembekezo cha kulekanitsidwa kaamba ka moyo pamene Yesu “adzadza mu ulemerero wake.” Kufupika kwa nthaŵi yotsalira dongosolo ili la zinthu kukuwonjezera kufunika kwa kugwira ntchito ndi mtima wonse pamene tikufunafuna awo “ofuna moyo wosatha.”—Mateyu 25:31-46; Machitidwe 13:48, NW.
16. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala olengeza Ufumu achangu?
16 Nthaŵi inathera dziko la m’tsiku la Nowa, ndipo posachedwapa idzathera dongosolo ili la zinthu. Choncho tiyenitu tikhale olengeza Ufumu achangu. Ntchito yathu yolalikira ikupita patsogolo, popeza kuti chaka chilichonse zikwi mazanamazana amabatizidwa kusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu. Iwo akukhala mbali ya gulu lodala la Yehova—“anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake.” (Salmo 100:3) Kulidi kosangalatsa chotani nanga kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira Ufumu imene imapatsa ambiri chiyembekezo “tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa” lisanafike!
17, 18. (a) Pamene tikulalikira, kodi tiyenera kuyembekezera kuti ena adzatani? (b) Kodi mosakayika nchiyani chidzapeza onyoza?
17 Monga Nowa, tili ndi chichirikizo cha Mulungu ndi chitetezo chake. Inde, anthu, angelo osanduka, ndi Anefili ayenera kuti ananyozera uthenga wa Nowa, koma iye sanaleke chifukwa cha zimenezo. Lerolino, ena amanyoza pamene tisonyeza umboni wosatsutsika wakuti tikukhala mu “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5) Kunyozera kumeneku kukukwaniritsa ulosi wa Baibulo wa kukhalapo kwa Kristu, popeza Petro analemba kuti: ‘Masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza [“kukhalapo,” NW] kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.”—2 Petro 1:16; 3:3, 4.
18 Onyoza amakono angalingalire kuti: ‘Chilengedwere zinthu, palibe zomwe zasintha. Moyo umangopitirizabe, anthu akudya, kumwa, kukwatira, ndi kukwatiwa ndi kukhala ndi mabanja. Ngakhale ngati Yesu alipo, sadzapereka chiweruzo m’tsiku langa.’ Ndi olakwika chotani nanga! Ngati safa ndi zifukwa zina pakali pano, mosakayikira tsiku loopsa la Yehova lidzawapeza monga mbali ya mbadwo uno woipa monganso momwe chiwonongeko chachikulucho pa Chigumula chinathera mbadwo woipa wa m’tsiku la Nowa.—Mateyu 24:34.
Yesetsani Kudikira
19. Kodi tiyenera kuiona motani ntchito yathu yopanga ophunzira?
19 Ngati tili odzipatulira kwa Yehova, tisagonetsedwe tulo ndi malingaliro olakwika. Ino ndiyo nthaŵi yodikira, kukhulupirira ulosi wa Mulungu, ndi kuchita ntchito yathu ‘yophunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 28:19, 20) Pamene dongosololi liyembekeza chimaliziro chake chotsiriza, sitingakhale ndi mwaŵi wina waukulu kuposa wotumikira Yehova Mulungu motsogozedwa ndi Yesu Kristu ndi kukhala ndi phande m’ntchito ya padziko lonse yolalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” chimaliziro chisanafike.—Mateyu 24:14; Marko 13:10.
20. Kodi Kalebi ndi Yoswa anaika chitsanzo chotani, ndipo kodi moyo wawo ukutisonyezanji?
20 Anthu ena a Yehova akhala akumtumikira zaka makumi ambiri, mwinanso moyo wawo wonse. Ndipo ngakhale tangoyamba kumene kulambira koona, tikhaletu ngati Kalebi wachiisrayeli, amene “analimbika ndi kutsata Yehova.” (Deuteronomo 1:34-36) Iyeyo ndi Yoswa anali okonzekera ndithu kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa mwamsanga Israyeli atangomasuka ku ukapolo wa Igupto. Komabe, Aisrayeli ambiri achikulire anasoŵa chikhulupiriro ndipo anatha zaka 40 m’chipululu, mmene anafera. Kalebi ndi Yoswa anapirira mavuto limodzi ndi iwo onse nthaŵi yonseyo, koma potsirizira pake amuna aŵiriwo analoŵa m’dziko la lonjezo. (Numeri 14:30-34; Yoswa 14:6-15) Ngati ‘tilimbika ndi kutsata Yehova’ ndi kungodikira mwauzimu, tidzasangalala kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu lolonjezedwa.
21. Kodi tidzaonanji ngati ife tingodikira mwauzimu?
21 Umboni ukusonyeza bwino lomwe kuti tikukhala m’nthaŵi yachimaliziro ndi kuti tsiku la lalikulu Yehova lili pafupi. Inoyo si nthaŵi yomaodzera ndi kunyalanyaza kuchita chifuniro cha Mulungu. Tidzadalitsidwa kokha ngati tidikira mwauzimu ndi kusunga zovala zathu zotidziŵikitsa monga atumiki achikristu ndi antchito a Yehova. Titsimikizetu mtima kuti ‘tidzadikira, kuchirimika m’chikhulupiriro, kudzikhalitsa amuna, kulimbika.’ (1 Akorinto 16:13) Monga atumiki a Yehova, aliyense wa ife akhaletu wokhazikika ndi wolimba mtima. Pomwepo tidzakhala pakati pa okonzekera pamene tsiku lalikulu la Yehova likantha, tikumatumikira mokhulupirika limodzi ndi anthu achimwemwe omwe akudikira.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi munganene kuti zovala zathu zophiphiritsira nchiyani, ndipo tingazisunge motani?
◻ Kodi njira zina zodikira mwauzimu ndi ziti?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyembekezera kukumana ndi onyoza, ndipo kodi tiyenera kuwaona motani?
◻ Kodi ntchito yathu yopanga ophunzira tiyenera kuiona motani m’masiku ano otsiriza?
[Mawu Otsindika patsamba 16]
Akristu ali ndi mzimu woyera wa Mulungu wowathandiza kudikira ndi kukwaniritsa mathayo awo
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi ndinu wotsimikiza mtima kuti mudzadikira mwauzimu ndi kusunga zovala zanu zophiphiritsira?