Chipulumutso
Tanthauzo: Kutetezeredwa kapena kulanditsidwa kuupandu kapena chiwonongeko. Uku kungakhale kulanditsidwa kwa otsendereza kapena ozunza. Kwa Akristu onse owona, Yehova amapereka kupyolera mwa Mwana wake chilanditso kudongosolo loipa liripoli la zinthu kudzanso chipulumutso ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Kwa khamu lalikulu la atumiki okhulupirika a Yehova kukhala ndi moyo mkati mwa “masiku otsiriza,” chipulumutso chidzaphatikizapo kutetezeredwa pa chisautso chachikulu.
Kodi Mulungu, mwa chifundo chake chachikulu, potsirizira pake adzapulumutsa anthu onse?
Kodi 2 Petro 3:9 amasonyeza kuti padzakhala chipulumutso cha anthu onse? Iye amati: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke [“samafuna kuti aliyense awonongedwe,” TEV], koma kuti onse afike kukulapa.” (RS) Chiri chikhumbo cha kukoma mtima kwa Mulungu kuti ana onse a Adamu alape, ndipo mokoma mtima iye wapanga makonzedwe a kupezera chikhululukiro cha machimo kwa awo amene amatero. Koma iye samakakamiza munthu aliyense kuvomereza makonzedwewo. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 30:15-20.) Ambiri amawakana. Iwo ali ngati munthu womira amene amakankhira kutali chopulumutsira moyo pamene chiponyeredwa kwa iye ndi munthu amene afuna kuthandiza. Komabe, kuyenera kudziŵika, kuti choloŵa mmalo mwa kulapa sindicho helo wamuyaya m’moto. Monga momwe 2 Petro 3:9 amasonyezera, osalapa adzawonongeka, kapena “kuwonongedwa.” Vesi 7 (RS) imasonyanso ku “chiwonongeko cha anthu osapembedza.” Panopa palibe lingaliro la chipulumutso cha anthu onse.—Wonaninso mutu wankhani waukulu wakuti “Helo.”
Kodi 1 Akorinto 15:22 amatsimikizira kuti anthu onse potsirizira pake adzapulumutsidwa? Amati: “Monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Kristu onse adzakhalitsidwa ndi moyo.” (RS) Monga momwe kwasonyezedwera m’mavesi ozungulira, chimene chikukambitsiridwa panopa ndicho chiukiriro. Kodi adzaukitsidwa ndani? Onse amene imfa yawo inachititsidwa ndi tchimo la Adamu (wonani vesi 21) koma amene mwa iwo okha sanachite machimo adala olembedwa pa Ahebri 10:26-29. Monga momwe Yesu anaukitsidwira ku Hade (Mac. 2:31), motero ena onse amene ali m’Hade ‘adzakhalitsidwa amoyo’ mwa chiukiriro. (Chiv. 1:18; 20:13) Kodi onse amenewa adzapeza chipulumutso chamuyaya? Mwaŵi umenewo udzakhala wowatsegukira, koma siyense amene adzapindula nawo, monga momwe kwasonyezedwera pa Yohane 5:28, 29, amene amasonyeza kuti chotulukapo kwa ena chidzakhala “chiweruzo” chotsutsa.
Bwanji za malemba onga Tito 2:11, limene linatchula “chipulumutso cha anthu onse,” mogwirizana ndi kumasulira kwa RS? Malemba ena, monga ngati Yohane 12:32, Aroma 5:18, ndi 1 Timoteo 2:3, 4, amapereka lingaliro lofanana mu RS, KJ, NE, TEV, ndi ena otero. Mawu Achigiriki omasuliridwa “onse” ndi “aliyense” m’mavesi amenewa ali m’mipangidwe ya kusiyanitsidwa kwa liwu lakuti pas. Monga momwe kwasonyezedwera mu Expository Dictionary of New Testament Words ya Vine (London, 1962, Vol. I, p. 46), pas angatanthauzenso “mtundu uliwonse kapena kusiyanasiyana.” Chotero, m’mavesi apamwamba, mmalo mwa “onse,” mawu akutiwo “mtundu uliwonse wa” angagwiritsiridwe ntchito; kapena “mitundu yonse ya,” monga momwe kwachitidwira mu NW. Kodi nkati kamene kali kolungama—“onse” kapena lingaliro loperekedwa ndi “mitundu yonse ya”? Eya, kodi ndikumasulira kuti kumene kulinso kogwirizana ndi mbali yotsala ya Baibulo? Yotsirizirayi ndiyo. Talingalirani Machitidwe 10:34, 35; Chivumbulutso 7:9, 10; 2 Atesalonika 1:9. (Tamverani: otembenuza ena amavomerezanso ganizo iri la liwu Lachigiriki, monga momwe kwasonyezedwera ndi kulimasulira kwawo pa Mateyu 5:11—“mitundu yonse ya,” RS, TEV; “mtundu uliwonse wa,” NE; “mkhalidwe wonse wa,” KJ.)
Kodi pali malemba amene amasonyeza motsimikizirika kuti ena sadzapulumutsidwa konse?
2 Ates. 1:9: “Adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha chowasiyanitsa kunkhope ya Ambuye, ndi kuulemerero wa mphamvu yake.” (Akanyenye awonjezeredwa.)
Chiv. 21:8: “Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse amabodza, cholandira chawo chidzakhala nyanja yotentha ndi moto ndi sulfure; ndiyo imfa yachiŵiri.”
Mat. 7:13, 14: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira ya kumuka nayo kukuwonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo ya kumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenechi ali oŵerengeka.”
Pamene munthu apulumutsidwa, kodi iye wapulumutsidwa nthaŵi yonse?
Yuda 5: “Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale mumadziŵa zonse kale, kuti Ambuye atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m’dziko la Aigupto, anawononganso iwo osakhulupirira.” (Kanyenye wawonjezeredwa.)
Mat. 24:13: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Chotero, chipulumutso chotsirizira chamunthu sichimatsimikiziridwa panyengo imene iye ayamba kukhulupirira Yesu.)
Afil. 2:12: “Monga momwe mumvera nthaŵi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira.” (Mawuŵa anaperekedwa kwa “asante,” kapena oyera mtima, ku Filipi, monga momwe kwalongosoledwera mu Afilipi 1:1. Paulo anawalimbikitsa kusakhala ndi chidaliro chopambanitsa koma kuzindikira kuti chipulumutso chawo chotsirizira chinali chisanatsimikiziridwebe.)
Aheb. 10:26, 27, RS: “Ngati tichimwa dala pambuyo pa kulandira chidziŵitso cha chowonadi, sipatsalanso nsembe ya machimo, koma chiyembekezo chochititsa mantha cha chiŵeruzo, ndi mkwiyo wa moto umene udzanyeketsa adani.” (Motero Baibulo silimayenderana ndi lingaliro lakuti ziribe kanthu ndi machimo amene munthu angachite pambuyo pa “kupulumutsidwa” kwake iye sadzatayikiridwa ndi chipulumutso chake. Limalimbikitsa kukhulupirika. Wonaninso Ahebri 6:4-6, kumene limasonyeza kuti ngakhale kumene munthuyo ali wodzozedwa ndi mzimu woyera angathe kutayikiridwa ndi chiyembekezo chake cha chipulumutso.)
Kodi pali kanthu kena kake koposa chikhulupiriro kamene kali kofunika kupezera chipulumutso?
Aef. 2:8, 9: “Muli opulumutsidwa ndi chisomo [“kukoma mtima kwachifundo,” NW] cha kuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chiri mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.” (Makonzedwe onse a chipulumutso ndiwo chisonyezero cha kukoma mtima kwapadera kwa Mulungu. Palibe njira imene mbadwa ya Adamu ingapezere chipulumutso mwa iyo yokha mulimonse mmene ntchito zake zingakhalire zabwino. Chipulumutso ndicho mphatso yochokera kwa Mulungu yopatsidwa kwa okhulupirira mu mtengo wa nsembe yotetezera machimo ya Mwana wake.)
Aheb. 5:9, RS: ‘Iye [Yesu] anakhala chipulumutso chosatha kwa onse akumvera iye.’ (Kanyenye wawonjezeredwa.) (Kodi zimenezi zimatsutsana ndi mawu akuti Akristu “amapulumutsidwa mwa chikhulupiriro”? Kutalitali. Kumvera kumangosonyeza kuti chikhulupiriro chawo chiri chenicheni.)
Yak. 2:14, 26: “Chipindulo chake nchiyani, abale anga, munthu akanena, Ndiri nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa? Pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.” (Munthu samalipidwa chipulumutso mwa ntchito zake. Koma aliyense amene ali ndi chikhulupiriro chowona adzakhala ndi ntchito zoyenderana nacho—ntchito za kumvera malamulo a Mulungu ndi Kristu, ntchito zimene zimasonyeza chikhulupiriro chake ndi chikondi. Popanda ntchito zotero, chikhulupiriro chake nchakufa.)
Mac. 16:30, 31, RS: “‘Amuna inu, kodi ndiyenera kuchitanji kuti ndipulumuke?’ Ndipo iwo [Paulo ndi Sila] anati, ‘Khulupirira mwa Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja pako.’” (Ngati mwamuna ameneyo ndi apabanja pake anakhulupiriradi, kodi sakachita mogwirizana ndi chikhulupiriro chawo? Ndithudi.)
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Ndine wopulumutsidwa’
Munganyankhe kuti: ‘Ndiri wokondwera kudziŵa zimenezo, chifukwa chakuti zikundiuza kuti mumakhulupirira Yesu Kristu. Ntchito imene ndikuchitayi ndiyo imene Yesu anaipereka kwa otsatira ake kuti aichite, ndiko kuti, kuuza ena za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wake. (Mat. 24:14)’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kodi Ufumuwo nchiyani? Kodi kudza kwake kudzatanthauzanji kudziko? (Dan. 2:44)’ (2) ‘Kodi ndimikhalidwe yotani imene idzakhala pano padziko lapansi m’boma lakumwamba limenelo? (Sal. 37:11; Chiv. 21:3, 4)’
Kapena munganene kuti: ‘Pamenepo inu mukuzindikira zimene mtumwi Petro adanena, pano pa Machitidwe 4:12, kodi sichoncho? . . . Kodi munayamba mwadabwa kuti kodi dzina la Yesu linaperekedwa ndi yani kwa ife kuti tilikhulupirire?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Yesu mwiniyo akutiuza. (Yoh. 17:3)’ (2) ‘Tawonani kuti Yesu adanena kuti anali atadziŵikitsa dzina la Atate wake. (Yoh. 17:6) Kodi dzina Lakelo ndani? Kodi ndi maunansi otani amene limakuganizitsani? (Eks. 3:15; 34:5-7)’
‘Kodi ndinu wopulumutsidwa?’
Mungayankhe kuti: ‘Kufikira nthaŵi ino, ndiri. Ndikutero chifukwa chakuti ndikuzindikiranso uphungu Wabaibulo wa kusakhala ndi chidaliro chopambanitsa m’khalidwe lathu. Kodi inu muli wozoloŵerana ndi lembali? (1 Akor. 10:12)’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Kodi nchiyani chimene chiri chifukwa cha zimenezo? Kwa anthu amene adabadwanso ndi okhala ndi chiyembekezo cha moyo wakumwamba (Aheb. 3:1), mtumwi Paulo analemba . . . (Aheb. 3:12-14) Kuli mwa kukula m’chidziŵitso cha Mawu a Mulungu kuti timalimbikitsa chikhulupiriro chathu.’
Kapena munganene kuti: ‘Ndingayankhe funsolo mwa kungonena kuti, Inde. Koma kodi munali kuzindikira kuti Baibulo limanena zowonjezereka koposa chipulumutso chimodzi? Mwachitsanzo, kodi munayamba mwalingalira tanthauzo la Chivumbulutso 7:9, 10, 14? . . . Chotero, padzakhala anthu amene adzapulumuka kupyola chisautso chachikulu, kudzakhala ndi moyo pompano padziko lapansi. (Mat. 5:5)’
‘Kodi mumavomereza Yesu kukhala Mpulumutsi wanu?’
Wonani tsamba 433, 434, pamutu wakuti “Yesu Kristu.”
‘Inu mumanena kuti 144 000 okha adzapulumuka’
Mungayankhe kuti: ‘Ndakondwera kuti mwatulutsa mfundoyo kotero kuti ndingathe kukuuzani zimene kwenikweni timakhulupirira. Chipulumutso chiri chotsegukiradi anthu ambiri amene adzasonyeza chikhulupiriro chowona m’makonzedwe amene Mulungu wawapanga kupyolera mwa Yesu. Koma Baibulo limanena kuti ali 144 000 okha amene adzapita kumwamba kukakhala ndi Kristu. Kodi munayamba mwawona zimenezo m’Baibulo? . . . Ziri pano pa Chivumbulutso 14:1, 3.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kodi iwo adzachitanji kumwamba? (Chiv. 20:6)’ (2) ‘Kuli kwachiwonekere kuti iwo adzakhala akulamulira pa anthu ena. Kodi amenewo angakhale ayani? . . . (Mat. 5:5; Mat. 6:10)’