Kumbukirani Tsiku la Yehova Nthaŵi Zonse
“Masiku otsiriza adzafika onyoza.”—2 PETRO 3:3.
1. Kodi Mkristu wina wamakono anasonyeza motani kuti amaona masiku ano kukhala ofulumira?
MTUMIKI wanthaŵi zonse kwa zaka zoposa 66 analemba kuti: “Nthaŵi zonse ndaona kuti masiku ano ngofulumira. Nthaŵi zonse ndakhala ndikuganiza kuti Armagedo ibwera mkucha. (Chivumbulutso 16:14, 16) Monga atate, ndi atate awo, ndakhala ndi moyo wanga monga analimbikitsira mtumwi [Petro], ‘kukumbukira nthaŵi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.’ Nthaŵi zonse ndaganiza kuti dziko latsopano lolonjezedwalo ndi ‘lenileni ngakhale nlosaoneka.’”—2 Petro 3:11, 12, NW; Ahebri 11:1, NW; Yesaya 11:6-9; Chivumbulutso 21:3, 4.
2. Kodi kukumbukira tsiku la Yehova nthaŵi zonse kumatanthauzanji?
2 Mawu a Petro akuti “kukumbukira nthaŵi zonse” tsiku la Yehova akutanthauza kuti sitiyenera kulichotsa m’maganizo mwathu. Sitiyenera kuiŵala kuti tsiku limene Yehova adzawononga dongosolo ili la zinthu poyamba kukhazikitsa dziko latsopano lolonjezedwalo layandikira kwambiri. Tiyenera kuliona kuti ndi lenileni, kuliona bwino, ngati kuti libwera maŵa. Ndi mmene aneneri akale a Mulungu analionera, ndipo nthaŵi zambiri anati layandikira.—Yesaya 13:6; Yoweli 1:15; 2:1; Obadiya 15; Zefaniya 1:7, 14.
3. Kodi mwachionekere nchiyani chinasonkhezera Petro kupereka uphungu wonena za tsiku la Yehova?
3 Kodi nchifukwa ninji Petro akutilimbikitsa kuona tsiku la Yehova ngati kuti lifika “mkucha,” titero kunena kwake? Chifukwa chakuti ena mwachionekere anayamba kunyoza lingaliro la kukhalapo kwa Kristu kolonjezedwa pamene oipa adzalangidwa. (2 Petro 3:3, 4) Chotero m’chaputala 3 cha kalata yake yachiŵiri, chimene tidzapenda tsopano, Petro akuyankha zonena za onyoza ameneŵa.
Anawachonderera Mwachikondi Kuti Azikumbukira
4. Kodi Petro akufuna kuti tizikumbukira chiyani?
4 Chikondi cha Petro pa abale ake chikuonekera mwa kuwatcha kwake “okondedwa” m’chaputala chimenechi mobwerezabwereza. Powachonderera mwachikondi kuti asaiŵale zimene anaphunzitsidwa, Petro akuyamba ndi kuti: “Okondedwa, . . . nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani; kuti mukumbukire mawu onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwa atumwi anu.”—2 Petro 3:1, 2, 8, 14, 17; Yuda 17.
5. Kodi aneneri ena ananena zotani pa tsiku la Yehova?
5 Kodi “mawu onenedwa kale ndi aneneri oyera” omwe Petro akulimbikitsa oŵerenga kalata yake kukumbukira ndi otani? Eya, aja onena za kukhalapo kwa Kristu m’mphamvu ya Ufumu ndi za chiweruzo cha osapembedza. Poyamba Petro anatchula mawu ameneŵa. (2 Petro 1:16-19; 2:3-10) Yuda akutchula Henoke, amene anali mneneri woyamba m’mbiri wochenjeza za chiweruzo choopsa cha Mulungu pa oipa. (Yuda 14, 15) Pambuyo pa Henoke panatsatira aneneri ena, ndipo Petro sakufuna kuti tiiŵale zomwe iwo analemba.—Yesaya 66:15, 16; Zefaniya 1:15-18; Zekariya 14:6-9.
6. Kodi ndi mawu ati a Kristu ndi atumwi ake omwe amatiuza za tsiku la Yehova?
6 Ndiponso, Petro akuuza oŵerenga kalata yake kukumbukira “lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi.” Lamulo la Yesu limaphatikizapo chenjezo lakuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe . . . , ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.” “Yang’anirani, dikirani, . . . pakuti simudziŵa nthaŵi yake.” (Luka 21:34-36; Marko 13:33) Petro akutilimbikitsanso kulabadira mawu a atumwi. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. Chifukwa chake tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.”—1 Atesalonika 5:2, 6.
Zilakolako za Onyoza
7, 8. (a) Kodi anthu omwe amanyoza mauthenga ochenjeza a Mulungu ali otani? (b) Kodi onyozawo amanenanji?
7 Monga tanenera kale, chinachititsa Petro kupereka uphungu nchakuti ena anayamba kunyozera machenjezo amenewo, monga momwedi Aisrayeli oyambirira ananyodolera aneneri a Yehova. (2 Mbiri 36:16) Petro akufotokoza kuti: ‘Ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni.’ (2 Petro 3:3) Yuda akunena kuti zilakolako za onyoza ameneŵa zili ‘zosapembedza.’ Akuwatcha “anthu auchinyama, opanda uzimu.”—Yuda 17-19, NW.
8 Aphunzitsi onama omwe Petro anati “akutsata zathupi, m’chilakolako cha zodetsa” ayenera kukhala pakati pa onyoza ameneŵa opanda uzimu. (2 Petro 2:1, 10, 14) Monyoza amafunsa Akristu okhulupirika kuti: “Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.”—2 Petro 3:4.
9. (a) Kodi nchifukwa ninji onyoza amayesa kufooketsa changu chopezeka m’Mawu a Mulungu? (b) Kodi kukumbukira tsiku la Yehova nthaŵi zonse kungatiteteze motani?
9 Nkunyozeranji motere? Nkuneneranji kuti kukhalapo kwa Kristu mwina sikudzachitika, kuti Mulungu sanaloŵererepo pa zochita za anthu ndipo sadzatero konse? Eya, mwa kufooketsa changu chopezeka m’Mawu a Mulungu, onyoza auchinyama ameneŵa amayesa kukopa ena kuti achite mphwayi mwauzimu ncholinga choti asamavute kuwanyengerera ndi dyera lawo. Zimenezi zikutilimbikitsa kwambiri lerolino kukhala ogalamuka mwauzimu! Tikumbukiretu tsiku la Yehova ndi kukumbukiranso kuti maso ake ali pa ife nthaŵi zonse! Motero tidzasonkhezereka kutumikira Yehova mokangalika ndi kusunga makhalidwe athu oyera.—Salmo 11:4; Yesaya 29:15; Ezekieli 8:12; 12:27; Zefaniya 1:12.
Ochita Zinthu Dala ndi Opusa
10. Kodi Petro akusonyeza motani kuti onyoza ali olakwa?
10 Onyoza oterowo amanyalanyaza mfundo yofunika kwambiri. Amainyalanyaza dala ndipo amayesa kuiŵalitsanso ena. Chifukwa? Kuti anyenge anthuwo mosavuta. ‘Pakuti ichi aiŵala dala,’ akulemba Petro. Kuiŵala chiyani? “Kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mawu a Mulungu; mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka.” (2 Petro 3:5, 6) Inde, Yehova anachotsadi kuipa padziko lapansi pa Chigumula cha m’tsiku la Nowa, zimenenso Yesu anagogomezera. (Mateyu 24:37-39; Luka 17:26, 27; 2 Petro 2:5) Chotero, kusiyana ndi zomwe onyoza anena, zinthu sizinakhalebe “monga chiyambire chilengedwe.”
11. Kodi ndi kusadekha kotani pa zimene Akristu oyambirira anali kuyembekezera komwe kunasonkhezera ena kuwanyoza?
11 Onyoza angakhale atanyodola Akristu okhulupirika chifukwa zomwe iwo ankayembekezera zinali zisanaonekebe. Yesu ali pafupi kufa, atumwi ake “anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.” Kenako iye ataukitsidwa, iwo anafunsa ngati Ufumu udzakhazikitsidwa pomwepo. Ndiponso, zaka ngati khumi Petro asanalembe kalata yake yachiŵiri, ena ‘anaopsedwa’ ndi “mawu” kapena “kalata,” zomwe anati zinachokera kwa mtumwi Paulo kapena anzake, “monga ngati tsiku la Ambuye lafika.” (Luka 19:11; 2 Atesalonika 2:2; Machitidwe 1:6) Komabe, zomwe ophunzira a Yesuwa anali kuyembekezera sizinali zonama, kokha kuti sanangodekha iwo. Tsiku la Yehova linali kudza!
Mawu a Mulungu Ngodalirika
12. Kodi Mawu a Mulungu akhala motani odalirika pa maulosi ake a “tsiku la Yehova”?
12 Monga tanenera kale, aneneri akale Chikristu chisanayambe nthaŵi zambiri anachenjeza kuti tsiku lobwezera la Yehova layandikira. ‘Tsiku la Yehova’ laling’ono linadza mu 607 B.C.E. pamene Yehova anabwezera chilango pa anthu opulupudza. (Zefaniya 1:14-18) Pambuyo pake, mitundu ina, kuphatikizapo Babulo ndi Igupto, inakumana nalo “tsiku la Yehova” limenelo. (Yesaya 13:6-9; Yeremiya 46:1-10; Obadiya 15) Mapeto a dongosolo lachiyuda m’zaka za zana loyamba analoseredwanso, ndipo anadza pamene magulu a nkhondo a Roma anasakaza Yudeya mu 70 C.E. (Luka 19:41-44; 1 Petro 4:7) Koma Petro akutchula “tsiku la Yehova” lamtsogolo, limene lidzaposa Chigumula cha dziko lonse kukula kwake!
13. Kodi ndi chitsanzo chotani m’mbiri chomwe chikusonyeza kuti mapeto a dongosolo ili la zinthu ngotsimikizirika?
13 Petro akuyamba kufotokoza chiwonongeko chikudzacho mwa kunena kuti: “Ndi mawu omwewo.” Anali atangomaliza kunena kuti “pa mawu a Mulungu,” dziko la Chigumula chisanakhaleko “lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi.” Mkhalidwe umenewo, wofotokozedwa m’mbiri ya Baibulo ya chilengedwe, unatheketsa Chigumula pamene madzi anagwa molamulidwa ndi Mulungu, kapena mawu ake. Petro akupitiriza kuti: “Miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo [a Mulungu] zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.” (2 Petro 3:5-7; Genesis 1:6-8) Tili ndi mawu odalirika a Yehova! Iye adzathetsa “miyamba ndi dziko”—dongosolo ili la zinthu—ndi mkwiyo wake waukali patsiku lake lalikululo! (Zefaniya 3:8) Koma ndi liti?
Kufunitsitsa Kuti Mapeto Adze
14. Nchifukwa ninji tili ndi chidaliro chakuti tsopano tili mu “masiku otsiriza”?
14 Ophunzira a Yesu anafuna kudziŵa pamene mapeto adzadza, chotero anamfunsa kuti: “Chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” Mwachionekere iwo anali kufunsa pamene dongosolo lachiyuda lidzatha, koma yankho la Yesu linagogomezera kwambiri pamene ‘miyamba ndi dziko’ lamakono zidzawonongedwa. Yesu analosera zinthu zonga nkhondo zazikulu, njala, zivomezi, matenda, ndi upandu. (Mateyu 24:3-14; Luka 21:5-36) Kuyambira chaka cha 1914, taona chizindikirocho chikukwaniritsidwa chimene Yesu anapereka cha “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano” limodzinso ndi zinthu zomwe mtumwi Paulo anati zidzadziŵikitsa “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5) Inde, umboni ngwochuluka wakuti tili m’nthaŵi ya mapeto a dongosolo ili la zinthu!
15. Kodi Akristu ayesa kutani mosasamala kanthu za chenjezo la Yesu?
15 Mboni za Yehova zafunitsitsa kudziŵa pamene tsiku la Yehova lidzadza. Chifukwa cha kufunitsitsa kwawoko izo nthaŵi zina zayesa kupeza nthaŵi pamene lidzadza. Koma mwa kuchita zimenezo, izo zakhala zikulephera kulabadira chenjezo la Mbuyawo lakuti ‘sitidziŵa nthaŵi yake,’ monganso anachitira ophunzira oyambirira a Yesu. (Marko 13:32, 33) Onyoza anyodola Akristu okhulupirika poyembekezera zinthu nthaŵi yake isanakwane. (2 Petro 3:3, 4) Ngakhale ndi tero, tsiku la Yehova lidzadza ndithu, akutsimikiza Petro, malinga ndi nthaŵi Yake yoikika.
Tifunika Kuona Zinthu Mmene Yehova Amazionera
16. Kodi ndi chenjezo lotani limene kuli kwanzeru kwa ife kulilabadira?
16 Tiyenera kuona nthaŵi mmene Yehova amaionera, monga akutikumbutsira Petro tsopano kuti: “Koma ichi chimodzi musaiŵale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.” Moyo wathu wazaka 70 kapena 80 ngwaufupi chotani nanga pouyerekezera ndi zimenezo! (2 Petro 3:8; Salmo 90:4, 10) Chotero ngati malonjezo a Mulungu aoneka kuti akuchedwa kukwaniritsidwa, tifunikira kulabadira chenjezo la mneneri wa Mulungu lakuti: ‘Ikachedwa [nthaŵi yoikika] uilindirire; popeza ifika ndithu, osazengereza.’—Habakuku 2:3.
17. Ngakhale kuti masiku otsiriza apitiriza nthaŵi yaitali imene ambiri sanayembekezere, kodi tili ndi chidaliro chotani?
17 Kodi nchifukwa ninji masiku otsiriza a dongosolo ili apitiriza nthaŵi yaitali yomwe ambiri sankayembekezera? Ndi chifukwa chabwino, Petro tsopano akufotokoza kuti: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Yehova amalingalira za ubwino wa anthu onse. Amadera nkhaŵa moyo wa anthu, popeza akuti: “Sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo.” (Ezekieli 33:11) Choncho tiyenera kukhala ndi chidaliro chakuti mapeto adzadza panthaŵi yake kukwaniritsa chifuno cha Mlengi wachikondi ndi wanzeru zonse!
Kodi Nchiyani Chidzapita?
18, 19. (a) Nchifukwa ninji Yehova watsimikiza kuwononga dongosolo ili la zinthu? (b) Kodi Petro akuwafotokoza motani mapeto a dongosolo ili, ndipo kwenikweni nchiyani chidzawonongedwa?
18 Chifukwa chakuti Yehova amakondadi aja amene akumtumikira, adzasesa onse amene amawasautsa. (Salmo 37:9-11, 29) Podziŵa, monganso anadziŵira Paulo poyamba, kuti chiwonongeko chimenechi chidzadza panthaŵi yosayembekezereka, Petro akulemba kuti: “Tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; mmene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa [“zidzadziŵika,” NW].” (2 Petro 3:10; 1 Atesalonika 5:2) Miyamba yeniyeni ndi dziko lapansi sizinawonongeke pa Chigumula, ndipo sizidzatero tsiku la Yehova. Nanga ‘chidzapita,’ kapena kuwonongedwa nchiyani?
19 Maboma aumunthu omwe alamulira anthu monga “miyamba” adzatha ngakhalenso “dziko,” kapena anthu osapembedza. “Chibumo chachikulu” mwina chikusonyeza kufulumira kumene miyamba idzapita nako. “Zam’mwamba,” mbali zimene zimapanga dongosolo lovunda la anthu “zidzakanganuka,” kapena kuwonongeka. Ndipo, “dziko,” kuphatikizapo ‘ntchito zili momwemo zidzadziŵika.’ Yehova adzavumbula kotheratu ntchito zoipa za anthu pamene adzathetsa moyenerera dongosolo lonse la dziko.
Sumikani Maganizo pa Chiyembekezo Chanu
20. Kodi moyo wathu uyenera kukhudzidwa motani ndi chidziŵitso cha zochitika zili mtsogolo?
20 Popeza kuti zochitika zazikulu zimenezi zayandikira, Petro akutero kuti tiyenera kutsata “mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” Palibe chokayikitsa konse! “Miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.” (2 Petro 3:11, 12) Kudziŵa kwathu kuti zochitika zazikulu zimenezi zingadze maŵa kuyenera kukhudza zochita zathu zonse kapena zolinga zathu.
21. Kodi zidzatenga malo a miyamba ndi dziko lamakono nchiyani?
21 Kenako Petro akutiuza zomwe zidzatenga malo a dongosolo lakale, kuti: “Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13; Yesaya 65:17) Aha, ati mpumulo wake kukoma! Kristu ndi olamulira anzake a 144,000 adzapanga boma la “miyamba yatsopano,” ndipo anthu omwe adzapulumuka mapeto a dzikoli adzapanga “dziko latsopano”.—1 Yohane 2:17; Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3.
Khalanibe Achangu ndi Oyera m’Makhalidwe
22. (a) Kodi chidzatithandiza nchiyani kupewa banga lililonse ndi chilema chilichonse chauzimu? (b) Kodi Petro akutichenjeza za ngozi yotani?
22 “Momwemo, okondedwa,” akupitiriza Petro, “popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema. Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso.” Kuliyembekezera mwachidwi tsiku la Yehova ndipo kooneka ngati kuchedwa kwakeko kukuyesa umboni wa kuleza mtima kwa Mulungu kudzatithandiza kupeŵa maŵanga auzimu alionse kapena chilema. Komabe, ngozi ilipo! Petro akuchenjeza kuti m’makalata a “mbale wathu wokondedwa Paulo . . . muli zina zovuta kuzizindikira, zimene anthu osaphunzira ndi osakhazikika apotoza, monganso atero nawo malembo ena, ndi kudziwononga nawo eni.”—2 Petro 3:14-16.
23. Kodi chenjezo lomaliza la Petro nlotani?
23 Mwachionekere aphunzitsi onama anapotoza makalata a Paulo onena za chisomo cha Mulungu, kuwagwiritsira ntchito monga chifukwa chotsatirira zilakolako zonyansa. Mwina Petro akuganiza zomwezo pamene akulemba chenjezo lake lotsazikirali: “Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osayeruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.” Ndiye akumaliza kalata yake, akumalimbikitsa kuti: “Kulani m’chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu.”—2 Petro 3:17, 18.
24. Kodi ndi maganizo otani omwe atumiki onse a Yehova ayenera kukhala nawo?
24 Ndithudi, Petro akufuna kulimbikitsa abale ake. Akulakalaka kuti onse akhale ndi maganizo a Mboni ya zaka 82 yogwidwa mawu poyamba nkhaniyi: “Ndakhala moyo wanga monga analimbikitsira mtumwiyo, ‘kukumbukira nthaŵi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.’ Nthaŵi zonse ndaganiza kuti dziko latsopano lolonjezedwalo ndi ‘lenileni ngakhale nlosaoneka.’” Ife tonse tikhaletu ndi moyo wathu chimodzimodzi.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ‘kukumbukira tsiku la Yehova nthaŵi zonse’ kumatanthauzanji?
◻ Kodi onyoza amanyalanyaza dala chiyani, ndipo chifukwa ninji?
◻ Kodi onyoza anyodola Akristu okhulupirika pachifukwa chotani?
◻ Kodi ndi maganizo otani omwe tiyenera kukhala nawo?
[Chithunzi patsamba 23]
Kumbukirani tsiku la Yehova nthaŵi zonse . . .
[Chithunzi patsamba 24]
. . . ndi dziko latsopano lomwe lidzatsatirapo