Mutu 20
Nthaŵi Zonse Kumbukirani Tsiku la Yehova
CHIMODZI mwa zinthu zoyambirira zimene munaphunzira m’Baibulo n’chakuti cholinga cha Yehova ndicho kuti dziko lonse lapansi likhale paradaiso. M’dziko latsopano limenelo, simudzakhalanso nkhondo, umbanda, umphaŵi, matenda, mavuto, ndi imfa. Ngakhale akufa adzauka. Komatu ndiye tikuyembekeza zinthu zosangalatsa kwambiri! Chimene chikusonyeza kuti zimenezi zayandikira kwambiri ndi umboni umene ulipo wakuti kukhalapo kwa Kristu kosaonekako monga Mfumu yolamulira kunayamba mu 1914 ndi kuti chichokereni nthaŵi imeneyo tili m’masiku otsiriza a dziko loipali. Mmene masiku otsirizaŵa azidzatha, Yehova adzawononga dziko ili ndi kubweretsa dziko latsopano limene walonjeza!
2 Baibulo limanena kuti nthaŵi ya chiwonongeko imene ikudzayo ndi “tsiku la Ambuye.” (2 Petro 3:10) Ndilo “tsiku la mkwiyo wa Yehova” woyakira dziko lonse la Satana. (Zefaniya 2:3) Tsiku limenelo lidzafika pa chimake mu ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse . . . , yotchedwa m’Chihebri Harmagedo [Armagedo],’ pamene “mafumu a dziko lonse” adzawonongedwa. (Chivumbulutso 16:14, 16) Kodi moyo wanu ukusonyezadi kuti mumakhulupirira zoti “tsiku la Yehova” layandikira?—Zefaniya 1:14-18; Yeremiya 25:33.
3 Baibulo silitiuza tsiku lenileni pamene Yesu Kristu adzadza monga Wakupha woikidwa ndi Yehova kudzawononga dziko la Satana. “Za tsiku ilo, kapena nthaŵi yake sadziŵa munthu, angakhale angelo m’Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye,” anatero Yesu. (Marko 13:32) Ngati ena sam’kondadi Yehova, amaiŵala za tsikulo ndipo amalondola zimene amafuna pamoyo wawo. Koma amene amam’kondadi amam’tumikira ndi moyo wawo wonse, ngakhale sakudziŵa kuti mapeto a dziko loipa limeneli afika liti.—Salmo 37:4; 1 Yohane 5:3.
4 Pochenjeza okonda Yehova, Yesu anati: “Yang’anirani, dikirani, . . . pakuti simudziŵa nthaŵi yake.” (Marko 13:33-37) Akutilimbikitsa kuti tisalole madyaidya ndi kuledzera kapena “zosamalira za moyo uno” kutitangwanitsa kwambiri moti n’kuiŵala kuopsa kwa nthaŵi imene tikukhala.—Luka 21:34-36; Mateyu 24:37-42.
5 Momwemonso, Petro akutilangiza kukumbukira nthaŵi zonse “kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, mmenemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam’mwamba [“zimene zimapanga miyamba ndi dziko,” NW] zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.” Maboma onse a anthu—“miyamba”—adzawonongeka, ngati mmenenso adzawonongekera anthu onse oipa—“dziko”—limodzinso ndi ‘zimene zimapanga dziko,’ kutanthauza maganizo ndi ntchito za m’dziko loipali, monga mzimu wake wosafuna kudalira Mulungu ndi moyo wake wachiwerewere ndi wokonda chuma. M’malo mwake, padzakhala “miyamba yatsopano [Ufumu wakumwamba wa Mulungu], ndi dziko latsopano [gulu latsopano la anthu apadziko lapansi]” mmene “mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:10-13) Zinthu zogwedeza dziko zimenezi zidzachitika modzidzimutsa ndipo tsiku lake ndi nthaŵi yake n’zosayembekezeka.—Mateyu 24:44.
Tikhale Atcheru Poona Chizindikiro
6 Chifukwa cha nthaŵi imene tikukhala, tifunika kudziŵa bwino mbali zonse za chizindikiro chimene chimasonyeza kuti ano ndi masiku otsiriza—“mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” Musaiŵale kuti pamene Yesu anayankha funso la ophunzira ake, lolembedwa pa Mateyu 24:3, zina zimene anafotokoza m’mavesi 4 mpaka 22 zinakwaniritsidwa pang’ono chabe pa dziko la Ayuda kuyambira mu 33 C.E. mpaka 70 C.E. Koma ulosi umenewu unayamba kukwaniritsidwa kwambiri kuyambira 1914, nthaŵi ya ‘[kukhalapo (kwa Kristu), NW] ndi ya mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.’ Mateyu 24:23-28 amasimba zimene zinachitika kuyambira mu 70 C.E. mpaka nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu. Zimene zikusimbidwa pa Mateyu 24:29–25:46 zikuchitika m’nthaŵi ya mapeto.
7 Ifetu aliyense payekha tifunika kukhala tcheru kuona zochitika ndi maganizo amene akukwaniritsa chizindikiro chimenecho. Tikamagwirizanitsa zimenezi ndi ulosi wa Baibulo, zidzatithandiza kuti nthaŵi zonse tizikumbukira tsiku la Yehova. Zidzatithandizanso kulankhula ndi mtima wonse pochenjeza ena kuti tsiku limenelo layandikira. (Yesaya 61:1, 2) Tili ndi zimenezi m’maganizo, tiyeni tipende mafunso otsatiraŵa amene akusonyeza mbali za chizindikiro chimenecho, zolembedwa pa Mateyu 24:7 ndi Luka 21:10, 11.
Kodi ndi motani mmene ‘kuukirana kwa mtundu umodzi ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina’ kumene analoserako kunakwaniritsidwira mwapadera kuyambira 1914? Tikanena za nkhondo, n’chiyani chachitika chichokereni nthaŵiyo?
Kodi mukukumbukira kuti ndi mliri uti umene mu 1918 unapha anthu ambiri kuposa nkhondo yoyamba ya padziko lonse? (Onani buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, tsamba 103, ndime 7.) Ngakhale kuti anthu akudziŵa zambiri za mankhwala, kodi ndi matendanso ena ati ambiri amene akuphabe anthu mamiliyoni ochuluka?
Kodi njala yakhudza motani dziko lapansi ngakhale kuti m’zaka za ma 1900 sayansi inapita patsogolo kwambiri?
Kodi chimakutsimikizirani n’chiyani kuti 2 Timoteo 3:1-5, 13 amasimba mmene zinthu zaipira pamene tikuyandikira mapeto a masiku otsiriza ndipo osati zoti ndi mmene moyo wakhalira nthaŵi zonse?
Kulekanitsa Anthu
8 Palinso zinthu zina zofunika zimene Yesu anati zidzachitika pa chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano. Mwa zimenezi pali kulekanitsa “ana a Ufumuwo” ndi “ana a woipayo.” Yesu analankhula zimenezi m’fanizo lake la munda wa tirigu umene mdani anabzalamonso namsongole. “Tirigu” m’fanizo lakelo akuimira Akristu oona odzozedwa. “Namsongole” ndi aja amene amadzitcha Akristu koma ali “ana a woipayo” chifukwa chokanirira m’dziko limene Mdyerekezi akulamulira. Ameneŵa akulekanitsidwa ndi ‘ana a Ufumu [wa Mulungu]’ ndipo akupita ku chiwonongeko. (Mateyu 13:24-30, 36-43) Kodi zimenezi zachitikadi?
9 Nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha, panali kulekanitsa onse odzitcha Akristu kukhala magulu aŵiri: (1) Atsogoleri a Matchalitchi Achikristu ndi anthu awo, amene ananena poyera kuti akugwirizana kwambiri ndi bungwe la League of Nations (lomwe tsopano ndi United Nations) uku ali okhulupirikabe ku dziko lawo, ndi (2) Akristu oona pambuyo pa nkhondoyo, amene ndi mtima wawo wonse anaima kumbali ya Ufumu Waumesiya wa Mulungu, osati kumbali ya mayikoŵa. (Yohane 17:16) Mwa kuyamba kuchita ntchito yolalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” padziko lonse lapansi, iwo anasonyeza kuti ndiwo atumiki enieni a Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Ndiye chinachitika n’chiyani?
10 Choyamba, otsalira a odzozedwa ndi mzimu wa Mulungu anasonkhanitsidwa, amene akuyembekeza kukakhala ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba. Ngakhale kuti iwo anali omwazikana mwa amitundu, anawasonkhanitsa m’gulu limodzi logwirizana. Nthaŵi yakuti asindikizidwe chizindikiro komaliza ikuyandikira.—Chivumbulutso 7:3, 4.
11 Kenako, ntchito yosonkhanitsa a “khamu lalikulu . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe” inayambika motsogozedwa ndi Kristu. Ameneŵa ndiwo a “nkhosa zina” zimene zidzapulumuka “chisautso chachikulu” n’kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. (Chivumbulutso 7:9, 14; Yohane 10:16) Ntchito imeneyi yolalikira Ufumu wa Mulungu mapeto asanadze ikupitiriza mpaka nthaŵi yathu ino. A khamu lalikulu la nkhosa zina, amene panopa chiŵerengero chawo chili m’mamiliyoni, akuthandiza mokhulupirika otsalira odzozedwa kulengeza uthenga umenewu wofunika kwambiri wa Ufumu. Uthenga umenewu ukumveka m’mayiko onse.
Kodi M’tsogolomu Muli Zotani?
12 Zonsezi zikutanthauza kuti masiku otsiriza ali pafupi kutha ndi kuti tsiku la Yehova layandikira kwambiri. Koma kodi alipo maulosi ena oti akwaniritsidwebe tsiku loopsa limenelo lisanafike? Inde. Makamaka, kulekanitsa anthu pa nkhani ya Ufumu sikunathebe. Madera ena kumene kunali chizunzo choopsa kwa zaka zambiri panopa ophunzira atsopano akuwonjezeka. Ngakhale kumene anthu amakana uthenga wabwino, tikamachitira umboni timaonetsa chifundo cha Yehova. Chotero, tiye nayoni ntchito! Yesu akutitsimikizira kuti ntchitoyi ikatha, mapeto afika.
13 Ulosi wina wa Baibulo wofunika kwambiri umati: “Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zoŵaŵa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.” (1 Atesalonika 5:2, 3) Mmene adzafuulire mawu ameneŵa akuti “mtendere ndi mosatekeseka” tidzaona nthaŵi yomweyo. Koma tikudziŵa kuti sadzatanthauza kuti olamulira dzikoli athetsadi mavuto a anthu. Amene nthaŵi zonse akukumbukira tsiku la Yehova sadzakopeka n’kutengeka ndi chilengezo chimenecho. Akudziŵa kuti nthaŵi yomweyo pasanapite nthaŵi, chiwonongeko chidzabwera.
14 Poyamba chisautso chachikulu, olamulira adzaukira Babulo Wamkulu , ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, ndipo adzamuwononga yense. (Mateyu 24:21; Chivumbulutso 17:15, 16) Zitatha zimenezo, amitundu adzaukira anthu amene akukweza ulamuliro wa Yehova, ndipo iwo akadzangotero, adzaputa mkwiyo wa Yehova umene udzayakira maboma onse andale ndi onse amene ali kumbali yawo, ndipo adzawonongedwa onse kosadzapezekanso. Imeneyotu idzakhala Armagedo, chimake cha chisautso chachikulu. Kenako, Satana ndi ziwanda zake adzaponyedwa m’phompho, ndipo sadzasokonezanso anthu. Mapeto a tsiku la Yehova adzakhala omwewo pamene dzina lake lidzakwezedwa.—Ezekieli 38:18, 22, 23; Chivumbulutso 19:11–20:3.
15 Mapeto a dzikoli adzafika panthaŵi yake yeniyeni, malinga ndi nthaŵi ya Mulungu. Sadzachedwa. (Habakuku 2:3) Kumbukirani, chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. chinafika mwamsanga, pamene Ayuda sanali kuchiyembekezera, komanso pamene anaganiza kuti kunalibenso chowaopsa. Nanga bwanji Babulo wakale? Anali wamphamvu, wodzidalira, ndipo anatetezedwa ndi malinga ake aakulu ndi aataliwo. Komatu anagwa usiku umodzi wokha. Ndi mmenenso chiwonongeko chamwadzidzidzi chidzafikira pa dziko loipa limeneli. Mmene chizidzatero, tidzapezeke ogwirizana pa kulambira koona, pokhala kuti tsiku la Yehovalo tinali kulikumbukira nthaŵi zonse.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• N’chifukwa chiyani tifunika nthaŵi zonse kukumbukira tsiku la Yehova? Ndipo tingachite zimenezo motani?
• Kodi kulekanitsa anthu kumene kukuchitikaku kukutikhudza bwanji ifeyo patokha?
• Kodi n’chiyani chidakali m’tsogolo tsiku la Yehova lisanayambe? Ndiye n’chiyani chimene aliyense wa ife afunika kumachita?
[Mafunso]
1. Kodi munamva bwanji nthaŵi yoyamba imene munaphunzira kuti anthu ali pafupi kulanditsidwa ku mavuto a dziko lakaleli?
2. Kodi “tsiku la Yehova” n’chiyani?
3. (a) Kodi tsiku la Yehova lidzafika liti? (b) Popeza kuti Yehova sanaulule za “tsiku ilo, kapena nthaŵi yake,” kodi ubwino wake ndi wotani?
4. Kodi Yesu anati chiyani potichenjeza?
5. Malinga ndi kufotokoza kwa Petro, kodi tsiku la Yehova lidzadzetsa chiyani?
6. (a) Kodi ndi mbali ziti za yankho la Yesu kwa ophunzira ake zimene zinakhudza mapeto a dziko la Ayuda? (b) Kodi ndi mbali ziti za yankho la Yesu zimene zikukhudza zochitika ndi maganizo a anthu kuyambira 1914?
7. (a) Kodi n’chifukwa chiyani ifeyo aliyense payekha tifunika kukhala tcheru poona mmene zinthu masiku ano zikukwaniritsira chizindikiro? (b) Yankhani mafunso ali kumapeto kwa ndimeyi, kusonyeza mmene chizindikiro chakwaniritsidwira kuyambira 1914.
8. (a) Kodi n’chiyani, chofotokozedwa pa Mateyu 13:24-30, 36-43, chimene Yesu anati chidzachitikanso pa chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano? (b) Kodi fanizo la Yesu limatanthauza chiyani?
9. (a) Nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha, kodi ndi ntchito yaikulu yotani yolekanitsa onse odzitcha Akristu imene inachitika? (b) Kodi Akristu odzozedwa anapereka motani umboni wakuti iwo ndiwo anali atumiki enieni a Ufumuwo?
10. Kodi ntchito yolalikira Ufumu inatheketsa chiyani choyamba?
11. (a) Kodi ndi ntchito yosonkhanitsa iti imene ikupitirira, ndipo ikugwirizana ndi ulosi uti? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu kukutanthauza chiyani?
12. Kodi ntchito yolalikira imene yatsala kuti ichitikebe lisanafike tsiku la Yehova ndi yaikulu bwanji?
13. Malinga ndi 1 Atesalonika 5:2, 3, kodi n’chiyani chapadera chimene chidzachitike, nanga chidzatanthauzanji kwa ifeyo?
14. Kodi pa chisautso chachikulu padzachitika zotani, ndipo zidzatsata ndondomeko yotani?
15. N’chifukwa chiyani kungakhale kupanda nzeru kuganiza kuti tsiku la Yehova lili kutali kwambiri?
[Zithunzi pamasamba 180, 181]
Masiku otsiriza atha posachedwa pamene dziko la Satana lidzawonongedwa