Onjezerani Mtendere Wanu mwa Chidziwitso Cholongosoka
“Kukoma mtima kwapadera ndi mtendere ziwonjezeredwetu kwa inu ndi chidziwitso cholongosoka cha Mulungu ndi cha Yesu Ambuye wathu.”—2 petro 1:2, NW.
1, 2. (a) Nchifukwa ninji unansi wamtendere ndi Mulungu ungayerekezedwe ndi ukwati? (b) Kodi ndimotani mmene tingalimbikitsire mtendere wathu ndi Mulungu?
UNANSI wa mtendere wokhazikitsidwa ndi Yehova Mulungu pa ubatizo wanu uli, mnjira zina, monga ukwati. Ngakhale kuti tsiku la ukwati liri losangalatsa, liri kokha chiyambi chaunansi wapadera. Ndi kuyesetsa, nthawi, ndi kuzolowera, unansi wa muukwati umakhala wosangalatsa kwambiri, kukhala ngaka mkati mwa nthawi za nsautso. Chotero, mwa kusamalitsa ndi thandizo la Yehova, mungawonjezere mtendere wanu ndi iye.
2 Mtumwi Petro analongosola ndimotani mmene awo amene “adalandira chikhulupiriro” angalimbikitsire mtendere wawo ndi Mulungu. Iye analemba: “Kukoma mtima kwapadera ndi mtendere ziwonjezeredwetu kwa inu ndi chidziwitso cholongosoka cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.”—2 Petro 1: 1, 2, NW.
“Chidziwitso Cholongosoka cha Mulungu”
3. Kodi nchiyani chimene kukhala ndi chidziwitso cholongosoka cha Yehova ndi Yesu kumatanthauza?
3 Liwu la Chigriki kaamba ka “chidziwitso cholongosoka” (e-pi’gno-sis) logwiritsidwa ntchito mu lembali limatanthauza nzeru yathithithi, yozama. Formu la verebu lingalozere ku chidziwitso chopezedwa mwachokumana nacho chaumwini ndipo likugwiritsidwa ntchito monga “kudziwitsa” pa Luka 1:4. Wophunzira wa Chigriki Culverwel akulongosola kuti kwa iye liwulo limatanthauza kukhala “wozolowerana bwino ndi chinthu chimene ndinadziwa kale; kawonedwe kachindunji ka chinthu chomwe ndinawona kale patali.” Kupeza “chidziwitso cholongosoka” kumaphatikizamo kumudziwa Yehova ndi Yesu mwathithithi monga anthu, kukhala ozolowerana bwino ndi mikhalidwe yawo.
4. Kodi ndimotani mmene tingawonjezerere chidziwitso chathu cha Mulungu, ndipo kodi nchifukwa ninji ichi chimawongolera mtendere wathu ndi iye?
4 Njira ziwiri zopezera chidziwitso chimenechi ziri mwaphunziro laumwini labwino ndi kupezeka mokhazikika pa misonkhano ndi anthu a Mulungu. M’njira zimenezi mudzaphunzira momvekera bwino ndimotani mmene Mulungu amakhalira ndi zimene iye amalingalira. Mudzapanga chifaniziro cha iye cha maganizo chotsimikizirika cha umunthu wake. Koma kudziwa Mulungu mwathithithi kumatanthauza kutsanzira ndi kusonyeza chifaniziro chimenechi. Mwachitsanzo, Yehova analongosola munthu yemwe amasonyeza kupanda dyera kwa umulungu, ndipo kenaka Iye anati: “Kodi kumeneko sikundidziwa ine?” (Yeremiya 22:15, 16; Aefeso 5:1) Kutsanzira Mulungu mwathithithi kumawonjezera mtendere wanu ndi iye chifukwa mumawongokera mwa kuvala umunthu watsopano, “umene mwa [chidziwitso cholongosoka, NW]uli kukonzedwa watsopano monga mwachifanizo cha iye amene anamlenga iye.” Mumakhala osangalatsa kwambiri kwa Mulungu.—Akolose 3:10.
5. (a) Kodi ndimotani mmene chidziwitso cholongosoka chinathandizira mkazi Wachikristu mmodzi? (b) Kodi ndi mnjira ziti mmene mokulira tingatsanzirire Yehova mosamalitsa?
5 Mkazi mmodzi Wachikristu wotchedwa Lynn anachipeza icho kukhala chovuta kukhululukira chifukwa chakusamvana ndi Mkristu mnzake. Koma phunziro laumwini losamalitsa la Lynn linamupangitsa iye kusanthula mkhalidwe wake. “Ndinakumbukira mtundu wa Mulungu umene Yehova ali, mmene iye sasungira udani,” iye anatero. “Ndinalingalira za zinthu zazing’ono zonse zimene timachita kwa Yehova tsiku liri lonse, koma iye sawerengera izo. Nkhani imeneyi ndi mlongo wanga Wachikristu inali yaing’ono kwambiri mkuyerekeza. Chotero nthawi iriyonse ndinamuwona iye, ndinanena kwa inemwini, ‘Yehova amamkonda iye monga mmene amandikondera ine.’ Ichi chinandithandiza ine kulaka vuto langa.” Kodi mumawona madera mmene inunso mumafunikira kutsanzira Yehova mosamalitsa?—Masalmo 18:35; 103:8, 9; Luka 6:36; Machitidwe 10:34, 35; 1 Petro 1:15, 16.
Chidziŵitso Cholongosoka cha Kristu
6. Kodi ndimotani mmene Yesu Kristu anasonyezera kuti ntchito yolalikira inali yoyambirira kwa iye?
6 Kukhala ndi chidziwitso cholongosoka cha Yesu kumafunikira kukhala ndi “maganizo a Yesu” ndi kumutsanzira iye. (1 Akorinto 2: 16) Yesu anali wolalikira wa chowonadi wanthumanzi. (Yohane 18:37) Mzimu wake wa kulalikira wamphamvu sunamangidwe ndi kunyada kwa anthu a m’mudziwo. Ngakhale kuti Ayuda ena anada a Samariya, iye anachitira umboni kwa mkazi wa Chisamariya pa chitsime. Nchifukwa, ngakhale kulankhula pabwalo kwanthawi yaitali ndi mkazi wina aliyense kungawonedwe moipa!a Koma Yesu sanalole maganizo a kumaloko kumuletsa iye kupereka umboni. Ntchito ya Mulungu inali yopatsa mpumulo. Iye anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” Chimwemwe chakuwona chivomerezo cha anthuwo, monga mkazi wa Chisamariya ndi ambiri a anthu a m’mudzimo, chinamukwaniritsa Yesu monga chakudya.—Yohane 4:4-42; 8:48.
7. (a) Chidziwitso cha Yesu chiyenera kutifulumiza ife kuchita chiyani? (b) Kodi Mulungu amayembekezera atumiki ake onse kuchita unyinji wofanana wa ntchito ya kulalikira? Longosolani.
7 Kodi mumaganiza monga Yesu? Mutapatsidwa, kuyamba kukambitsirana ponena za Baibulo ndi mlendo kuli kovuta kwa ambiri ndipo kawirikawiri kumanyazitsidwa ndi ena a mudera. Komabe, kukhala ndi kaimidwe ka maganizo kofanana ndi kamene Yesu anali nako, sitingapulumuke chenicheni ichi: Tiyenera kuchitira umboni. Ngakhale kuli tero, sikuti onse angachite unyinji wofananawo wa kulalikira. Ichi chimasiyana malinga ndi kuthekera kwathu ndi mikhalidwe. Chotero musaganize kuti Mulungu sakhutiritsidwa ndi utumiki wanu wopatulika. Chidziwitso chathu cha Yesu, ngakhale kuli tero, chiyenera kutifulumiza ife kuchita kuthekera kwathu. Yesu anayamikira utumiki wa mtima wonse.—Mateyu 13:1823; 22:37.
Kufunika kwa Kuda Choipa
8, 9. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene Mulungu amadana nazo, ndipo kodi ndimotani mmene tingasonyezere chidani chofananacho?
8 Chidziwitso cholongosoka chimatithandizanso ife kuyamikira ndi zinthu ziti zimene zimadedwa ndi Yesu ndi Yehova. (Ahebri 1:9; Yesaya61:8) “Ziripo zinthu zisanu ndi chimodzi Mulungu azida; ngakhale zisanu ndiziwiri zimnyansa: maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu mmangu mmangu; mboni yonama yonong’ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.” (Miyambo 6:16-19) Kawonedwe kamenekandi mtundu umenewu wa khalidwe uli “wonyansa mu moyowake.” Liwu la Chihebri logwiritsidwa ntchito pano kaamba ka “chonyansa” limachokera ku liwu lotanthauza “kunyansidwa, kufuna kusanzitsa,” “kukhala woipidwa ku, monga ngati ku chimene chiri choipa ku malingaliro onse; kunyansidwa nacho, kudana nachomwaukali.” Chotero kuti tikhale pa mtenderendi Mulungu, tiyenera kukhala ndi kudana ndi choipa kofananako.
9 Mwachitsanzo, chotsani “maso onyenga” kapena kuwonetsera kuli konse kwa kunyada. Pambuyo pa ubatizo ena amadzimva kuti safunanso thandizo lokhazikika la awo amene anawaphunzitsa iwo. Koma Akristu atsopano ayenera modzichepetsa kulandira thandizo pamene akukhala ozikidwa bwino mchowonadi. (Agalatiya 6:6) Ndiponso, pewani kujeda, kumene mokhweka kungayambitse “kupikisanitsa abale.” Mwakufalitsa mphekesera yopanda chifundo, kunyodola kosalungamitsidwa, kapena bodza, sitingakhale tikukhetsa” mwazi wosachimwa, koma mowonadi tingawononge khalidwe labwino la wina. Sitingakhale pa mtendere ndi Mulungu ngati sitiri pa mtendere ndi abale athu. (Miyambo 17:9; Mateyu 5: 23, 24) Mulungu amanenanso m’Mawu ake kuti “adana nako kulekana.” (Malaki 2:14, 16) Ngati muli wokwatira, kodi inu, chotero, mumagwirirapo ntchito kusunga ukwati wanu kukhala wamphamvu? Kodi kutyasira ndi kutenga mwawi wosayenerera ndi mkazi wa mnzanu kuli konyansa kwa inu? Kodi inu, mofanana ndi Yehova, mumadana nalo dama la chigololo? (Deutronomo 23:17, 18) Kudana nawo machitachita amenewa sikuli kokhweka, popeza zimenezi zimawoneka zosangalatsa ku thupi lathu lochimwa, ndipo zimamwetuliridwa ndi dziko.
10. Kodi ndimotani mmene tingakulitsire udani kaamba ka choipa?
10 Monga thandizo kukulitsa chidani kaamba ka choipa, pewani kusangalatsidwa ndi makanema, maprogramu amawailesi akanema, kapena mabuku osonyeza kukhulupirira mizimu, dama, kapena chiwawa. (Deutronomo 18:1012; Masalmo 11:5) Mwakupanga kuchita cholakwa kuwoneka ‘kukhala kosaipa kwenikweni’ kapena kukhala kosangalatsa, zosangulutsa zoterozo zimalepheretsa kuyesetsa kwakukulitsa kudana nacho kwa umulungu kwa icho. Kumbali ina, pemphero lofunitsitsa lingathandize, popeza Yesu anati: “Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m’kuyesedwa. Mzimutu uli wakufuna, koma thupi liri lolefuka.” (Mateyu 26:41) Ponena za kukumanizidwa ndi chikhumbo champhamvu chakuthupi, Mkristu mmodzi ananena kuti: “Ndimadzipanga inemwini kupemphera. Nthawi zina ndimadziwona kukhala wosayenera kumufikira Yehova, koma mwakudzipanga inemwini kupanga icho, mwakudandaulira kwa iye, ndimapeza mphamvu yofunikira.” Mungachite bwino kumamvetsetsa nchifukwa ninji Yehova amanyansidwa ndi kuchita cholakwa ngati mubwe-reramo m’maganizo anu mu zotulukapo zake zochititsa chisoni.—2 Petro 2:12, 13.
11. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingativute ife nthawi zina?
11 Mosasamala kanthu za kukhala ndi mtendere ndi Mulungu, inu nthawi zina mungavutitsidwe ndi zitsenderezo za tsiku ndi tsiku ndi mayesero ndipo mwinamwake ndi kufooka kwa inuenu. kumbukirani, mwadzipanga inu mwini kukhala chandamali chapadera cha Satana. Iye amamenya nkhondo motsutsana ndi awo amene amasunga malamulo a Mulungu ndipo ali Mboni za Yehova! (Chivumbulutso 12:17) Ndimotani, nanga, mmene mtendere wanu wa mkatikati ungasungidwire?
Kuchita Nawo Masautso Osokoneza Mtendere
12. (a) Kodi nchiyani chimene chiri chiyambi cha oahpo 34? (b) Kodi ndimotani mmene malemba amalongosolera maganizo a Davide mkati mwa chokumana nacho chimenechi?
12 “Masautso a olungama mtima achuluka,” analemba motero Davide pa Masalmo 34:19. Malinga ndi mawu apamwamba pa Salmo limeneli, Davide analilemba pamene lye anali pafupi kuyang’anizana ndi imfa. Kuthaŵa kuchokera kwa Mfumu Sauli, Davide anapita kukabisala kwa Akisi, mfumu ya Chifilisiti ya ku Gati. Antchito a mfumu imeneyo anamuzindikira Davide ndipo, kukumbukira zigonjetso zake zakale za nkhondo kaamba ka Aisrayeli, anadandaula kwa Akisi. Pamene Davide anamvera kukambitsiranako, iye “anasunga mawu awa m’mtima mwake, nawopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati.” (1 Samueli 21:10-12) Ndiko nkomwe, iyi inali tauni yakwawo kwa Goliati, ndipo Davide anali atapha ngwazi yawo—anali atanyamula ngakhale lupanga la chimphonacho! Kodi iwo tsopano adzagwiritsira ntchito lupanga lalikululo kudula mutu wake? Kodi nchiyani chimene iye anachita?—1 Samueli 17:4; 21:9.
13. Kodi nchiyani chimene Davide anachita mkati mwa nsautso imeneyi, ndipo kodi ndimotani mmene ife tingatsanzirire chitsanzo chake?
13 Davide anapembedzera Mulungu ndi kulilitsa kaamba ka thandizo. “Munthu uyu wozunzika anapfuula, ndipo Yehova anamumva. Nampulumutsa m’masautso ake onse,” anatero Davide; Iye anatinso: “Nandilanditsa m’mantha anga onse.” (Masalmo 34:4, 6, 15, 17) Kodi inunso mwaphunzira kupembedzera Yehova, kukhuthula mtima wanu mkati mwa nthawi zakudera nkhawa? (Aefeso 6:18; Masalmo 62:8) Ngakhale kuti nsautso yanu singakhale yofanana ndi ya Davide, komabe, mudzapeza kuti Mulungu adzakupatsani inu thandizo panthawi yoyenerera. (Ahebri 4:16) Koma Davide anachita zoposa kupemphera
14. Kodi ndimotani mmene Davide anagwiritsira ntchito “nzeru yakulingalira,“ ndipo kodi nchiyani chimene Mulungu wapereka kutithandiza ife kuchita chofananacho?
14 “Nazisanduliza [Davide] makhalidwe ake pamaso pawo, nadziwonetsera m’manja mwawo ngati wamisala. . . . tsono Akisi ananena ndi anyamata ake. ‘Tawonani, mupenya kuti munthuyo ngwa misala; mwabwera naye kwa ine chifukwa ninji?’” (1 Samueli 21:13-15)Davide analingalira njira mwa imene iye anapulumukira. Yehova anadalitsa zoyesayesa zake. Mofananamo, pamene tayang’anizana ndi mavuto ovuta koposa, Yehova amatiyembekezera ife kugwiritsira ntchito nzeru yathu ya kulingalira ndipo osati kungodikira iye kuti agwirepo ntchito pa iwo kaamba ka ife. Iye watipatsa ife Mawu ake ouziridwa, “kuchenjeza achibwana, . .. chidziwitso ndi nzeru yakulingalira.” (Miyambo 1:4; 2 Timoteo 3:16 ,17) Mulungu waperekanso akulu mu mpingo, omwe angatithandize ife kudziwa ndimotani mmene tingasungire makhalidwe a Mulungu. (1 Atesalomka 4:1, 2) Nthawi zambiri, amuna amenewa angakuthandizeni inu kufufuza zofalitsidwa za Watch Tower Society kaamba kathandizo mkupanga chosankha choyenera kapena kuchita nawo mavuto.
15. Kodi nchifukwa ninji Salmo 34:18 liri lotonthoza?
15 Ngakhale pamene mitima yathu yatipweteka chifukwa cha kufooka kwathupi kapena kulephera, ngati tiri ndi kawonedwe kabwino, tingasunge mtendere wathu ndi Mulungu. Davide anapempha pa Masalmo 34:18: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” Ngati tipempha kaamba ka chikhululukiro ndi kutenga masitepi oyenerera kuwongolera zinthu (makamaka pa zolakwa zazikulu), Yehova adzakhala pafupi nafe, kutichirikiza ife mwa malingaliro.—Miyambo 28:13; Yesaya 55:7; 2 Akorinto 7:9-11.
Chidziwitso Chaumwini Chimapereka Mtendere
16. (a) Kodi ndi iti imene iri njira ina mu imene tingapezere chidziwitso cholongosoka. cha Mulungu? (b) Longosolani mawu a Davide, “talawani, ndipo wonani kuti Yehova ndiye wabwino.”
16 Njira ina mu imene timapezera chidziwitso cholongosoka cha Mulungu, pambali pa kutenga chidziwitso chauzimu, iri kukumana mwaumwini ndi thandizo lake lachikondi. (Masalmo 41:10, 11) Kupulumutsidwa kuchokera ku masautso nthawi zonse sikumatanthauza kutha kwa mwamsanga kapena kutheratu kwa vuto; mungayenere kupitirira kupirira iro. (1 Akorinto 10:13) Ngakhale kuti moyo wa Davide unapulumutsidwa ku Gati, iye anakhalabe wothawa lamulo kwa zaka zingapo, kuyang’anizana ndi tsoka limodzi pambuyo pa Unzake. Kupyola mu izo zonse, Davide anawona chisamaliro ndi chichirikizo cha Yehova. Iye anapitirizabe ndi kupeza mtendere ndi Mulungu, ndipo anaphunzira kuti awo amene amachita tero “sasowa chabwino.” Kuzindikira mwa chokumana nacho chaumwini mmene Yehova anamuchirikizira iye mkati mwa nsautso, Davide anati: “Talawani ndipo wonani kuti Yehova ndiye wabwino, [anthu inu, NW] wodala munthuyo wakukhulupirira iye.”—Masalmo 34:8-10, 14, 15.
17. Mkati mwa nsautso, kodi ndi chotulukapo chotani chimene kubisala mwa Yehova kunakhala nacho pa banja limodzi?
17 Kubisala mwa Yehova mkati mwamavuto kudzakutheketsaninso inu “kulawa ndi kuwona kuti Yehova ndiye wabwino.” Chifukwa changozi, Mkristu wakudera lapakati cha kumadzulo kwa United States anataya ntchito yokhala ndi malipiro abwino yomwe anakhala nayo kwa zaka 14. Popeza analibe ndalama, iye ndi banja lake anapemphera kwa Mulungu. Panthawi imodzimodziyo, ngakhale kuli tero, iwo anachepetsa ndalama zimene amawononga, kuchita kunkha mu minda yapafupipo, ndi kuwedza nsomba kaamba ka chakudya. Ndithandizo lochokera kwa ena mu mpingo ndi mwakugwira ntchito yapakanthawi ngati inapezeka, banja limeneli la anthu anayi linakhoza kupita patsogolo. Chaka chimodzi pambuyo pangoziyo, mayi wanyumbayo anawunikira: “Tingadzinyenge ife eni kuganizira kuti tikudalira pa Yehova. Pamene! kwenikwenidi tikudalira pakuthekera kwathu, mnzathu wa mu ukwati, kapena ntchito yathu. Ife ngakhale kuli tero, taphunziradi kudalira iye yekha. Zinthu zina izi zingachotsedwe, koma Yehova sanatisiye ife nkomwe—osati ngakhale kwakamphindi. Ngakhale kuti tiri kokha ndi zoyenerera zokha, unansi wathu ndi Yehova monga banja uli wathithithi koposa.”
18. Kodi nchiyani chimene chidzakutheketsani inu kupirira ngakhale mavuto opitirira?
18 Inde, vuto la zachuma lingakhale lopita mtsogolo. Kapena mwinamwake wina angakanthidwe ndi matenda osatha akuthupi; kuwombana kwa umunthu ndi wina; kusokonezeka kwa maganizo monga ngati kupsyinjika; kapena unyinji wa mavuto ena. Komabe, mwakudziwa Mulungu mowonadi, mudzakhala ndi chikhulupiriro muchirikizo lake. (Yesaya 43: 10) Chikhulupiriro chosasweka chimenechi chidzakuthandizani inu kupirira ndipo ndi kukhala “ndi mtendere wa umulungu umene umapyola zolingalira zonse.”—Afilipi 4:7.
19. Kodi timadziwa motani kuti Yehova samawona kuvutika kwathu mopepuka?
19 Pamene mukupita pansi pa chokumana nacho chovuta, musaiwale kuti Yehova akudziwa kuti mukuvutika. Mu salmo limene linapangidwa pamene iye anawunikira pa chokumana nacho chake ku Gati, Davide anapempha Yehova: “Sungani misozi yanga m’nsupa yanu; kodi siikhala m’bukhu mwanu?” (Masalmo 56:8) Motsimikizirika, Mulungu anamvetsera pempho la Davide. Ndi chotonthoza chotani nanga kudziwa kuti Mulungu adzasonkhanitsa misozi imeneyo yopangidwa ndi kusauka ndi nkhawa ndi kuika iyi, monga mmene kunaliri, mu nsupa yake, monga mmene wina angaikire mu chotengera choterocho vinyo wapadera kapena madzi akumwa! Misozi yoteroyo nthawi zonse idzakumbukiridwa, inde, kulembedwa m’bukhu la Mulungu. Ndi kuoolowa chotani nanga kulingalira kwa Yehova!
20. Kodi ndimotani mmene tingawonjezereremtendere wathu ndi Mulungu?
20 Chotero ubatizo wanu uli chiyambi cha unansi wa mtendere ndi Mulungu. Mwakukhala wozolowerana bwino ndi mikhalidwe ya umunthu ya Mulungu ndi Yesu, ndipo mwaumwini kukumana ndi chirikizo la Yenova mkati mwa mayeso, mudzawonjezera mtendere wanu ndi Mulungu. Sikokha kuti mudzakhala ndi unansi ndi Yehova womwe umakhala ngaka yachisungiko tsopano koma mudzakhalanso ndi chiyembekezo chapadera chakukhala ndi moyo kosatha mu Paradaiso, kumene mudzapeza “chikondwerero mu mtendere wochuluka.”—Masalmo 37:11, 29.
[Mawu a m’munsi]
a Malinga ndi kunena kwa Talmud, arabi akale analangiza kuti: “Wophunzira sayenera kulankhula ndi mkazi mkhwalala.” Ngati mwambo umenewu unalipo mtsiku la Yesu, mwinamwake chingakhale chifukwa chimene ophunzira ake “anazizwa kuti anali kulankhula ndi mkazi.”—Yohane 4:27.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Kodi ndi mnjira zotani mmene tingapezere chidziwitso cholongosoka cha Mulungu ndi Yesu?
◻ Kutsanzira Mulungu ndi Yesu kudzatipangitsa ife kupanga chiyani?
◻ Kodi ndimotani mmene timatsanzirira kudana ndi choipa kwa Mulungu?
◻ Kodi ndimotani mmene tingasungire mtendere mosasamala kanthu zamavuto?
[Chithunzi patsamba 17]
Yesu anakana kulola kunyada kwapfuko kuletsa kupereka kwake umboni. Kodi mumatsanzira changu chake kaamba ka kulalikira?
[Chithunzi patsamba 18]
Pamene anayang’anizana ndi vuto lalikulu, Davide anapemphera kwa Yehova . . . . . . ndi kusandulika monga wamsala kukonzekera kuthawa. Yehova anamva pemphero la Davide