Mutu 3
Bwenzi Lonyenga la Baibulo
M’mutu uno, tikufotokoza chifukwa chachikulu chimene ambiri a kumaiko osakhala Achikristu amakana kulandira Baibulo monga Mawu a Mulungu. Mogwirizana ndi mbiri, Chikristu cha Dziko chadzinenera kukhala chikukhulupirira m’Baibulo ndi kukhala wolisunga wake. Koma magulu achipembedzo Achikristu cha Dziko agwirizanitsidwa ndi nkhanza zoipa kopambana za mbiri, kuyambira pa Nkhondo za Mtanda ndi zipupula za m’Nyengo Yapakati kukafika ku chipiyoyo cha m’nthaŵi yathu. Kodi khalidwe la Chikristu cha Dziko liri chifukwa chabwino chokanira Baibulo? Chowonadi nchakuti, Chikristu cha Dziko chatsimikizira kukhala bwenzi lonyenga la Baibulo. Ndithudi, pamene Chikristu cha Dziko chinabuka m’zaka za zana lachinayi C.E., nkhondo yomenyera kupulumuka kwa Baibulo inali isanathe konse.
1, 2. (Phatikizamoni mawu oyamba.) (a) Kodi nchifukwa ninji ambiri amakana kulandira Baibulo monga Mawu a Mulungu? (b) Kodi ndintchito yabwino yotani imene inachitidwa mkati mwa zaka za zana loyamba ndi lachiŵiri, komabe kodi ndichochitika chaupandu chotani chimene chinalinkudza?
PODZAFIKA kumapeto kwa zaka za zana loyamba, kulembedwa kwa mabukhu onse a Baibulo kunali kutatsirizidwa. Kuyambira panthaŵi imeneyo kumkabe mtsogolo, Akristu anali patsogolo pa kukopa ndi kufalitsa Baibulo lathunthu. Panthaŵi imodzimodziyo, iwo anali otanganitsidwa kulitembenuzira m’zinenero zofala kopambana za m’nthaŵi imeneyo. Komabe, pamene kuli kwakuti mpingo Wachikristu unali wotanganitsidwa ndi ntchito yokondweretsa imeneyi, kanthu kena kanayamba kupangika kamene kakatsimikizira kukhala kaupandu kwambiri kukupulumuka kwa Baibulo.
2 Chochitika chimenechi chinanenedweratu ndi Baibulo lenilenilo. Panthaŵi ina Yesu anapereka fanizo la mwauna amene anafesa m’munda mwake mbewu zabwino za tirigu. Koma “mmene anthu analinkugona,” mdani anafesa mbewu zimene zikabala namsongole. Mitundu yonse iŵiri ya mbewu inamera, ndipo kwakanthaŵi namsongoleyo anabisa tirigu kuti asawoneke. Mwafanizo limeneli, Yesu anasonyeza kuti chipatso cha ntchito yake chikakhala Akristu owona koma kuti pambuyo pa imfa yake, Akristu onyenga akakwaŵira mumpingo. Potsiriziri pake, kukakhala kovuta kulekanitsa enieni ndi onyenga.—Mateyu 13:24-30, 36-43.
3. Malinga nkunena kwa mtumwi Petro, kodi nchiyani chimene chikakhala chiyambukiro cha “Akristu” onga namsongole ponena za chikhulupiriro chawo m’Baibulo?
3 Mtumwi Petro anachenjeza mwachigogogo za chiyambukiro chimene “Akristu” onga namsongole ameneŵa akakhala nacho panjira ya mmene anthu akawonera Chikristu ndi Baibulo. Iye anachenjeza kuti: “Padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Ameneŵawa adzaloŵetsamo mwakachetechete timipatuko towonongetsa ndipo adzakana ngakhale mbuye wawo amene anawagula, akumadzetsera chiwonongeko cha mwamsanga pa iwo eni. Ndiponso, ambiri adzatsata machitidwe awo a khalidwe loipa, ndipo chifukwa cha ameneŵa, njira ya chowonadi idzanyozedwa.”—2 Petro 2:1, 2, NW.
4. Kodi ndimotani mmene maulosi a Yesu ndi Petro anakwaniritsidwira mkati mwa zaka za zana loyamba?
4 Ngakhale mkati mwa zaka za zana loyamba, maulosi a Yesu ndi Petro anali kukwaniritsidwa. Amuna okhumbira malo anakwaŵira mumpingo Wachikristu nafesa mgaŵano. (2 Timoteo 2:16-18; 2 Petro 2:21, 22; 3 Yohane 9, 10) Mkati mwa zaka mazana aŵiri zotsatirapo, chiyero cha chowonadi cha Baibulo chinaipitsidwa ndi nthanthi Yachigriki, ndipo ambiri molakwika anafikira pa kulandira ziphunzitso zachikunja monga chowonadi cha Baibulo.
5. Kodi nkusintha kwa njira yoyendetsera zinthu kotani kumene Constantine anayambitsa kuchiyambiyambi kwa zaka za zana lachinayi?
5 M’zaka za zana lachinayi, mfumu Yachiroma Constantine analandira “Chikristu” monga chipembedzo cha Boma Laufumu Wachiroma. Koma “Chikristu” chimene iye anachidziŵa chinali chosiyana ndi chipembedzo chimene chinalalikiridwa ndi Yesu. Pofika panthaŵiyo, “namsongole” anali kufunga, monga momwedi Yesu anali ataneneratu. Komabe, tingathe kukhala otsimikizira kuti mkati mwa nthaŵi yonseyo, panali ena amene anaimira Chikristu chowona ndipo anagwira ntchito zolimba kutsatira Baibulo monga Mawu ouziridwa a Mulungu.—Mateyu 28:19, 20.
Kutembunza Baibulo Kutsutsidwa
6. Kodi ndiliti pamene Chikristu cha Dziko chinayamba kuumbika, ndipo kodi chipembedzo cha Chikristu cha Dziko chinasiyana motani ndi Chikristu cha Baibulo?
6 Munali m’nthaŵi ya Constantine kuti Chikristu cha Dziko monga momwe tikuchidziŵira lerolino chinayamba kuumbika. Kuyambira panthaŵi imeneyo kumkabe mtsogolo, mpangidwe Wachikristu choluluzika chimene chinayamba kumera mizu sichinalinso gulu lachipembedzo chabe. Chinali mbali ya boma, ndipo atsogoleri ake anachita mbali yaikulu m’ndale zadziko. Potsirizira pake, tchalitchi chopatuka chinagwiritsira ntchito mphamvu zake za ndale zadziko m’njira imene inali yotsutsana kotheratu ndi Chikristu cha Baibulo, chikumayambitsa chiwopsezo china chaupandu ku Baibulo. Motani?
7, 8. Kodi ndiliti pamene papa anasonyeza chitsutso m’kutembenuzidwa kwa Baibulo, ndipo kodi nchifukwa ninji iye anatero?
7 Pamene Chilatini chinazimiririka monga chinenero cha tsiku ndi tsiku, matembenuzidwe atsopano a Baibulo anali kufunika. Koma Tchalitchi Chachikatolika sichinafunenso zimenezi. Mu 1079 Vratislaus, amene pambuyo pake anakhala mfumu ya ku Bohemia, anapempha chilolezo kwa Papa Gregory VII kuti atembenuzire Baibulo m’chinenero cha nzika zake. Yankho la papa linali lakuti toto. Iye anafotokoza kuti: “Kuli kowonekera bwino kwa awo amene amalisinkhasinkha kaŵirikaŵiri, kuti sikunali kopanda chifukwa kuti kunakondweretsa Mulungu Wamphamvuyonse kuti malemba opatulika ayenera kukhala chinsinsi mmalo ena, kuwopera kuti, ngati akanakhala owonekera bwino kwa anthu onse, mwamwaŵi iwo akanaŵerengedwa kukhala amtengo wapatali mochepera ndi kukhala okhoza kunyozedwa; kapena likamvedwa moluluzika ndi awo amene anali osaphunzira mokwanira, ndi kutsogolera ku cholakwa.”1
8 Papa anafuna kuti Baibulo lisungidwe m’chinenero Chachilatini chimene panthaŵi ino chinali chakufa. Zamkati mwake zinayenera kusungidwa ziri “chinsinsi,” osati kuzitembenuzira m’chinenero cha anthu wamba.a Vulgate Yachilatini ya Jerome, imene inatulutsidwa m’zaka za zana lachi 5 inapangitsa Baibulo kukhala lopezeka kwa onse, tsopano inakhala njira yolisungira kukhala lobisika.
9, 10. (a) Kodi kutsutsa kwa Roma Katolika ku kutembenuzidwa kwa Baibulo kunabuka motani? (b) Kodi nchiyani chimene chinali chifuno cha chitsutso cha Tchalitchi ku Baibulo?
9 Pamene Zaka za m’Zana la Pakati zinapitirizabe, kaimidwe ka Tchalitchi kotsutsana ndi Mabaibulo a anthu a pamalopo kanauma kwambiri. Mu 1199 Papa Innocent III analemba kalata yamphamvu kwambiri kwa bishopo wamkulu wa Metz, Jeremani, kwakuti bishopo wamkuluyo anawotcha Mabaibulo onse achinenero Chachijeremani amene iye akanatha kuwapeza.3 Mu 1229 sinodi ya Toulouse, France, inapereka lamulo lakuti “anthu wamba” sakayenera kukhala konse ndi mabukhu a Baibulo m’chinenero cha anthu wamba.4 Mu 1233 sinodi ya chigawo cha Tarragona, Spanya, idalamula kuti mabukhu onse a “Chipangano Chakale kapena Chatsopano” ayenera kuperekedwa kuti awotchedwe.5 Mu 1407 sinodi ya atsogoleri achipembedzo oitanidwa kudza pa Oxford, Mangalande, ndi Bishopo Wamkulu Thomas Arundel anakaniza kwantheradi kutembenuzidwa kwa Baibulo kuloŵa m’Chingelezi kapena m’chinenero china chirichonse chamakono.6 Mu 1431, m’Mangalande momwemo, Bishopo Stafford wa ku Wells anakaniza kutembenuzidwa kwa Baibulo m’Chingelezi ndi kukhala ndi matembenuzidwe oterowo.7
10 Akuluakulu achipembedzo ameneŵa sanali kuyesa kuwononga Baibulo. Iwo anali kuyesa kulikwirira, kulisunga m’chinenero chimene oŵerengeka chabe akatha kuliŵerenga. Mwanjira imeneyi iwo anayembekezera kuletsa chimene iwo anachitcha chipanduko koma chimene kwenikweni chinakhala zitokoso kuulamuliro wawo. Ngati iwo akadapambana, Baibulo likadangokhala chinthu chofuna kudziŵidwa ndi anthu anzeru zapamwamba chabe, lokhala ndi chiyambukiro chochepa kapena kusoŵeratu m’miyoyo ya anthu wamba.
Akatswiri a Baibulo
11. Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Julián Hernández anazembetsera Mabaibulo achinenero cha Chispanya m’Spanya?
11 Komabe, mosangalalatsa, anthu ambiri owona mtima anakana kutsatira zilengezo zimenezi. Koma kukana kumeneko kunawaika paupandu. Anthu ena anavutika kwambiri kaamba ka “tchimo” la kukhala ndi Baibulo. Mwachitsanzo, talingalirani, chochitika cha Msipanya wotchedwa Julián Hernández. Malinga ndi kunena kwa History of Christian Martyrdom ya Foxe, Julián (kapena, Juliano) “anatsimikizira kukapereka kuchokera ku Jeremani kukaloŵetsa m’dziko la kwawo chiŵerengero chachikulu cha Mabaibulo, obisidwa m’mikunda, ndi kulongedzedwa ngati vinyo wa ku Rhine.” Iye anaperekedwa ndi kugwidwa ndi Bwalo Lofunsa Mafunso la Roma Katolika. Awo kwa amene Mabaibulo anali kumka “anazunzidwa onse mosasankha, ndiyeno ochuluka a iwo anaweruziridwa kuti apatsidwe zilango zosiyanasiyana. Juliano anawotchedwa, makumi aŵiri a iwo anakazingidwa ataikidwa pambano, angapo anaikidwa m’ndende kwa moyo wawo wonse, ena anakwapulidwa ndi chamboko poyera, ena anatumizidwa kuzibalo zokapalasa mabwato kunyanja.”8
12. Kodi tikudziŵa bwanji kuti akuluakulu achipembedzo a m’Zaka za Nyengo ya Pakati sanaimire Chikristu cha Baibulo?
12 Ha, ndi kugwiritsiridwa ntchito molakwa chotani nanga kwaulamuliro kowopsa! Mwachiwonekere, akuluakulu achipembedzo ameneŵa sanali konse oimira a Chikristu Chabaibulo! Baibulo lenilenilo linavumbula kuti iwo anali ayani pamene iro linati: “Mmenemo awoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi, yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. Pakuti uwu ndiuthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo namupha mbale wake.”—1 Yohane 3:10-12.
13, 14. (a) Kodi nchenicheni chapadera chotani ponena za Baibulo mkati mwa Zaka za Nyengo ya Pakati chimene chimasonyeza kukhala kwake ndi chiyambi chaumulungu? (b) Kodi ndimotani mmene mkhalidwewo unasinthira ponena za Baibulo mu Ulaya?
13 Komabe, nkwapadera chotani nanga kuti amuna ndi akazi anali ofunitsitsa kudziika pachiswe mwa kukumana ndi kuchitiridwa moipa koteroko kokha kuti akhale ndi Baibulo! Ndipo zitsanzo zoterozo zachulukitsidwa nthaŵi zingapo mpaka kudzafika kunthaŵi yathu ino. Kudzipereka kozama kumene Baibulo lasonkhezera mwa anthu, kufunitsitsa kuvutika modekha ndi kugonjera mosaŵiringula kuimfa zowopsa popanda kubwezera kwa owazunza awo, ndiko umboni wakuti Baibulo liri Mawu a Mulungu.—1 Petro 2:21.
14 Potsirizira pake, pambuyo pa kugalukira ulamuliro wa Tchalitchi cha Chikatolika kwa Chiprotestante m’zaka za zana lachi 16, Tchalitchi cha Roma Katolika chenichenicho chinakakamizika kutulutsa matembenuzidwe a Baibulo m’zinenero za ku Ulaya. Koma ngakhale panthaŵi imeneyo, Baibulo linagwirizanitsidwa kwambiri ndi Chiprotestante koposa ndi Chikatolika. Monga momwe wansembe wa Roma Katolika Edward J. Ciuba analembera kuti: “Munthu akayenera kuvomereza mowona mtima kuti chimodzi cha zotulukapo zowopsa kwambiri za Kusintha kwa Chiprotestante chinali kunyalanyazidwa kwa Baibulo pakati pa Akatolika okhulupirika. Pamene kuli kwakuti silinaiŵalidwe kotheratu, Baibulo linali bukhu lotsekedwa kwa Akatolika ochuluka.”9
Chisulizo Chachikulu Kwambiri
15, 16. Kodi nchifukwa ninji Chiprotestante sichiri chopanda liwongo ponena za chitsutso chake ku Baibulo?
15 Matchalitchi Achiprotestante saali opanda liwongo ponena za kutsutsa Baibulo. Pamene zaka zinalinkupita, ophunzira ena Achiprotestante anayambitsa mtundu wina wachiukiro pabukhulo: chiukiro cha anthu anzeru. Mkati mwa zaka za zana la 18 ndi 19, iwo anayambitsa njira yophunzirira Baibulo yotchedwa chisulizo chachikulu kwambiri. Osuliza apamwamba kwambiriwo anaphunzitsa kuti mbali yochuluka ya Baibulo inali itapangidwa ndi nthano ndi nthanthi. Ena anafikiradi pa kunena kuti Yesu sanakhaleko nkomwe. Mmalo mwa kutchedwa Mawu a Mulungu, Baibulo linatchedwa ndi akatswiri Achiprotestante ameneŵa kukhala mawu a anthu, ndipo analidi mawu ocholoŵanacholoŵana.
16 Pamene kuli kwakuti malingaliro opambanitsa ameneŵa sakukhulupiridwanso, chisulizo chachikulu kwambiri chikuphunzitsidwabe m’maseminale, ndipo sikwachilendo kumva atsogoleri achipembedzo Achiprotestante akukana poyera zigawo zazikulu za Baibulo. Motero, mtsogoleri wina wachipembedzo Wachianglikani anagwidwa mawu m’nyuzipepala ya ku Australia kukhala akunena kuti zochuluka zimene ziri m’Baibulo “nzolakwika. Ina ya mbiri yake njolakwika. Mfundo zina ziri mwachiwonekere zopotozedwa.” Kuganiza kumeneku ndiko chipatso cha chisulizo chachikulu kwambiri.
“Kuneneredwa Monyoza”
17, 18. Kodi ndimotani mmene khalidwe la Chikristu cha Dziko ladzetsera chitonzo pa Baibulo?
17 Komabe, mwinamwake, ndilo khalidwe la Chikristu cha Dziko limene lapanga chopinga chachikulu kopambana kukulandira kwa anthu Baibulo monga Mawu a Mulungu. Chikristu cha Dziko chimadzinenera kukhala chikutsatira Baibulo. Komabe, khalidwe lake ladzetsa chitonzo chachikulu pa Baibulo ndi padzina lenilenilo Mkristu. Monga momwe mtumwi Petro ananeneratu, njira ya chowonadi ‘yaneneredwa mwachipongwe.’—2 Petro 2:2.
18 Mwachitsanzo, pamene tchalitchi chinali kuletsa kutembenuzidwa kwa Baibulo, papa anali kumachirikiza zoyesayesa zazikulu za nkhondo yolimbana ndi Chisilamu ku Middle East. Zimeneyi zinafikira pa kutchedwa Nkhondo Zamtanda “zoyera,” koma panalibe chirichonse choyera ponena za izo. Yoyamba—yotchedwa “Nkhondo Yamtanda ya Anthu”—inasonyeza chimene chinalinkudza. Lisananyamuke kuchoka ku Ulaya, gulu la nkhondo losalamulirika, losonkhezeredwa ndi alaliki, linaukira Ayuda mu Jeremani, likumawapha m’tauni lirilonse. Chifukwa ninji? Wolemba mbiri Hans Eberhard Mayer akunena kuti: “Chigomeko chakuti Ayuda, monga adani a Kristu, anali oyenerera kulangidwa chinali chabe kuyesayesa kopanda mphamvu kwa kubisa cholinga chenicheni: umbombo.”10
19-21. Kodi ndimotani mmene Nkhondo ya Zaka Makumi Atatu, kudzanso zoyesayesa za amishonale a ku Ulaya ndi kufutukulidwa kwautsamunda, zatumikirira kudzetsa chitonzo pa Baibulo?
19 Kugaluka kwa Aprotestante m’zaka za zana la 16 kunachotsa muulamuliro Chikatolika cha Roma m’maiko ambiri a ku Ulaya. Chotulukapo chimodzi chinali Nkhondo ya Zaka Makumi Atatu (1618-48)—“imodzi ya nkhondo zowopsa kopambana m’mbiri ya ku Ulaya,” malinga ndi kunena kwa The Universal History of the World. Kodi choyambitsa chachikulu cha nkhondoyo nchiyani? “Udani wa Akatolika kwa Aprotestante, ndi wa Aprotestante kwa Akatolika.”11
20 Pofika panthaŵi ino, Chikristu cha Dziko chinali chitayamba kufutukuka kupyola ku Ulaya, kutengera kutsungula kwa “Chikristu” m’mbali zina za dziko lapansi. Kufutukuka kwa nkhondo kumeneku kunasonyezedwa ndi nkhanza ndi umbombo. Kumaiko onse a America, Asipanya olanda maikowo mwamsanga anawononga kutsungula kwa eni nthaka Achimereka. Bukhu lina la mbiri linati: “Kunena mwachisawawa, abwanamkubwa Achisipanya anawononga kutsungula kwa eni nthaka, popanda kusonyeza kwa ku Ulaya. Kulakalaka kwawo golidi ndiko kumene kunali cholinga chachikulu chimene chinachititsa kumka ku Dziko Latsopano”.12
21 Amishonale Achiprotesitante nawonso anatuluka kuchoka ku Ulaya kumka kumakontinenti ena. Chimodzi cha zotulukapo za ntchito yawo chinali kupititsidwa patsogolo kwa kufutukulidwa kwa utsamunda. Lingaliro lofala lerolino la kuyesayesa kwa amishonale Achiprotestante ndilo lakuti: “M’zochitika zambiri ntchito yaumishonale yagwiritsiridwa ntchito monga cholungamitsira kapena kuphimbira kulamulira anthu. Kugwirizana kwa pakati pa mishoni, maluso azopangapanga, ndi kulamulira maiko achilendo kuli kodziŵika bwino lomwe.”13
22. Kodi ndimotani mmene Chikristu cha Dziko chadzetsera chitonzo padzina Lachikristu mkati mwa zaka za zana la 20?
22 Kugwirizana kwambiri kwa pakati pa zipembedzo Zachikristu cha Dziko ndi boma kwapitirizabe kufikira m’tsiku lathu. Nkhondo ziŵiri zapitazo zinamenyedwa kwakukulukulu pakati pa mitundu “Yachikristu.” Atsogoleri achipembedzo a kumbali zonse ziŵiri analimbikitsa anyamata awo kumenya nkhondo ndi kuyesa kupha mdani—amene kaŵirikaŵiri anali wachipembedzo chimodzi. Monga momwe kunasonyezedwera m’bukhu lakuti If the Churches Want World Peace: “Ndithudi sikukumapereka thamo ku [matchalitchi] kuti dongosolo la nkhondo la lerolino lakula ndipo lachititsa kuvutika maganizo kwakukulu kopambana pakati pa maboma odzipereka kunjira Yachikristu.”14
Mawu a Mulungu Akalipobe
23. Kodi ndimotani mmene mbiri ya Chikristu cha Dziko imasonyezera kuti Baibulo liri Mawu a Mulungu?
23 Tikufotokoza mbiri yaitali imeneyi, yomvetsa chisoni Yachikristu cha Dziko kuti tigogomezere mfundo ziŵiri. Yoyamba, zochitika zoterozo ziri kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo. Kunanenedweratu kuti ambiri odzinenera kukhala Akristu akadzetsa chitonzo pa Baibulo ndi padzina Lachikristu, ndipo chenicheni chakuti zimenezo zachitika chikusonyeza Baibulo kukhala lowona. Komabe, sitiyenera kutaikiridwa ndi kapenyedwe ponena za chenicheni chakuti khalidwe la Chikristu cha Dziko silimaimira Chikristu chozikidwa pa Baibulo.
24. Kodi nchiyani chimene chimadziŵikitsa Akristu owona ndipo motero kutsutsa mwachiwonekere Chikristu cha Dziko kukhala chosakhala cha Chikristu?
24 Njira imene Akristu enieni angathe kuzindikiridwa nayo inafotokozedwa ndi Yesu iye mwini: “Mwa ichi onse adzadziŵa kuti muli akuphunzira anga, ngati muli ndi chikondi pakati panu.” (Yohane 13:35, NW) Ndiponso, Yesu anati: “Iwo saali mbali ya dziko, monga momwe ine sindiri mbali ya dziko.” (Yohane 17:16, NW) M’zochitika zonse ziŵirizo, Chikristu cha Dziko chimadzisonyeza chokha mowonekera bwino kukhala osati chikuimira Chikristu cha Baibulo. Chimadzinenera kukhala bwenzi la Baibulo, koma icho chakhala bwenzi lonyenga.
25. Kodi nchifukwa ninji Baibulo linapulumuka zisautso zake zonse kudzafika m’nthaŵi yathu?
25 Mfundo yachiŵiri ndiyo iyi: Polingalira chenicheni chakuti Chikristu cha Dziko chonse chathunthu chachita kwambiri mosemphana ndi zikondwerero Zabaibulo, kulidi kwapadera, kuti bukhulo lapitirizabe kukhalapo kufikira lerolino ndipo likuperekabe chiyambukiro chachikulu pamiyoyo ya anthu ambiri. Baibulo lapulumuka chitsutso chachikulu cha kulitembenuza, ziukiro za akatswiri achimakono, ndi khalidwe losakhala Lachikristu la bwenzi lake lonyenga, Chikristu cha Dziko. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Baibulo liri bukhu losafanana ndi bukhu lina lirilonse lolembedwa. Baibulo silingathe kufa. Ndilo Mawu a Mulungu, ndipo Baibulo lenilenilo limatiuza kuti: “Udzu umanyala, maluŵa amafota, koma mawu a Mulungu amakhalabe kosatha.”—Yesaya 40:8, The New English Bible.
[Mawu a M’munsi]
a Matembenuzidwe oŵerengeka kuloŵa m’zinenero za anthu a pamalopo anapangidwa. Koma iwo kaŵirikaŵiri anatulutsidwa movutikira m’zolembedwa zapamanja zolembedwa movuta kumvetsetsa ndipo ndithudi sizinali zooti nkugwiritsiridwa ntchito ndi onse.2
[Mawu Otsindika patsamba 34]
Matchalitchi aakulu Achiprotestante atenga phande m’chiukiro chachikulu cha anzeru pa Baibulo
[Chithunzi patsamba 26]
Mbiri ya Chikristu cha Dziko inayambadi pamene Constantine anapangitsa “Chikristu” cha m’tsiku lake kukhala chalamulo
[Zithunzi patsamba 29]
Papa Gregory VII ndi Innocent III anali otchuka m’nkhondo ya Tchalitchi cha Katolika ya kuletsa Baibulo kutembenuzidwira m’chinenero cha tsiku ndi tsiku cha anthu
[Chithunzi patsamba 33]
Khalidwe lochititsa manyazi la Chikristu cha Dziko lachititsa ambiri kukaikira kuti Baibulo liridi Mawu a Mulungu
[Chithunzi patsamba 35]
Mkati mwa nkhondo yoyamba yadziko, asilikali ankhondo Achirasha aŵa akuŵerama pamaso pa fano asananyamuke kupita kukapha “Akristu” anzawo